ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمهٔ چوایی * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: سوره نحل   آیه:

سوره نحل

أَتَىٰٓ أَمۡرُ ٱللَّهِ فَلَا تَسۡتَعۡجِلُوهُۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Lamulo la Allah lidzafika, (ndithu) choncho, musalifulumizitse; (ndipo khulupirirani kuti Iye ndi Allah) Woyera Wopatukana ndi mbiri zopunguka, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo.
تفسیرهای عربی:
يُنَزِّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ بِٱلرُّوحِ مِنۡ أَمۡرِهِۦ عَلَىٰ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦٓ أَنۡ أَنذِرُوٓاْ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱتَّقُونِ
Amatumiza angelo pansi pamodzi ndi chivumbulutso mwa lamulo Lake (Allah), kwa omwe wawafuna mwa akapolo Ake (powauza) kuti: “Achenjezeni (anthu zakuti): ‘Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha, choncho ndiopeni.”
تفسیرهای عربی:
خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۚ تَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi (osati mwakungoseweretsa chabe) ndipo watukuka kuzimene akumphatikiza nazo (ophatikiza Allah ndi mafano).
تفسیرهای عربی:
خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِن نُّطۡفَةٖ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٞ مُّبِينٞ
Adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna. Ha! kenaka iye (munthuyo) wakhala wotsutsana naye (Allah) woonekera.[247]
[247] Apa Allah akunenetsa kuti adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna wopanda pake. Koma munthu pambuyo pokwanira chilengedwe chake akukhala wotsutsana ndi Mlengi wake ndi kumchitira mwano modzitukumula chikhalirecho adalengedwa kuti akhale kapolo wa Allah, osati wopikisana naye.
تفسیرهای عربی:
وَٱلۡأَنۡعَٰمَ خَلَقَهَاۖ لَكُمۡ فِيهَا دِفۡءٞ وَمَنَٰفِعُ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ
Ndipo adalenga ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi) mwa izo mukupeza zofunda, ndi zothandiza (zina zambiri), ndipo zina mwa izo mumazidya.
تفسیرهای عربی:
وَلَكُمۡ فِيهَا جَمَالٌ حِينَ تُرِيحُونَ وَحِينَ تَسۡرَحُونَ
Ndipo mumakondwa ndi kunyadira chifukwa cha kukongola kwa izo mukamabwera nazo (kuchokera kubusa mimba zitakhuta), ndi popita nazo (kubusa zikuyenda mwandawala).
تفسیرهای عربی:
وَتَحۡمِلُ أَثۡقَالَكُمۡ إِلَىٰ بَلَدٖ لَّمۡ تَكُونُواْ بَٰلِغِيهِ إِلَّا بِشِقِّ ٱلۡأَنفُسِۚ إِنَّ رَبَّكُمۡ لَرَءُوفٞ رَّحِيمٞ
Ndipo zimasenza mitolo yanu (yolemera) kukafika nayo ku midzi yakutali komwe simumatha kukafikako popanda kuvutika kwambiri. Ndithu Mbuye wanu Ngodekha kwabasi, Ngwachisoni zedi.
تفسیرهای عربی:
وَٱلۡخَيۡلَ وَٱلۡبِغَالَ وَٱلۡحَمِيرَ لِتَرۡكَبُوهَا وَزِينَةٗۚ وَيَخۡلُقُ مَا لَا تَعۡلَمُونَ
(Adalenganso) akavalo, nyumbu ndi abulu kuti muzizikwera ndi kutinso zizikhala chokometsera chanu (cholowetsa chisangalalo m’mitima yanu); ndipo adzalenga (zokwera zina) zomwe simukuzidziwa.
تفسیرهای عربی:
وَعَلَى ٱللَّهِ قَصۡدُ ٱلسَّبِيلِ وَمِنۡهَا جَآئِرٞۚ وَلَوۡ شَآءَ لَهَدَىٰكُمۡ أَجۡمَعِينَ
Ndipo ndi udindo wa Allah kusonyeza njira yolungama (yomwe ingakufikitseni ku Munda wamtendere), koma zilipo njira zina zokhota (zomwe sizifikitsa ku choonadi). Ndipo Allah akadafuna, akadakuongolani nonsenu (mwa chifuniro chanu ndi mopanda chifuniro chanu. Koma Iye adakupatsani nzeru kuti musankhe nokha njira imene mufuna).
تفسیرهای عربی:
هُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗۖ لَّكُم مِّنۡهُ شَرَابٞ وَمِنۡهُ شَجَرٞ فِيهِ تُسِيمُونَ
Iye ndi Amene akukutsitsirani madzi kuchokera ku mitambo, madziwo mumamwa (pothetsa ludzu lanu), ndipo ndi madziwo mitengo imamera; mitengo yomwe mumadyetsera ziweto (zanu).
تفسیرهای عربی:
يُنۢبِتُ لَكُم بِهِ ٱلزَّرۡعَ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلنَّخِيلَ وَٱلۡأَعۡنَٰبَ وَمِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
Ndi madzi omwewo amakumeretserani mmera, (mitengo ya) mzitona, kanjedza, mphesa, ndi mitundu ina yonse ya zipatso. Ndithu kupezeka kwa zimenezi ndi chisonyezo (chosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu olingalira.[248]
[248] Ndithudi, m’kutsika kwa madzi kuchokera ku mitambo ndi kumeretsa zipatso, muli zisonyezo zoonekera poyera kukhoza kwa Allah ndi umodzi wake kwa anthu omwe amalingalira za zolengedwa Zake. Ndipo potero amakhulupilira Allah Kodi simukuona mbewu imodzi ikaikidwa m’nthaka ndi kupitapo nyengo yodziwika, imafunafuna potulukira ndi kung’amba nthaka ndi kukula kusanduka mtengo? Zonsezi nzododometsa kwa anthu olingalira.
تفسیرهای عربی:
وَسَخَّرَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ وَٱلنُّجُومُ مُسَخَّرَٰتُۢ بِأَمۡرِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
Ndipo chifukwa cha inu adagonjetsa usiku ndi usana; dzuwa ndi mwezi; (zonse zidalengedwa kuti zibwere ndi zokomera inu). Nazo nyenyezi zidagonjetsedwa mwa lamulo Lake. Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu anzeru.
تفسیرهای عربی:
وَمَا ذَرَأَ لَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُخۡتَلِفًا أَلۡوَٰنُهُۥٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَذَّكَّرُونَ
Ndiponso ndi zimene adakulengerani m’nthaka (zinthu zododornetsa monga nyama, mmera, miyala yamtengo wapatali, zamoyo ndi zopanda moyo), zautoto wosiyanasiyana ndi maonekedwe osiyanasiyana; ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa anthu olalikika.
تفسیرهای عربی:
وَهُوَ ٱلَّذِي سَخَّرَ ٱلۡبَحۡرَ لِتَأۡكُلُواْ مِنۡهُ لَحۡمٗا طَرِيّٗا وَتَسۡتَخۡرِجُواْ مِنۡهُ حِلۡيَةٗ تَلۡبَسُونَهَاۖ وَتَرَى ٱلۡفُلۡكَ مَوَاخِرَ فِيهِ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Ndipo Iye ndi Yemwe adagonjetsa nyanja kuti mudye nyama yamatumbi (ya) m’menemo (nsomba) ndikuti mutulutse m’menemo zodzikongoletsera zomwe mumavala; ndipo uona zombo zikuluzikulu zikung’amba (mafunde) m’menemo kuti mufunefune zabwino zake (njira ya malonda), ndi kuti muthokoze (Mbuye wanu Allah).
تفسیرهای عربی:
وَأَلۡقَىٰ فِي ٱلۡأَرۡضِ رَوَٰسِيَ أَن تَمِيدَ بِكُمۡ وَأَنۡهَٰرٗا وَسُبُلٗا لَّعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ
Ndipo adaika panthaka mapiri ataliatali kuti (nthaka) isagwedezeke nanu; ndipo (adaika) mitsinje ndi misewu kuti muongoke (potsata njira yeniyeni ndikukafika komwe mukufuna).[249]
[249] Allah adakhazikitsa mapiri ataliatali, olimba kuti nthaka isamagwedezeke pafupipafupi. Abu Suud adati: “Ndithudi nthaka idalengedwa ngati mpira ndikukhala yogwedezeka pazifukwa zochepa asanailengere mapiri monga momwe zimagwedezekera nyenyezi zinzake. koma pamene adailengera mapiri idakhazikika. Zoterezi ndi pachifukwa chakuti anthu akhazikike bwino.
تفسیرهای عربی:
وَعَلَٰمَٰتٖۚ وَبِٱلنَّجۡمِ هُمۡ يَهۡتَدُونَ
Ndipo (adaikanso) zizindikiro zina, ndiponso kupyolera m’nyenyezi, iwo amalondola njira.
تفسیرهای عربی:
أَفَمَن يَخۡلُقُ كَمَن لَّا يَخۡلُقُۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
Kodi Yemwe amalenga angalingane ndi omwe salenga? Kodi simungakumbukire (ndikudziwa kulakwa kwanu pomuyerekeza Allah ndi mafano)?
تفسیرهای عربی:
وَإِن تَعُدُّواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ لَا تُحۡصُوهَآۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَغَفُورٞ رَّحِيمٞ
Ngati mutayesera kuwerengera mtendere wa Allah simungathe kuuwerengera (wonse); ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا تُسِرُّونَ وَمَا تُعۡلِنُونَ
Ndipo Allah akuzidziwa zimene mukuzibisa, ndi zomwe mukuwonetsera.
تفسیرهای عربی:
وَٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَا يَخۡلُقُونَ شَيۡـٔٗا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ
Ndipo zomwe mukuzipembedza kusiya Allah, sizilenga chilichonse, ndipo izo nzolengedwa.
تفسیرهای عربی:
أَمۡوَٰتٌ غَيۡرُ أَحۡيَآءٖۖ وَمَا يَشۡعُرُونَ أَيَّانَ يُبۡعَثُونَ
Zakufa zopanda moyo; ndipo sizizindikira kuti nliti akufa adzaukitsidwa (m’manda mwawo).
تفسیرهای عربی:
إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۚ فَٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ قُلُوبُهُم مُّنكِرَةٞ وَهُم مُّسۡتَكۡبِرُونَ
Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi Yekha; koma amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, mitima yawo ikukana (kukhulupirira umodzi wa Allah), ndipo iwo akudzitukumula.
تفسیرهای عربی:
لَا جَرَمَ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُسۡتَكۡبِرِينَ
Palibe chikaiko, Allah akudziwa zomwe akubisa, ndi zomwe akuzilengeza. Ndithudi, Iye sakonda odzikuza.
تفسیرهای عربی:
وَإِذَا قِيلَ لَهُم مَّاذَآ أَنزَلَ رَبُّكُمۡ قَالُوٓاْ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Ndipo (osakhulupirira) akafunsidwa: “Kodi Mbuye wanu watumizanji (kwa Mneneri Muhammad {s.a.w})?” Akunena: “(Sadatumize chilichonse koma) nthano zabodza za anthu akale.”[250]
[250] Omasulira Qur’an akunena kuti, opembedza mafano amaima m’njira zolowera mu mzinda wa Makka ndi cholinga chopatula anthu kwa Mtumiki (s.a.w). Anthu odzachita Hajj akawafunsa kuti: “Kodi nchiyani chavumbulutsidwa kwa Muhammad?” Iwo amati: “Ndi nthano zabodza za anthu akale osati mawu a Allah.”
تفسیرهای عربی:
لِيَحۡمِلُوٓاْ أَوۡزَارَهُمۡ كَامِلَةٗ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَمِنۡ أَوۡزَارِ ٱلَّذِينَ يُضِلُّونَهُم بِغَيۡرِ عِلۡمٍۗ أَلَا سَآءَ مَا يَزِرُونَ
(Motero akuwasokeretsa anthu) kuti akasenze mitolo yawo (ya machimo) yokwanira pa tsiku la Qiyâma, ndiponso gawo lamitolo ya omwe akuwasokeretsa popanda kuzindikira (osokerawo). Tamverani! Ndi yoipa kwabasi mitolo yomwe azikaisenza!
تفسیرهای عربی:
قَدۡ مَكَرَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَأَتَى ٱللَّهُ بُنۡيَٰنَهُم مِّنَ ٱلۡقَوَاعِدِ فَخَرَّ عَلَيۡهِمُ ٱلسَّقۡفُ مِن فَوۡقِهِمۡ وَأَتَىٰهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِنۡ حَيۡثُ لَا يَشۡعُرُونَ
Adachita ndale omwe adalipo patsogolo pawo; choncho Allah adagumula maziko anyumba zawo. Ndipo madenga adawagwera pamwamba pawo; ndipo chilango chidawadzera kuchokera komwe sadali kukudziwa.
تفسیرهای عربی:
ثُمَّ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يُخۡزِيهِمۡ وَيَقُولُ أَيۡنَ شُرَكَآءِيَ ٱلَّذِينَ كُنتُمۡ تُشَٰٓقُّونَ فِيهِمۡۚ قَالَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ إِنَّ ٱلۡخِزۡيَ ٱلۡيَوۡمَ وَٱلسُّوٓءَ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ
Kenako tsiku la Qiyâma adzawayalutsa ndi kunena: “Ali kuti omwe mudali kundiphatikiza nawo, omwe chifukwa cha iwo mudali kukangana (ndi Mtumiki)?” Adzanena omwe apatsidwa nzeru: “Ndithu kuyaluka ndi tsoka loipa zili pa osakhulupirira lero.”
تفسیرهای عربی:
ٱلَّذِينَ تَتَوَفَّىٰهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ ظَالِمِيٓ أَنفُسِهِمۡۖ فَأَلۡقَوُاْ ٱلسَّلَمَ مَا كُنَّا نَعۡمَلُ مِن سُوٓءِۭۚ بَلَىٰٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Omwe angelo akutenga miyoyo yawo atadzichitira okha zoipa (ponyoza Allah). Choncho adzadzipereka (kwa angelowa, kuti atenge miyoyo yawo akunena:) “Sitidali kuchita choipa chilichonse.” (Angelo adzati:) “Zoona, palibe chikaiko, Allah akudziwa kwambiri zomwe munkachita.”
تفسیرهای عربی:
فَٱدۡخُلُوٓاْ أَبۡوَٰبَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ فَلَبِئۡسَ مَثۡوَى ٱلۡمُتَكَبِّرِينَ
“Choncho, lowani makomo a ku Jahannam; mukakhala m’menemo nthawi yaitali.” Taonani kuipitsitsa kwa malo a anthu odzikweza!
تفسیرهای عربی:
۞ وَقِيلَ لِلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ مَاذَآ أَنزَلَ رَبُّكُمۡۚ قَالُواْ خَيۡرٗاۗ لِّلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٞۚ وَلَدَارُ ٱلۡأٓخِرَةِ خَيۡرٞۚ وَلَنِعۡمَ دَارُ ٱلۡمُتَّقِينَ
Ndipo kukanenedwa kwa omwe akuopa Allah (kuti): “Kodi nchiyani watumiza Mbuye wanu?” Amati: “Zabwino.” Kwa omwe achita zabwino padziko ili lapansi, awapatsanso zabwino, ndipo Nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwambiri, ndipo taonani ubwino wa Nyumba ya oopa (Allah)!
تفسیرهای عربی:
جَنَّٰتُ عَدۡنٖ يَدۡخُلُونَهَا تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ لَهُمۡ فِيهَا مَا يَشَآءُونَۚ كَذَٰلِكَ يَجۡزِي ٱللَّهُ ٱلۡمُتَّقِينَ
Minda yamuyaya adzailowa, pansi pake padzakhala pakuyenda mitsinje (ndi patsogolo pake), chokhumba chilichonse akachipeza mmenemo (popanda kuchivutikira); umo ndi momwe Allah amawalipirira omuopa (iye).
تفسیرهای عربی:
ٱلَّذِينَ تَتَوَفَّىٰهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ طَيِّبِينَ يَقُولُونَ سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمُ ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Amene miyoyo yawo angelo amaitenga iwo ali abwino, uku akuwauza: “Mtendere uli pa inu, lowani ku Munda wamtendere chifukwa cha (zabwino) zija zomwe mudali kuzichita.”
تفسیرهای عربی:
هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّآ أَن تَأۡتِيَهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَوۡ يَأۡتِيَ أَمۡرُ رَبِّكَۚ كَذَٰلِكَ فَعَلَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ وَمَا ظَلَمَهُمُ ٱللَّهُ وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
Kodi akuyembekezera china, awa osakhulupirira, posakhala kuti angelo awadzere ndikuwaononga; kapena kuti liwadzere lamulo la Mbuye wako (lakuwalanga)? Momwemo ndi m’mene adachitiranso omwe adalipo patsogolo pawo. Koma Allah sadawachitire choipa koma adadzichitira okha choipa.
تفسیرهای عربی:
فَأَصَابَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا عَمِلُواْ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Choncho, zoipa za zomwe adachita zidawapeza, ndipo chilango chidawazinga pa zomwe ankazichita mwachipongwe.
تفسیرهای عربی:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ لَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا عَبَدۡنَا مِن دُونِهِۦ مِن شَيۡءٖ نَّحۡنُ وَلَآ ءَابَآؤُنَا وَلَا حَرَّمۡنَا مِن دُونِهِۦ مِن شَيۡءٖۚ كَذَٰلِكَ فَعَلَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ فَهَلۡ عَلَى ٱلرُّسُلِ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
Ndipo aja amapembedza mafano akuti: “Allah akadafuna, sitikadapembedza chilichonse kusiya Iye, ife ngakhale makolo athu; ndiponso palibe chomwe tikadachiyesa choletsedwa popanda lamulo Lake.” Momwemo ndimo adachitiranso aja omwe adalipo patsogolo pawo. Kodi atumiki ali ndi udindo winanso, osati kufikitsa uthenga woonekera (womveka?)
تفسیرهای عربی:
وَلَقَدۡ بَعَثۡنَا فِي كُلِّ أُمَّةٖ رَّسُولًا أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱجۡتَنِبُواْ ٱلطَّٰغُوتَۖ فَمِنۡهُم مَّنۡ هَدَى ٱللَّهُ وَمِنۡهُم مَّنۡ حَقَّتۡ عَلَيۡهِ ٱلضَّلَٰلَةُۚ فَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ
Ndipo ndithu ku mtundu uliwonse tidatumiza mtumiki (amene amawauza kuti): “Pembedzani Allah, ndi kumpewa (Iblis) woipa.” Choncho alipo ena mwa iwo omwe Allah adawaongola, ndipo alipo ena mwa iwo omwe kusokera kudatsimikizika pa iwo. Choncho yendani pa dziko ndikuyang’ana (kuti) kodi adali bwanji mathero a otsutsa.
تفسیرهای عربی:
إِن تَحۡرِصۡ عَلَىٰ هُدَىٰهُمۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَن يُضِلُّۖ وَمَا لَهُم مِّن نَّٰصِرِينَ
Ngati uwumilira kwambiri kuti uwaongole, komatu Allah saongola yemwe akusokeretsa (ena), ndipo sadzapeza wowathangata.
تفسیرهای عربی:
وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَا يَبۡعَثُ ٱللَّهُ مَن يَمُوتُۚ بَلَىٰ وَعۡدًا عَلَيۡهِ حَقّٗا وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo iwo adalumbilira m’dzina la Allah, kulumbilira kwawo kwamphamvu (kuti) Allah sadzaukitsa amene afa; nchotani (kuti asawaukitse?) Ili ndi lonjezo lokakamizika kwa Iye, (kuwaukitsa ndi kuwalipira); koma anthu ambiri sadziwa.
تفسیرهای عربی:
لِيُبَيِّنَ لَهُمُ ٱلَّذِي يَخۡتَلِفُونَ فِيهِ وَلِيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَنَّهُمۡ كَانُواْ كَٰذِبِينَ
(Adzawaukitsa) kuti awafotokozere za zomwe adali kusiyana ndi kuti amene sadakhulupirire adziwe kuti ndithu iwo adali abodza.
تفسیرهای عربی:
إِنَّمَا قَوۡلُنَا لِشَيۡءٍ إِذَآ أَرَدۡنَٰهُ أَن نَّقُولَ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ
Ndithu liwu Lathu pa chinthu chimene tikuchifuna kuti chichitike ndikuchiuza basi kuti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi.
تفسیرهای عربی:
وَٱلَّذِينَ هَاجَرُواْ فِي ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مَا ظُلِمُواْ لَنُبَوِّئَنَّهُمۡ فِي ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٗۖ وَلَأَجۡرُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
Ndipo omwe adasamuka chifukwa cha Allah (kusiya midzi yawo) pambuyo poponderezedwa (kumeneko,) ndithu tiwakhazika mwaubwino pa dziko lapansi; ndipo malipiro a tsiku la chimaliziro (omwe akuwayembekezera), ngakulu zedi, akadakhala akudziwa (awa oipa).
تفسیرهای عربی:
ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ
(Amene adzapeza zimenezi, ndi) omwe adapirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo.
تفسیرهای عربی:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ إِلَّا رِجَالٗا نُّوحِيٓ إِلَيۡهِمۡۖ فَسۡـَٔلُوٓاْ أَهۡلَ ٱلذِّكۡرِ إِن كُنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ
Ndipo patsogolo pako (aneneri) omwe tidawatuma adalinso amuna, omwe tidawavumbulutsira chivumbulutso. Choncho afunseni eni chikumbumtima (za m’mabuku a Allah akale) ngati inu simukudziwa.
تفسیرهای عربی:
بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَٱلزُّبُرِۗ وَأَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلذِّكۡرَ لِتُبَيِّنَ لِلنَّاسِ مَا نُزِّلَ إِلَيۡهِمۡ وَلَعَلَّهُمۡ يَتَفَكَّرُونَ
(Tidabwera) ndi zisonyezo zoonekera pamodzi ndi mabuku; ndipo takuvumbulutsira ulaliki kuti uwafotokozere anthu zomwe zavumbulutsidwa kwa iwo kuti aganizire.
تفسیرهای عربی:
أَفَأَمِنَ ٱلَّذِينَ مَكَرُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ أَن يَخۡسِفَ ٱللَّهُ بِهِمُ ٱلۡأَرۡضَ أَوۡ يَأۡتِيَهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِنۡ حَيۡثُ لَا يَشۡعُرُونَ
Kodi adziika pachitetezo, amene akuchita ndale zoipa, kuti Allah sangawakwilire ndi nthaka, kapena chilango kuwadzera kuchokera komwe sadali kukudziwa (sadali kukuyembekezera)?
تفسیرهای عربی:
أَوۡ يَأۡخُذَهُمۡ فِي تَقَلُّبِهِمۡ فَمَا هُم بِمُعۡجِزِينَ
Kapena (Allah) kuwalanga mkuyenda kwawo kwa uku ndi uko? Pomwe iwo sangathe kumulepheretsa Allah kuchita chomwe wafuna pa iwo?
تفسیرهای عربی:
أَوۡ يَأۡخُذَهُمۡ عَلَىٰ تَخَوُّفٖ فَإِنَّ رَبَّكُمۡ لَرَءُوفٞ رَّحِيمٌ
Kapena kuwalanga uku ali ndi mantha oyembekezera chilango (pakulanga m’modzim’modzi kufikira onse atatha)? Ndithu Mbuye wanu Ngodekha Ngwachisoni chosatha.
تفسیرهای عربی:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ إِلَىٰ مَا خَلَقَ ٱللَّهُ مِن شَيۡءٖ يَتَفَيَّؤُاْ ظِلَٰلُهُۥ عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَٱلشَّمَآئِلِ سُجَّدٗا لِّلَّهِ وَهُمۡ دَٰخِرُونَ
Kodi sadaone chinthu chilichonse (molingalira) m’zimene Allah adalenga zomwe zithuzi zake zimazungulira kudzanjadzanja ndi kumanzere, kulambira Allah uku zili zodzichepetsa kwa Iye? (Nanga iwo osakhulupirira akudzikweza chotani pamaso pa Allah?)
تفسیرهای عربی:
وَلِلَّهِۤ يَسۡجُدُۤ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ مِن دَآبَّةٖ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَهُمۡ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ
Ndipo zimalambira Allah zonse za kumwamba ndi zapansi, nyama ndi angelo; iwo sadzikuza (pa mapemphero).
تفسیرهای عربی:
يَخَافُونَ رَبَّهُم مِّن فَوۡقِهِمۡ وَيَفۡعَلُونَ مَا يُؤۡمَرُونَ۩
Amaopa Mbuye wawo Yemwe ali pamwamba pawo; ndipo amachita zokhazo zomwe alamulidwa.
تفسیرهای عربی:
۞ وَقَالَ ٱللَّهُ لَا تَتَّخِذُوٓاْ إِلَٰهَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِۖ إِنَّمَا هُوَ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞ فَإِيَّٰيَ فَٱرۡهَبُونِ
Ndipo Allah wanena: “Musadzipangire milungu ina iwiri. Ndithudi, Iye ndi Mulungu Mmodzi. Choncho opani Ine ndekha.”
تفسیرهای عربی:
وَلَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَهُ ٱلدِّينُ وَاصِبًاۚ أَفَغَيۡرَ ٱللَّهِ تَتَّقُونَ
Zonse zakumwamba ndi pansi nza Iye, ndipo kumumvera ndi kumugonjera nkwake nthawi zonse. Kodi muopa wina amene sali Allah?
تفسیرهای عربی:
وَمَا بِكُم مِّن نِّعۡمَةٖ فَمِنَ ٱللَّهِۖ ثُمَّ إِذَا مَسَّكُمُ ٱلضُّرُّ فَإِلَيۡهِ تَجۡـَٔرُونَ
Ndipo mtendere wonse umene muli nawo udachokera kwa Allah (koma inu simuthokoza), ndipo masautso akakukhudzani Iye ndi amene mumamulilira.
تفسیرهای عربی:
ثُمَّ إِذَا كَشَفَ ٱلضُّرَّ عَنكُمۡ إِذَا فَرِيقٞ مِّنكُم بِرَبِّهِمۡ يُشۡرِكُونَ
Koma akakuchotserani masautso, pompo gulu lina la mwa inu limamphatikiza Mbuye wake (ndi mafano).
تفسیرهای عربی:
لِيَكۡفُرُواْ بِمَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡۚ فَتَمَتَّعُواْ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ
Ncholinga choti akane mtendere umene tawapatsa, choncho sangalalani pang’ono, posachedwapa mudziwa (mapeto a zochita zanu).
تفسیرهای عربی:
وَيَجۡعَلُونَ لِمَا لَا يَعۡلَمُونَ نَصِيبٗا مِّمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡۗ تَٱللَّهِ لَتُسۡـَٔلُنَّ عَمَّا كُنتُمۡ تَفۡتَرُونَ
Ndipo gawo la zomwe tawapatsa akuliikira (milungu yawo yabodza) yomwe siizindikira chilichonse. Tallahi, (ndikulumbira Allah,) ndithudi, mudzafunsidwa pa zimene munkapeka.
تفسیرهای عربی:
وَيَجۡعَلُونَ لِلَّهِ ٱلۡبَنَٰتِ سُبۡحَٰنَهُۥ وَلَهُم مَّا يَشۡتَهُونَ
Ndipo (mwaumbuli) akumuikira Allah ana aakazi (ponena kuti adabereka ana aakazi) Subuhana! (Wayera Allah kuzimenezi!) Ndipo iwo (eni) amadzifunira amene amawakonda (omwe ndi ana achimuna)!
تفسیرهای عربی:
وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِٱلۡأُنثَىٰ ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدّٗا وَهُوَ كَظِيمٞ
Ndipo mmodzi wawo akauzidwa nkhani ya (kuti wabereka) mwana wamkazi nkhope yake imada, ndipo amadzala ndi madandaulo.
تفسیرهای عربی:
يَتَوَٰرَىٰ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ مِن سُوٓءِ مَا بُشِّرَ بِهِۦٓۚ أَيُمۡسِكُهُۥ عَلَىٰ هُونٍ أَمۡ يَدُسُّهُۥ فِي ٱلتُّرَابِۗ أَلَا سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ
Amadzibisa kwa anthu chifukwa chankhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira): Kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa anthu), kapena angomkwilira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo.[251]
[251] Ophatikiza Allah ndi mafano adali kuda ana aakazi. Kubala mwana wamkazi amachiona monga chochititsa manyazi pamaso pa anthu kotero kuti ena mwa iwo akawauza kuti mkazi wawo wabala mwana wamkazi, amakamkwilira mwanayo ali wamoyo chifukwa choopa kunyozedwa pamaso pa anthu, pomwe iwo amawayesa angelo ngati ana aakazi a Allah. Chimene amachida, amampachika nacho Allah, ndipo chomwe amachikonda amati ndicho chawochawo. Izi nzamwano, zomwe osakhulupilira adali kumuyankhulira Allah.
تفسیرهای عربی:
لِلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ مَثَلُ ٱلسَّوۡءِۖ وَلِلَّهِ ٱلۡمَثَلُ ٱلۡأَعۡلَىٰۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Kwa awo amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, ali ndi mbiri yoipa; koma Allah ali ndi mbiri zapamwamba; ndipo Iye Ngwanyonga, Ngwanzeru zakuya.
تفسیرهای عربی:
وَلَوۡ يُؤَاخِذُ ٱللَّهُ ٱلنَّاسَ بِظُلۡمِهِم مَّا تَرَكَ عَلَيۡهَا مِن دَآبَّةٖ وَلَٰكِن يُؤَخِّرُهُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗىۖ فَإِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ لَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ سَاعَةٗ وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ
Ndipo Allah akadakhala akulanga anthu (mwachangu) pa zolakwa zawo, sakadasiya ngakhale nyama imodzi pamwamba pa nthaka; koma akuwachedwetsera (chilangocho) mpaka panthawi yoikidwa; ndipo ikadzadza nthawi yawoyo, sangathe kuichedwetsa ngakhale ola limodzi; ndiponso sangathe kuifulumizitsa (ngakhale ola limodzi.)
تفسیرهای عربی:
وَيَجۡعَلُونَ لِلَّهِ مَا يَكۡرَهُونَۚ وَتَصِفُ أَلۡسِنَتُهُمُ ٱلۡكَذِبَ أَنَّ لَهُمُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ لَا جَرَمَ أَنَّ لَهُمُ ٱلنَّارَ وَأَنَّهُم مُّفۡرَطُونَ
Ndipo akumuikira Allah zimene (iwo) akuzida (omwe ndi ana aakazi pomati Allah adabala ana aakazi), ndipo malirime awo akunena bodza kuti iwo adzapeza zabwino (kwa Allah); palibe chikaiko, ndithu Moto ndi wawo, ndipo iwo adzasiidwa (mmenemo).
تفسیرهای عربی:
تَٱللَّهِ لَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰٓ أُمَمٖ مِّن قَبۡلِكَ فَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَهُوَ وَلِيُّهُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Pali Mulungu! Ndithudi tidatumiza (atumiki) kumitundu yomwe idalipo patsogolo pako, koma satana adawakometsera zochita zawo (zoipa ankaziona kuti nzabwino napitiriza kuzichita). Choncho iye (satana) ndi bwenzi wawo lero, (koma pa tsiku la chimaliziro, adzadana naye kwambiri), ndipo iwo adzapata chilango chowawa.
تفسیرهای عربی:
وَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ إِلَّا لِتُبَيِّنَ لَهُمُ ٱلَّذِي ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Ndipo sitidakutumizire buku (ili) koma kuti uwafotokozere zomwe akusiyana pa izo ndi kuti (likhale) chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira.
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَآۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَسۡمَعُونَ
Ndipo Allah watsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo akuipatsa moyo nthaka ndi madziwo (pomeretsa mbewu) pambuyo poti nthakayo idali yakufa; ndithu m’zimenezo muli chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah) kwa anthu amene amamva.
تفسیرهای عربی:
وَإِنَّ لَكُمۡ فِي ٱلۡأَنۡعَٰمِ لَعِبۡرَةٗۖ نُّسۡقِيكُم مِّمَّا فِي بُطُونِهِۦ مِنۢ بَيۡنِ فَرۡثٖ وَدَمٖ لَّبَنًا خَالِصٗا سَآئِغٗا لِّلشَّٰرِبِينَ
Palibe chikaiko, m’ziweto muli phunziro ndi lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwa izo, (zomwe zimatuluka) pakati pa ndowe ndi magazi, (omwe ndi) mkaka woyera, wabwino wokoma kwa oumwa.
تفسیرهای عربی:
وَمِن ثَمَرَٰتِ ٱلنَّخِيلِ وَٱلۡأَعۡنَٰبِ تَتَّخِذُونَ مِنۡهُ سَكَرٗا وَرِزۡقًا حَسَنًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
Ndipo kuchokera ku zipatso za tende ndi mphesa, mumakonza zakumwa zoledzeretsa (zomwe nzoletsedwa) ndikupezanso rizq labwino (m’zipatsozo); ndithudi m’zimenezo muli lingaliro kwa anthu oganiza mwanzeru.
تفسیرهای عربی:
وَأَوۡحَىٰ رَبُّكَ إِلَى ٱلنَّحۡلِ أَنِ ٱتَّخِذِي مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتٗا وَمِنَ ٱلشَّجَرِ وَمِمَّا يَعۡرِشُونَ
Ndipo Mbuye wako adaizindikiritsa njuchi kuti: “Dzikonzere nyumba m’mapiri, m’mitengo, ndi (m’ming’oma) imene (anthu) amakonza.”
تفسیرهای عربی:
ثُمَّ كُلِي مِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِ فَٱسۡلُكِي سُبُلَ رَبِّكِ ذُلُلٗاۚ يَخۡرُجُ مِنۢ بُطُونِهَا شَرَابٞ مُّخۡتَلِفٌ أَلۡوَٰنُهُۥ فِيهِ شِفَآءٞ لِّلنَّاسِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
“Tsono idya zipatso zamtundu uliwonse ndikuyenda m’njira za Mbuye wako zimene wazifewetsa (kuziyenda).” Chimatuluka m’mimba mwake chakumwa cha utoto wosiyanasiyana (uchi), mwa icho muli kuchilitsa kwa anthu (kumatenda ochuluka), ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu oganiza (zinthu) mwakuya.
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ خَلَقَكُمۡ ثُمَّ يَتَوَفَّىٰكُمۡۚ وَمِنكُم مَّن يُرَدُّ إِلَىٰٓ أَرۡذَلِ ٱلۡعُمُرِ لِكَيۡ لَا يَعۡلَمَ بَعۡدَ عِلۡمٖ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٞ قَدِيرٞ
Ndipo Allah adakulengani, kenako akukupatsani imfa (nthawi ya moyo wanu ikatha); ndipo mwa inu alipo ena amene akubwezedwa ku moyo wonyozeka (waukalamba wogwa nkumina) kotero kuti asadziwe kanthu pambuyo pakudziwa (zambiri); ndithudi Allah Ngodziwa kwambiri Wokhoza (chilichonse chimene wafuna kuti chichitike).
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ فَضَّلَ بَعۡضَكُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ فِي ٱلرِّزۡقِۚ فَمَا ٱلَّذِينَ فُضِّلُواْ بِرَآدِّي رِزۡقِهِمۡ عَلَىٰ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَهُمۡ فِيهِ سَوَآءٌۚ أَفَبِنِعۡمَةِ ٱللَّهِ يَجۡحَدُونَ
Ndipo Allah wapereka zopereka Zake mochuluka kwa ena kuposa ena; ndipo amene apatsidwa mochulukawo sangagawire zopatsidwa zawo omwe manja awo adzanjadzanja apeza (akapolo awo) kuti akhale ofanana pa zopatsidwazo, (nanga bwanji inu mukuti Allah ngofanana ndi akapolo Ake pomwe inu simufuna kufanana ndi akapolo anu?) Nanga kodi mtendere wa Allah akuukana?
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّنۡ أَنفُسِكُمۡ أَزۡوَٰجٗا وَجَعَلَ لَكُم مِّنۡ أَزۡوَٰجِكُم بَنِينَ وَحَفَدَةٗ وَرَزَقَكُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِۚ أَفَبِٱلۡبَٰطِلِ يُؤۡمِنُونَ وَبِنِعۡمَتِ ٱللَّهِ هُمۡ يَكۡفُرُونَ
Ndiponso Allah adakulengerani akazi a mtundu wanu, ndipo adakupangirani ana ndi zidzukulu kuchokera mwa akazi anuwo; ndipo adakupatsani zinthu zabwinozabwino, kodi akukhulupirira zachabe, ndi kuchikana chisomo cha Allah?
تفسیرهای عربی:
وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَمۡلِكُ لَهُمۡ رِزۡقٗا مِّنَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ شَيۡـٔٗا وَلَا يَسۡتَطِيعُونَ
Ndipo akumusiya Allah ndikupembedza zomwe sizingawapezere zopatsa ngakhale pang’ono, zochokera kumwamba ndi pansi ndipo sizikhoza chilichonse.
تفسیرهای عربی:
فَلَا تَضۡرِبُواْ لِلَّهِ ٱلۡأَمۡثَالَۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ وَأَنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ
Choncho, musaponyere mafanizo Allah. Ndithudi Allah akudziwa, pomwe inu simudziwa (chinsinsi cha zinthu.)
تفسیرهای عربی:
۞ ضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلًا عَبۡدٗا مَّمۡلُوكٗا لَّا يَقۡدِرُ عَلَىٰ شَيۡءٖ وَمَن رَّزَقۡنَٰهُ مِنَّا رِزۡقًا حَسَنٗا فَهُوَ يُنفِقُ مِنۡهُ سِرّٗا وَجَهۡرًاۖ هَلۡ يَسۡتَوُۥنَۚ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Allah akuponya fanizo la (anthu awiri: Wina ndi) kapolo wopatidwa (wokhala pansi pa ulamuliro wa munthu wina); yemwe alibe mphamvu pa chilichonse; ndi (munthu) yemwe tampatsa zabwino zochokera kwa Ife, ndipo iye nkupereka rizqlo mobisa ndi moonekera; kodi angafanane (awiriwa? Nanga bwanji mukufananitsa Allah ndi mafano?) Kuyamikidwa konse nkwa Allah. Koma ambiri aiwo sadziwa (kuyamika Allah).
تفسیرهای عربی:
وَضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلٗا رَّجُلَيۡنِ أَحَدُهُمَآ أَبۡكَمُ لَا يَقۡدِرُ عَلَىٰ شَيۡءٖ وَهُوَ كَلٌّ عَلَىٰ مَوۡلَىٰهُ أَيۡنَمَا يُوَجِّههُّ لَا يَأۡتِ بِخَيۡرٍ هَلۡ يَسۡتَوِي هُوَ وَمَن يَأۡمُرُ بِٱلۡعَدۡلِ وَهُوَ عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Ndipo Allah waponyanso fanizo la anthu (ena) awiri: Mmodzi ndi bubu (wosatha kuyankhula), alibe mphamvu pa chilichonse; ndipo iye ndi mtolo wolemetsa chabe bwana wake; kulikonse kumene wamulunjikitsa, sabwerako ndi chabwino (chifukwa cha umbutuma wake). Kodi iye angafanane ndi yemwe akulamula mwa chilungamo, yemwenso ali pa njira yolunjika?
تفسیرهای عربی:
وَلِلَّهِ غَيۡبُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَآ أَمۡرُ ٱلسَّاعَةِ إِلَّا كَلَمۡحِ ٱلۡبَصَرِ أَوۡ هُوَ أَقۡرَبُۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Ndipo chinsinsi cha (za) kumwamba ndi (za) pansi ncha Allah Yekha, (Iye ndiye amene akudziwa zochitika m’menemo, osati wina wake). Ndipo kuchitika kwa Qiyâma kuli ngati kuphetira kwa diso, kapena kufulumilirapo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ أَخۡرَجَكُم مِّنۢ بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ شَيۡـٔٗا وَجَعَلَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Ndipo Allah adakutulutsani m’mimba mwa amayi anu pomwe simudali kudziwa chilichonse; ndipo adakupatsani kumva, kuona ndi mitima kuti muthokoze.
تفسیرهای عربی:
أَلَمۡ يَرَوۡاْ إِلَى ٱلطَّيۡرِ مُسَخَّرَٰتٖ فِي جَوِّ ٱلسَّمَآءِ مَا يُمۡسِكُهُنَّ إِلَّا ٱللَّهُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Kodi saona mbalame mu mlengalenga zikugonjera (Allah)? Palibe amene akuzigwira (kuti zisagwe) koma Allah Yekha. Ndithudi m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira.
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّنۢ بُيُوتِكُمۡ سَكَنٗا وَجَعَلَ لَكُم مِّن جُلُودِ ٱلۡأَنۡعَٰمِ بُيُوتٗا تَسۡتَخِفُّونَهَا يَوۡمَ ظَعۡنِكُمۡ وَيَوۡمَ إِقَامَتِكُمۡ وَمِنۡ أَصۡوَافِهَا وَأَوۡبَارِهَا وَأَشۡعَارِهَآ أَثَٰثٗا وَمَتَٰعًا إِلَىٰ حِينٖ
Ndipo Allah adakuikirani nyumba zanu kuti zikhale mokhala (mwanu), ndiponso adakupangirani zikopa za ziweto (kukhala zotheka kuzikonza) kukhala nyumba, zomwe mumaziona kuti nzopepuka kuzitenga panthawi Ya ulendo wanu ndi panthawi ya kukhazikika kwanu (pamalo); ndipo kuchokera ku bweya wake wautaliutali ndi bweya wake wa manyunyu (ung’onoung’ono), ndi tsitsi lake (la ziwetozo,) mumakonza ziwiya (zovala) zosangalatsa, kwa kanthawi.
تفسیرهای عربی:
وَٱللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّمَّا خَلَقَ ظِلَٰلٗا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡجِبَالِ أَكۡنَٰنٗا وَجَعَلَ لَكُمۡ سَرَٰبِيلَ تَقِيكُمُ ٱلۡحَرَّ وَسَرَٰبِيلَ تَقِيكُم بَأۡسَكُمۡۚ كَذَٰلِكَ يُتِمُّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُسۡلِمُونَ
Ndipo mwa zina zomwe Allah adapanga, adakupangirani zodzetsa mthunzi; ndipo adakupangirani mokhala kumapiri (monga mapanga akuluakulu). Adakupangiraninso nsalu (zathonje ndi ubweya) zokutetezani ku kutentha (ndi kuzizira), ndiponso (adakupangirani) zovala (za chitsulo) zokutetezani pankhondo zanu. Umo ndi momwe akukukwaniritsirani chisomo Chake kuti mugonjere (Iye).
تفسیرهای عربی:
فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَإِنَّمَا عَلَيۡكَ ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
Koma ngati anyoza, basi palibe udindo wina pa iwe koma kufikitsa uthenga womveka (popanda kubisapo kalikonse).
تفسیرهای عربی:
يَعۡرِفُونَ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ ثُمَّ يُنكِرُونَهَا وَأَكۡثَرُهُمُ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Akuchidziwa chisomo cha Allah; koma akuchikana, ndipo ambiri a iwo ngosakhulupirira.
تفسیرهای عربی:
وَيَوۡمَ نَبۡعَثُ مِن كُلِّ أُمَّةٖ شَهِيدٗا ثُمَّ لَا يُؤۡذَنُ لِلَّذِينَ كَفَرُواْ وَلَا هُمۡ يُسۡتَعۡتَبُونَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse; kenako sikudzaloledwa, kwa amene sadakhulupirire, (kupereka madandaulo) ndipo iwo sadzauzidwa kuti afunefune chiyanjo cha Allah (koma chilango basi).
تفسیرهای عربی:
وَإِذَا رَءَا ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ ٱلۡعَذَابَ فَلَا يُخَفَّفُ عَنۡهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ
Ndipo amene achita zoipa akadzachiona chilango (ndikuyamba kudandaula ndi kulira), sichidzachepetsedwa kwa iwo (chilangocho), ndipo sadzapatsidwa mwayi wina.
تفسیرهای عربی:
وَإِذَا رَءَا ٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ شُرَكَآءَهُمۡ قَالُواْ رَبَّنَا هَٰٓؤُلَآءِ شُرَكَآؤُنَا ٱلَّذِينَ كُنَّا نَدۡعُواْ مِن دُونِكَۖ فَأَلۡقَوۡاْ إِلَيۡهِمُ ٱلۡقَوۡلَ إِنَّكُمۡ لَكَٰذِبُونَ
Ndipo amene ankam’phatikiza Allah akadzawaona aphatikizi awowo adzati: “Mbuye wathu! Awa ndiaphatikizi athu omwe tidali kuwapembedza m’malo mwa Inu.” Ndipo (aphatikiziwo akadzamva mawu awa) adzawaponyera mawu awo (nkunena kuti): “Ndithu inu ndi abodza.”
تفسیرهای عربی:
وَأَلۡقَوۡاْ إِلَى ٱللَّهِ يَوۡمَئِذٍ ٱلسَّلَمَۖ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Ndipo tsiku limenelo onse adzadzitula kwa Allah; ndipo zidzawataika zomwe adali kuzipeka.
تفسیرهای عربی:
ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ زِدۡنَٰهُمۡ عَذَابٗا فَوۡقَ ٱلۡعَذَابِ بِمَا كَانُواْ يُفۡسِدُونَ
Tsono amene sadakhulupirire ndi kumaletsa anthu kunjira ya Allah tidzawaonjezera chilango pamwamba pa chilango chifukwa chakuononga kwawo.
تفسیرهای عربی:
وَيَوۡمَ نَبۡعَثُ فِي كُلِّ أُمَّةٖ شَهِيدًا عَلَيۡهِم مِّنۡ أَنفُسِهِمۡۖ وَجِئۡنَا بِكَ شَهِيدًا عَلَىٰ هَٰٓؤُلَآءِۚ وَنَزَّلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ تِبۡيَٰنٗا لِّكُلِّ شَيۡءٖ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُسۡلِمِينَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse zochokera mwa iwo omwe adzawachitira umboni (pa zomwe zinkachitika ndi iwo); ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni pa awa (anthu ako); ndiponso takuvumbulutsira buku ili lomwe likufotokoza za chinthu chilichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere ndiponso ndinkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Allah).
تفسیرهای عربی:
۞ إِنَّ ٱللَّهَ يَأۡمُرُ بِٱلۡعَدۡلِ وَٱلۡإِحۡسَٰنِ وَإِيتَآيِٕ ذِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَيَنۡهَىٰ عَنِ ٱلۡفَحۡشَآءِ وَٱلۡمُنكَرِ وَٱلۡبَغۡيِۚ يَعِظُكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ
Ndithudi, Allah akulamula (kuchita) chilungamo, ndikuchita zabwino, ndi kupatsa achinansi, ndipo akuletsa zauve ndi zoipa ndi kupyola malire; akukulangizani kuti muzindikire ndi kukumbukira.
تفسیرهای عربی:
وَأَوۡفُواْ بِعَهۡدِ ٱللَّهِ إِذَا عَٰهَدتُّمۡ وَلَا تَنقُضُواْ ٱلۡأَيۡمَٰنَ بَعۡدَ تَوۡكِيدِهَا وَقَدۡ جَعَلۡتُمُ ٱللَّهَ عَلَيۡكُمۡ كَفِيلًاۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا تَفۡعَلُونَ
Ndipo kwaniritsani lonjezo (limene mukupereka mdzina) la Allah pamene mulonjeza, ndipo musaswe malonjezowo pambuyo pakuwalimbikitsa; pomwe mwasankha Allah kukhala mboni yanu; ndithu Allah akudziwa (zonse) zimene mukuchita.
تفسیرهای عربی:
وَلَا تَكُونُواْ كَٱلَّتِي نَقَضَتۡ غَزۡلَهَا مِنۢ بَعۡدِ قُوَّةٍ أَنكَٰثٗا تَتَّخِذُونَ أَيۡمَٰنَكُمۡ دَخَلَۢا بَيۡنَكُمۡ أَن تَكُونَ أُمَّةٌ هِيَ أَرۡبَىٰ مِنۡ أُمَّةٍۚ إِنَّمَا يَبۡلُوكُمُ ٱللَّهُ بِهِۦۚ وَلَيُبَيِّنَنَّ لَكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ مَا كُنتُمۡ فِيهِ تَخۡتَلِفُونَ
Ndipo musakhale monga mkazi yemwe adakhulula ulusi wake pambuyo pouluka mwamphamvu, mukukuchita kulumbira kwanu pakati panu kukhala kwa chinyengo, chifukwa chakuti gulu la mtundu wina nlochuluka kwambiri kuposa gulu la mtundu wina (powasiya omwe mudalonjezana nawo chifukwa chakuwaona kuchepa, ndi kukagwirizana ndi omwe simudalonjezane nawo chifukwa chakuwaona kuchuluka); ndithu Allah akukuyesani mayeso pa njira yotere; ndipo ndithu pa tsiku la Qiyâma adzakufotokozerani za zomwe mudali kusiyana.
تفسیرهای عربی:
وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَعَلَكُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَلَٰكِن يُضِلُّ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَلَتُسۡـَٔلُنَّ عَمَّا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo Allah akadafuna, ndithu akadakuchitani kukhala gulu limodzi, (nonsenu mukadamumvera monga momwe adawachitira angelo, koma adakupatsani ufulu kuti muchite chimene mufuna); komatu amamulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo amamuongola wamfuna; ndipo, ndithu mudzafunsidwa pa zomwe munkachita.
تفسیرهای عربی:
وَلَا تَتَّخِذُوٓاْ أَيۡمَٰنَكُمۡ دَخَلَۢا بَيۡنَكُمۡ فَتَزِلَّ قَدَمُۢ بَعۡدَ ثُبُوتِهَا وَتَذُوقُواْ ٱلسُّوٓءَ بِمَا صَدَدتُّمۡ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَلَكُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٞ
Ndipo musakuchite kulumbira kwanu kukhala njira yonyengelerana pakati panu, kuopera kuti mwendo ungatelere (pa njira yolungama nkukagwera ku Moto) pambuyo pokhazikika mwendowo (pa njirapo) ndi kukazilawa zoipa chifukwa chakutsekereza kwanu (anthu) ku njira ya Allah, ndipo nkupeza chilango chachikulu (tsiku lachimaliziro).
تفسیرهای عربی:
وَلَا تَشۡتَرُواْ بِعَهۡدِ ٱللَّهِ ثَمَنٗا قَلِيلًاۚ إِنَّمَا عِندَ ٱللَّهِ هُوَ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Ndipo musagulitse mapangano a Allah ndi mtengo wochepa (wa zomwe mukupeza pano pa dziko lapansi). Chimene chili kwa Allah, ndicho chabwino kwa inu ngati mukudziwa.
تفسیرهای عربی:
مَا عِندَكُمۡ يَنفَدُ وَمَا عِندَ ٱللَّهِ بَاقٖۗ وَلَنَجۡزِيَنَّ ٱلَّذِينَ صَبَرُوٓاْ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Zomwe mulinazo nzakutha ndipo zili kwa Allah ndizo zosatha. Ndithudi Ife tidzawapatsa malipiro (aakulu zedi) amene adapirira oposera zabwino zimene ankachita.
تفسیرهای عربی:
مَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا مِّن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَلَنُحۡيِيَنَّهُۥ حَيَوٰةٗ طَيِّبَةٗۖ وَلَنَجۡزِيَنَّهُمۡ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali wokhulupirira timkhazika ndi moyo wabwino (pano pa dziko, ndi tsiku la Qiyâma) tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe ankachita.
تفسیرهای عربی:
فَإِذَا قَرَأۡتَ ٱلۡقُرۡءَانَ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ ٱلرَّجِيمِ
Ndipo ukafuna kuwerenga Qur’an dzitchinjirize ndi Allah kwa satana wopirikitsidwa (ponena kuti Awudhu Billahi mina Shaitwani Rajim).
تفسیرهای عربی:
إِنَّهُۥ لَيۡسَ لَهُۥ سُلۡطَٰنٌ عَلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ
Ndithu iye (satana) alibe mphamvu pa amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo.
تفسیرهای عربی:
إِنَّمَا سُلۡطَٰنُهُۥ عَلَى ٱلَّذِينَ يَتَوَلَّوۡنَهُۥ وَٱلَّذِينَ هُم بِهِۦ مُشۡرِكُونَ
Ndithudi mphamvu zake zili pa amene akumusankha (amulola) kukhala bwenzi lawo (mlangizi wawo) ndiponso ndi omwe akumphatikiza iye (ndi Allah).
تفسیرهای عربی:
وَإِذَا بَدَّلۡنَآ ءَايَةٗ مَّكَانَ ءَايَةٖ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُنَزِّلُ قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مُفۡتَرِۭۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo tikasintha Ayah (ndime) ndikubwera ndi Ina pamalopo, pomwe Allah akudziwa zimene akuvumbulutsa, akunena: “Ndithu iwe ndiwe wopeka.” Koma ambiri a iwo sadziwa (chilichonse).
تفسیرهای عربی:
قُلۡ نَزَّلَهُۥ رُوحُ ٱلۡقُدُسِ مِن رَّبِّكَ بِٱلۡحَقِّ لِيُثَبِّتَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَهُدٗى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُسۡلِمِينَ
Nena: “Mzimu woyera (Gabriel) waitsitsa (Qur’an) kuchokera kwa Mbuye wako mwachoonadi kuti awalimbikitse nayo amene akhulupirira ndi kuti ikhale chiongoko ndi nkhani yabwino kwa amene alowa m’Chisilamu (amene agonjera Allah).
تفسیرهای عربی:
وَلَقَدۡ نَعۡلَمُ أَنَّهُمۡ يَقُولُونَ إِنَّمَا يُعَلِّمُهُۥ بَشَرٞۗ لِّسَانُ ٱلَّذِي يُلۡحِدُونَ إِلَيۡهِ أَعۡجَمِيّٞ وَهَٰذَا لِسَانٌ عَرَبِيّٞ مُّبِينٌ
Ndithu tikudziwa kuti iwo akunena: “Pali munthu amene akumphunzitsa.” (Koma) chiyankhulo cha amene akumganizirayo nchachilendo, ndipo ichi (chiyankhulo cha Qur’an) ndi chiyankhulo cha Chiarabu chomveka.
تفسیرهای عربی:
إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ لَا يَهۡدِيهِمُ ٱللَّهُ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٌ
Ndithudi amene sakhulupirira Ayah (ndime) za Allah, Allah sawaongolera (kunjira ya choonadi), choncho adzapeza chilango chowawa.
تفسیرهای عربی:
إِنَّمَا يَفۡتَرِي ٱلۡكَذِبَ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡكَٰذِبُونَ
Ndithudi amene sakhulupirira Ayah (ndime) za Allah ndi amene amapeka bodza (ndi kumalifalitsa kwa anthu) ndipo iwowo ndiwo onama.
تفسیرهای عربی:
مَن كَفَرَ بِٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ إِيمَٰنِهِۦٓ إِلَّا مَنۡ أُكۡرِهَ وَقَلۡبُهُۥ مُطۡمَئِنُّۢ بِٱلۡإِيمَٰنِ وَلَٰكِن مَّن شَرَحَ بِٱلۡكُفۡرِ صَدۡرٗا فَعَلَيۡهِمۡ غَضَبٞ مِّنَ ٱللَّهِ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٞ
Amene akukana Allah, pambuyo pomukhulupirira, (chilango chachikulu chikumuyembekezera), kupatula yemwe adakakamizidwa, uku mtima wake utakhazikika pa chikhulupiliro; koma amene akutsekulira mtima wake kusakhulupirira, mkwiyo wa Allah uli pa iwo (ndipo anthu otere) adzapata chilango chachikulu.[252]
[252] Omasulira Qur’an akunena kuti ndime iyi idatsika chifukwa cha Ammar Bun Yasir. Opembedza mafano adamgwira ndi kumuvutitsa zedi kufikira iye adawapatsa chomwe iwo ankafuna kwa iye momkakamiza kutero. Anthu adati: “Ndithudi, Ammar watuluka m’Chisilamu.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Ndithudi, Ammar ngodzaza ndi chikhulupiliro kuyambira kumutu mpaka kumapazi. Chikhulupiliro chasakanikirana ndi minofu ndi magazi ake.” Zitatero Ammar adabwera kwa Mtumiki (s.a.w) uku akulira. Mtumiki (s.a.w) adati kwa iye: “Kodi ukupeza bwanji mtima wako?” Iye adati: “Ngokhazikika pa chikhulupiliro.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Ngati abwereranso iwenso bwerezanso zimene wanenazo.”
تفسیرهای عربی:
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمُ ٱسۡتَحَبُّواْ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا عَلَى ٱلۡأٓخِرَةِ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakonda moyo wa dziko lapansi kwambiri kuposa wa pambuyo pa imfa; ndi kutinso Allah saongola anthu osakhulupirira.
تفسیرهای عربی:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ طَبَعَ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ وَسَمۡعِهِمۡ وَأَبۡصَٰرِهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡغَٰفِلُونَ
Iwo ndi omwe Allah adawadinda m’mitima mwawo, m’makutu mwawo, ndi m’maso mwawo (chifukwa cha kusimbwa kwawo). Ndipo iwo ngonyalanyaza (malamulo a Allah) kwambiri.
تفسیرهای عربی:
لَا جَرَمَ أَنَّهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
Palibe chikaiko chakuti iwo ngotaika kwambiri pa tsiku la chimaliziro.
تفسیرهای عربی:
ثُمَّ إِنَّ رَبَّكَ لِلَّذِينَ هَاجَرُواْ مِنۢ بَعۡدِ مَا فُتِنُواْ ثُمَّ جَٰهَدُواْ وَصَبَرُوٓاْ إِنَّ رَبَّكَ مِنۢ بَعۡدِهَا لَغَفُورٞ رَّحِيمٞ
Ndithudi kenako Mbuye wako, kwa amene adasamuka pambuyo pakusautsidwa (kufikira adanena zosayenera) komanso nkuchita Jihâd ndikupirira (chifukwa cha chipembedzo), ndithu Mbuye wako pambuyo pa zimenezo, Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosantha.
تفسیرهای عربی:
۞ يَوۡمَ تَأۡتِي كُلُّ نَفۡسٖ تُجَٰدِلُ عَن نَّفۡسِهَا وَتُوَفَّىٰ كُلُّ نَفۡسٖ مَّا عَمِلَتۡ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
(Akumbutse za) tsiku lomwe mzimu uliwonse udzadza ukudziteteza wokha (wosalabadira za mwana wake, mkazi wake ndi abale ake), ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa molingana ndi zochita zake zimene unkachita, ndipo iwo sadzachitidwa chinyengo (pochepetsedwa mphoto yawo yoti alandire.)
تفسیرهای عربی:
وَضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلٗا قَرۡيَةٗ كَانَتۡ ءَامِنَةٗ مُّطۡمَئِنَّةٗ يَأۡتِيهَا رِزۡقُهَا رَغَدٗا مِّن كُلِّ مَكَانٖ فَكَفَرَتۡ بِأَنۡعُمِ ٱللَّهِ فَأَذَٰقَهَا ٱللَّهُ لِبَاسَ ٱلۡجُوعِ وَٱلۡخَوۡفِ بِمَا كَانُواْ يَصۡنَعُونَ
Ndipo Allah waponya fanizo lamudzi womwe udakhala mwa mtendere mokhazikika, rizq lake (madalitso) linkaudzera mochuluka kuchokera malo aliwonse; koma (mudziwo) udakana mtendere wa Allah (pakusathokoza); choncho Allah adaulawitsa chovala cha njala ndi mantha chifukwa cha (zoipa) zomwe (anthu ake) adali kuchita.
تفسیرهای عربی:
وَلَقَدۡ جَآءَهُمۡ رَسُولٞ مِّنۡهُمۡ فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَهُمُ ٱلۡعَذَابُ وَهُمۡ ظَٰلِمُونَ
Ndipo adawadzera mtumiki wochokera mwa iwo, koma adamtsutsa; choncho chilango chidawafika uku ali odzichitira okha zoipa.
تفسیرهای عربی:
فَكُلُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ حَلَٰلٗا طَيِّبٗا وَٱشۡكُرُواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ إِيَّاهُ تَعۡبُدُونَ
Choncho idyani zimene Allah wakupatsani zomwe zili zahalali, zabwino; ndipo yamikani mtendere wa Allah ngatidi mukupembedza Iye.
تفسیرهای عربی:
إِنَّمَا حَرَّمَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡمَيۡتَةَ وَٱلدَّمَ وَلَحۡمَ ٱلۡخِنزِيرِ وَمَآ أُهِلَّ لِغَيۡرِ ٱللَّهِ بِهِۦۖ فَمَنِ ٱضۡطُرَّ غَيۡرَ بَاغٖ وَلَا عَادٖ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
Ndithu wakuletsani (kudya) zakufa zokha, magazi (liwende), nyama ya nkhumba ndi chimene chazingidwa posatchula dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nadya choletsedwa) mosafuna kapena kupyoza muyeso (Allah amkhululukira), ndithudi Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni.
تفسیرهای عربی:
وَلَا تَقُولُواْ لِمَا تَصِفُ أَلۡسِنَتُكُمُ ٱلۡكَذِبَ هَٰذَا حَلَٰلٞ وَهَٰذَا حَرَامٞ لِّتَفۡتَرُواْ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ لَا يُفۡلِحُونَ
Ndipo musanene chifukwa chabodza lomwe malirime anu akunena (kuti) “Ichi nchololedwa; ichi ncholetsedwa; (popanda umboni).” Kuopera kuti mungampekere bodza Allah. Ndithu amene akupekera bodza Allah, sangapambane.
تفسیرهای عربی:
مَتَٰعٞ قَلِيلٞ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Ndichisangalalo chochepa (cha m’dziko lapansi chimene chikuwachititsa zimenezo); ndipo iwo adzapata chilango chowawa.
تفسیرهای عربی:
وَعَلَى ٱلَّذِينَ هَادُواْ حَرَّمۡنَا مَا قَصَصۡنَا عَلَيۡكَ مِن قَبۡلُۖ وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
Ndipo kwa Ayuda tidawaletsa kale zimene takusimbira. Ndipo sitidawachitire chinyengo (pakuwaletsa zimenezo), koma iwo okha adali kudzichitira chinyengo.
تفسیرهای عربی:
ثُمَّ إِنَّ رَبَّكَ لِلَّذِينَ عَمِلُواْ ٱلسُّوٓءَ بِجَهَٰلَةٖ ثُمَّ تَابُواْ مِنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ وَأَصۡلَحُوٓاْ إِنَّ رَبَّكَ مِنۢ بَعۡدِهَا لَغَفُورٞ رَّحِيمٌ
Kenako ndithu Mbuye wako, kwa amene achita zoipa mwaumbuli ndipo nkulapa pambuyo pazimenezo nachita zabwino, ndithudi Mbuye wako pambuyo pa zimenezo Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
تفسیرهای عربی:
إِنَّ إِبۡرَٰهِيمَ كَانَ أُمَّةٗ قَانِتٗا لِّلَّهِ حَنِيفٗا وَلَمۡ يَكُ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Ndithu Ibrahim adali mtsogoleri (chitsanzo chabwino kwa anthu), womvera Allah, wopendekera ku choonadi ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano).
تفسیرهای عربی:
شَاكِرٗا لِّأَنۡعُمِهِۚ ٱجۡتَبَىٰهُ وَهَدَىٰهُ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
(Adali) wothokoza mtendere Wake (Allah); adamsankha ndipo adamuongolera ku njira yolunjika.
تفسیرهای عربی:
وَءَاتَيۡنَٰهُ فِي ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٗۖ وَإِنَّهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ لَمِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Ndipo tidampatsa zabwino padziko lapansi, ndipo ndithudi, iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala m’gulu la anthu abwino.
تفسیرهای عربی:
ثُمَّ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ أَنِ ٱتَّبِعۡ مِلَّةَ إِبۡرَٰهِيمَ حَنِيفٗاۖ وَمَا كَانَ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Kenako takuvumbulutsira (iwe Muhammad{s.a.w} mawu) akuti: “Tsatira njira (chipembedzo) ya Ibrahim (yemwe adali) wokwanira mkulungama, ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano.)”
تفسیرهای عربی:
إِنَّمَا جُعِلَ ٱلسَّبۡتُ عَلَى ٱلَّذِينَ ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِۚ وَإِنَّ رَبَّكَ لَيَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Ndithudi Sabata idaikidwa kwa amene adatsutsana pa za iyo (Sabatayo); ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zomwe adali kusiyana.
تفسیرهای عربی:
ٱدۡعُ إِلَىٰ سَبِيلِ رَبِّكَ بِٱلۡحِكۡمَةِ وَٱلۡمَوۡعِظَةِ ٱلۡحَسَنَةِۖ وَجَٰدِلۡهُم بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ
Itanira (anthu) ku njira ya Mbuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino; ndipo tsutsana nawo mkutsutsana kwabwino (osati motukwanana kapena monyozana). Ndithu Mbuye wako Iye Ngodziwa kwambiri za amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye Ngodziwa kwambiri za amene aongoka.
تفسیرهای عربی:
وَإِنۡ عَاقَبۡتُمۡ فَعَاقِبُواْ بِمِثۡلِ مَا عُوقِبۡتُم بِهِۦۖ وَلَئِن صَبَرۡتُمۡ لَهُوَ خَيۡرٞ لِّلصَّٰبِرِينَ
Ndipo ngati mukubwezera (choipa chimene mwachitiridwa), bwezerani cholingana ndi chimene mwachitiridwacho, koma ngati mutapirira (posiya kubwezera), ndithu kutero ndi ubwino kwa opirira.
تفسیرهای عربی:
وَٱصۡبِرۡ وَمَا صَبۡرُكَ إِلَّا بِٱللَّهِۚ وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَلَا تَكُ فِي ضَيۡقٖ مِّمَّا يَمۡكُرُونَ
Ndipo pirira. Kupirira kwakoko kusakhale pa china chake koma Allah basi. Ndipo usadandaule chifukwa cha iwo, (iwo akudzisokeretsa okha). Ndipo usakhale wobanika chifukwa cha chiwembu chomwe akuchita.
تفسیرهای عربی:
إِنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَواْ وَّٱلَّذِينَ هُم مُّحۡسِنُونَ
Ndithu Allah ali pamodzi ndi amene akumuopa ndi amenenso akuchita zabwino.
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: سوره نحل
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمهٔ چوایی - لیست ترجمه ها

ترجمهٔ معانی قرآن کریم به زبان چوایی، برگردان: خالد ابراهیم بیتالا. نسخهٔ سال ۲۰۲۰ میلادی.

بستن