Check out the new design

ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: مائده   آیه:
لُعِنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ عَلَىٰ لِسَانِ دَاوُۥدَ وَعِيسَى ٱبۡنِ مَرۡيَمَۚ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَواْ وَّكَانُواْ يَعۡتَدُونَ
Adatembeleredwa amene sadakhulupirire nwa ana a Israyeli kupyolera m’lirime la Daud ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Zimenezo nchifukwa chakuti adanyoza ndipo adali opyola malire.
تفسیرهای عربی:
كَانُواْ لَا يَتَنَاهَوۡنَ عَن مُّنكَرٖ فَعَلُوهُۚ لَبِئۡسَ مَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ
Sadali kuletsana choipa chomwe adali kuchichita. Taona kuipitsitsa zomwe adali kuchita.
تفسیرهای عربی:
تَرَىٰ كَثِيرٗا مِّنۡهُمۡ يَتَوَلَّوۡنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ لَبِئۡسَ مَا قَدَّمَتۡ لَهُمۡ أَنفُسُهُمۡ أَن سَخِطَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ وَفِي ٱلۡعَذَابِ هُمۡ خَٰلِدُونَ
Uwaona ambiri a iwo akupalana ubwenzi ndi omwe sadakhulupirire Allah, (opembedza mafano ndi cholinga chomenya nkhondo chipembedzo cha Chisilamu). Nzoipa kwambiri zomwe adadzitsogozera okha. Tero Allah adawakwiira ndipo m’masautso adzakhalamo nthawi yaitali.
تفسیرهای عربی:
وَلَوۡ كَانُواْ يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلنَّبِيِّ وَمَآ أُنزِلَ إِلَيۡهِ مَا ٱتَّخَذُوهُمۡ أَوۡلِيَآءَ وَلَٰكِنَّ كَثِيرٗا مِّنۡهُمۡ فَٰسِقُونَ
Ndipo akadamkhulupirira Allah (moyenera) ndi mneneriyo (Muhammad {s.a.w}) ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iye sakadawachita abwenzi. Koma ambiri a iwo ngopandukira chilamulo cha Allah.
تفسیرهای عربی:
۞ لَتَجِدَنَّ أَشَدَّ ٱلنَّاسِ عَدَٰوَةٗ لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱلۡيَهُودَ وَٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْۖ وَلَتَجِدَنَّ أَقۡرَبَهُم مَّوَدَّةٗ لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱلَّذِينَ قَالُوٓاْ إِنَّا نَصَٰرَىٰۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّ مِنۡهُمۡ قِسِّيسِينَ وَرُهۡبَانٗا وَأَنَّهُمۡ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ
۞ Ndithudi, uwapeza anthu amene ali oyipitsitsa pa chidani ndi anthu okhulupirira (Asilamu) ndi Ayuda komanso opembedza mafano. Ndipo uwapeza oyandikira ubwenzi ndi okhulupirira (Asilamu) ndi awo akunena kuti: “Ife ndi Akhrisitu.” Zimenezo n’chifukwa chakuti mwa iwo alipo ophunzira ndi oopa Allah, ndi chifukwanso chakuti iwo (Akhirisitu) sadzitukumula.
تفسیرهای عربی:
وَإِذَا سَمِعُواْ مَآ أُنزِلَ إِلَى ٱلرَّسُولِ تَرَىٰٓ أَعۡيُنَهُمۡ تَفِيضُ مِنَ ٱلدَّمۡعِ مِمَّا عَرَفُواْ مِنَ ٱلۡحَقِّۖ يَقُولُونَ رَبَّنَآ ءَامَنَّا فَٱكۡتُبۡنَا مَعَ ٱلشَّٰهِدِينَ
Ndipo akamva zomwe zavumbulutsidwa kwa Mtumiki, uona maso awo akugwetsa misozi chifukwa cha choonadi chomwe achizindikira. Akunena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboni (choonadi).”
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: مائده
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا - لیست ترجمه ها

مترجم: خالد ابراهیم بیتالا.

بستن