E inu amene mwakhulupirira! Kwaniritsani mapangano onse (omwe ali pakati panu ndi anthu anzanu). Kwalolezedwa kwa inu (kudya nyama ya) ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi), kupatula chomwe mukuuzidwa (kuti ncholetsedwa). Koma nkosaloledwa kwa inu kuchita ulenje mutalowa m’mapemphero a Hajj, (kapena muli m’nthaka yopatulika ya ku Makka). Ndithudi, Allah akulamula chimene wafuna.[155]
Lero mwaloledwa zonse zabwino ndi chakudya cha omwe adapatsidwa buku nchololedwa kwa inu, ndiponso chakudya chanu nchololedwa kwa iwo, ndipo (mukuloledwa kuwakwatira) akazi abwino a mwa okhulupirira ndi akazi abwino a mwa omwe adapatsidwa ma buku kale, ngati mwawapatsa chiwongo chawo m’njira yomanga nawo ukwati, osati mochita nao chiwerewere, osatinso mochita nao zibwenzi. Ndipo amene akane kukhulupirira, ndiye kuti yaonongeka ntchito yake; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mwa oluza (otaiyika).[158]
[158] Chakudya chozingidwa sichingakhale chovomerezeka kwa Asilamu pokhapokha chitazingidwa ndi Asilamu. Izi zili ngati atatsatira malamulo akazingidwe, osati kupotokola khosi, kapena kumenya ndimyala kapena chibonga. Tsono chakudya chozingidwa nchovomerezeka kwa Msilamu kuchidya ngakhale chitakonzedwa ndi achikunja (akafiri) ngati:- (a) simudaone kuti athiramo najisi (uve) (b) Sichili chakudya choletsedwa. Nkovomerezeka kwa mwamuna wa Chisilamu kukwatira:- (a) Mkazi wa Chiyuda (b) Mkazi wa Chikhrisitu ngati makolo awo adali Ayuda kapena Akhrisitu chisilamu chisanadze.
N.B! Koma awa a Mishoni omwe alowa m’Chikhrisitu posachedwapa nkosaloledwa kuwakwatira pokhapokha atayamba alowa m’Chisilamu Tsono mkazi wa Chisilamu nkosaloledwa kukwatiwa ndi myuda kapena mkhrisitu. Ndipo apa apitirizanso machitidwe achiwerewere chomangira nyumba ndi chapatchire. Munthu akafuna kukwatira mkazi atsate mfundo zikudzazi kuti ukwati wakewo ukhale wovomerezeka pa malamulo a Chisilamu:- (a) Mkazi alole kukwatiwa ndi mwamunayo. (b) Myang’aniri wa wamkazi apereke kwa munthu chilolezo choti akwatitsire mkazi uja, kapena amkwatitse iye mwini pomuuza mkwati kuti “Ndakukwatitsa uje mwana wa uje.’’ (c) Mkwati avomereze kuti: “Ndavomera kumkwatira uje, mwana wa uje’.’ (d) Pakhale anthu aamuna oikira umboni osachepera pa awiri. Anthuwo akhale aulemu wawo pamaso pa anthu. (e) Chiperekedwe chiongo. (f) Iwerengedwe khutba ya ukwati.
“E inu amene mwakhulupirira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pa mitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo. Ngati muli ndi janaba dziyeretseni (sambani thupi lonse); ndipo ngati muli odwala kapena muli paulendo, kapena mmodzi wanu wachokera kokadzithandiza kapenanso mwakhalira limodzi ndi mkazi, ndiye simudapeze madzi, chitani Tayammamu ndi dothi labwino ndipo pakani ku nkhope zanu ndi mmanja mwanu. Allah sakufuna kukuvutitsani, koma akufuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa chisomo chake pa inu kuti muthokoze.
Ndipo kumbukirani chisomo cha Allah pa inu ndi pangano lake lomwe mudapangana Naye, pamene mudati: “Tamva, ndipo tamvera.” Muopeni Allah. Ndithudi Allah Ngodziwa za m’mitima.
E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani mtendere wa Allah omwe uli pa inu, pamene anthu ena adatsimikiza kukutambasulirani manja awo (pofuna kuchita nanu nkhondo) koma (Allah) adawatsekereza manja awo kukufikani inu. Choncho opani Allah. Ndipo kwa Allah Yekha, ayadzamire okhulupirira.
Ndipo ndithudi, Allah adamanga pangano ndi ana a Israyeli, ndipo tidawaikira Akuluakulu khumi ndi awiri mwa iwo. Ndipo Allah adati: “Ndithudi Ine ndili pamodzi ndi inu, ngati mupemphera Swala ndikupereka chopereka, ndikukhulupirira atumiki Anga, ndi kuwalemekeza ndi kumkongoza Allah Ngongole yabwino, ndithudi ndikufafanizirani zoipa zanu, ndikudzakulowetsani m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje. Koma amene akane mwa inu pambuyo pa (chipangano) ichi, ndithu wasochera njira yowongoka.”
Naonso aja amene akuti: “Ife ndife Akhrisitu,” tidalandira pangano lawo koma adasiya gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Tero tidabzala pakati pawo chidani ndi kusakondana mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah adzawawuza zimene adali kuchita.[160]
[160] Ndime iyi ikusonyeza kupatukana komwe kuli pakati pawo kotero kuti mpingo wina umayesa unzake monga wakunja. Monga mpingo wa Roman Catholic umaiona mipingo ina monga ya Protestant, Orthodox ndi yambiri ngati mipingo ya chikunja. Zonsezi nchifukwa cha kusatsatira zophunzitsa zenizeni za Chikhrisitu.
E inu anthu a buku! Ndithudi wakufikani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani poyera zambiri zomwe munkabisa za m’buku. Koma akusiya zambiri (posazilongosola). Ndithudi kwakudzerani kuunika kochokera kwa Allah ndi buku lomwe likufotokoza mwatchutchutchu (chinthu chilichonse).
Ndi bukulo Allah akuwatsogolera kunjira zamtendere amene akutsata chiyanjano chake ndikuwatulutsa mu m’dima ndi kuwaika m’kuunika mwa lamulo Lake, ndi kuwatsogolera kunjira yoongoka.
Ndithudi, amukana (Allah) amene akunena kuti Mulungu ndiye Mesiya Mwana wa Mariya. Nena: “Ndani akadatha kuletsa chilichonse kwa Allah ngati Iye akadafuna kuononga Mesiya mwana wa Mariya ndi mayi wakeyo, ndi onse omwe ali m’dziko lapansi? Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake ngwa Allah. Amalenga chimene wafuna. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”[161]
[161] Mndime iyi atchula zoyankhula zawo za machimo zoti Isa (Yesu) ndi mwana wa Mulungu, kapena ndi Mulungu amene, kapena ndi mmodzi mmilungu itatu. Ndipo akunenetsa za kufooka kwa mneneri Isa (Yesu) pamaso pa Allah monga kulili kufookanso kwa zolengedwa zina.
Ndimeyi ikunenetsanso kuti Allah monga amalenga mkalengedwe kamene Iye wafuna, mchosadabwitsa kwa Iye kulenga Isa (Yesu) popanda tate. Ndipo nchosadabwitsanso kwa Iye kulenga Adam popanda tate ndi mayi. Nanga nchotani kuti Akhrisitu azimuyesa Mneneri Isa (Yesu) kuti ndi mwana wa Mulungu kamba koti alibe tate? Bwanji nanga Adam naye sakumuyesa mwana wa Mulungu poti nayenso alibe tate ndi mayi? Ndibwino kutsata choonadi ngakhale choonadicho chikuchokera kwa mdani. Choonadi ndi choonadi.
Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu akunena: “Ife ndife ana a Mulungu ndiponso okondeka ake.” Nena: (Iwe Mtumiki) “Nchifukwa ninji Allah amakukhaulitsani kamba ka machimo anu? Koma inu ndinu anthu chabe mwa omwe adawalenga. Amamkhululukira amene wamfuna; ndipo amamulanga amene wamfuna. Ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi za pakati pake ngwa Allah. Ndipo kwa Iye nkobwerera.”
(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Ndithudi, ine ndilibe nyonga (yokakamizira aliyense kutsatira lamulo Lanu) koma pa ine ndekha ndi pa m’bale wanga. Choncho tisiyanitseni ndi anthu awa opandukira chilamulo.”
Ndipo awerengere nkhani mwachoonadi ya ana awiri a Adam, pamene adapereka nsembe. Ndipo idalandiridwa ya mmodzi wawo, koma ya winayo siidalandiridwe. (Amene nsembe yake siidalandiridwe) adati (kwa mnzake): “Ndithudi ndikupha.” Mnzakeyo adati: “Ndithudi, Allah amalandira nsembe ya amene akuopa (Allah).”[163]
“Ngati utambasula dzanja lako pa ine kuti undiphe, ine sinditambasula dzanja langa pa iwe kuti ndikuphe. Ndithudi, ine ndikuopa Allah Mbuye wa zolengedwa.”
“Ine ndikufuna kuti usenze machimo anga pamodzi ndi machimo ako, choncho ukakhale m’gulu la anthu a ku Moto. Ndipo awo ndio malipiro a anthu ochita zoipa.”
Pachifukwa chazimenezo, tidawalamula ana a Israyeli kuti amene wapha munthu popanda iye (wophedwayo) kupha munthu, kapena kuchita chisokonezo pa dziko, ali ngati wapha anthu onse. Ndipo amene wamuleka munthu ali ndi moyo, ali ngati awapatsa moyo anthu onse. Ndithudi, atumiki Athu adawadzera iwo ndi zisonyezo zoonekera. Koma ndithu ambiri a iwo, pambuyo pa zimenezo, adapitirizabe kuononga pa dziko.
Ndithu mphoto ya amene akulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake (pochita zomwe waletsa) ndi kudzetsa chionongeko pa dziko, aphedwe kapena apachikidwe pa mtanda, kapena adulidwe manja awo ndi miyendo yawo mosemphanitsa (dzanja lakumanja ndi phazi lakumanzere, ndipo dzanja lakumanzere ndi phazi lakumanja); kapena apirikitsidwe mdzikomo. Uku ndikuyaluka kwawo pa dziko lapansi. Ndipo iwo pa tsiku lachimaliziro adzalandira chilango chachikulu.[164]
Ndipo wakuba wamwamuna ndi wakuba wamkazi, aduleni manja awo; kukhala mphoto ya zomwe achita ndi chilango chochokera kwa Allah. Allah Ngwanyonga zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Koma amene walapa pambuyo pakuchita kwake zoipa, namachita zabwino, Allah alandira kulapa kwake. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha.[165]
[165] Taona chifundo cha Allah! Iye akulonjeza wochimwa kuti ngati asiya machimo ake amlandira. Tero munthu asadzione kuti waonongeka kotero kuti Allah sangamlandire. Iyayi! Abwelere ndi mtima wake wonse kwa Allah ndipo Allah amlandira.
Ndipo m’menemo (m’buku la Taurat) tidawalamula kuti: “Munthu aphedwe chifukwa chopha mnzake, ndi kuti diso kwa diso, mphuno kwa mphuno; khutu kwa khutu; dzino kwa dzino, ndiponso kubwezerana mabala.” Koma amene wakhululuka ndiye kuti dipo likhala kwa iye. Ndipo amene saweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa iwowo ndiwo anthu ochita zoipa.
Ndipo tidatsatiza pa mapazi a aneneriwo, Isa (Yesu) mwana wa Mariya kudzatsimikizira zomwe zidali patsogolo pake m’buku la Taurat. Ndipo tidampatsa Injili yomwe m’kati mwake muli chiongoko ndi kuunika; ndikutsimikizira zomwe zidali patsogolo pake za m’buku la Taurat. Ndipo ndi chiongoko ndi ulaliki wabwino kwa oopa (Allah).
Anthu abuku la Injili alamulire potsatira zimene Allah adavumbulutsa mmenemo. Ndipo amene asiya kulamulira ndi zomwe Allah wavumbulutsa iwo ndiwo opandukira malamulo (a Allah).
Weruza pakati pawo ndi chimene Allah wavumbulutsa, ndipo usatsate zofuna zawo, koma chenjera nawo kuti angakusokoneze nkusiya zina mwa zimene Allah wavumbulutsa kwa iwe. Ndipo ngati anyozera dziwa kuti Allah afuna kuwapatsa chilango cha ena mwa machimo awo. Ndithudi, anthu ambiri ngopandukira (malamulo a Allah).
Kodi iwo akufuna chiweruzo cha nthawi yaumbuli (chamasiku aumbuli, Chisilamu chisanadze)? Kodi ndani ali wabwino poweruza kuposa Allah kwa anthu otsimikiza (kuti Allah alipo)?
E inu amene mwakhulupirira! Ayuda ndi Akhrisitu musawapale ubwenzi (nkumawauza chinsinsi chanu). Iwo pakati pawo ndi abwenzi ndi atetezi kwa wina ndi mnzake. Amene awapale ubwenzi mwa inu, ndiye kuti iye ndi m’modzi wa iwo. Ndithudi, Allah satsogolera anthu ochita zoipa.
E inu amene mwakhulupirira! Amene mwa inu asiye chipembedzo chake, ndiye kuti posachedwapa Allah abweretsa anthu omwe awakonda, nawonso amkonda; odzichepetsa kwa okhulupirira (anzawo); amphamvu kwa osakhulupirira; omenyera nkhondo chipembedzo cha Allah, saopa kudzudzula kwa odzudzula. Umenewu ndi ubwino wa Allah; amaupereka kwa amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mataya; Ngodziwa kwambiri.
Ndipo amene achite Allah ndi Mtumiki Wake, ndi omwe akhulupirira kukhala atetezi ake, (ndithu iwo ndi a chipani cha Allah). Ndithu chipani cha Allah ndicho chopambana.
Nena: “E inu anthu a buku! Kodi mukuona cholakwika kwa ife kaamba kakuti takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwenso zidavumbulutsidwa kale? Ndithudi, ambiri mwa inu ndi opandukira chilamulo (cha Allah).”
Nena: “Kodi ndikuuzeni za uja amene ali ndi malipiro oipa kwa Allah kuposa izi? Ndiomwe Allah wawatembelera ndi kuwakwiira ndi kuwasandutsa ena kukhala anyani ndi nkhumba, ndi opembeza satana. Awo ndiwo okhala ndi malo oipa, ndiponso osokera njira yowongoka.”
Ndipo (achinyengo) akakudzerani, akunena: “Takhulupirira,” pamene alowa kwa inu ali osakhulupirira ndipo atulukanso ali osakhulupirira. Koma Allah Ngodziwa kwambiri zomwe akhala akubisa.
Bwanji odziwa za malamulo ndi akuluakulu a chipembedzo sadawaletse zoyankhula za uchimo ndi kudya kwawo zinthu zoletsedwa? Ndithudi, zomwe akhala akuchitazo ndi zoipa zedi.
Ndipo Ayuda adati: “Dzanja la Allah lafumbatika (sitikupeza chuma ngati kale). (Koma sichoncho); manja awo ndiwo afumbatika (posachita zabwino ndi kuchenjelera anthu). Ndipo atembeleredwa chifukwa cha zomwe anena. Koma manja ake (Allah) ngotambasuka. Amapatsa mmene wafunira. Ndithudi, zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, ziwaonjezera ambiri a iwo (Ayuda) kulumpha malire ndi kusakhulupirira. Ndipo taika chidani ndi kusakondana pakati pawo mpaka tsiku la chimariziro. Nthawi iliyonse akayatsa moto wa nkhondo, Allah amauzimitsa. Ndipo amayesetsa kudzetsa chisokonezo pa dziko, (koma Allah sawathandiza). Ndipo Allah sakonda owononga.
Akadakhala kuti iwo adaigwiritsa ntchito Taurat ndi Injili, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwo kuchokera kwa Mbuye wawo (monga Qurani), ndithudi akanadya za kumwamba ndi za pansi pa myendo yawo. Mwa iwo alipo amene akutsatira njira yabwino. Komanso ambiri mwa iwo nzoipa zedi zomwe akuchita.
E iwe Mtumiki! Fikitsa (kwa anthu) zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako. Ngati suchita, ndiye kuti sudafikitse uthenga Wake. Ndipo Allah akuteteza kwa anthu; (usaope aliyense). Ndithudi, Allah satsogolera anthu osakhulupirira.
Nena: “E inu anthu a buku! Simuli kanthu (pa chipembedzo chanu) mpaka muimilire (kutsatira malamulo) a Taurat ndi Injili ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu, ziwaonjezera kulakwa ndi kusakhulupirira ambiri a iwo zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, choncho usadandaule za anthu osakhulupirira.
Ndithudi, amene akhulupirira ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi Asabayi, ndi Akhrisitu, - amene akhulupirire Allah ndi tsiku lachimaliziro, (monga momwe akulangizira Mtumiki Muhammad {s.a.w}) nachita zabwino, - palibe mantha kwa iwo ndiponso sadzadandaula.
Ndithudi, tidalandira pangano kwa ana a Israyeli (kuti adzamvera Allah) ndipo tidawatumizira atumiki. Nthawi iliyonse akawadzera mtumiki ndi chomwe mitima yawo siinkafuna, adawatsutsa ena (mwa atumikiwo), ndipo ena ankawapha kumene.
Ndithudi am’kana Allah amene anena kuti, Mulungu ndiye Isa (Yesu) mwana wa Mariya.” Pomwe Mesiya adati: “Inu ana a Israyeli! Pembedzani Allah Yemwe ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.” Ndithudi, amene aphatikize Allah ndi chinthu china, ndithudi Allah waletsa kwa iye kukalowa ku Munda wamtendere, ndipo malo ake ndi ku Moto. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi.
Mesiya mwana wa Mariya sali chilichonse koma ndi Mtumiki wa Allah chabe. Ndithudi, atumiki ambiri adapita kale patsogolo pake. Nayenso mayi wake ndi mkazi wachoonadi, onse awiri adali kudya chakudya, (ndipo chotsatira chake amapita kokadzithandiza. Nanga ndi milungu yotani yopita kukadzithandiza?) Taona momwe tikufotokozera kwa iwo zizindikiro. Taonanso mmene akutembenuziridwa (kusiya choonadi).
Adatembeleredwa amene sadakhulupirire nwa ana a Israyeli kupyolera m’lirime la Daud ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Zimenezo nchifukwa chakuti adanyoza ndipo adali opyola malire.
Ndipo akadamkhulupirira Allah (moyenera) ndi mneneriyo (Muhammad {s.a.w}) ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iye sakadawachita abwenzi. Koma ambiri a iwo ngopandukira chilamulo cha Allah.
۞ Ndithudi, uwapeza anthu amene ali oyipitsitsa pa chidani ndi anthu okhulupirira (Asilamu) ndi Ayuda komanso opembedza mafano. Ndipo uwapeza oyandikira ubwenzi ndi okhulupirira (Asilamu) ndi awo akunena kuti: “Ife ndi Akhrisitu.” Zimenezo n’chifukwa chakuti mwa iwo alipo ophunzira ndi oopa Allah, ndi chifukwanso chakuti iwo (Akhirisitu) sadzitukumula.
E inu amene mwakhulupirira! Ndithudi, mowa (kutchova) njuga, kupembedza mafano ndi kuombeza maula, (zonsezi) ndi uve, mwa ntchito za satana. Choncho zipeweni kuti mupambane.
E inu amene mwakhulupirira! Ndithu Allah akuyesani ndi nyama zina zozichita ulenje, zomwe manja anu ndi mikondo yanu ingazifikire, kuti Allah amuwonetsere poyera amene akumuopa mwanseri. Ndipo amene alumphe malire (posaka nyamayo ndi kupha) pambuyo pa zomwe mwauzidwazo, adzapeza chilango chopweteka.
E inu amene mwakhulupirira! Musaphe nyama ya mtchire pomwe inu muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Ndipo mwa inu amene angaphe mwadala nyama ya mtchireyo, dipo (lake likhale kuzinga) yofanana ndi yomwe waphayo, mu mtundu wa nyama zowetedwa, (monga mmene) angaweruzire olungama awiri a mwa inu, kukhala nsembe yoperekedwa ku Ka’aba (kuti ikazingidwe kumeneko ndi kuwagawira osauka); kapena alipe dipo la chakudya kudyetsa masikini; kapena m’malo mwake asale kuti alawe kupweteka kwa chinthu chakecho. Ndipo Allah afafaniza zomwe zidapita kale. Koma amene achitenso, Allah amukhaulitsa ndi chilango chochokera kwa Iye. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wokhaulitsa koopsa
Nkololezedwa kwa inu kusaka nyama za m’nyanja ndi chakudya chake (chomwe chapezeka m’nyanjamo chitafa chokha). Chimenecho ndi kamba wanu (inu amene simuli pa ulendo) ndiponso a pa ulendo. Kwaletsedwa kwa inu kusaka za pamtunda pomwe muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Opani Allah Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.
Allah wapanga Ka’aba kukhala nyumba yopatulika, ndikukhala pamalo popezera zosowa za anthu. Ndipo adapanganso miyezi (inayi) yopatulika, ndi kupereka nyama zansembe ku Makka zovekedwa makoza monga zisonyezo (kusonyeza kuti zikupita ku Makka). Zonsezi nkuti mudziwe kuti Allah akudziwa za kumwamba ndi pansi, ndikuti Allah Ngodziwa chilichonse.
E inu amene mwakhulupirira! Musamafunse za zinthu zomwe zitasonyezedwa kwa inu zikuipirani. Ndipo ngati muzifunsa pomwe Qur’an ikuvumbulutsidwa, zionetsedwa kwa inu. Allah wakhululuka zimenezo. Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza.
Kumbukiraninso pamene Allah adzati: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya! Kumbuka chisomo Changa pa iwe ndi pa mayi wako, pamene ndinakuthandiza ndi mzimu woyera (Gabriel), (kotero kuti) udalankhula kwa anthu (mawu omveka) pamene udali mchikuta ndiponso pamene udali wamkulu. Ndipo (kumbuka) pamene ndidakuphunzitsa kulemba, nzeru; (ndinakuzindikiritsanso buku la) Taurat ndi Injili. (Kumbukanso) pamene udaumba dongo chithunzi chambalame mwa lamulo Langa. Utatero udauziramo ndipo zidasanduka mbalame mwa lamulo Langa. Ndipamene udali kuchiza akhungu ndi achinawa, mwa lamulo Langa. Ndipamene unkawatulutsa (m’manda) ena mwa akufa mwa lamulo Langa. Ndipamene ndinawatsekereza ana a Israyeli kwa iwe (kuti asakuzunze) pamene udawadzera ndi zisonyezo zooneka, ndipo aja mwa iwo omwe sadakhulupirire, adati: “Ichi sichina, koma ndi matsenga owonekera.”
Isa (Yesu) mwana wa Mariya adati: “Inu Allah Mbuye wathu! Titsitsireni chakudya kuchokera kumwamba kuti chikhale chikondwelero cha oyambilira ndi omalizira mwa ife, komanso chikhale chisonyezo chochokera kwa Inu; choncho tipatseni ndithu inu ndinu Abwino popatsa kuposa opatsa.”
Allah adati: “Ndithu Ine ndikuchitsitsa kwa inu. Koma amene adzatsutse mwa inu pambuyo pa ichi, ndithu Ine ndidzamulanga ndi chilango chomwe sindidamulangepo nacho aliyense mwa zolengedwa.”
Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adzanena: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi iwe udauza anthu kuti: ‘Ndiyeseni ine ndi mayi wanga monga milungu iwiri m’malo mwa Allah?” (Mneneri Isa {Yesu}) adzaati: “Ulemelero ukhale pa Inu. Sikoyenera kwa ine kunena zomwe sizili zoyenera (kwa ine mawu amenewa ngabodza). Ngati ndikadanena, ndiye kuti mukadadziwa. Inu mukudziwa zomwe zili mu mtima mwanga, pomwe ine sindidziwa zomwe zili mwa Inu. Ndithudi, Inu ndinu Wodziwa zamseri.”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
தேடல் முடிவுகள்:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".