ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمهٔ چوایی * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: سوره قدر   آیه:

سوره قدر

إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ فِي لَيۡلَةِ ٱلۡقَدۡرِ
Ndithu taivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wa Qadr (usiku wolemekezeka).[464]
[464] Qur’an mwachidziwikire idali kuvumbulutsidwa pang’onopang’ono kuchokera ku thambo loyamba (Baitul Izza). Choncho, usiku umene idatsika kuchokera ku thambo la seveni (Lauh Mahafudwi) kupita ku thambo loyamba udali usiku wotchedwa Laila-tul-Qadr (usiku wolemekezeka kwambiri) ndipo ndichifukwa chake kukunenedwa kuti Qur’an idatsitsidwa mu usiku wa Qadr. Umenewu ndi usiku umodzi mkati mwa mwezi wa Ramadan omwe uli wodalitsidwa kuposa miyezi chikwi chimodzi. Tanthauzo lake apa ndikuti munthu ngati achita ntchito zabwino mu usiku umenewu amapeza malipiro kuposa a yemwe wachita ntchito zabwino kokwanira miyezi chikwi chimodzi. Koma Allah adaubisa usiku umenewu. Sukudziwika kuti uli pa deti lanji ncholinga choti anthu alimbike kuchita mapemphero mwezi wonse wa Ramadan; koma ukuyembekezedwa kuti uli mu masiku khumi omaliza, makamaka usiku wodzukira pa 21, 23, 25, 27 ndi 29 kwa yemwe akufuna kupeza madalitso a usiku umenewu alimbike kuchita mapemphero kwambiri mwezi wonse.
تفسیرهای عربی:
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا لَيۡلَةُ ٱلۡقَدۡرِ
Ndi chiyani chingakudziwitse za usiku wolemekezekawu?
تفسیرهای عربی:
لَيۡلَةُ ٱلۡقَدۡرِ خَيۡرٞ مِّنۡ أَلۡفِ شَهۡرٖ
Usiku olemekezekawu uli wabwino kuposa miyezi chikwi chimodzi (1000 yomwe mulibe Laila-tul-Qadr).
تفسیرهای عربی:
تَنَزَّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَٱلرُّوحُ فِيهَا بِإِذۡنِ رَبِّهِم مِّن كُلِّ أَمۡرٖ
Amatsika angelo ndi Jiburil mmenemo mwa chilolezo cha Mbuye wawo kudzalongosola chinthu chilichonse.
تفسیرهای عربی:
سَلَٰمٌ هِيَ حَتَّىٰ مَطۡلَعِ ٱلۡفَجۡرِ
Mtendere usiku umenewo! (Palibe mavuto ndi zoipa) mpaka m’bandakucha.[465]
[465] Adanena Baidawi kuti tanthauzo la Ayah iyi ndikuti mu usiku umenewu Allah amalamula kuti kukhale mtendere wokhawokha. Koma mu usiku wina amalamula kuti kukhale mtendere ndi masoka.
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: سوره قدر
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمهٔ چوایی - لیست ترجمه ها

ترجمهٔ معانی قرآن کریم به زبان چوایی، برگردان: خالد ابراهیم بیتالا. نسخهٔ سال ۲۰۲۰ میلادی.

بستن