Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Firo siisiiwo * - Tippudi firooji ɗii


Firo maanaaji Simoore: Simoore wimmboolo hayre   Aaya:

Simoore wimmboolo hayre

ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ عَلَىٰ عَبۡدِهِ ٱلۡكِتَٰبَ وَلَمۡ يَجۡعَل لَّهُۥ عِوَجَاۜ
Kutamandidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adavumbulutsa kwa kapolo Wake (Mtumiki Muhammad{s.a.w}), buku (ili lopatulika), ndipo sadalikhotetse (koma m’menemo muli zoona zokhazokha.)
Faccirooji aarabeeji:
قَيِّمٗا لِّيُنذِرَ بَأۡسٗا شَدِيدٗا مِّن لَّدُنۡهُ وَيُبَشِّرَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ أَجۡرًا حَسَنٗا
(Walichita kukhala) loongoka kuti lichenjeze anthu za chilango chokhwima chochokera kwa Iye (Allah), ndikuti liwasangalatse okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti adzapeza malipiro abwino.
Faccirooji aarabeeji:
مَّٰكِثِينَ فِيهِ أَبَدٗا
Adzakhalamo (mumtendere wosathawo) muyaya.
Faccirooji aarabeeji:
وَيُنذِرَ ٱلَّذِينَ قَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ وَلَدٗا
Ndikuti liwachenjeze amene akunena (kuti): “Allah wadzipangira Mwana.”
Faccirooji aarabeeji:
مَّا لَهُم بِهِۦ مِنۡ عِلۡمٖ وَلَا لِأٓبَآئِهِمۡۚ كَبُرَتۡ كَلِمَةٗ تَخۡرُجُ مِنۡ أَفۡوَٰهِهِمۡۚ إِن يَقُولُونَ إِلَّا كَذِبٗا
Iwo pabodza lawolo alibe kuzindikira chinthu chilichonse chanzeru ngakhale makolo awo. Lakula kwabasi liwu lomwe likutuluka mkamwa mwawo. Sanena china koma bodza basi.
Faccirooji aarabeeji:
فَلَعَلَّكَ بَٰخِعٞ نَّفۡسَكَ عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِمۡ إِن لَّمۡ يُؤۡمِنُواْ بِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ أَسَفًا
Mwina udziwononga wekha pakuwadandaulira chikhalidwe chawo kuti sakhulupirira nkhani iyi. (Iyayi! Usakhale wodandaula ndi zimenezo).
Faccirooji aarabeeji:
إِنَّا جَعَلۡنَا مَا عَلَى ٱلۡأَرۡضِ زِينَةٗ لَّهَا لِنَبۡلُوَهُمۡ أَيُّهُمۡ أَحۡسَنُ عَمَلٗا
Ndithu Ife tazichita zomwe zili pamwamba pa nthaka kukhala zokometsera nthakayo, ndikuti (mwa izo) tiwayese mayeso kuti (ndani) mwa iwo ali wochita zabwino kwambiri.
Faccirooji aarabeeji:
وَإِنَّا لَجَٰعِلُونَ مَا عَلَيۡهَا صَعِيدٗا جُرُزًا
Ndipo ndithu Ife ndi Amene tidzazichita zomwe zili pamenepo kukhala monga nthaka yoguga (yopanda mmera).
Faccirooji aarabeeji:
أَمۡ حَسِبۡتَ أَنَّ أَصۡحَٰبَ ٱلۡكَهۡفِ وَٱلرَّقِيمِ كَانُواْ مِنۡ ءَايَٰتِنَا عَجَبًا
Kodi ukuganiza kuti eni phanga ndi eni nkhani zomwe zidalembedwa m’mabuku, adali mwa zizindikiro zathu zododometsa kwambiri? (Iyayi, zilipo zododometsa kwabasi kuposa zimenezo.)
Faccirooji aarabeeji:
إِذۡ أَوَى ٱلۡفِتۡيَةُ إِلَى ٱلۡكَهۡفِ فَقَالُواْ رَبَّنَآ ءَاتِنَا مِن لَّدُنكَ رَحۡمَةٗ وَهَيِّئۡ لَنَا مِنۡ أَمۡرِنَا رَشَدٗا
Pamene anyamata adathawira kuphanga nati: “Mbuye wathu! Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu, ndipo tikonzereni chiongoko m’zochita zathu.”[256]
[256] Nkhani ya eni phanga monga momwe adaifotokozera omasulira Qur’an, idali motere:-
Mfumu yomwe idapondereza anthu inkatchedwa Dikiyanusu idali mu m’zinda wina kudziko la Roma umene unkatchedwa Tartusi, Mneneri Isa (Yesu) atapita kale. Mfumuyi idali kuitana anthu kuti azipembedza mafano. Ndipo imapha aliyense wokhulupilira mwa Allah amene sadali kuvomereza uthenga wake wopotokawo kufikira chisokonezo ndi masautso zidawakulira anthu okhulupilira Allah. Anyamata omwe adali okhulupilira Allah ataona zimenezo, anadandaula kwambiri. Ndipo nkhani ya anyamata idamufika mfumu yopondereza anthuyo ndipo adatumiza mithenga kuti akawatenge anyamatawo. Anyamatawo pamene adaimilira pamaso pa mfumu, iyo idawaopseza kuti iwapha ngati akana kupembedza mafano ndi kukana kupereka nsembe. Koma iwo adatsutsana nayo naonetsera poyera chikhulupiliro chawo mwa Allah. Adati: ‘‘Mbuye wathu ndi Mbuye wathambo ndi nthaka. Sitingapembedze mulungu wina kusiya Iye.”
Mfumu idati kwa iwo: “ Inu ndinu anyamata amisinkhu yochepa, choncho ndikukupatsani mwayi mpaka mawa kuti mukaganize bwino.” Tero iwo adathawa usiku namdutsa m’busa yemwe adali ndi galu. M’busayo pamodzi ndi galu wake adawatsatira, ndipo pamene kudacha adabisala m’phanga lalikulu la m’phiri. Mfumu pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsatira mpaka kukafika ku phangalo. Koma anthu ake adaopa kulowa m’phangamo ndipo mfumu idati: “Atsekereni khomo laphangali kuti afere komweko ndi njala ndi ludzu. Ndipo Allah adawagoneka tulo anyamata a kuphanga aja; adakhala ali mtulo chigonere osadziwa kanthu mpaka padapita zaka zikwi zitatu (300) ndi zaka zisanu ndi zinayi (9). Kenako Allah adawaukitsa. Ndipo iwo amaganiza kuti akhala kuphangako tsiku limodzi, kapena theka la tsiku. Ndipo adayamba kumva njala namtuma m’modzi wawo kuti akawagulire chakudya. Koma adamulangiza akadzibise ndiponso akachenjere kuti anthu asamuzindikire. Choncho iye adapita mpaka kukafika m’mudzimo. Kuja anapeza zizindikiro za mudziwo zasintha.
Palibe aliyense mwa nzika zam’mudzimo amene adamdziwa. Yekha adadzinong’oneza: “Mwinatu ine ndasokera njira yakumudzi kwathu kuja.” Komabe adagula chakudya. Ndipo pamene adapereka ndalama kwa wogulitsa adayamba kuitembenuzatembenuza ndalama ija m’manja mwake. Adati: “Mwaipeza kuti ndalama iyi?” Choncho anthu adasonkhana nayang’ana ndalama ija modabwa nati: “Kodi mnyamata iwe ndiwe yani, kapenatu mwatulukira chuma chomwe chidabisidwa m’nthaka ndi anthu akale?” Iye adati kwa iwo “lyayi. Ndikulumbira Allah, sindidapeze chuma chokwiliridwa m’nthaka. Iyi ndi ndalama yomwe mtundu wanga umagwiritsa ntchito.” Iwo adati kwa iye: “Ndalamayi njakale kwambiri, m’nyengo ya mfumu Dikiyanusu.” Iye adati modabwa: “Adatani Dikiyanusiyo?” Iwo adati, “Adafa kalekale!” Iye adati:” Ndikulumbira Allah, sangandikhulupirire aliyense zimene nditi ndikuuzeni. Ife tidali anyamata. Ndipo mfumuyo idatikakamiza kupembedza mafano. Choncho tidaithawa usiku wadzulo nkupita kukabisala kuphanga. Tere lero anzanga andituma kuti ndikagule chakudya. Choncho tiyeni pamodzi kuphangalo kuti nkakuonetseni anzangawo. Iwo adadodoma ndi zonena zakezo nadziwitsa mfumu ya nthawi imeneyo nkhani za munthuyu. Mfumuyo idali yokhulupilira Allah. Ndipo iyo itamva nkhaniyi, idapita pamodzi ndi ankhondo ake ndi nzika za m’mudziwo. Atafika kuja pafupi ndi phangalo, anthu akuphangalo adamva phokoso ndi migugu yamahatchi ndipo adaganiza kuti adali ankhondo a Dikiyanusu. Choncho onse adaimilira kupemphera. Ndipo mfumu idalowa nkuwapeza akupemphera. Pamene adamaliza kupemphera mfumu idagwirana nawo chanza niiwauza kuti iyo imakhulupilira Allah, ndikuti Dikiyanusu adamwalira kalekale. Kenako mfumuyo idamvera nkhani yawo niidziwa kuti, Allah wawaukitsa kuti chikhale chisonyezo kwa anthu kuti Allah adzawaukitsa anthu akufa. Kenako Allah adawagonekanso natenga mizimu yawo iwo ali mtulo chomwecho. Ndipo anthu adayamba kunena: “Timange Msikiti pomwe pali iwowapa wopembedzamo Allah.”
Faccirooji aarabeeji:
فَضَرَبۡنَا عَلَىٰٓ ءَاذَانِهِمۡ فِي ٱلۡكَهۡفِ سِنِينَ عَدَدٗا
Tidagonthetsa makutu awo, (ndikugona kosamva nako kanthu) kwa zaka zambirimbiri m’phanga.
Faccirooji aarabeeji:
ثُمَّ بَعَثۡنَٰهُمۡ لِنَعۡلَمَ أَيُّ ٱلۡحِزۡبَيۡنِ أَحۡصَىٰ لِمَا لَبِثُوٓاْ أَمَدٗا
Kenako tidawautsa, kuti tiwayese (kuti) ndani mwa magulu awiriwa amadziwa kuwerengera nthawi imene (anyamatawa) adakhala (m’phangamo).
Faccirooji aarabeeji:
نَّحۡنُ نَقُصُّ عَلَيۡكَ نَبَأَهُم بِٱلۡحَقِّۚ إِنَّهُمۡ فِتۡيَةٌ ءَامَنُواْ بِرَبِّهِمۡ وَزِدۡنَٰهُمۡ هُدٗى
Ife tikusimbira (iwe mtumiki{s.a.w}) nkhani zawo mwachoonadi; ndithu iwo adali anyamata amene adakhulupirira Mbuye wawo, ndipo tidawaonjezera chiongoko.
Faccirooji aarabeeji:
وَرَبَطۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ إِذۡ قَامُواْ فَقَالُواْ رَبُّنَا رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ لَن نَّدۡعُوَاْ مِن دُونِهِۦٓ إِلَٰهٗاۖ لَّقَدۡ قُلۡنَآ إِذٗا شَطَطًا
Ndipo tidalimbikitsa mitima yawo pa chikhulupiliro pamene adaimilira (pamaso pa mfumu yawo yosakhulupirira) ndikunena: “Mbuye wathu ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka. Sitipembedza mulungu wina m’malo mwa Iye. Ngati titatero ndiye kuti tanena zoipa zopyola muyeso.
Faccirooji aarabeeji:
هَٰٓؤُلَآءِ قَوۡمُنَا ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةٗۖ لَّوۡلَا يَأۡتُونَ عَلَيۡهِم بِسُلۡطَٰنِۭ بَيِّنٖۖ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا
Awa anthu athu adzipangira milungu ina kusiya Allah, nanga bwanji sakubweretsa pa za iyo (milunguyo) umboni woonekera (wosonyeza kuti iyo ndi milungudi)? Kodi ndani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akupekera bodza Allah?
Faccirooji aarabeeji:
وَإِذِ ٱعۡتَزَلۡتُمُوهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ إِلَّا ٱللَّهَ فَأۡوُۥٓاْ إِلَى ٱلۡكَهۡفِ يَنشُرۡ لَكُمۡ رَبُّكُم مِّن رَّحۡمَتِهِۦ وَيُهَيِّئۡ لَكُم مِّنۡ أَمۡرِكُم مِّرۡفَقٗا
(Adauzana pakati pawo): “Ndipo ngati muwapatuka ndizimene akuzipembedza kusiya Allah, thawirani kuphanga; Mbuye wanu akutambasulirani chifundo Chake ndikukufewetserani zinthu zanu zonse.”
Faccirooji aarabeeji:
۞ وَتَرَى ٱلشَّمۡسَ إِذَا طَلَعَت تَّزَٰوَرُ عَن كَهۡفِهِمۡ ذَاتَ ٱلۡيَمِينِ وَإِذَا غَرَبَت تَّقۡرِضُهُمۡ ذَاتَ ٱلشِّمَالِ وَهُمۡ فِي فَجۡوَةٖ مِّنۡهُۚ ذَٰلِكَ مِنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِۗ مَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَلَن تَجِدَ لَهُۥ وَلِيّٗا مُّرۡشِدٗا
(Zidali tere) ukadakhala ukuliona dzuwa pamene linkatuluka (ndikuyamba kukwera), ukadaliona likulambalala kumbali kwa phanga lawo mbali yakudzanjadzanja, ndipo pamene linkalowa limawadutsa mbali yakumanzere (popanda kuwalunjika) pomwe iwo adali pamtetete mmenemo. Zimenezo ndi zina mwa zisonyezo za Allah (zosonyeza kukhoza Kwake). Amene Allah wamuongola iyeyo ndiye woongoka; ndipo amene wamulekelera kuti asokere, simungampezere mtetezi kapena muongoli.
Faccirooji aarabeeji:
وَتَحۡسَبُهُمۡ أَيۡقَاظٗا وَهُمۡ رُقُودٞۚ وَنُقَلِّبُهُمۡ ذَاتَ ٱلۡيَمِينِ وَذَاتَ ٱلشِّمَالِۖ وَكَلۡبُهُم بَٰسِطٞ ذِرَاعَيۡهِ بِٱلۡوَصِيدِۚ لَوِ ٱطَّلَعۡتَ عَلَيۡهِمۡ لَوَلَّيۡتَ مِنۡهُمۡ فِرَارٗا وَلَمُلِئۡتَ مِنۡهُمۡ رُعۡبٗا
Ndipo ungawaganizire kuti ali maso pomwe iwo ali mtulo, uku tikuwatembenuzira mbali yakumanja ndi yakumanzere (kuti nthaka isadye matupi awo), ukunso galu wawo atatambasula miyendo yake (yakutsogolo) pakhomo. Ngati ukadawaona ukadatembenuka kuwathawa; ndipo ndithu ukadadzadzidwa mantha ndi iwo.
Faccirooji aarabeeji:
وَكَذَٰلِكَ بَعَثۡنَٰهُمۡ لِيَتَسَآءَلُواْ بَيۡنَهُمۡۚ قَالَ قَآئِلٞ مِّنۡهُمۡ كَمۡ لَبِثۡتُمۡۖ قَالُواْ لَبِثۡنَا يَوۡمًا أَوۡ بَعۡضَ يَوۡمٖۚ قَالُواْ رَبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَا لَبِثۡتُمۡ فَٱبۡعَثُوٓاْ أَحَدَكُم بِوَرِقِكُمۡ هَٰذِهِۦٓ إِلَى ٱلۡمَدِينَةِ فَلۡيَنظُرۡ أَيُّهَآ أَزۡكَىٰ طَعَامٗا فَلۡيَأۡتِكُم بِرِزۡقٖ مِّنۡهُ وَلۡيَتَلَطَّفۡ وَلَا يُشۡعِرَنَّ بِكُمۡ أَحَدًا
Ndipo momwemonso tidawautsa kuti afunsane pakati pawo (zanthawi imene akhala ali chigonere). Adanena wonena mwa iwo: “Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?” Adati: “Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku.” (Ena) adati: “Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala. Choncho mtumeni mmodzi wa inu ndindalama zanuzi za siliva kumudzi ndipo akayang’ane chakudya chake nchotani chomwe chili choyera bwino, ndikubwerera nacho chakudyacho; koma izi akachite mochenjera ndipo asamzindikiritse aliyense za inu.”[257]
[257] Omasulira Qur’an adati:- Adalowa kuphangako nthawi yam’bandakucha, ndipo Allah adawaukitsa madzulo. Ichi nchifukwa chake ena ankati akhala theka la tsiku poganizira kuti adakhalamo usana umodzi, pomwe ena amati adakhala tsiku lathunthu. Kenako nati Allah ndi amene akudziwa nyengo imene takhalamo. Ndime iyi ndiumboni waukulu wotsimikiza kuti mizimu ya anthu abwino sidzaona kutalika nyengo yokhalira m’manda.
Faccirooji aarabeeji:
إِنَّهُمۡ إِن يَظۡهَرُواْ عَلَيۡكُمۡ يَرۡجُمُوكُمۡ أَوۡ يُعِيدُوكُمۡ فِي مِلَّتِهِمۡ وَلَن تُفۡلِحُوٓاْ إِذًا أَبَدٗا
“Ndithu iwo akakudziwani (pamene mulipa), akugendani ndi miyala; apo ai akubwezerani ku chipeinbedzo chawo (chopotoka), zikatero ndiye kuti simudzapambananso mpaka kalekale.”
Faccirooji aarabeeji:
وَكَذَٰلِكَ أَعۡثَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ لِيَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَأَنَّ ٱلسَّاعَةَ لَا رَيۡبَ فِيهَآ إِذۡ يَتَنَٰزَعُونَ بَيۡنَهُمۡ أَمۡرَهُمۡۖ فَقَالُواْ ٱبۡنُواْ عَلَيۡهِم بُنۡيَٰنٗاۖ رَّبُّهُمۡ أَعۡلَمُ بِهِمۡۚ قَالَ ٱلَّذِينَ غَلَبُواْ عَلَىٰٓ أَمۡرِهِمۡ لَنَتَّخِذَنَّ عَلَيۡهِم مَّسۡجِدٗا
(Koma anthu anazindikira pamene adaona ndalama yakale), momwemonso tidawazindikiritsa (kwa anthu) kuti adziwe kuti lonjezo la Allah (loukitsa ku imfa zolengedwa) nloona, ndikuti nthawi ya chimaliziro njosakaikitsa, (ndipo kumbukani) pamene adakangana pakati pawo pa chinthu chaochi, ena adati: “Mangani chomanga pa iwo (kuti anthu asamadze kudzawasuzumira), Mbuye wawo za iwo akudziwa bwino, koma amene adapambana paganizo lawolo adanena: “Ndithu ife timanga Msikiti wa iwowa (pa phanga lawoli).”
Faccirooji aarabeeji:
سَيَقُولُونَ ثَلَٰثَةٞ رَّابِعُهُمۡ كَلۡبُهُمۡ وَيَقُولُونَ خَمۡسَةٞ سَادِسُهُمۡ كَلۡبُهُمۡ رَجۡمَۢا بِٱلۡغَيۡبِۖ وَيَقُولُونَ سَبۡعَةٞ وَثَامِنُهُمۡ كَلۡبُهُمۡۚ قُل رَّبِّيٓ أَعۡلَمُ بِعِدَّتِهِم مَّا يَعۡلَمُهُمۡ إِلَّا قَلِيلٞۗ فَلَا تُمَارِ فِيهِمۡ إِلَّا مِرَآءٗ ظَٰهِرٗا وَلَا تَسۡتَفۡتِ فِيهِم مِّنۡهُمۡ أَحَدٗا
(Ena) akhala akunena (kuti) adali anthu atatu, wachinayi ndi galu wawo; ndipo (ena) akuti adali asanu, wachisanu ndichimodzi ndigalu wawo. (Akunena) mwakungoganizira chabe zomwe sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti adali asanu ndi awiri, ndipo wachisanu ndi chitatu ndi galu wawo. Nena: “Mbuye wanga ndiye akudziwa bwinobwino za chiwerengero chawo. Palibe amene akudziwa (za iwo) koma ndi ochepa chabe.” Choncho usatsutsane nawo za iwo, kupatula kutsutsana kwa pa zinthu zodziwika, ndipo usamfunse aliyense mwa iwo za iwo.
Faccirooji aarabeeji:
وَلَا تَقُولَنَّ لِشَاْيۡءٍ إِنِّي فَاعِلٞ ذَٰلِكَ غَدًا
Ndipo usanene ngakhale pang’ono zachilichonse kuti: “Ndichita mawa.”
Faccirooji aarabeeji:
إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ وَٱذۡكُر رَّبَّكَ إِذَا نَسِيتَ وَقُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَهۡدِيَنِ رَبِّي لِأَقۡرَبَ مِنۡ هَٰذَا رَشَدٗا
“Koma (utsogoze liwu lakuti): Insha Allah, (Allah akafuna!)” Ndipo mukumbuke Mbuye wako ukaiwala ponena kuti: “Mwina Mbuye wanga anditsogolera pa njira yapafupi pachiongoko kuposa iyi.”[258]
[258] Ayuda adamufunsa Mneneri (s.a.w) zankhani ya anyamata a kuphangawo. Iye adayankha kuti: “Ndikuuzani mawa,” sadanene kuti Allah akafuna ndikuuzani mawa.”
Choncho chivumbulutso sichidadze kwa iye ndipo anavutika kwambiri kusowa chowauza anthu aja. Kenako Allah adamuuza zoti ngati unena pa chinthu kuti chimenechi ndichichita mawa, nenanso mawu oti ngati Allah afuna.
Faccirooji aarabeeji:
وَلَبِثُواْ فِي كَهۡفِهِمۡ ثَلَٰثَ مِاْئَةٖ سِنِينَ وَٱزۡدَادُواْ تِسۡعٗا
Ndipo adakhala m’phanga lawolo (ali mtulo) zaka zikwi zitatu (300) ndikuonjezera zisanu ndi zinayi (9).
Faccirooji aarabeeji:
قُلِ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا لَبِثُواْۖ لَهُۥ غَيۡبُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ أَبۡصِرۡ بِهِۦ وَأَسۡمِعۡۚ مَا لَهُم مِّن دُونِهِۦ مِن وَلِيّٖ وَلَا يُشۡرِكُ فِي حُكۡمِهِۦٓ أَحَدٗا
Nena: “Allah akudziwa bwinobwino nyengo imene (iwo) adakhala; zobisika za kumwamba ndi za pansi nza Iye (Allah basi); taona Allah kuonetsetsa! Taona Allah kumvetsetsa! (Allah Ngoona chilichonse, ndipo Ngwakumva chilichonse). Ndipo iwo alibe mtetezi popanda Iye (Allah); ndipo Iye sagawira aliyense udindo Wake wakulamula.
Faccirooji aarabeeji:
وَٱتۡلُ مَآ أُوحِيَ إِلَيۡكَ مِن كِتَابِ رَبِّكَۖ لَا مُبَدِّلَ لِكَلِمَٰتِهِۦ وَلَن تَجِدَ مِن دُونِهِۦ مُلۡتَحَدٗا
Ndipo werenga zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe za m’buku la Mbuye wako, palibe amene angathe kusintha mau Ake, ndipo nawe sungapeze potsamira ndi pothawira (kuti Allah asakupeze.)
Faccirooji aarabeeji:
وَٱصۡبِرۡ نَفۡسَكَ مَعَ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ رَبَّهُم بِٱلۡغَدَوٰةِ وَٱلۡعَشِيِّ يُرِيدُونَ وَجۡهَهُۥۖ وَلَا تَعۡدُ عَيۡنَاكَ عَنۡهُمۡ تُرِيدُ زِينَةَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَا تُطِعۡ مَنۡ أَغۡفَلۡنَا قَلۡبَهُۥ عَن ذِكۡرِنَا وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ وَكَانَ أَمۡرُهُۥ فُرُطٗا
Ndipo dzikakamize kukhala pamodzi ndi amene akupempha Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo uku akufunafuna nkhope Yake (chiyanjo Chake), ndipo maso ako asachoke pa iwo ndi (kuyang’ana ena) ncholinga chofuna zokongoletsa za moyo wa dziko lapansi; ndipo usamumvere amene mtima wake tauiwalitsa kutikumbukira ndikumangotsatira zilakolako zake, ndipo zinthu zake nkukhala zotaika (zosalongosoka).[259]
[259] Ndime iyi idavumbulutsidwa pamene Uyaina Bun Huswaini ndi mnzake adadza kwa Mtumiki ndi kumpeza atakhala pamodzi ndi omtsatira (Maswahaba) osauka monga: Ammaru, Suhaibu ndi Bilali ndi ena onga iwo. Iwo adati kwa Mtumiki (s.a.w): “Ukadawapirikitsa anthu wambawa, ndiye kuti tikadakhala nawe nkumamvera zimene ukulalikira. Koma ife tikunyansidwa ndi ulaliki wako poona kuti nthawi zonse ukukhala ndi anthu onyozeka amene simabwana.” Choncho Qur’an idatsika kumuuza Mtumiki (s.a.w) kuti: “Usawathamangitse anthu omwe akupempha Allah m’mawa ndi madzulo ngakhale kuti ndionyozeka.”
Faccirooji aarabeeji:
وَقُلِ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكُمۡۖ فَمَن شَآءَ فَلۡيُؤۡمِن وَمَن شَآءَ فَلۡيَكۡفُرۡۚ إِنَّآ أَعۡتَدۡنَا لِلظَّٰلِمِينَ نَارًا أَحَاطَ بِهِمۡ سُرَادِقُهَاۚ وَإِن يَسۡتَغِيثُواْ يُغَاثُواْ بِمَآءٖ كَٱلۡمُهۡلِ يَشۡوِي ٱلۡوُجُوهَۚ بِئۡسَ ٱلشَّرَابُ وَسَآءَتۡ مُرۡتَفَقًا
Ndipo nena (kwa osakhulupirirawo, kuti): “Ichi ndi choonadi chimene chachokera kwa Mbuye wanu.” Choncho amene afuna, akhulupirire; ndipo amene afuna (kusachikhulupirira) asakhulupirire. Ndithu achinyengo tawakonzera Moto, womwe mipanda yake ikawazinga. Ndipo akakapempha chithandizo (chifukwa cha ludzu loopsya lomwe likawapeza), akathandizidwa popatsidwa madzi (otentha kwambiri) monga madzi a chitsulo chosungunuka, omwe adzasupula nkhope zawo. Taona kuipa chakumwa! ndi kuipa malo wotsamira!
Faccirooji aarabeeji:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ إِنَّا لَا نُضِيعُ أَجۡرَ مَنۡ أَحۡسَنَ عَمَلًا
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, (tidzawalipira pa ubwino wawowo), ndithu Ife sitisokoneza malipiro a amene wagwira ntchito yabwino.
Faccirooji aarabeeji:
أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ جَنَّٰتُ عَدۡنٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمُ ٱلۡأَنۡهَٰرُ يُحَلَّوۡنَ فِيهَا مِنۡ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٖ وَيَلۡبَسُونَ ثِيَابًا خُضۡرٗا مِّن سُندُسٖ وَإِسۡتَبۡرَقٖ مُّتَّكِـِٔينَ فِيهَا عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِۚ نِعۡمَ ٱلثَّوَابُ وَحَسُنَتۡ مُرۡتَفَقٗا
Iwo adzapeza minda yamuyaya; yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; m’menemo adzawakongoletsa powaveka zibangiri za golide, ndipo adzavala nsalu zobiriwira; zasilika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atatsamira makhushoni mmenemo. Taonani kukhala bwino malipiro! Ndi pamalo potsamira pokongola (popeza mpumulo wabwino)!
Faccirooji aarabeeji:
۞ وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلٗا رَّجُلَيۡنِ جَعَلۡنَا لِأَحَدِهِمَا جَنَّتَيۡنِ مِنۡ أَعۡنَٰبٖ وَحَفَفۡنَٰهُمَا بِنَخۡلٖ وَجَعَلۡنَا بَيۡنَهُمَا زَرۡعٗا
Ndipo apatse fanizo la anthu awiri mmodzi wa iwo tidampangira minda iwiri ya mphesa ndi kuizunguliza ndi mitengo ya kanjedza; ndipo pakati pa iyo tidaikapo mbewu (zina).
Faccirooji aarabeeji:
كِلۡتَا ٱلۡجَنَّتَيۡنِ ءَاتَتۡ أُكُلَهَا وَلَمۡ تَظۡلِم مِّنۡهُ شَيۡـٔٗاۚ وَفَجَّرۡنَا خِلَٰلَهُمَا نَهَرٗا
Minda yonse iwiriyi idapatsa zipatso zake ndipo siidapungule chilichonse mzipatso zake. Ndipo pakati pake tidapititsapo mitsinje.
Faccirooji aarabeeji:
وَكَانَ لَهُۥ ثَمَرٞ فَقَالَ لِصَٰحِبِهِۦ وَهُوَ يُحَاوِرُهُۥٓ أَنَا۠ أَكۡثَرُ مِنكَ مَالٗا وَأَعَزُّ نَفَرٗا
Ndipo iye adali ndi chuma (china) nati kwa mnzakeyo mokambirana naye: “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe, (ndilinso) ndi mphamvu zambiri chifukwa cha onditsatira (omwe ndili nawo).”
Faccirooji aarabeeji:
وَدَخَلَ جَنَّتَهُۥ وَهُوَ ظَالِمٞ لِّنَفۡسِهِۦ قَالَ مَآ أَظُنُّ أَن تَبِيدَ هَٰذِهِۦٓ أَبَدٗا
Ndipo adalowa m’munda mwake uku akudzichitira yekha zoipa. Adati: “Sindiganiza ngakhale mpang’ono pomwe kuti (munda) uwu udzaonongeka.”
Faccirooji aarabeeji:
وَمَآ أَظُنُّ ٱلسَّاعَةَ قَآئِمَةٗ وَلَئِن رُّدِدتُّ إِلَىٰ رَبِّي لَأَجِدَنَّ خَيۡرٗا مِّنۡهَا مُنقَلَبٗا
“Ndiponso sindiganiza kuti Qiyâma (chimaliziro) idzachitikadi. Ngati (itapezekadi Kiyamayo), ine nkubwezedwa kwa Mbuye wanga, ndithu ndikapeza malo abwino wobwererako kuposa awa. (Monga momwe ndapezera mwayi kuno, ukonso ndikapeza, ngati Kiyamayo ilikodi).”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ لَهُۥ صَاحِبُهُۥ وَهُوَ يُحَاوِرُهُۥٓ أَكَفَرۡتَ بِٱلَّذِي خَلَقَكَ مِن تُرَابٖ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٖ ثُمَّ سَوَّىٰكَ رَجُلٗا
Mnzake adanena kwa iye mokambirana naye: “Kodi ukumukana yemwe adakulenga ndi dongo, kenako ndi dontho lamadzi a umuna ndiponso adakupanga kukhala munthu wolingana?”
Faccirooji aarabeeji:
لَّٰكِنَّا۠ هُوَ ٱللَّهُ رَبِّي وَلَآ أُشۡرِكُ بِرَبِّيٓ أَحَدٗا
“Koma ine ndikukhulupirira kuti Iye ndi Mulungu Mbuye wanga, ndipo sindiphatikiza aliyense ndi Mbuye wanga.”
Faccirooji aarabeeji:
وَلَوۡلَآ إِذۡ دَخَلۡتَ جَنَّتَكَ قُلۡتَ مَا شَآءَ ٱللَّهُ لَا قُوَّةَ إِلَّا بِٱللَّهِۚ إِن تَرَنِ أَنَا۠ أَقَلَّ مِنكَ مَالٗا وَوَلَدٗا
“Ndipo pamene umalowa m’munda wako ukadanena kuti izi ndi zimene wandifunira Allah, mphamvu sizikadapezeka koma kupyolera mwa Allah (zikadakhala zabwino kwa iwe). Ngati ukundiona ine kuti ndili ndi chuma chochepa ndi ana ochepa kuposa iwe (koma sindisiya kutamanda Allah).”
Faccirooji aarabeeji:
فَعَسَىٰ رَبِّيٓ أَن يُؤۡتِيَنِ خَيۡرٗا مِّن جَنَّتِكَ وَيُرۡسِلَ عَلَيۡهَا حُسۡبَانٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فَتُصۡبِحَ صَعِيدٗا زَلَقًا
“Mwina Mbuye wanga angandipatse zabwino kuposa munda wakowo ndi kuutumizira mliri wachiphaliwali kuchokera kumwamba, ndipo ndikusanduka nthaka yotelera (yoguga).”
Faccirooji aarabeeji:
أَوۡ يُصۡبِحَ مَآؤُهَا غَوۡرٗا فَلَن تَسۡتَطِيعَ لَهُۥ طَلَبٗا
“Kapena madzi ake nkumangophwa kotero kuti sungathe kuwapeza.”
Faccirooji aarabeeji:
وَأُحِيطَ بِثَمَرِهِۦ فَأَصۡبَحَ يُقَلِّبُ كَفَّيۡهِ عَلَىٰ مَآ أَنفَقَ فِيهَا وَهِيَ خَاوِيَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا وَيَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي لَمۡ أُشۡرِكۡ بِرَبِّيٓ أَحَدٗا
Tsono mliri unagwa pa zipatso zakezo (ndikuziononga motheratu), ndipo adayamba kutembenuza manja modandaulira zomwe adaonongera m’menemo; (mindayo) mitengo yake itagwera pansi. Ndipo adati: “Kalanga ine! Ndikadapanda kumphatikiza Mbuye wanga ndi aliyense (zoterezi sizikadachitika.)”
Faccirooji aarabeeji:
وَلَمۡ تَكُن لَّهُۥ فِئَةٞ يَنصُرُونَهُۥ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَمَا كَانَ مُنتَصِرًا
Ndipo sadakhale ndi anthu omthangata pamene Allah adamtaya, ngakhale iye mwini sadadzithandize.
Faccirooji aarabeeji:
هُنَالِكَ ٱلۡوَلَٰيَةُ لِلَّهِ ٱلۡحَقِّۚ هُوَ خَيۡرٞ ثَوَابٗا وَخَيۡرٌ عُقۡبٗا
Pamalo potere chitetezo chimakhala cha Allah Yekha Woona. Iye Ngolipira bwino, ndiponso Wabwino (pakudza) ndi malekezero abwino.
Faccirooji aarabeeji:
وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا كَمَآءٍ أَنزَلۡنَٰهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ فَٱخۡتَلَطَ بِهِۦ نَبَاتُ ٱلۡأَرۡضِ فَأَصۡبَحَ هَشِيمٗا تَذۡرُوهُ ٱلرِّيَٰحُۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ مُّقۡتَدِرًا
Ndipo apatse fanizo la moyo wadziko lapansi, uli ngati madzi amene tikutsitsa kuchokera kumitambo kenako (madziwo) amasakanikirana ndi mmera wa m’nthaka (ndikuyamba kumera mokongola), kenako (mmerawo) nkukhala masamba ouma odukaduka omwe mphepo ikuwaulutsa uku ndi uku. Ndipo Allah ali ndi mphamvu pachilichonse.
Faccirooji aarabeeji:
ٱلۡمَالُ وَٱلۡبَنُونَ زِينَةُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَٱلۡبَٰقِيَٰتُ ٱلصَّٰلِحَٰتُ خَيۡرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابٗا وَخَيۡرٌ أَمَلٗا
Chuma ndi ana ndizokometsera za moyo wa dziko lapansi, koma ntchito zabwino zopitirira ndizo zabwino kwa Mbuye wako, monga mphoto ndi chiyembekezo chabwino.
Faccirooji aarabeeji:
وَيَوۡمَ نُسَيِّرُ ٱلۡجِبَالَ وَتَرَى ٱلۡأَرۡضَ بَارِزَةٗ وَحَشَرۡنَٰهُمۡ فَلَمۡ نُغَادِرۡ مِنۡهُمۡ أَحَدٗا
Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzayendetsa mapiri (powaulutsa ngati ubweya mu mlengalenga), ndipo udzaiona nthaka ili tetetee, (itatambasuka yosakhwinyata ndi mapiri kapena zitunda), ndipo tidzawasonkhanitsa (tsiku limenelo), ndipo sitidzasiya aliyense mwa iwo (oyamba ndi omaliza).
Faccirooji aarabeeji:
وَعُرِضُواْ عَلَىٰ رَبِّكَ صَفّٗا لَّقَدۡ جِئۡتُمُونَا كَمَا خَلَقۡنَٰكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةِۭۚ بَلۡ زَعَمۡتُمۡ أَلَّن نَّجۡعَلَ لَكُم مَّوۡعِدٗا
Ndipo adzabwera nawo kwa Mbuye wako atandanda m’mizere (ndikuuzidwa): “Ndithu mwatidzera monga tidakulengerani pachiyambi (opanda nsapato, amaliseche ndiponso opanda chilichonse chuma ndi ana). Koma mumaganiza kuti sitikuikirani lonjezo (ili louka ku imfa ndi kuweruzidwa).”
Faccirooji aarabeeji:
وَوُضِعَ ٱلۡكِتَٰبُ فَتَرَى ٱلۡمُجۡرِمِينَ مُشۡفِقِينَ مِمَّا فِيهِ وَيَقُولُونَ يَٰوَيۡلَتَنَا مَالِ هَٰذَا ٱلۡكِتَٰبِ لَا يُغَادِرُ صَغِيرَةٗ وَلَا كَبِيرَةً إِلَّآ أَحۡصَىٰهَاۚ وَوَجَدُواْ مَا عَمِلُواْ حَاضِرٗاۗ وَلَا يَظۡلِمُ رَبُّكَ أَحَدٗا
Ndipo kaundula adzaikidwa (pamaso pawo), ndipo udzaaona oipa ali oopa chifukwa cha zomwe zili m’menemo, ndipo adzanena: “Kalanga ife taonongeka! Ngotani kaundula uyu, sasiya chaching’ono ngakhale chachikulu, koma zonse kuzilemba.” Ndipo adzapeza zonse zimene adazichita zitalembedwa m’menemo. Ndipo Mbuye wako sapondereza aliyense (pomusenzetsa zomwe sizake, kapena kumchitira zomwe sizikumuyenera).
Faccirooji aarabeeji:
وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ كَانَ مِنَ ٱلۡجِنِّ فَفَسَقَ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهِۦٓۗ أَفَتَتَّخِذُونَهُۥ وَذُرِّيَّتَهُۥٓ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِي وَهُمۡ لَكُمۡ عَدُوُّۢۚ بِئۡسَ لِلظَّٰلِمِينَ بَدَلٗا
Ndipo (kumbuka) pamene tidawauza angelo: “Mchitireni sijida Adam (mugwadireni momulemekeza).” Onse adachitadi sijida kupatula Iblis. Iye adali mmodzi wa ziwanda, ndipo adatuluka m’chilamulo cha Mbuye wake. Kodi iye ndi mbumba yake mukuwalola kukhala abwenzi (anu) kusiya Ine, pomwe iwo ndiadani anu? Taonani kuipa kusintha kwa anthu oipa!
Faccirooji aarabeeji:
۞ مَّآ أَشۡهَدتُّهُمۡ خَلۡقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَا خَلۡقَ أَنفُسِهِمۡ وَمَا كُنتُ مُتَّخِذَ ٱلۡمُضِلِّينَ عَضُدٗا
Sindidawachite (iwo) kukhala mboni nkulenga kwa thambo ndi nthaka, ngakhale kuwalenga kwawo ndipo sindidawalole osokeretsa kukhala athandizi (Anga).
Faccirooji aarabeeji:
وَيَوۡمَ يَقُولُ نَادُواْ شُرَكَآءِيَ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُمۡ فَدَعَوۡهُمۡ فَلَمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَهُمۡ وَجَعَلۡنَا بَيۡنَهُم مَّوۡبِقٗا
Ndipo (kumbukani) tsiku lomwe (Allah) adzanena: “Aitaneni aja omwe munkandiphatikiza nawo omwe munkati (ndi milungu inzanga).” Choncho, adzaiitana koma siidzawayankha; ndipo tidzaika chionongeko pakati pawo (ndipo sadzakumananso).
Faccirooji aarabeeji:
وَرَءَا ٱلۡمُجۡرِمُونَ ٱلنَّارَ فَظَنُّوٓاْ أَنَّهُم مُّوَاقِعُوهَا وَلَمۡ يَجِدُواْ عَنۡهَا مَصۡرِفٗا
Ndipo woipa adzauona moto (panthawi imeneyo) ndikutsimikiza kuti iwo alowa m’menemo. Ndipo sadzapeza pouzembera.
Faccirooji aarabeeji:
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لِلنَّاسِ مِن كُلِّ مَثَلٖۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ أَكۡثَرَ شَيۡءٖ جَدَلٗا
Ndipo ndithu tawafotokozera anthu mwatsatanetsatane m’Qur’aniyi fanizo la mtundu uliwonse; koma munthu wapambana chinthu chilichonse pa makani.
Faccirooji aarabeeji:
وَمَا مَنَعَ ٱلنَّاسَ أَن يُؤۡمِنُوٓاْ إِذۡ جَآءَهُمُ ٱلۡهُدَىٰ وَيَسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّهُمۡ إِلَّآ أَن تَأۡتِيَهُمۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ أَوۡ يَأۡتِيَهُمُ ٱلۡعَذَابُ قُبُلٗا
Ndipo palibe chimene chaletsa anthu kukhulupirira (tsopano) pamene chiongoko choonadi chawadzera ndikupempha chikhululuko kwa Mbuye wawo, koma akuyembekezera kuti chiwadzere chikhalidwe cha anthu oyamba, kapena chiwadzere chilango masomphenya.
Faccirooji aarabeeji:
وَمَا نُرۡسِلُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّا مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَۚ وَيُجَٰدِلُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِٱلۡبَٰطِلِ لِيُدۡحِضُواْ بِهِ ٱلۡحَقَّۖ وَٱتَّخَذُوٓاْ ءَايَٰتِي وَمَآ أُنذِرُواْ هُزُوٗا
Ndiponso sitituma atumiki (ndi cholinga choti adzetse chilango), koma kuti akhale onena nkhani zabwino ndi ochenjeza. Ndipo amene sadakhulupirire, akuchita makani ndi chabodza kuti kupyolera m’chabodzacho achotse choonadi, ndipo Ayah Zanga ndi zomwe achenjezedwa nazo, akuzichitira chipongwe!
Faccirooji aarabeeji:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ فَأَعۡرَضَ عَنۡهَا وَنَسِيَ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُۚ إِنَّا جَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٗاۖ وَإِن تَدۡعُهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ فَلَن يَهۡتَدُوٓاْ إِذًا أَبَدٗا
Ndindani woipitsitsa kwabasi woposa yemwe akukumbutsidwa ndi Ayah za Mbuye wake, koma iye nkuzinyoza, ndipo nkuiwala (zoipa) zimene manja ake adatsogoza? Ndithu Ife taika m’mitima mwawo zitsekelero kuti asazizindikire. Ndiponso m’makutu mwawo mwalemedwa ndi ugonthi. Ndipo ukawaitanira kuchiongoko (choonadi), salola kuongoka ngakhale pang’ono.
Faccirooji aarabeeji:
وَرَبُّكَ ٱلۡغَفُورُ ذُو ٱلرَّحۡمَةِۖ لَوۡ يُؤَاخِذُهُم بِمَا كَسَبُواْ لَعَجَّلَ لَهُمُ ٱلۡعَذَابَۚ بَل لَّهُم مَّوۡعِدٞ لَّن يَجِدُواْ مِن دُونِهِۦ مَوۡئِلٗا
Ndipo Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri mwini chifundo. Ndipo akadawathira m’dzanja pa zoipa zomwe akhala akuchita, ndiye kuti ndithu akadawapatsa chilango mwachangu; koma iwo ali nalo lonjezo ndipo sadzapeza pothawira paliponse ndikulipewa.
Faccirooji aarabeeji:
وَتِلۡكَ ٱلۡقُرَىٰٓ أَهۡلَكۡنَٰهُمۡ لَمَّا ظَلَمُواْ وَجَعَلۡنَا لِمَهۡلِكِهِم مَّوۡعِدٗا
Ndipo imeneyo ndi midzi tidawaononga (okhalamo) pamene adadzichitira zoipa; ndipo tidawaikira lonjezo la nthawi yoikidwa la kuonongeka kwawo.
Faccirooji aarabeeji:
وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِفَتَىٰهُ لَآ أَبۡرَحُ حَتَّىٰٓ أَبۡلُغَ مَجۡمَعَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ أَوۡ أَمۡضِيَ حُقُبٗا
Ndipo (kumbukani) pamene Mûsa adanena kwa mnyamata wake (Yusha’ Ibn Nun): “Ndipitiriza kuyenda kufikira ndikafike pamajiga pa nyanja ziwiri, kapena ndizingoyenda zaka ndi zaka (kufikira nditakumana naye amene ndikumfunayo).”
Faccirooji aarabeeji:
فَلَمَّا بَلَغَا مَجۡمَعَ بَيۡنِهِمَا نَسِيَا حُوتَهُمَا فَٱتَّخَذَ سَبِيلَهُۥ فِي ٱلۡبَحۡرِ سَرَبٗا
Choncho pamene adafika pamajiga (pa nyanja ziwirizo) adaiwala nsomba yawo yomwe idatenga njira yake kunka m’nyanja ngati una (Mûsa adaiwala kumfunsa mnyamata wake za nsombayo; naye mnyamata adaiwala kumfotokozera Mûsa zomwe zidachitika ndi nsoinbayo).
Faccirooji aarabeeji:
فَلَمَّا جَاوَزَا قَالَ لِفَتَىٰهُ ءَاتِنَا غَدَآءَنَا لَقَدۡ لَقِينَا مِن سَفَرِنَا هَٰذَا نَصَبٗا
Pamene adapita patsogolo, adauza mnyamata wake, (kuti): “Tipatseni chakudya chathu chammawa; ndithu pa ulendo wathuwu takumana ndi zotopetsa.”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ أَرَءَيۡتَ إِذۡ أَوَيۡنَآ إِلَى ٱلصَّخۡرَةِ فَإِنِّي نَسِيتُ ٱلۡحُوتَ وَمَآ أَنسَىٰنِيهُ إِلَّا ٱلشَّيۡطَٰنُ أَنۡ أَذۡكُرَهُۥۚ وَٱتَّخَذَ سَبِيلَهُۥ فِي ٱلۡبَحۡرِ عَجَبٗا
(Mnyamata) adati: “Kodi mwaona pamene tidapumula paja, pathanthwe ndipomwe ndidaiwala (kuti ndikuuzeni) za nsombayo ndipo palibe wandiiwalitsa koma satana basi, kuti ndisaikumbukire. Iyo idatenga njira yake kunka m’nyanja, mododometsa.”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ ذَٰلِكَ مَا كُنَّا نَبۡغِۚ فَٱرۡتَدَّا عَلَىٰٓ ءَاثَارِهِمَا قَصَصٗا
(Mûsa) adati : “Pamenepo ndi pomwe timafuna.” Choncho adabwerera m’mbuyo potsatira njira yawo (yomweyo).
Faccirooji aarabeeji:
فَوَجَدَا عَبۡدٗا مِّنۡ عِبَادِنَآ ءَاتَيۡنَٰهُ رَحۡمَةٗ مِّنۡ عِندِنَا وَعَلَّمۡنَٰهُ مِن لَّدُنَّا عِلۡمٗا
Ndipo adampeza kapolo (Khidwiri) yemwe ndi m’modzi wa akapolo athu amene tidampatsa chifundo chochokera kwa Ife, (yemwenso) tidamphunzitsa maphunziro ambiri kuchokera kwa Ife.
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ لَهُۥ مُوسَىٰ هَلۡ أَتَّبِعُكَ عَلَىٰٓ أَن تُعَلِّمَنِ مِمَّا عُلِّمۡتَ رُشۡدٗا
Mûsa adati kwa iye: “Kodi ndingakutsate kuti undiphunzitse chiongoko chomwe waphunzitsidwa?”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ إِنَّكَ لَن تَسۡتَطِيعَ مَعِيَ صَبۡرٗا
Adati: “Ndithu iwe siutha kupirira nane! (Uwona zomwe sungathe kupirira nazo).”
Faccirooji aarabeeji:
وَكَيۡفَ تَصۡبِرُ عَلَىٰ مَا لَمۡ تُحِطۡ بِهِۦ خُبۡرٗا
“Kodi ungapirire bwanji ndi zinthu zomwe sukuzidziwa chinsinsi chake?”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ صَابِرٗا وَلَآ أَعۡصِي لَكَ أَمۡرٗا
(Mûsa) adati: “Ngati Allah afuna, undipeza ndili wopirira; ndipo sindinyoza lamulo lako.”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ فَإِنِ ٱتَّبَعۡتَنِي فَلَا تَسۡـَٔلۡنِي عَن شَيۡءٍ حَتَّىٰٓ أُحۡدِثَ لَكَ مِنۡهُ ذِكۡرٗا
Adati: “Ngati unditsata usandifunse za chilichonse (chimene uchione) kufikira ine nditakuuza.”
Faccirooji aarabeeji:
فَٱنطَلَقَا حَتَّىٰٓ إِذَا رَكِبَا فِي ٱلسَّفِينَةِ خَرَقَهَاۖ قَالَ أَخَرَقۡتَهَا لِتُغۡرِقَ أَهۡلَهَا لَقَدۡ جِئۡتَ شَيۡـًٔا إِمۡرٗا
Choncho onse awiri adanyamuka kufikira pamene adakakwera m’chombo adachiboola. (Mûsa) adati: “Kodi wachiboola kuti uwamize ali m’menemo? Ndithu wachita chinthu chachikulu choipa.”[260]
[260] Tanthauzo lake nkuti pamene onse awiri adanyamuka adali kuyenda m’mphepete mwanyanja kufikira chombo chidawadutsa. Eni chombowo adamdziwa Khidhiru nawakweza onse awiri popanda malipiro. Atakwera m’chombomo Khidhiru adatenga nkhwangwa ndi kuzula thabwa limodzi la m’chombomo pomwe chombocho chidali pakatikati pa nyanja.
Musa ataona anati: “Bwanji ukuboola chombo pomwe anthuwa atinyamula mwaulere?” Ndipo adatenga kasanza nkuika pomwe panachotsedwa thabwapo.
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ أَلَمۡ أَقُلۡ إِنَّكَ لَن تَسۡتَطِيعَ مَعِيَ صَبۡرٗا
Adati: “Kodi sindidanene kuti iwe sutha kupirira nane?”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ لَا تُؤَاخِذۡنِي بِمَا نَسِيتُ وَلَا تُرۡهِقۡنِي مِنۡ أَمۡرِي عُسۡرٗا
(Mûsa) adati: “Usandidzudzule chifukwa chakuiwala kwanga, ndipo usandipatse zovuta kwambiri pa khumbo langali (lofuna kukutsata).”
Faccirooji aarabeeji:
فَٱنطَلَقَا حَتَّىٰٓ إِذَا لَقِيَا غُلَٰمٗا فَقَتَلَهُۥ قَالَ أَقَتَلۡتَ نَفۡسٗا زَكِيَّةَۢ بِغَيۡرِ نَفۡسٖ لَّقَدۡ جِئۡتَ شَيۡـٔٗا نُّكۡرٗا
Ndipo adanyamuka; mpaka pomwe adakumana ndi mnyamata wochepa, ndipo (mneneri Khidir) adamupha. Mûsa adati: “Ha! Wapha munthu wopanda cholakwa, pomwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu wachita chinthu choipitsitsa.”
Faccirooji aarabeeji:
۞ قَالَ أَلَمۡ أَقُل لَّكَ إِنَّكَ لَن تَسۡتَطِيعَ مَعِيَ صَبۡرٗا
۞ Adati: “Kodi sindidakuuze (kuti) ndithu iwe sutha kupirira nane?”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ إِن سَأَلۡتُكَ عَن شَيۡءِۭ بَعۡدَهَا فَلَا تُصَٰحِبۡنِيۖ قَدۡ بَلَغۡتَ مِن لَّدُنِّي عُذۡرٗا
(Mûsa) adati: “Ngati ndikufunsanso chilichonse pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Ndiye kuti wakwaniritsa dandaulo lako pa ine.”
Faccirooji aarabeeji:
فَٱنطَلَقَا حَتَّىٰٓ إِذَآ أَتَيَآ أَهۡلَ قَرۡيَةٍ ٱسۡتَطۡعَمَآ أَهۡلَهَا فَأَبَوۡاْ أَن يُضَيِّفُوهُمَا فَوَجَدَا فِيهَا جِدَارٗا يُرِيدُ أَن يَنقَضَّ فَأَقَامَهُۥۖ قَالَ لَوۡ شِئۡتَ لَتَّخَذۡتَ عَلَيۡهِ أَجۡرٗا
Choncho adamuka; kufikira pamene adawapeza eni mudzi ndipo adawapempha eni mudziwo chakudya, koma adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo adapezamo khoma lili pafupi kugwa, (ndipo Khidhiriyo) adaliimika. (Mûsa) adati: “Ngati ukadafuna, ukadalandira malipiro (pa ntchitoyi kuti tigulire chakudya).”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ هَٰذَا فِرَاقُ بَيۡنِي وَبَيۡنِكَۚ سَأُنَبِّئُكَ بِتَأۡوِيلِ مَا لَمۡ تَسۡتَطِع عَّلَيۡهِ صَبۡرًا
(Khidhiri) adati: “Awa ndiwo malekano pakati pa ine ndi iwe. Tsopano ndikuuza tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”[261]
[261] Mtumiki Muhammad (s.a.w) adati pankhani iyi ya Musa ndi Khidhiri: “Allah amchitire chifundo Musa. Ndikulakalaka kuti iye akadapilira kukhala limodzi ndi mnzakeyo, akadaona zodabwitsa, ndipo Allah akadatisimbira zambiri za iwo.”
Faccirooji aarabeeji:
أَمَّا ٱلسَّفِينَةُ فَكَانَتۡ لِمَسَٰكِينَ يَعۡمَلُونَ فِي ٱلۡبَحۡرِ فَأَرَدتُّ أَنۡ أَعِيبَهَا وَكَانَ وَرَآءَهُم مَّلِكٞ يَأۡخُذُ كُلَّ سَفِينَةٍ غَصۡبٗا
“Tsopano chombo chija, chidali cha masikini ogwira ntchito pa nyanja, ndipo ndidafuna kuchiononga (mwadala) chifukwa patsogolo pawo padali mfumu yomwe imatenga chombo chilichonse (chabwino) molanda.”
Faccirooji aarabeeji:
وَأَمَّا ٱلۡغُلَٰمُ فَكَانَ أَبَوَاهُ مُؤۡمِنَيۡنِ فَخَشِينَآ أَن يُرۡهِقَهُمَا طُغۡيَٰنٗا وَكُفۡرٗا
“Ndipo mnyamata uja, makolo ake adali okhulupirira, ndipo tidaopera kuti angawachititse zoipa (makolo akewo) ndi za kusakhulupirira (mwa Allah).
Faccirooji aarabeeji:
فَأَرَدۡنَآ أَن يُبۡدِلَهُمَا رَبُّهُمَا خَيۡرٗا مِّنۡهُ زَكَوٰةٗ وَأَقۡرَبَ رُحۡمٗا
Choncho tidafuna kuti Mbuye wawo awasinthire ndi wabwino kuposa iye pa kuyera, ndi wachifundo chapafupi (kwa makolo ake.)”
Faccirooji aarabeeji:
وَأَمَّا ٱلۡجِدَارُ فَكَانَ لِغُلَٰمَيۡنِ يَتِيمَيۡنِ فِي ٱلۡمَدِينَةِ وَكَانَ تَحۡتَهُۥ كَنزٞ لَّهُمَا وَكَانَ أَبُوهُمَا صَٰلِحٗا فَأَرَادَ رَبُّكَ أَن يَبۡلُغَآ أَشُدَّهُمَا وَيَسۡتَخۡرِجَا كَنزَهُمَا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ وَمَا فَعَلۡتُهُۥ عَنۡ أَمۡرِيۚ ذَٰلِكَ تَأۡوِيلُ مَا لَمۡ تَسۡطِع عَّلَيۡهِ صَبۡرٗا
“Tsopano chipupa chija, chidali cha ana awiri amasiye mu mzindamo; ndipo pansi pake padali chuma chawo (chimene adawasiira bambo wawo) ndipo tate wawo adali munthu wabwino choncho Mbuye wako adafuna kuti akule misinkhu yawo ndipo adzadzitulutsire chuma chawocho; ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo ine sindidachite zinthu zimenezi mwandekha. Limenelo ndilo tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”[262]
[262] Nkhani ya Musa ndi Al-Khidhiri yomwe ikupezeka mu Sahihi Bukhari ndi Muslim, Ubayu bun Kaabi adailandira kuchokera kwa Mtumiki wa Allah (s.a.w) kuti iye adati: “Ndithudi, Musa adaimilira kulalikira kwa ana a Isiraeli, ndipo adamufunsa kuti: “Ndani mwa anthu yemwe ngodziwa kwambiri?” Iye adati: “Ndine.” Ndipo Allah adamudzudzula pa yankho lake lotere. Choncho Allah adamuzindikiritsa iye nati: “Ndithu ine ndilinaye kapolo pamajiga panyanja ziwiri yemwe ngodziwa kwambiri kuposa iwe”.
Musa adati: “E Mbuye wanga! Ndingampeze bwanji iyeyo”? Allah adati: ‘Tenga nsomba, uiike muswanda (Basikete). Pamene nsombayo ikakusowe, ndiye kuti iye ali pamenepo.” Tero Musa pamodzi ndi mnyamata wake (Yusha Bun Nun) adaubutsa ulendo mpaka kukafika pa thanthwe. Adasamiritsa mitu yawo pamenepo mpaka kugona tulo. Ndipo nsomba idapiripita m’swanda muja, nkutuluka kukagwera mnyanja. Koma Allah adamanga kuyenda kwa madzi pamene nsombayo idagwera adangounjikana chimulu pompo.
Pamene adauka, mnyamata uja adaiwala kumuuza za nsombayo, naayenda usana ndi usiku kufikira mmawa mwake mwa tsiku limenelo. Musa adati kwa mnyamata wake, “Tipatseni chakudya chathu cham’mawa; ndithu tapeza zotopetsa pa ulendo wathupa.” Adati Musa sadamve kutopa kufikira pamene adadutsa pamalo pomwe Allah adamulamulapo. Mnyamata wake adati: “Kodi mwaona? Titafika pathanthwe ine ndidaiwala nkhani ya nsomba ija. Komatu palibe amene wandiiwalitsa kuikumbukira, koma satana basi. Idatenga njira yake kunka m’nyanja mododometsa.” Musa adati: “Pamenepo mpomwe timafuna.” Choncho adabwerera kulondola mapazi awo mpaka kukafika pathanthwe lija. Apo adaona munthu atadzifundika nsalu. Musa adampatsa salaamu, ndipo Al-Khidhiri adati: “Yachokera kuti salaamu yotere m’dziko lako! Kodi ndiwe yani? Adati “Ine ndine Musa.” Iye adati Musa wa ana a Isiraeli?” Musa adavomera kuti inde, ndadza kuti mundiphunzitse zomwe mwaphunzitsidwa za chiongoko.” Munthu uja adati: “Ndithudi, iwe suutha kupilira nane chifukwa ine ndili ndi maphunziro anga omwe Allah wandiphunzitsa, amene iwe sukuwadziwa.” Musa adati; “Undipeza ndili wopilira ngati Allah afuna. Sindinyoza chilichonse cha iwe. Al-Khidhiri adati kwa iye: “Ngati unditsatedi usandifunse kufikira nditakufotokozera.” Choncho onse awiri adachoka nayenda m’mphepete mwanyanja. Chidawadutsa chombo ndipo adawalankhula eni chombowo kuti awanyamule. Eni chombowo adamdziwa Al-Khidhiri ndipo adawanyamula popanda malipiro. Atakwera m’chombomo Al-Khidhiri adagulula thabwa la chombocho ndi nkhwangwa.
Musa adati: “Nchiyani ichi; anthuwa atitenga popanda malipiro ndiye ukuboola chombo chawo? Kodi ukufuna kuti uwamize eni chombowo? Ndithudi, wachita chinthu choipa kwambiri.” Kenaka adachoka m’chombo muja nayamba kuyenda m’phepete mwanyanja. Pompo Al-Khidhiri adaona mwana akusewera ndi mzake ndipo adamgwira mwana uja mutu wake ndikuuzula, nkumpheratu. Musa adati kwa iye: “Bwanji wapha munthu wosalakwa yemwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu wachita chinthu chonyansa kwabasi,”. Munthu uja adati; “Kodi sindidakuuze kuti sutha kupilira nane”? Musa adati: “Ngati ndikufunsanso chinthu china pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Apo tsono ndiye kuti kundidandaula kwako kwakwanira pa ine.” Tero adachoka mpaka kufika pamudzi wina. Apo adapempha chakudya kwa eni mudziwo. Adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo kenaka adapeza khorna lili pafupi kugwa, Al-Khidhiri adati ndi mkono wake “Ima chonchi,” - polilozera ndi mkono wake. Ndipo lidaimadi njoo!. Musa adati: “Ha! Anthu akuti tawadzera pamudzi, ndipo sanatipatse chakudya sanatilandirenso ngati alendo! Apatu ukadafuna ukadaitanitsa malipiro.” Munthu uja adati: “Awa ndiwo malekano a iwe ndi ine. Komabe ndikuuza matanthauzo a zomwe sudathe kupilira nazo.”
Izi ndi zina zododometsa za Allah zomwe amazichita kupyolera m’manja mwa anthu ake olungama. Ngati tidzakhala olungama ndiye kuti Allah adzatipatsa mphamvu zochita zinthu zododometsa.
Faccirooji aarabeeji:
وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَن ذِي ٱلۡقَرۡنَيۡنِۖ قُلۡ سَأَتۡلُواْ عَلَيۡكُم مِّنۡهُ ذِكۡرًا
Ndipo akukufunsa nkhani za Thul-Qarnain. Auze: “Ndikulakatulirani zina mwa nkhani zake.”
Faccirooji aarabeeji:
إِنَّا مَكَّنَّا لَهُۥ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَءَاتَيۡنَٰهُ مِن كُلِّ شَيۡءٖ سَبَبٗا
Ndithu tidampatsa mphamvu zokhalira pa dziko ndikumpatsa njira yopezera chilichonse.
Faccirooji aarabeeji:
فَأَتۡبَعَ سَبَبًا
Choncho adatsata njira.
Faccirooji aarabeeji:
حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ مَغۡرِبَ ٱلشَّمۡسِ وَجَدَهَا تَغۡرُبُ فِي عَيۡنٍ حَمِئَةٖ وَوَجَدَ عِندَهَا قَوۡمٗاۖ قُلۡنَا يَٰذَا ٱلۡقَرۡنَيۡنِ إِمَّآ أَن تُعَذِّبَ وَإِمَّآ أَن تَتَّخِذَ فِيهِمۡ حُسۡنٗا
Mpaka pomwe adafika kumlowero kwa dzuwa (ku maiko a kuzambwe), adaliona (ngati) likulowa pa dziwe la matope ambiri. Ndipo pompo adapeza anthu; tidati: “E iwe Thul-Qarnain! Alange, kapena achitire zabwino.”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ أَمَّا مَن ظَلَمَ فَسَوۡفَ نُعَذِّبُهُۥ ثُمَّ يُرَدُّ إِلَىٰ رَبِّهِۦ فَيُعَذِّبُهُۥ عَذَابٗا نُّكۡرٗا
Adati: “Koma amene achita zosalungama timulanga; ndipo kenako adzabwezedwa kwa Mbuye wake; ndipo akamukhaulitsa ndi chilango choipa.
Faccirooji aarabeeji:
وَأَمَّا مَنۡ ءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَلَهُۥ جَزَآءً ٱلۡحُسۡنَىٰۖ وَسَنَقُولُ لَهُۥ مِنۡ أَمۡرِنَا يُسۡرٗا
Koma amene akhulupirire ndikuchita ntchito zabwino, apeza mphoto yabwino; ndipo timuuza zomwe zili zofewa m’zinthu zathu.”
Faccirooji aarabeeji:
ثُمَّ أَتۡبَعَ سَبَبًا
Kenako adatsata njira.
Faccirooji aarabeeji:
حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ مَطۡلِعَ ٱلشَّمۡسِ وَجَدَهَا تَطۡلُعُ عَلَىٰ قَوۡمٖ لَّمۡ نَجۡعَل لَّهُم مِّن دُونِهَا سِتۡرٗا
Mpaka adafika ku mtulukiro kwa dzuwa (ku maiko akuvuma). Adalipeza (dzuwalo) likuwatulukira anthu omwe sitidawaikire chowatchinga ku ilo.
Faccirooji aarabeeji:
كَذَٰلِكَۖ وَقَدۡ أَحَطۡنَا بِمَا لَدَيۡهِ خُبۡرٗا
Momwemo, tidali kudziwa bwino nkhani zonse zomwe zidali ndi iye.
Faccirooji aarabeeji:
ثُمَّ أَتۡبَعَ سَبَبًا
Kenako adatsata njira.
Faccirooji aarabeeji:
حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ بَيۡنَ ٱلسَّدَّيۡنِ وَجَدَ مِن دُونِهِمَا قَوۡمٗا لَّا يَكَادُونَ يَفۡقَهُونَ قَوۡلٗا
Mpaka pomwe adafika pakatikati pa mapiri awiri adapeza pafupi ndi mapiriwo anthu omwe sikudali kwapafupi kumva chiyankhulo.
Faccirooji aarabeeji:
قَالُواْ يَٰذَا ٱلۡقَرۡنَيۡنِ إِنَّ يَأۡجُوجَ وَمَأۡجُوجَ مُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَهَلۡ نَجۡعَلُ لَكَ خَرۡجًا عَلَىٰٓ أَن تَجۡعَلَ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَهُمۡ سَدّٗا
Adati: “E iwe Zul-Qarnain! Ndithu Yaajuju ndi Maajuju akuononga pa dziko. Kodi sikungatheke kuti tikupatse malipiro kuti uike pakati pathu ndi pakati pawo, chotchinga (mpanda)?”
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ مَا مَكَّنِّي فِيهِ رَبِّي خَيۡرٞ فَأَعِينُونِي بِقُوَّةٍ أَجۡعَلۡ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُمۡ رَدۡمًا
(Iye) adati: “Zomwe Mbuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi mphamvu zanu (zonse pantchito imeneyi) ndiika chotchinga cholimba pakati panu ndi pakati pawo.”
Faccirooji aarabeeji:
ءَاتُونِي زُبَرَ ٱلۡحَدِيدِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا سَاوَىٰ بَيۡنَ ٱلصَّدَفَيۡنِ قَالَ ٱنفُخُواْۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَعَلَهُۥ نَارٗا قَالَ ءَاتُونِيٓ أُفۡرِغۡ عَلَيۡهِ قِطۡرٗا
“Ndipatseni zidutswa za zitsulo.” Kufikira pamene adadzaza ndi zitsulozo mpata umene udalipo pakati pa mapiri awiriwo, adati: “Pemelerani (moto).” Mpaka (chitsulocho) chidafiira monga moto, adati: “Ndibweretsereni mtovu wosungunuka ndiuthire pamwamba pake (pa chitsulocho).”
Faccirooji aarabeeji:
فَمَا ٱسۡطَٰعُوٓاْ أَن يَظۡهَرُوهُ وَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ لَهُۥ نَقۡبٗا
Choncho (Yaajuju ndi Maajuju) sadathe kukwera pamwamba pake, ndiponso sadathe kuchiboola.
Faccirooji aarabeeji:
قَالَ هَٰذَا رَحۡمَةٞ مِّن رَّبِّيۖ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ رَبِّي جَعَلَهُۥ دَكَّآءَۖ وَكَانَ وَعۡدُ رَبِّي حَقّٗا
(Iye) adati: “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wanga; koma likadzafika lonjezo la Mbuye wanga (kudza kwa Qiyâma), adzachiswanyaswanya; ndipo lonjezo la Mbuye wanga nloona.”
Faccirooji aarabeeji:
۞ وَتَرَكۡنَا بَعۡضَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ يَمُوجُ فِي بَعۡضٖۖ وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَجَمَعۡنَٰهُمۡ جَمۡعٗا
Ndipo patsiku limenelo tidzawasiya ena a iwo (oipa) akuchita chipolowe pa ena; ndipo lidzaimbidwa lipenga. Pamenepo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi.
Faccirooji aarabeeji:
وَعَرَضۡنَا جَهَنَّمَ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡكَٰفِرِينَ عَرۡضًا
Ndipo tsiku limenelo, tidzayionetsa poyera Jahannam kwa osakhulupirira.
Faccirooji aarabeeji:
ٱلَّذِينَ كَانَتۡ أَعۡيُنُهُمۡ فِي غِطَآءٍ عَن ذِكۡرِي وَكَانُواْ لَا يَسۡتَطِيعُونَ سَمۡعًا
(Osakhulupirira) omwe maso awo adali ophimbidwa pakusalabadira ulaliki Wanga, ndipo sadali kutha kumva (zimene akuuzidwa).
Faccirooji aarabeeji:
أَفَحَسِبَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَن يَتَّخِذُواْ عِبَادِي مِن دُونِيٓ أَوۡلِيَآءَۚ إِنَّآ أَعۡتَدۡنَا جَهَنَّمَ لِلۡكَٰفِرِينَ نُزُلٗا
Kodi osakhulupirira akuganiza kuti angawasandutse akapolo Anga kukhala atetezi kusiya Ine? Ndithu taikonza Jahannam kukhala malo ofikirapo osakhulupirira.
Faccirooji aarabeeji:
قُلۡ هَلۡ نُنَبِّئُكُم بِٱلۡأَخۡسَرِينَ أَعۡمَٰلًا
Nena: “Kodi tikudziwitseni eni kuluza (kulephera) pa zochita zawo?”
Faccirooji aarabeeji:
ٱلَّذِينَ ضَلَّ سَعۡيُهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَهُمۡ يَحۡسَبُونَ أَنَّهُمۡ يُحۡسِنُونَ صُنۡعًا
“Iwo ndi omwe khama lawo lataika m’moyo wa pa dziko lapansi, pomwe iwowo akuganiza kuti akuchita zabwino”.[263]
[263] M’ndime iyi akutiuza kuti amene sadakhulupirire Allah, pa tsiku lachimaliziro ndiye kuti zonse zochita zawo zidzakhala zowonongeka. Ntchito zabwino za munthu kuti zikalandiridwe kwa Allah, poyamba akhulupirire Allah ndiponso akhulupirire kuti tsiku lachimaliziro lilipo. Koma ngati sakhulupilira, ndiye kuti zochita zake sizikayesedwa pasikelo koma akangomponya kung’anjo yamoto. Pankhaniyi Mtumiki (s.a.w) adati: “Tsiku la Qiyâma padzabwera munthu wamtali, wakudyabwino, wakumwa zomwaimwa, koma kwa Allah adzakhala wopepuka wosafanana ngakhale ndikulemera kwa phiko la udzudzu.” Hadisiyi adainena ndi Al -Hafizi Ibn Hajar m’buku la Fatuhul Bari, Volume 8 tsamba la 324.
Faccirooji aarabeeji:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ وَلِقَآئِهِۦ فَحَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡ فَلَا نُقِيمُ لَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَزۡنٗا
Iwowo ndi amene sadakhulupirire zisonyezo za Mbuye wawo, ndipo (sadakhulupirire) zakukumana Naye. Choncho zochita zawo zaonongeka (zapita pachabe), ndipo pa tsiku la chiweruziro sitidzawaikira sikelo.
Faccirooji aarabeeji:
ذَٰلِكَ جَزَآؤُهُمۡ جَهَنَّمُ بِمَا كَفَرُواْ وَٱتَّخَذُوٓاْ ءَايَٰتِي وَرُسُلِي هُزُوًا
Zimenezo, mphoto yawo ndi Jahannam chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, ndipo Ayah Zanga ndi atumiki Anga adazichitira chipongwe.
Faccirooji aarabeeji:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ كَانَتۡ لَهُمۡ جَنَّٰتُ ٱلۡفِرۡدَوۡسِ نُزُلًا
Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, malo awo ofikira adzakhala ku minda ya “Firdaus.”
Faccirooji aarabeeji:
خَٰلِدِينَ فِيهَا لَا يَبۡغُونَ عَنۡهَا حِوَلٗا
Adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo sadzafuna kuchokamo.
Faccirooji aarabeeji:
قُل لَّوۡ كَانَ ٱلۡبَحۡرُ مِدَادٗا لِّكَلِمَٰتِ رَبِّي لَنَفِدَ ٱلۡبَحۡرُ قَبۡلَ أَن تَنفَدَ كَلِمَٰتُ رَبِّي وَلَوۡ جِئۡنَا بِمِثۡلِهِۦ مَدَدٗا
Nena: “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo (nyanjazo zikadatha, mawu a Allah akalipobe).”
Faccirooji aarabeeji:
قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يُوحَىٰٓ إِلَيَّ أَنَّمَآ إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۖ فَمَن كَانَ يَرۡجُواْ لِقَآءَ رَبِّهِۦ فَلۡيَعۡمَلۡ عَمَلٗا صَٰلِحٗا وَلَا يُشۡرِكۡ بِعِبَادَةِ رَبِّهِۦٓ أَحَدَۢا
Nena: “Ndithu ine ndi munthu monga inu, (chosiyana nchakuti) ine ndikupatsidwa chivumbulutso (chonena kuti) ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi Yekha. Ndipo amene afuna kukumana ndi Mbuye wake, achite zochita zabwino ndipo asaphatikizepo aliyense pa mapemphero a Mbuye wake.”
Faccirooji aarabeeji:
 
Firo maanaaji Simoore: Simoore wimmboolo hayre
Tippudi cimooje Tonngoode hello ngoo
 
Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Firo siisiiwo - Tippudi firooji ɗii

Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo fayde e ɗemngal siisii, fari ɗum ko Kaaliid piitalaa. Tummbutere hitaande 2020

Uddude