Lamulo la Allah lidzafika, (ndithu) choncho, musalifulumizitse; (ndipo khulupirirani kuti Iye ndi Allah) Woyera Wopatukana ndi mbiri zopunguka, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo.
Amatumiza angelo pansi pamodzi ndi chivumbulutso mwa lamulo Lake (Allah), kwa omwe wawafuna mwa akapolo Ake (powauza) kuti: “Achenjezeni (anthu zakuti): ‘Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha, choncho ndiopeni.”
Adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna. Ha! kenaka iye (munthuyo) wakhala wotsutsana naye (Allah) woonekera.[247]
[247] Apa Allah akunenetsa kuti adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna wopanda pake. Koma munthu pambuyo pokwanira chilengedwe chake akukhala wotsutsana ndi Mlengi wake ndi kumchitira mwano modzitukumula chikhalirecho adalengedwa kuti akhale kapolo wa Allah, osati wopikisana naye.
Ndipo ndi udindo wa Allah kusonyeza njira yolungama (yomwe ingakufikitseni ku Munda wamtendere), koma zilipo njira zina zokhota (zomwe sizifikitsa ku choonadi). Ndipo Allah akadafuna, akadakuongolani nonsenu (mwa chifuniro chanu ndi mopanda chifuniro chanu. Koma Iye adakupatsani nzeru kuti musankhe nokha njira imene mufuna).
Ndi madzi omwewo amakumeretserani mmera, (mitengo ya) mzitona, kanjedza, mphesa, ndi mitundu ina yonse ya zipatso. Ndithu kupezeka kwa zimenezi ndi chisonyezo (chosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu olingalira.[248]
[248] Ndithudi, m’kutsika kwa madzi kuchokera ku mitambo ndi kumeretsa zipatso, muli zisonyezo zoonekera poyera kukhoza kwa Allah ndi umodzi wake kwa anthu omwe amalingalira za zolengedwa Zake. Ndipo potero amakhulupilira Allah Kodi simukuona mbewu imodzi ikaikidwa m’nthaka ndi kupitapo nyengo yodziwika, imafunafuna potulukira ndi kung’amba nthaka ndi kukula kusanduka mtengo? Zonsezi nzododometsa kwa anthu olingalira.
Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi Yekha; koma amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, mitima yawo ikukana (kukhulupirira umodzi wa Allah), ndipo iwo akudzitukumula.
Ndipo kukanenedwa kwa omwe akuopa Allah (kuti): “Kodi nchiyani watumiza Mbuye wanu?” Amati: “Zabwino.” Kwa omwe achita zabwino padziko ili lapansi, awapatsanso zabwino, ndipo Nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwambiri, ndipo taonani ubwino wa Nyumba ya oopa (Allah)!
Ndipo ndithu ku mtundu uliwonse tidatumiza mtumiki (amene amawauza kuti): “Pembedzani Allah, ndi kumpewa (Iblis) woipa.” Choncho alipo ena mwa iwo omwe Allah adawaongola, ndipo alipo ena mwa iwo omwe kusokera kudatsimikizika pa iwo. Choncho yendani pa dziko ndikuyang’ana (kuti) kodi adali bwanji mathero a otsutsa.
Ndipo iwo adalumbilira m’dzina la Allah, kulumbilira kwawo kwamphamvu (kuti) Allah sadzaukitsa amene afa; nchotani (kuti asawaukitse?) Ili ndi lonjezo lokakamizika kwa Iye, (kuwaukitsa ndi kuwalipira); koma anthu ambiri sadziwa.
Kodi sadaone chinthu chilichonse (molingalira) m’zimene Allah adalenga zomwe zithuzi zake zimazungulira kudzanjadzanja ndi kumanzere, kulambira Allah uku zili zodzichepetsa kwa Iye? (Nanga iwo osakhulupirira akudzikweza chotani pamaso pa Allah?)
Ndipo (mwaumbuli) akumuikira Allah ana aakazi (ponena kuti adabereka ana aakazi) Subuhana! (Wayera Allah kuzimenezi!) Ndipo iwo (eni) amadzifunira amene amawakonda (omwe ndi ana achimuna)!
Palibe chikaiko, m’ziweto muli phunziro ndi lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwa izo, (zomwe zimatuluka) pakati pa ndowe ndi magazi, (omwe ndi) mkaka woyera, wabwino wokoma kwa oumwa.
Ndipo Allah wapereka zopereka Zake mochuluka kwa ena kuposa ena; ndipo amene apatsidwa mochulukawo sangagawire zopatsidwa zawo omwe manja awo adzanjadzanja apeza (akapolo awo) kuti akhale ofanana pa zopatsidwazo, (nanga bwanji inu mukuti Allah ngofanana ndi akapolo Ake pomwe inu simufuna kufanana ndi akapolo anu?) Nanga kodi mtendere wa Allah akuukana?
Ndiponso Allah adakulengerani akazi a mtundu wanu, ndipo adakupangirani ana ndi zidzukulu kuchokera mwa akazi anuwo; ndipo adakupatsani zinthu zabwinozabwino, kodi akukhulupirira zachabe, ndi kuchikana chisomo cha Allah?
Allah akuponya fanizo la (anthu awiri: Wina ndi) kapolo wopatidwa (wokhala pansi pa ulamuliro wa munthu wina); yemwe alibe mphamvu pa chilichonse; ndi (munthu) yemwe tampatsa zabwino zochokera kwa Ife, ndipo iye nkupereka rizqlo mobisa ndi moonekera; kodi angafanane (awiriwa? Nanga bwanji mukufananitsa Allah ndi mafano?) Kuyamikidwa konse nkwa Allah. Koma ambiri aiwo sadziwa (kuyamika Allah).
Ndipo Allah waponyanso fanizo la anthu (ena) awiri: Mmodzi ndi bubu (wosatha kuyankhula), alibe mphamvu pa chilichonse; ndipo iye ndi mtolo wolemetsa chabe bwana wake; kulikonse kumene wamulunjikitsa, sabwerako ndi chabwino (chifukwa cha umbutuma wake). Kodi iye angafanane ndi yemwe akulamula mwa chilungamo, yemwenso ali pa njira yolunjika?
Ndipo Allah adakuikirani nyumba zanu kuti zikhale mokhala (mwanu), ndiponso adakupangirani zikopa za ziweto (kukhala zotheka kuzikonza) kukhala nyumba, zomwe mumaziona kuti nzopepuka kuzitenga panthawi Ya ulendo wanu ndi panthawi ya kukhazikika kwanu (pamalo); ndipo kuchokera ku bweya wake wautaliutali ndi bweya wake wa manyunyu (ung’onoung’ono), ndi tsitsi lake (la ziwetozo,) mumakonza ziwiya (zovala) zosangalatsa, kwa kanthawi.
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse zochokera mwa iwo omwe adzawachitira umboni (pa zomwe zinkachitika ndi iwo); ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni pa awa (anthu ako); ndiponso takuvumbulutsira buku ili lomwe likufotokoza za chinthu chilichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere ndiponso ndinkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Allah).
Ndithudi, Allah akulamula (kuchita) chilungamo, ndikuchita zabwino, ndi kupatsa achinansi, ndipo akuletsa zauve ndi zoipa ndi kupyola malire; akukulangizani kuti muzindikire ndi kukumbukira.
Ndipo musagulitse mapangano a Allah ndi mtengo wochepa (wa zomwe mukupeza pano pa dziko lapansi). Chimene chili kwa Allah, ndicho chabwino kwa inu ngati mukudziwa.
Amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali wokhulupirira timkhazika ndi moyo wabwino (pano pa dziko, ndi tsiku la Qiyâma) tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe ankachita.
Ndipo tikasintha Ayah (ndime) ndikubwera ndi Ina pamalopo, pomwe Allah akudziwa zimene akuvumbulutsa, akunena: “Ndithu iwe ndiwe wopeka.” Koma ambiri a iwo sadziwa (chilichonse).
Amene akukana Allah, pambuyo pomukhulupirira, (chilango chachikulu chikumuyembekezera), kupatula yemwe adakakamizidwa, uku mtima wake utakhazikika pa chikhulupiliro; koma amene akutsekulira mtima wake kusakhulupirira, mkwiyo wa Allah uli pa iwo (ndipo anthu otere) adzapata chilango chachikulu.[252]
[252] Omasulira Qur’an akunena kuti ndime iyi idatsika chifukwa cha Ammar Bun Yasir. Opembedza mafano adamgwira ndi kumuvutitsa zedi kufikira iye adawapatsa chomwe iwo ankafuna kwa iye momkakamiza kutero. Anthu adati: “Ndithudi, Ammar watuluka m’Chisilamu.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Ndithudi, Ammar ngodzaza ndi chikhulupiliro kuyambira kumutu mpaka kumapazi. Chikhulupiliro chasakanikirana ndi minofu ndi magazi ake.” Zitatero Ammar adabwera kwa Mtumiki (s.a.w) uku akulira. Mtumiki (s.a.w) adati kwa iye: “Kodi ukupeza bwanji mtima wako?” Iye adati: “Ngokhazikika pa chikhulupiliro.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Ngati abwereranso iwenso bwerezanso zimene wanenazo.”
Iwo ndi omwe Allah adawadinda m’mitima mwawo, m’makutu mwawo, ndi m’maso mwawo (chifukwa cha kusimbwa kwawo). Ndipo iwo ngonyalanyaza (malamulo a Allah) kwambiri.
Ndipo Allah waponya fanizo lamudzi womwe udakhala mwa mtendere mokhazikika, rizq lake (madalitso) linkaudzera mochuluka kuchokera malo aliwonse; koma (mudziwo) udakana mtendere wa Allah (pakusathokoza); choncho Allah adaulawitsa chovala cha njala ndi mantha chifukwa cha (zoipa) zomwe (anthu ake) adali kuchita.
Ndithu Ibrahim adali mtsogoleri (chitsanzo chabwino kwa anthu), womvera Allah, wopendekera ku choonadi ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano).
Kenako takuvumbulutsira (iwe Muhammad{s.a.w} mawu) akuti: “Tsatira njira (chipembedzo) ya Ibrahim (yemwe adali) wokwanira mkulungama, ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano.)”
Ndithudi Sabata idaikidwa kwa amene adatsutsana pa za iyo (Sabatayo); ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zomwe adali kusiyana.
Itanira (anthu) ku njira ya Mbuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino; ndipo tsutsana nawo mkutsutsana kwabwino (osati motukwanana kapena monyozana). Ndithu Mbuye wako Iye Ngodziwa kwambiri za amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye Ngodziwa kwambiri za amene aongoka.
Ndipo pirira. Kupirira kwakoko kusakhale pa china chake koma Allah basi. Ndipo usadandaule chifukwa cha iwo, (iwo akudzisokeretsa okha). Ndipo usakhale wobanika chifukwa cha chiwembu chomwe akuchita.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Résultats de la recherche:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".