Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa * - Lexique des traductions


Traduction des sens Verset: (272) Sourate: AL-BAQARAH
۞ لَّيۡسَ عَلَيۡكَ هُدَىٰهُمۡ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَهۡدِي مَن يَشَآءُۗ وَمَا تُنفِقُواْ مِنۡ خَيۡرٖ فَلِأَنفُسِكُمۡۚ وَمَا تُنفِقُونَ إِلَّا ٱبۡتِغَآءَ وَجۡهِ ٱللَّهِۚ وَمَا تُنفِقُواْ مِنۡ خَيۡرٖ يُوَفَّ إِلَيۡكُمۡ وَأَنتُمۡ لَا تُظۡلَمُونَ
Siudindo wako kuwaongola, koma Allah amamuongola amene wamfuna, (udindo wako nkulalikira kokha). Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke, (phindu lake) lili pa inu eni, ndipo musapereke pokhapokha pofunafuna chikondi cha Allah. Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke adzakubwezerani mokwanira (mphoto yake), ndipo simudzaponderezedwa.[55]
[55] Apa akumuuza Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi aliyense wolamula kuchita zabwino ndikuletsa kuchita zoipa kuti udindo wawo nkufikitsa uthengawo. Pa iwo palibe vuto ngati anthuwo savomereza, iwo adzapezabe mphoto yolamulira zabwino ndikuletsa zoipa ngakhale kuti sanawatsatire.
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Verset: (272) Sourate: AL-BAQARAH
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa - Lexique des traductions

Traduction des sens du noble Coran en langue chewa, par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ (édition 2020).

Fermeture