Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa * - Lexique des traductions


Traduction des sens Verset: (14) Sourate: AT-TAGHÂBOUN
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ مِنۡ أَزۡوَٰجِكُمۡ وَأَوۡلَٰدِكُمۡ عَدُوّٗا لَّكُمۡ فَٱحۡذَرُوهُمۡۚ وَإِن تَعۡفُواْ وَتَصۡفَحُواْ وَتَغۡفِرُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٌ
E inu amene mwakhulupirira! Ndithu ena mwa akazi anu ndi ana anu ndiadani anu (chifukwa chakuti amakuchotsani kumbali yomvera Allah pofuna kuti mukwaniritse zofuna zawo). Chenjerani nawo. Ngati muwakhululukira ndi kunyalanyaza ndi kubisa zolakwa zawo ndibwino kwambiri, ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.[366]
[366] (Ndime 14-15) Pakufunika kuti munthu akhale ndi muyeso wabwino. Chinthu chilichonse achipatse choyenera chake. Nthawi zambiri kumapezeka kuti munthu amalakwira Allah chifukwa cha kufunitsitsa chuma, kapena chifukwa chofuna kukondweretsa ana ake ndi mkazi wake ndi kunyalanyaza malamulo a Allah. Choncho apa, chuma chake, ana ake ndi mkazi wake amasanduka adani ake okamuika m’mavuto kwa Allah. Nkofunika kwa munthu kukondweretsa Allah ndi kumkonda asanakondweretse ndi kukonda china chilichonse.
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Verset: (14) Sourate: AT-TAGHÂBOUN
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa - Lexique des traductions

Traduction des sens du noble Coran en langue chewa, par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ (édition 2020).

Fermeture