Check out the new design

Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ * - Lexique des traductions


Traduction des sens Sourate: Al A'raf   Verset:
أُبَلِّغُكُمۡ رِسَٰلَٰتِ رَبِّي وَأَنَا۠ لَكُمۡ نَاصِحٌ أَمِينٌ
“Ndikufikitsa kwa inu uthenga wa Mbuye wanga. Ndipo ine ndine mlangizi wanu (wokufunirani zabwino), wokhulupirika.”
Les exégèses en arabe:
أَوَعَجِبۡتُمۡ أَن جَآءَكُمۡ ذِكۡرٞ مِّن رَّبِّكُمۡ عَلَىٰ رَجُلٖ مِّنكُمۡ لِيُنذِرَكُمۡۚ وَٱذۡكُرُوٓاْ إِذۡ جَعَلَكُمۡ خُلَفَآءَ مِنۢ بَعۡدِ قَوۡمِ نُوحٖ وَزَادَكُمۡ فِي ٱلۡخَلۡقِ بَصۜۡطَةٗۖ فَٱذۡكُرُوٓاْ ءَالَآءَ ٱللَّهِ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ
“Kodi mukudabwa pokudzerani ulaliki kuchokera kwa Mbuye wanu kupyolera mwa munthu wochokera mwa inu kuti akuchenjezeni? Kumbukirani (mtendere wa Allah) pamene adakuikani kukhala amlowam’malo pambuyo pa anthu a Nuh, ndipo akuonjezerani m’kalengedwe kukhala a misinkhu itali-itali ndi amphamvu. Kumbukiraninso mtendere wa Allah (pothokoza) kuti mupambane.”
Les exégèses en arabe:
قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا لِنَعۡبُدَ ٱللَّهَ وَحۡدَهُۥ وَنَذَرَ مَا كَانَ يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَا فَأۡتِنَا بِمَا تَعِدُنَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Iwo adati: “Kodi watidzera kuti timpembedze Allah Yekha ndikusiya zomwe ankapembedza makolo athu? Tibweretsere chimene ukutilonjezacho ngati uli mmodzi mwa onena zoona.”
Les exégèses en arabe:
قَالَ قَدۡ وَقَعَ عَلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُمۡ رِجۡسٞ وَغَضَبٌۖ أَتُجَٰدِلُونَنِي فِيٓ أَسۡمَآءٖ سَمَّيۡتُمُوهَآ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُم مَّا نَزَّلَ ٱللَّهُ بِهَا مِن سُلۡطَٰنٖۚ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ
(Iye) adati: “Palibe chikaiko, chilango ndi mkwiyo wochokera kwa Mbuye wanu zakugwerani. Kodi mukukangana nane pa za maina (a mafano) omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, pomwe Allah sadatsitse umboni uliwonse pa milungu yanu yabodzayo? Choncho, dikirani. Inenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”
Les exégèses en arabe:
فَأَنجَيۡنَٰهُ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٖ مِّنَّا وَقَطَعۡنَا دَابِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۖ وَمَا كَانُواْ مُؤۡمِنِينَ
Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye mwa chifundo chathu, ndipo tidadula mizu ya omwe adatsutsa zivumbulutso Zathu. Ndipo sadali okhulupirira.
Les exégèses en arabe:
وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ قَدۡ جَآءَتۡكُم بَيِّنَةٞ مِّن رَّبِّكُمۡۖ هَٰذِهِۦ نَاقَةُ ٱللَّهِ لَكُمۡ ءَايَةٗۖ فَذَرُوهَا تَأۡكُلۡ فِيٓ أَرۡضِ ٱللَّهِۖ وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءٖ فَيَأۡخُذَكُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Ndipo kwa Asamudu tidamtumiza m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Gwadirani Allah; inu mulibe mulungu wina koma Iye basi. Chizindikiro chochokera kwa Mbuye wanu chadza kwa inu. Iyi ndi ngamira ya Allah monga chisonyezo chanu (chizizwa chanu), choncho, isiyeni izidya m’dziko la Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopera kuti chingakugwereni chilango chowawa kwambiri.”
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Sourate: Al A'raf
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ - Lexique des traductions

Traduit par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ.

Fermeture