Check out the new design

क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला * - अनुवादों की सूची


अर्थों का अनुवाद सूरा: ग़ाफ़िर   आयत:
قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ تَكُ تَأۡتِيكُمۡ رُسُلُكُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِۖ قَالُواْ بَلَىٰۚ قَالُواْ فَٱدۡعُواْۗ وَمَا دُعَٰٓؤُاْ ٱلۡكَٰفِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَٰلٍ
(Alonda aja) adzati: “Kodi sadakudzereni aneneri anu ndi umboni oonekera poyera?” Iwo adzati: “Inde, (adatidzera. Koma ife tidanyoza).” (Ndipo) adzawauza: “Choncho pemphani nokha. Koma pempho la okanira silili la kanthu, ndi lotaika basi.”
अरबी तफ़सीरें:
إِنَّا لَنَنصُرُ رُسُلَنَا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَيَوۡمَ يَقُومُ ٱلۡأَشۡهَٰدُ
Ndithu Ife timapulumutsa aneneri Athu ndi amene akhulupirira pa moyo wa dziko lapansi ndi tsiku limene zidzaimilira mboni (kupereka umboni).
अरबी तफ़सीरें:
يَوۡمَ لَا يَنفَعُ ٱلظَّٰلِمِينَ مَعۡذِرَتُهُمۡۖ وَلَهُمُ ٱللَّعۡنَةُ وَلَهُمۡ سُوٓءُ ٱلدَّارِ
Tsiku limene achinyengo sadzawathandiza madandaulo awo, ndipo matembelero adzakhala pa iwo, ndipo pokhala pawo padzakhala poipa kwambiri.
अरबी तफ़सीरें:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡهُدَىٰ وَأَوۡرَثۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡكِتَٰبَ
Ndithu Mûsa tidampatsa chiongoko, ndipo tidawasiira buku ana a Israyeli.
अरबी तफ़सीरें:
هُدٗى وَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ
(Lomwe lidali) chiongoko ndi chikumbutso kwa eni nzeru.
अरबी तफ़सीरें:
فَٱصۡبِرۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لِذَنۢبِكَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِبۡكَٰرِ
Choncho pirira, ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Ndipo pempha chikhululuko cha machimo ako (ukachimwa), ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda madzulo ndi m’mawa.
अरबी तफ़सीरें:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ سُلۡطَٰنٍ أَتَىٰهُمۡ إِن فِي صُدُورِهِمۡ إِلَّا كِبۡرٞ مَّا هُم بِبَٰلِغِيهِۚ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
Ndithu amene akutsutsana pa zisonyezo za Allah popanda umboni umene udawadzera, mmitima mwawo mulibe chilichonse koma kudzitukumula (ndikufuna ukulu), koma saufikira. Dzitchinjirize mwa Allah, ndithu Iye Ngwakumva, Ngopenya.
अरबी तफ़सीरें:
لَخَلۡقُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ أَكۡبَرُ مِنۡ خَلۡقِ ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndithu kulenga kwa thambo ndi nthaka nkwakukulu kuposa kulenga kwa anthu. Koma anthu ambiri sakudziwa.
अरबी तफ़सीरें:
وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَلَا ٱلۡمُسِيٓءُۚ قَلِيلٗا مَّا تَتَذَكَّرُونَ
Ndipo sali wolingana wakhungu ndi wopenya ndiponso amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi wochita zoipa. Zimene inu mukumbukira nzochepa, ndithu!
अरबी तफ़सीरें:
 
अर्थों का अनुवाद सूरा: ग़ाफ़िर
सूरों की सूची पृष्ठ संख्या
 
क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला - अनुवादों की सूची

अनुवाद ख़ालिद इबराहीम बेताला।

बंद करें