Check out the new design

क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला * - अनुवादों की सूची


अर्थों का अनुवाद सूरा: फ़ुस्सिलत   आयत:
وَقَالُواْ لِجُلُودِهِمۡ لِمَ شَهِدتُّمۡ عَلَيۡنَاۖ قَالُوٓاْ أَنطَقَنَا ٱللَّهُ ٱلَّذِيٓ أَنطَقَ كُلَّ شَيۡءٖۚ وَهُوَ خَلَقَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Ndipo adzanena (adani a Allah) ku makungu awo: “Bwanji mukutiperekera umboni woipa?” Zidzati: “Allah watiyankhulitsa, Amene amayankhulitsa chilichonse; ndipo Iye ndi Amene adakulengani (mkulenga) koyamba (pomwe simudali kanthu), ndiponso kwa Iye Yekha ndiko mudzabwezedwa.
अरबी तफ़सीरें:
وَمَا كُنتُمۡ تَسۡتَتِرُونَ أَن يَشۡهَدَ عَلَيۡكُمۡ سَمۡعُكُمۡ وَلَآ أَبۡصَٰرُكُمۡ وَلَا جُلُودُكُمۡ وَلَٰكِن ظَنَنتُمۡ أَنَّ ٱللَّهَ لَا يَعۡلَمُ كَثِيرٗا مِّمَّا تَعۡمَلُونَ
Simudathe kubisa (ntchito zanu zoipa ku ziwalo zanu) poopera kuti kumva kwanu ndi kuyang’ana kwanu ndi makungu anu zingakuperekereni umboni woipa! Koma mudali kuganiza kuti Allah sadziwa zambiri zomwe mukuchita (mobisa).
अरबी तफ़सीरें:
وَذَٰلِكُمۡ ظَنُّكُمُ ٱلَّذِي ظَنَنتُم بِرَبِّكُمۡ أَرۡدَىٰكُمۡ فَأَصۡبَحۡتُم مِّنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Ndipo amenewo ndi maganizo anu omwe mudali kumganizira (nawo) Mbuye wanu adakuonongani, ndipo (lero tsiku la Qiyâma) muli m’gulu la otaika.”
अरबी तफ़सीरें:
فَإِن يَصۡبِرُواْ فَٱلنَّارُ مَثۡوٗى لَّهُمۡۖ وَإِن يَسۡتَعۡتِبُواْ فَمَا هُم مِّنَ ٱلۡمُعۡتَبِينَ
Choncho ngakhalc atapirira (ku zopweteka zawo), moto ndiwo mabwelero awo ndi kokhazikika kwawo kwa muyaya. Ngati atapempha chiyanjo cha Allah pa iwo, iwo sadzakhala m’gulu la oyanjidwa.
अरबी तफ़सीरें:
۞ وَقَيَّضۡنَا لَهُمۡ قُرَنَآءَ فَزَيَّنُواْ لَهُم مَّا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَحَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقَوۡلُ فِيٓ أُمَمٖ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِهِم مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ خَٰسِرِينَ
Ndipo tidawakonzera iwo abwenzi oipa (padziko lapansi), choncho adawakometsera zamtsogolo mwawo ndi za pambuyo pawo ndipo liwu la chilango lidatsimikizika pa iwo pamodzi ndi mibadwo yomwe idapita kale ya ziwanda ndi anthu, ndithu iwo adali otaika.
अरबी तफ़सीरें:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَا تَسۡمَعُواْ لِهَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ وَٱلۡغَوۡاْ فِيهِ لَعَلَّكُمۡ تَغۡلِبُونَ
Akunena okanira (kuuzana okhaokha): “Musamvetsere Qur’an iyi, koma sokoserani pomwe ikuwerengedwa (kuti asaimvere aliyense) kuti mwina mupambane.”
अरबी तफ़सीरें:
فَلَنُذِيقَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ عَذَابٗا شَدِيدٗا وَلَنَجۡزِيَنَّهُمۡ أَسۡوَأَ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndithu tiwalawitsa amene akanira chilango choopsa (pa zochita zawo zoipa, makamaka pakuithira Qur’an nkhondo), ndipo ndithu tiwalipira malipiro oipitsitsa chifukwa cha zoipa zomwe adali kuchita.
अरबी तफ़सीरें:
ذَٰلِكَ جَزَآءُ أَعۡدَآءِ ٱللَّهِ ٱلنَّارُۖ لَهُمۡ فِيهَا دَارُ ٱلۡخُلۡدِ جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَجۡحَدُونَ
Imeneyo ndi mphoto yoyenera ya adani a Allah, yomwe ndi Moto. Mmenemo adzakhala muyaya. Imeneyi ndi mphoto ya zimene adali kuzikanira m’zisonyezo Zathu.
अरबी तफ़सीरें:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ رَبَّنَآ أَرِنَا ٱلَّذَيۡنِ أَضَلَّانَا مِنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ نَجۡعَلۡهُمَا تَحۡتَ أَقۡدَامِنَا لِيَكُونَا مِنَ ٱلۡأَسۡفَلِينَ
Ndipo okanira adzanena (ali mkati mwa Moto): “E Mbuye wathu! Tisonyezeni (magulu awiri) amene adatisokeretsa ochokera m’ziwanda ndi anthu kuti tiwaike pansi pa mapazi athu, kuti akhale mwa apansi (mu ulemelero ndi malo).”
अरबी तफ़सीरें:
 
अर्थों का अनुवाद सूरा: फ़ुस्सिलत
सूरों की सूची पृष्ठ संख्या
 
क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला - अनुवादों की सूची

अनुवाद: ख़ालिद इबराहीम बेताला।

बंद करें