Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa * - Daftar isi terjemahan


Terjemahan makna Ayah: (168) Surah: Surah Al-Baqarah
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ كُلُواْ مِمَّا فِي ٱلۡأَرۡضِ حَلَٰلٗا طَيِّبٗا وَلَا تَتَّبِعُواْ خُطُوَٰتِ ٱلشَّيۡطَٰنِۚ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٌ
E, inu anthu! Idyani zabwino zimene zili m’nthaka zomwe zili zololedwa; ndipo musatsate mapazi a satana. Iye kwa inu ndi mdani woonekeratu.[11]
[11] E inu anthu! Idyani za mdziko lapansi zomwe zili zabwino zimene Allah wakulolezani ndipo musapenekere chilolezo chake. Musadye chinthu chosaloledwa monga kudya chinthu cha wina m’njira ya chinyengo. Musakwatule chuma chamnzanu.
Ndipo chenjerani ndi njira za satana yemwe amakukometserani zoipa. Dziwani kuti iyeyu ndi mdani wanu monga adalili mdani watate wanu Adam. Dziwaninso kuti satanayo salamula kuchita zabwino koma zoipa zokhazokha.
Tafsir berbahasa Arab:
 
Terjemahan makna Ayah: (168) Surah: Surah Al-Baqarah
Daftar surah Nomor Halaman
 
Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Daftar isi terjemahan

Terjemahan Makna Al-Qur`ān Al-Karīm ke Bahasa Chichewa oleh Khalid Ibrahim Betala. Edisi 2020 M

Tutup