Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa * - Indice Traduzioni


Traduzione dei significati Sura: At-Tûr   Versetto:

At-Tûr

وَٱلطُّورِ
Ndikulumbilira phiri la Turi (ku Sinai pamene Mûsa adalankhulana ndi Allah).
Esegesi in lingua araba:
وَكِتَٰبٖ مَّسۡطُورٖ
Ndi buku lolembedwa.
Esegesi in lingua araba:
فِي رَقّٖ مَّنشُورٖ
M’mipukutu yazikopa zotambasuka (zosavuta kuwerenga).
Esegesi in lingua araba:
وَٱلۡبَيۡتِ ٱلۡمَعۡمُورِ
Ndi nyumba yopitako kawirikawiri (pochitamo mapemphero).
Esegesi in lingua araba:
وَٱلسَّقۡفِ ٱلۡمَرۡفُوعِ
Ndi thambo limene latukulidwa (popanda mzati).
Esegesi in lingua araba:
وَٱلۡبَحۡرِ ٱلۡمَسۡجُورِ
Ndi nyanja yodzadza ndi madzi.
Esegesi in lingua araba:
إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ لَوَٰقِعٞ
Ndithu chilango cha Mbuye wako (chimene wawalonjeza nacho osakhulupirira) chiwapeza (popanda chipeneko).
Esegesi in lingua araba:
مَّا لَهُۥ مِن دَافِعٖ
Palibe wochichotsa (pa iwo).
Esegesi in lingua araba:
يَوۡمَ تَمُورُ ٱلسَّمَآءُ مَوۡرٗا
Pa tsikulo thambo lidzagwedezeka; kugwedezeka kwamphamvu.
Esegesi in lingua araba:
وَتَسِيرُ ٱلۡجِبَالُ سَيۡرٗا
Ndipo mapiri adzayenda mwamphavu (kuchoka m’malo mwake).
Esegesi in lingua araba:
فَوَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ
Kuonongeka koopsa pa tsiku limenelo kuzakhala pa otsutsa choonadi.
Esegesi in lingua araba:
ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي خَوۡضٖ يَلۡعَبُونَ
Iwo amene akungosewera mzinthu zopanda pake.
Esegesi in lingua araba:
يَوۡمَ يُدَعُّونَ إِلَىٰ نَارِ جَهَنَّمَ دَعًّا
Tsiku limene adzakankhidwira mwamphamvu ku Jahannam (ku Moto Woopsa).
Esegesi in lingua araba:
هَٰذِهِ ٱلنَّارُ ٱلَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Uwu ndi Moto uja umene mudali kuutsutsa (pa dziko lapansi)
Esegesi in lingua araba:
أَفَسِحۡرٌ هَٰذَآ أَمۡ أَنتُمۡ لَا تُبۡصِرُونَ
Kodi awa ndi matsenga kapena inu simukuona?
Esegesi in lingua araba:
ٱصۡلَوۡهَا فَٱصۡبِرُوٓاْ أَوۡ لَا تَصۡبِرُواْ سَوَآءٌ عَلَيۡكُمۡۖ إِنَّمَا تُجۡزَوۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Lowanimo, (mulawe kupsereza kwake) pirirani (ndi mavuto ake) kapena musapirire, ndichimodzimodzi kwa inu. Ndithu mulipidwa pazimene munkachita.”
Esegesi in lingua araba:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَنَعِيمٖ
Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda yamtendere ndi chisangalalo chachikulu.
Esegesi in lingua araba:
فَٰكِهِينَ بِمَآ ءَاتَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ وَوَقَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ
Uku akukondwelera pazimene wawapatsa Mbuye wawo ndipo Mbuye wawo azawatchinjiriza ku chilango cha Jahena.
Esegesi in lingua araba:
كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani (chakudya chamtendere); ndipo imwani mosangalala kukhala malipiro pazimene munkachita (pa dziko lapansi).”
Esegesi in lingua araba:
مُتَّكِـِٔينَ عَلَىٰ سُرُرٖ مَّصۡفُوفَةٖۖ وَزَوَّجۡنَٰهُم بِحُورٍ عِينٖ
Uku atakhala moyadzamira pa makama ondandika bwino ndi kuyalidwa bwino; ndipo tidzawakwatitsa akazi ophanuka maso mokongola.
Esegesi in lingua araba:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَٱتَّبَعَتۡهُمۡ ذُرِّيَّتُهُم بِإِيمَٰنٍ أَلۡحَقۡنَا بِهِمۡ ذُرِّيَّتَهُمۡ وَمَآ أَلَتۡنَٰهُم مِّنۡ عَمَلِهِم مِّن شَيۡءٖۚ كُلُّ ٱمۡرِيِٕۭ بِمَا كَسَبَ رَهِينٞ
Ndipo amene akhulupirira ndipo ana awo nkuwatsatira pa chikhulupiliro tidzawakumanitsa iwo ndi ana awowo ndipo sitikawachepetsera kalikonse m’mphoto za ntchito zawo; munthu aliyense adzakoledwa ndi zochita zake;
Esegesi in lingua araba:
وَأَمۡدَدۡنَٰهُم بِفَٰكِهَةٖ وَلَحۡمٖ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ
Ndipo tidzawaonjezera zipatso ndi nyama imene adzakhala akuilakalaka.
Esegesi in lingua araba:
يَتَنَٰزَعُونَ فِيهَا كَأۡسٗا لَّا لَغۡوٞ فِيهَا وَلَا تَأۡثِيمٞ
Azikalandirana m’menemo (mwachikondi wina ndi mnzake) chikho chodzaza ndi zakumwa; sipakakhala kwa iwo zolankhula zachabe ngakhale zochita zamachimo.
Esegesi in lingua araba:
۞ وَيَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ غِلۡمَانٞ لَّهُمۡ كَأَنَّهُمۡ لُؤۡلُؤٞ مَّكۡنُونٞ
Ndipo azikawazungulira anyamata owatumikira onga ngale yosungidwa m’chigoba chake (kukongola kwawo).
Esegesi in lingua araba:
وَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ
Azidzatembenukirana wina ndi mnzake uku akufunsana (za kukula kwa mtendere umene adzakhala nawo ndi kuti adaupeza chotani).
Esegesi in lingua araba:
قَالُوٓاْ إِنَّا كُنَّا قَبۡلُ فِيٓ أَهۡلِنَا مُشۡفِقِينَ
Adzanena: “Ife tidali oopa chilango cha Allah pakati pa maanja athu (tisadalandire mtenderewu).
Esegesi in lingua araba:
فَمَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡنَا وَوَقَىٰنَا عَذَابَ ٱلسَّمُومِ
Ndipo Allah watidalitsa ndipo watitchinjiriza ku chilango cha Moto.
Esegesi in lingua araba:
إِنَّا كُنَّا مِن قَبۡلُ نَدۡعُوهُۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡبَرُّ ٱلرَّحِيمُ
Ndithu ife timampembedza (kalero pa dziko lapansi) ndithu Iye Yekha Ngwabwino, Ngwachifundo.”
Esegesi in lingua araba:
فَذَكِّرۡ فَمَآ أَنتَ بِنِعۡمَتِ رَبِّكَ بِكَاهِنٖ وَلَا مَجۡنُونٍ
Choncho kumbutsa, iwe suli mlosi kapena wamisala pamtendere wa Mbuye wako.
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ يَقُولُونَ شَاعِرٞ نَّتَرَبَّصُ بِهِۦ رَيۡبَ ٱلۡمَنُونِ
Kapena akunena kuti ndiwe mlakatuli, tikumuyembekezera imfa impeze.
Esegesi in lingua araba:
قُلۡ تَرَبَّصُواْ فَإِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُتَرَبِّصِينَ
Nena: “Yembekezerani! Ndithu ine ndili nanu mwa mmodzi woyembekezera.”
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ تَأۡمُرُهُمۡ أَحۡلَٰمُهُم بِهَٰذَآۚ أَمۡ هُمۡ قَوۡمٞ طَاغُونَ
Kapena nzeru zawo ndizo zikuwauza izi kapena iwo ndi anthu opyola malire.
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ يَقُولُونَ تَقَوَّلَهُۥۚ بَل لَّا يُؤۡمِنُونَ
Kodi akunena kuti: “Wadzipekera (Mtumiki {s.a.w} Qur’an)?” Iyayi, koma iwo sakukhulupirira.
Esegesi in lingua araba:
فَلۡيَأۡتُواْ بِحَدِيثٖ مِّثۡلِهِۦٓ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ
Tero abwere ndi nkhani yofanana ndi iyo (Qur’an) ngati ali owona m’kuyankhula kwawo (koti Mtumiki{s.a.w} wapeka Qur’an.)
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ خُلِقُواْ مِنۡ غَيۡرِ شَيۡءٍ أَمۡ هُمُ ٱلۡخَٰلِقُونَ
Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha (nchifukwa sakuvomereza za Mlengi Wopembedzedwayo?)
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ خَلَقُواْ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَۚ بَل لَّا يُوقِنُونَ
Kapena ndiwo adalenga thambo ndi nthaka? Koma satsimikiza (zoyenera kumchitira Mlengi).
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَبِّكَ أَمۡ هُمُ ٱلۡمُصَۜيۡطِرُونَ
Kapena nkhokwe (za zabwino) za Mbuye wako zili ndi iwo (kotero kuti akuzigwiritsa ntchito mmene angafunire?) Kapena iwo ngopambana?
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ لَهُمۡ سُلَّمٞ يَسۡتَمِعُونَ فِيهِۖ فَلۡيَأۡتِ مُسۡتَمِعُهُم بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ
Nanga kapena ali nawo makwelero (amene akukwelera kumwamba) kotero kuti akumvetsera zimene Allah akulamula? Choncho, omvetsera awo abwere nawo umboni owonekera (osonyeza kuona kwawo pa zimene akunenazi).
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ لَهُ ٱلۡبَنَٰتُ وَلَكُمُ ٱلۡبَنُونَ
Kapena Iye (Allah) ndiye ali ndi ana akazi ndipo inu muli ndi ana amuna?
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرٗا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٖ مُّثۡقَلُونَ
Kapena ukuwapempha malipiro alionse (pofikitsa uthenga); kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira (uthengawu)?
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ
Kapena iwo amadziwa zamseri kotero kuti iwo akumalemba (zimene afuna)?
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ يُرِيدُونَ كَيۡدٗاۖ فَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ هُمُ ٱلۡمَكِيدُونَ
Kapena akufuna kukuchitira chiwembu (ndikuononga uthenga wako?) Koma amene sadakhulupirire ndiwo omwe chiwabwelere chiwembu (chawo.)
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ لَهُمۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Kodi ali naye wompembedza, osati Allah (amene angawateteze ku chilango cha Allah)? Allah wapatukana ndi zimene akumuphatikiza nazo.
Esegesi in lingua araba:
وَإِن يَرَوۡاْ كِسۡفٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ سَاقِطٗا يَقُولُواْ سَحَابٞ مَّرۡكُومٞ
Koma akaona gawo lathambo likugwa (kuti liwalange) akunena (mwamakani ndi kunyada): “Uwu ndi mtambo umene wasonkhanitsa madzi a mvula.”
Esegesi in lingua araba:
فَذَرۡهُمۡ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي فِيهِ يُصۡعَقُونَ
Choncho asiye; (usalabadire za iwo) mpaka pomwe adzakumana ndi tsiku lawo limene adzaonongedwa.
Esegesi in lingua araba:
يَوۡمَ لَا يُغۡنِي عَنۡهُمۡ كَيۡدُهُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ
Tsiku lomwe chiwembu chawo sichidzawathandiza chilichonse; ndipo iwo sadzapulumutsidwa.
Esegesi in lingua araba:
وَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ عَذَابٗا دُونَ ذَٰلِكَ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo ndithu amene achita zosalungama ali nacho chilango china chosakhala chimenecho (chisanawapeze chilango cha ku Âkhira)! Koma ambiri a iwo sadziwa (zimenezi).
Esegesi in lingua araba:
وَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ فَإِنَّكَ بِأَعۡيُنِنَاۖ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ حِينَ تَقُومُ
Ndipo pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndithu iwe ndiwe wosungidwa ndi kuyang’aniridwa ndi Ife; ndipo lemekeza ndi kumuyamika Mbuye ako pamene ukuimilira (kupemphera).
Esegesi in lingua araba:
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡهُ وَإِدۡبَٰرَ ٱلنُّجُومِ
Ndipo m’gawo la usiku mlemekeze Iye ndi nthawi yolowa nyenyezi.
Esegesi in lingua araba:
 
Traduzione dei significati Sura: At-Tûr
Indice delle Sure Numero di pagina
 
Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Indice Traduzioni

Traduzione dei significati del Nobile Corano in lingua chicheŵa, a cura di Khaled Ibrahim Beitala، ed. 2020

Chiudi