クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 * - 対訳の目次


対訳 節: (4) 章: 平伏礼章
ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ مَا لَكُم مِّن دُونِهِۦ مِن وَلِيّٖ وَلَا شَفِيعٍۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ
Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu); (kukhazikika kolingana ndi ulemelero Wake, kumene Iye Mwini wake akukudziwa). Inu mulibe mtetezi ngakhale muomboli kupatula Iye. Nanga kodi bwanji simulingalira?[315]
[315] M’ndime iyi Allah akutiuza kuti adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi. Komatu nthawi ya masiku amenewa, palibe amene akudziwa tsatanetsatane wake koma Allah Yekha. Choncho tisaganizire kuti masikuwo adali olingana ndi masiku a moyo uno wadziko lapansi.
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 節: (4) 章: 平伏礼章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - 対訳の目次

クルアーン・チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

閉じる