クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 * - 対訳の目次


対訳 章: カーフ章   節:

カーフ章

قٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡمَجِيدِ
Qaf. Ndikulumbira Qur’an yolemekezeka.
アラビア語 クルアーン注釈:
بَلۡ عَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٞ مِّنۡهُمۡ فَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا شَيۡءٌ عَجِيبٌ
Koma akudabwa chifukwa chowadzera Mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adanena: “Ichi nchinthu chodabwitsa.”
アラビア語 クルアーン注釈:
أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗاۖ ذَٰلِكَ رَجۡعُۢ بَعِيدٞ
Kodi tikadzafa ndi kukhala fumbi (tidzaukanso?) Kubwerera kumeneko nkwakutali kwambiri, (nkosatheka).”
アラビア語 クルアーン注釈:
قَدۡ عَلِمۡنَا مَا تَنقُصُ ٱلۡأَرۡضُ مِنۡهُمۡۖ وَعِندَنَا كِتَٰبٌ حَفِيظُۢ
Ndithu tikudziwa chimene nthaka ikuchepetsa m’matupi mwawo (akalowa m’manda). Ndipo kwa Ife kuli kaundula wosungidwa.
アラビア語 クルアーン注釈:
بَلۡ كَذَّبُواْ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ فَهُمۡ فِيٓ أَمۡرٖ مَّرِيجٍ
Koma adatsutsa choona pamene chidawadzera. Ndipo iwo ali m’chinthu chosokonezeka.
アラビア語 クルアーン注釈:
أَفَلَمۡ يَنظُرُوٓاْ إِلَى ٱلسَّمَآءِ فَوۡقَهُمۡ كَيۡفَ بَنَيۡنَٰهَا وَزَيَّنَّٰهَا وَمَا لَهَا مِن فُرُوجٖ
Kodi sawona thambo pamwamba pawo m’mene tidalimangira ndi kulikongoletsa? Ndipo lilibe ming’alu?
アラビア語 クルアーン注釈:
وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجِۭ بَهِيجٖ
Ndipo nthaka tidaiyala; ndi kuika mapiri m’menemo ndi kumeretsamo m’mera Wokongola wamtundu uliwonse.
アラビア語 クルアーン注釈:
تَبۡصِرَةٗ وَذِكۡرَىٰ لِكُلِّ عَبۡدٖ مُّنِيبٖ
(Kuti zimenezi zikhale) chotsekula maso ndi chikumbutso kwa munthu aliyense wotembenukira (kwa Allah).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَنَزَّلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ مُّبَٰرَكٗا فَأَنۢبَتۡنَا بِهِۦ جَنَّٰتٖ وَحَبَّ ٱلۡحَصِيدِ
Ndipo tatsitsa madzi odalitsidwa kuchokera ku mitambo, ndipo kupyolera m’madziwo, tameretsa (mmera) m’minda ndi mbewu zokololedwa.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَٱلنَّخۡلَ بَاسِقَٰتٖ لَّهَا طَلۡعٞ نَّضِيدٞ
Ndi mitengo italiitali ya kanjedza yokhala ndi mikoko yazipatso zothothana.
アラビア語 クルアーン注釈:
رِّزۡقٗا لِّلۡعِبَادِۖ وَأَحۡيَيۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗاۚ كَذَٰلِكَ ٱلۡخُرُوجُ
(Kuti chikhale) chakudya cha akapolo (a Allah); ndi madziwo taukitsa dziko lakufa (louma). Momwemo ndimmene kudzakhalira kutuluka m’manda (muli moyo).
アラビア語 クルアーン注釈:
كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ وَأَصۡحَٰبُ ٱلرَّسِّ وَثَمُودُ
Kale, iwo kulibe, adatsutsa anthu a Nuh ndi eni chitsime ndi Asamudu.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَعَادٞ وَفِرۡعَوۡنُ وَإِخۡوَٰنُ لُوطٖ
Ndi Âdi, ndi Farawo ndi Abale a Luti.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ وَقَوۡمُ تُبَّعٖۚ كُلّٞ كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ وَعِيدِ
Ndi anthu a m’mitengo (ya Aika), ndi anthu a Tubba; onsewo adatsutsa Aneneri; choncho chenjezo Langa lidatsimikizika (pa iwo).
アラビア語 クルアーン注釈:
أَفَعَيِينَا بِٱلۡخَلۡقِ ٱلۡأَوَّلِۚ بَلۡ هُمۡ فِي لَبۡسٖ مِّنۡ خَلۡقٖ جَدِيدٖ
Kodi tidatopa nkulenga koyamba? Koma iwo ali m’maganizo osokonezeka m’zakalengedwe katsopano.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ وَنَعۡلَمُ مَا تُوَسۡوِسُ بِهِۦ نَفۡسُهُۥۖ وَنَحۡنُ أَقۡرَبُ إِلَيۡهِ مِنۡ حَبۡلِ ٱلۡوَرِيدِ
Ndithu tidamulenga munthu, ndipo Ife tikudziwa zimene mtima wake ukumunong’oneza; ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wam’khosi mwake (wolumikizana ndi mtima).
アラビア語 クルアーン注釈:
إِذۡ يَتَلَقَّى ٱلۡمُتَلَقِّيَانِ عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَعَنِ ٱلشِّمَالِ قَعِيدٞ
Ndipo pamene amalandira olandira awiri (angelo), wina amakhala kudzanja lamanja, wina kudzanja lamanzere.
アラビア語 クルアーン注釈:
مَّا يَلۡفِظُ مِن قَوۡلٍ إِلَّا لَدَيۡهِ رَقِيبٌ عَتِيدٞ
Palibe chilichonse chimene amayankhula koma pafupi ndi iye pali mlonda amene wakonzekera (kulemba).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَجَآءَتۡ سَكۡرَةُ ٱلۡمَوۡتِ بِٱلۡحَقِّۖ ذَٰلِكَ مَا كُنتَ مِنۡهُ تَحِيدُ
Ndipo kuledzera kwa imfa kukam’dzera mwa choona, (pamenepo adzauzidwa): “Ichi ndi chomwe mumachithawa chija.”
アラビア語 クルアーン注釈:
وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِۚ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلۡوَعِيدِ
Ndipo lipenga lidzaimbidwa; limenelo ndilo tsiku lamavuto (tsiku lachiweruziro).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَجَآءَتۡ كُلُّ نَفۡسٖ مَّعَهَا سَآئِقٞ وَشَهِيدٞ
Ndipo udzadza mzimu uliwonse pamodzi ndi m’busa (wake) ndi mboni (yake).
アラビア語 クルアーン注釈:
لَّقَدۡ كُنتَ فِي غَفۡلَةٖ مِّنۡ هَٰذَا فَكَشَفۡنَا عَنكَ غِطَآءَكَ فَبَصَرُكَ ٱلۡيَوۡمَ حَدِيدٞ
(Adzauzidwa): “Ndithu udali wosalabadira zinthu izi; basi takuvundukulira (chomwe) chimakuphimba, ndipo kuyang’ana kwako lero nkwakuthwa!”
アラビア語 クルアーン注釈:
وَقَالَ قَرِينُهُۥ هَٰذَا مَا لَدَيَّ عَتِيدٌ
Ndipo (Mngelo) yemwe adali naye (pamodzi ndikumalemba zochita zake) adzanena (kwa Mngelo wachilango): “Izi ndizimene zidakonzedwa ndi ine.”
アラビア語 クルアーン注釈:
أَلۡقِيَا فِي جَهَنَّمَ كُلَّ كَفَّارٍ عَنِيدٖ
Mponyeni ku Moto aliyense wokanira, wamakani,”
アラビア語 クルアーン注釈:
مَّنَّاعٖ لِّلۡخَيۡرِ مُعۡتَدٖ مُّرِيبٍ
“Wotsekereza zabwino, wolumpha malire, wokaika.”
アラビア語 クルアーン注釈:
ٱلَّذِي جَعَلَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَأَلۡقِيَاهُ فِي ٱلۡعَذَابِ ٱلشَّدِيدِ
“Amene adampangira Allah mulungu wina. Chomwecho mponyeni ku chilango chaukali.”
アラビア語 クルアーン注釈:
۞ قَالَ قَرِينُهُۥ رَبَّنَا مَآ أَطۡغَيۡتُهُۥ وَلَٰكِن كَانَ فِي ضَلَٰلِۭ بَعِيدٖ
Mnzake (satana) adzanena: “E Mbuye wathu! Sindidamsokeretse, koma iye mwini adali wosokera kutali kwambiri ndi choonadi”.
アラビア語 クルアーン注釈:
قَالَ لَا تَخۡتَصِمُواْ لَدَيَّ وَقَدۡ قَدَّمۡتُ إِلَيۡكُم بِٱلۡوَعِيدِ
(Allah) adzanena: “Musakangane kwa Ine; ndidakutsogozerani kale chenjezo (Langa).”
アラビア語 クルアーン注釈:
مَا يُبَدَّلُ ٱلۡقَوۡلُ لَدَيَّ وَمَآ أَنَا۠ بِظَلَّٰمٖ لِّلۡعَبِيدِ
Liwu Langa silisinthidwa kwa Ine, ndipo Ine siwopondereza akapolo (Anga).
アラビア語 クルアーン注釈:
يَوۡمَ نَقُولُ لِجَهَنَّمَ هَلِ ٱمۡتَلَأۡتِ وَتَقُولُ هَلۡ مِن مَّزِيدٖ
Tsiku limene tidzaifunsa Jahannam: “Kodi wadzaza?” Iyo idzanena: “Kodi kuli zoonjezera?”
アラビア語 クルアーン注釈:
وَأُزۡلِفَتِ ٱلۡجَنَّةُ لِلۡمُتَّقِينَ غَيۡرَ بَعِيدٍ
Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa pafupi kwa oopa (Allah).
アラビア語 クルアーン注釈:
هَٰذَا مَا تُوعَدُونَ لِكُلِّ أَوَّابٍ حَفِيظٖ
“Izi ndizimene mumalonjezedwa, za aliyense wotembenukira kwa Allah, Wosunga (malamulo Ake).
アラビア語 クルアーン注釈:
مَّنۡ خَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِ وَجَآءَ بِقَلۡبٖ مُّنِيبٍ
Amene adaopa (Allah), Wachifundo chambiri, pomwe samamuona ndi maso, ndipo adadza ndi mtima wotembenukira (kwa Iye).”
アラビア語 クルアーン注釈:
ٱدۡخُلُوهَا بِسَلَٰمٖۖ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلۡخُلُودِ
(Adzauzidwa): “Uloweni mwamtendere.” Limeneli ndi tsiku lokhazikika mpaka muyaya.
アラビア語 クルアーン注釈:
لَهُم مَّا يَشَآءُونَ فِيهَا وَلَدَيۡنَا مَزِيدٞ
M’menemo adzapeza chilichonse (chimene) adzafune, ndipo kwa Ife kuli zoonjezera.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هُمۡ أَشَدُّ مِنۡهُم بَطۡشٗا فَنَقَّبُواْ فِي ٱلۡبِلَٰدِ هَلۡ مِن مَّحِيصٍ
Ndipo kodi ndi mibadwo ingati tidainonga kale iwo kulibe, yamphamvu kuposa iwo? Adayendayenda padziko. Kodi padalipo pothawira?
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكۡرَىٰ لِمَن كَانَ لَهُۥ قَلۡبٌ أَوۡ أَلۡقَى ٱلسَّمۡعَ وَهُوَ شَهِيدٞ
Ndithu m’zimenezi muli chikumbutso kwa yemwe ali ndi mtima ndi yemwe akutchelera khutu (uku) iye ali pompo (ndi maganizo ake).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ وَمَا مَسَّنَا مِن لُّغُوبٖ
Ndithu tidalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo sikudatikhuze kutopa kulikonse.
アラビア語 クルアーン注釈:
فَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ قَبۡلَ طُلُوعِ ٱلشَّمۡسِ وَقَبۡلَ ٱلۡغُرُوبِ
Choncho, pirira nazo zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako pomutamanda dzuwa lisadatuluke, (Swala ya Subh), ndi (dzuwa) lisadalowe, (Swala ya Asr),
アラビア語 クルアーン注釈:
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡهُ وَأَدۡبَٰرَ ٱلسُّجُودِ
Ndi gawo lausiku, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso (mulemekeze) pambuyo pa mapemphero (popemphera Swala za Sunna).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَٱسۡتَمِعۡ يَوۡمَ يُنَادِ ٱلۡمُنَادِ مِن مَّكَانٖ قَرِيبٖ
Ndipo mvetsera (za) tsiku limene woitana adzaitana kuchokera pamalo apafupi.
アラビア語 クルアーン注釈:
يَوۡمَ يَسۡمَعُونَ ٱلصَّيۡحَةَ بِٱلۡحَقِّۚ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلۡخُرُوجِ
Tsiku limene adzamva phokoso mwa choonadi: limenelo ndilo tsiku lodzatuluka (m’manda).
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِۦ وَنُمِيتُ وَإِلَيۡنَا ٱلۡمَصِيرُ
Ndithu Ife ndi amene timapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo kobwerera Nkwathu.
アラビア語 クルアーン注釈:
يَوۡمَ تَشَقَّقُ ٱلۡأَرۡضُ عَنۡهُمۡ سِرَاعٗاۚ ذَٰلِكَ حَشۡرٌ عَلَيۡنَا يَسِيرٞ
(Akumbutse za) tsiku limene nthaka idzang’ambike kwa iwo mwachangu; kusonkhanitsa kumeneko nkosavuta kwa Ife.
アラビア語 クルアーン注釈:
نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَقُولُونَۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِجَبَّارٖۖ فَذَكِّرۡ بِٱلۡقُرۡءَانِ مَن يَخَافُ وَعِيدِ
Ife tikudziwa bwino zimene akunena; iwe siuli wowakakamiza. Choncho mukumbutse ndi Qur’an yemwe akuopa chilango Changa.
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 章: カーフ章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - 対訳の目次

クルアーン・チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

閉じる