クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 * - 対訳の目次


対訳 節: (2) 章: 集合章
هُوَ ٱلَّذِيٓ أَخۡرَجَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ مِن دِيَٰرِهِمۡ لِأَوَّلِ ٱلۡحَشۡرِۚ مَا ظَنَنتُمۡ أَن يَخۡرُجُواْۖ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُم مَّانِعَتُهُمۡ حُصُونُهُم مِّنَ ٱللَّهِ فَأَتَىٰهُمُ ٱللَّهُ مِنۡ حَيۡثُ لَمۡ يَحۡتَسِبُواْۖ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلرُّعۡبَۚ يُخۡرِبُونَ بُيُوتَهُم بِأَيۡدِيهِمۡ وَأَيۡدِي ٱلۡمُؤۡمِنِينَ فَٱعۡتَبِرُواْ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَبۡصَٰرِ
Iye ndi Amene adatulutsa osakhulupirira ena mwa anthu a buku m’nyumba zawo mkusamusidwa koyamba (pa chilumba cha Arabu). Simunkaganizira kuti angatuluke (m’nyumba zawozo). Ndipo iwo amaganiza kuti malinga awo awateteza kwa Allah. Koma Allah adawalanga kupyolera mmene samayembekezera, ndipo adathira mantha oopsa m’mitima mwawo (potumiza Mtumiki Wake kwa iwo), adagumula nyumba zawo ndi manja awo ndi manja a okhulupirira. Choncho lingalirani (zimenezi) E inu eni nzeru! [353]
[353] Ayah imeneyi ikulongosola nkhani ya kusamutsidwa kwa Ayuda otchedwa Bani Nadhir mu mzinda wa Madina. Ayuda adasamutsidwa mu mzinda wa Madina chifukwa cha kuswa mapangano okhalirana mwa mtendere ndi Asilamu.
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 節: (2) 章: 集合章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - 対訳の目次

クルアーン・チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

閉じる