Check out the new design

クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim * - 対訳の目次


対訳 章: 家畜章   節:
۞ إِنَّ ٱللَّهَ فَالِقُ ٱلۡحَبِّ وَٱلنَّوَىٰۖ يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَمُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتِ مِنَ ٱلۡحَيِّۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ
Ndithu Allah ndi Yemwe amang’amba njere ndi mbewu ya zipatso (kuti zimere). Amatulutsa chamoyo m’chakufa. Ndiponso Ngotulutsa chakufa m’chamoyo. Ameneyu ndi Allah, nanga mukutembenuzidwa chotani?
アラビア語 クルアーン注釈:
فَالِقُ ٱلۡإِصۡبَاحِ وَجَعَلَ ٱلَّيۡلَ سَكَنٗا وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ حُسۡبَانٗاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ
Iye ndi Yemwe ali Wotsekula m’bandakucha, ndipo amaupanga usiku kukhala wabata (nthawi yopumula) ndi dzuwa ndi mwezi kukhala zowerengera masiku ndi zaka (kalendala). Ichi nchikonzero cha Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلنُّجُومَ لِتَهۡتَدُواْ بِهَا فِي ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۗ قَدۡ فَصَّلۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ
Iye ndi amene anakupangirani nyenyezi kuti mulondole njira kudzera mwa izo mu m’dima wa pamtunda ndi panyanja. Ndithu talongosola mokwanira zizindikiro (zathu) kwa anthu odziwa.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَكُم مِّن نَّفۡسٖ وَٰحِدَةٖ فَمُسۡتَقَرّٞ وَمُسۡتَوۡدَعٞۗ قَدۡ فَصَّلۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَفۡقَهُونَ
Ndipo Iye ndi yemwe adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi. (Kwa inu) alipo malo okhalapo (dziko lapansi kapena m’mimba mwa mayi) ndiponso posungirapo (mmanda kapena munsana mwa bambo). Ndithu tafotokoza zizindikiro (Zathu) kwa anthu ozindikira.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ نَبَاتَ كُلِّ شَيۡءٖ فَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهُ خَضِرٗا نُّخۡرِجُ مِنۡهُ حَبّٗا مُّتَرَاكِبٗا وَمِنَ ٱلنَّخۡلِ مِن طَلۡعِهَا قِنۡوَانٞ دَانِيَةٞ وَجَنَّٰتٖ مِّنۡ أَعۡنَابٖ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلرُّمَّانَ مُشۡتَبِهٗا وَغَيۡرَ مُتَشَٰبِهٍۗ ٱنظُرُوٓاْ إِلَىٰ ثَمَرِهِۦٓ إِذَآ أَثۡمَرَ وَيَنۡعِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكُمۡ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Iye ndi Yemwe amavumbwitsa mvula kuchokera kumwamba. Ndi madzi a mvulayo timameretsa mmera wa chinthu chilichonse. Ndipo m’menemo tikuphukitsa masamba obiriwira, tikutulutsa mmenemo njere zosanjikana; ndiponso m’kanjedza m’mikoko mwake mumatuluka maphava ogoweka (ndizipatso). Ndipo amakumeretserani minda ya mphesa, mzitona ndi makomamanga, ofanana ndi osafanana. Tapenyani zipatso zake pamene zikupatsa ndi kupsa kwake. Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَجَعَلُواْ لِلَّهِ شُرَكَآءَ ٱلۡجِنَّ وَخَلَقَهُمۡۖ وَخَرَقُواْ لَهُۥ بَنِينَ وَبَنَٰتِۭ بِغَيۡرِ عِلۡمٖۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يَصِفُونَ
Ndipo (pamwamba pa izi) anthu ampangira Allah ziwanda kukhala athandizi (Ake), pomwe Iye ndi Yemwe adazilenga. Ndipo akumnamizira kuti ali ndi ana aamuna ndi aakazi popanda kudziwa. Ali kutali Wolemekezekayo, ndipo watukuka kuzimene akusimbazo.
アラビア語 クルアーン注釈:
بَدِيعُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ أَنَّىٰ يَكُونُ لَهُۥ وَلَدٞ وَلَمۡ تَكُن لَّهُۥ صَٰحِبَةٞۖ وَخَلَقَ كُلَّ شَيۡءٖۖ وَهُوَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
Iye ndiye Mlengi wathambo ndi nthaka, zingatheke bwanji kukhala ndi mwana pomwe Iye alibe mkazi? Ndipo ndi Yemwe adalenga chinthu chilichonse. Ndiponso Iye Ngodziwa zedi chinthu chilichonse.
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 章: 家畜章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim - 対訳の目次

カリード・イブラヒーム・ビタラの翻訳

閉じる