[1] Sura iyi yayamba ndi malembo a Alifabeti, monga Alif, Laam, Miim. kusonyeza kuti Qur’an yalembedwa ndi malembo amenewa omwe anthu amawagwiritsa ntchito m’zoyankhula ndi m’zolembalemba zawo. Uku ndikuwauza osakhulupilira kuti abweretse buku lawo lolembedwa ndi malembo omwe akuwadziwawo pamene iwo amanena kuti Qur’an adangoipeka yekha Muhammadi (s.a.w) siidavumbulutsidwe ndi Allah. Choncho Allah adawachalenja kuti alembe buku lawo lofanana ndi Qur’an, koma adalephera. Choncho, kulephera kwawo ndi umboni wosonyeza kuti Qur’an ndi buku lovumbulutsidwa ndi Allah.
Ndi amene akukhulupirira zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwe, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kale iwe usadadze, nakhulupiriranso motsimikiza kuti lilipo tsiku lachimaliziro.
Iwowo (omwe ali ndi chikhalidwe chotere), ali pachiongoko chochokera kwa Mbuye wawo (Allah), ndipo iwowo ndi omwe ali opambana (pokapeza ulemelero wapamwamba ku Minda ya mtendere).
Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: “Takhulupirira.” Koma akakhala pa okha ndi asatana awo, amati: “Ndithudi ife tili pamodzi nanu. Timangowachita chipongwe basi.”
Choncho ngati simutha (kubweretsa sura imodzi yonga ya m’Qurani) ndiye kuti simudzatha. Choncho opani Moto omwe nkhuni zake ndi anthu ndi miyala umene wakonzedwera kwa osakhulupirira.
Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake).
Omwe akuswa chipangano cha Allah pambuyo pochimanga (kuti adzachikwaniritsa; ndi kutsatira malamulo a Allah), ndiponso amadula (chibale) chomwe Allah adalamula kuti chilumikizidwe, naononga pa dziko (poyambitsa nkhondo ndi ziwawa); iwo ndiamene ali otayika.
Iye ndi Yemwe adakulengerani zonse za m’dziko lapansi, kenako adalunjika ku thambo nakonza thambo zisanu ndi ziwiri. Iye Ngodziwa chinthu chilichonse.[2]
[2] Adalunjika ku thambo molingana ndi mmene Allah yo alili osati mofanana ndi zolengedwa Zake.
E inu ana a Israyeli! Kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho. Ndithudi, Ine ndinakuchitirani ubwino kuposa zolengedwa zonse (pa nthawiyo).
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona.
Ndithu amene akhulupirira (aneneri akale), ndi Ayuda, ndi Akhirisitu ndi Asabayi[3]; aliyense wa iwo amene akhulupirire Allah (tsopano, monga momwe akunenera Mneneri Muhammad (s.a.w) nakhulupiriranso za tsiku lachimaliziro, uku akuchita ntchito zabwino, akalandira mphoto yawo kwa Mbuye wawo. Pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula.
[3] Amenewa ndi anthu amene adali kunena mau oti Laa ilaaha illa Allah, adali kuwerenga Zabur koma si Ayuda kapena Akhrisitu.
Koma pambuyo pazimenezo mudatembenuka ndikunyoza. Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, mukadakhala mwa otayika (oonongeka pa dziko lapansi).
Iwo adati: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atifotokozere bwino za ng’ombeyo.” Iye adati: “Ndithudi Iye akunena kuti ng’ombeyo simkota kapena mthanthi, koma yapakatikati pa zimenezi. Tero chitani zimene mukulamulidwa.”
Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: Takhulupirira (kuti uyu, Muhammad (s.a.w) ndi mneneri woona, ndipo watchulidwa m’mabuku athu).” Koma akakhala kwaokha kuseli, amati: “Mukuwauza iwo (Asilamu) zimene Allah anakufotokozerani (m’buku la Taurat) kuti adzakhale ndi mtsutso pa inu kwa Mbuye wanu? Kodi mulibe nzeru?
Chilango cha ukali chili pa amene akulemba buku ndi manja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” (akunena bodzalo) kuti apeze zinthu za mtengo wochepa (za m’dziko lapansi); choncho kuonongeka kuli pa iwo chifukwa cha zomwe manja awo alemba, ndiponso kuonongeka n’kwawo chifukwa cha zomwe akupeza.
Ndipo (akumbutse nkhani iyinso) pamene tidalandira pangano lamphamvu la ana a Israyeli kuti: Musapembedze aliyense koma Allah; ndipo muwachitire zabwino makolo anu ndi achibale anu, ndi amasiye, ndi masikini (osoŵedwa); ndipo nenani kwa anthu mwaubwino; ndipo pempherani Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, kenako mudatembenuka monyozera kupatula ochepa mwa inu, ndipo inu ndinu onyozera.
Tsono inu nomwe ndi amene mukuphana ndikuwatulutsa ena a inu m’nyumba zawo; mukuthandiza adani anu powachitira (abale anu masautso) mwauchimo ndi molumpha malire. Koma akakudzerani akaidi ogwidwa ku nkhondo, mukuwaombola, pomwe nkoletsedwa kwa inu kuwatulutsa. Kodi mukukhulupirira mbali ina ya buku, mbali ina nkuikana? Choncho palibe mphoto kwa ochita izi mwa inu koma kuyaluka pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo tsiku la chiweruziro adzalowetsedwa ku chilango chokhwima kwambiri. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita[4].
[4] Ndime iyi ikukamba za Ayuda omwe amapezeka ku Madina nthawi ya Mtumiki (s.a.w). Iwo munthawi ya umbuli adapalana ubwenzi ndi ma Arabu aku Madina. Ena a iwo anali paubwenzi ndi mtundu wa Khazraj, ndipo ena mwa iwo anali paubwenzi ndi mtundu wa Aws. Choncho ikachitika nkhondo pakati pawo, Ayuda ambali iyi adali kupha Ayuda ambali inayi ndikulanda katundu wawo ndikuwagwira ukapolo, zomwe ndizoletsedwa malingana ndi Tora. Kenako nkhondo ikatha adali kuwamasula akapolo aja, pogwiritsa ntchito lamulo la Tora. Nchifukwa chake Allah akuwafunsa mowadzudzula kuti: “Kodi mukukhulupilira mbali ina ya buku, mbali ina nkuikana?”
Ndithudi Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) ndipo tidatsatiza pambuyo pake atumiki (ena). Ndipo Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zizizwa zoonekera, ndi kumulimbikitsa ndi Mzimu Woyera (Gabrieli). Nthawi iliyonse akakudzerani mtumiki ndi chomwe mitima yanu siikonda, mumadzikweza. Ena mudawatsutsa ndipo ena mudawapha.
(Iwo) adati: “Mitima yathu yakutidwa, (potero tikulephera kumvetsa ulaliki wako, iwe Muhammad (s.a.w).’’ Iwo ngabodza pa zimene akunenazi. Koma Allah wawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Tero n’zochepa zimene akuzikhulupirira.
Ndipo pamene buku lidawadzera (m’nyengo ya mtumiki Muhammad {s.a.w}) lochokera kwa Allah, loikira umboni zomwe zili pamodzi ndi iwo (adalikana), pomwe kale (lisadadze bukulo) adali kupempha chithandizo (kupyolera kwa mtumiki wolonjezedwa) chogonjetsera amene sadakhulupirire. Koma pamene chidawadzera chimene adachidziwa, (Qur’an) adachikana. Choncho matembelero a Allah ali pa osakhulupirira.
N’choipa zedi chimene asinthanitsira (chisangalalo cha tsiku lachimaliziro cha) mitima yawo pa kukana kwao zimene Allah adavumbulutsa, chifukwa cha njiru basi kuti Allah watsitsira chifundo chake amene wamfuna mwa akapolo Ake (amene sali Myuda). Potero adabwerera ndi mkwiyo wa Allah kuonjezera pa mkwiyo wakale. Ndipo osakhulupirira adzakhala ndi chilango chosambula.
Koma sadzailakalaka (imfa) ngakhale pang’ono, chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza (chifukwa cha machimo omwe adadzichitira). Ndipo Allah akudziwa bwino za anthu oipa.
Nena: “Amene akhale mdani wa Gaburieli (chifukwa chobweretsa chivumbulutso kwa Muhammad {s.a.w}, iyeyo ndi mdani wa Allah). Ndithudi, iye waivumbulutsa Qur’an mumtima mwako mwachilolezo cha Allah. Kudzatsimikidzira zomwe zidali patsogolo pake, ndiponso ndi chiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira.
Ndipo pamene (Ayuda) adawadzera Mtumiki wochokera kwa Allah uku akutsimikidzira chomwe iwo ali nacho, gulu lina mwa omwe adapatsidwa buku adataya buku la Allah kumbuyo kwa misana yawo ngati kuti sakulidziwa.
Amene sadakhulupirire mwa anthu a mabuku (Ayuda ndi Akhirisitu) ndi omphatikiza Allah (Arabu), safuna kuti chabwino chilichonse chochokera kwa Mbuye wanu chitsitsidwe kwa inu (Asilamu). Koma Allah amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino ochuluka.
Ayi, koma amene nkhope yake yagonjera kwa Allah uku akuchita zabwino (kwa anthu anzawo) iye ndi amene adzapeza mphoto yake kwa Mbuye wake. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso iwo sadzadandaula.
Ndipo (osakhulupirira) akumanena: “Allah wadzipangira mwana.” (Allah) wapatukana ndi zimenezo. Koma (zolengedwa) zonse za kumwamba ndi pansi Nzake. Zonse zikumumvera Iye.
Anthu omwe tidawapatsa buku naliwerenga kuwerenga koyenera (kopanda kusintha mawu ake ndi matanthauzo ake), iwo ndi amene akulikhulupirira (bukuli la Qur’an). Koma amene angalikane iwowa ndi omwe ali oonongeka.
Ndipo kumbukirani pamene Ibrahim Mbuye wake (Allah) adamuyesa iye mayeso ndi malamulo ambiri; ndipo iye adakwaniritsa. Adamuuza: “Ndithudi, Ine ndichita iwe kukhala mtsogoleri wa anthu.” (Ibrahim adayankha kuti): “Kodi ndi ana anga omwe?” Adati: “(Inde; koma) lonjezo langa silingawafike ochita zoipa.”
Ndipo (kumbukirani nkhani iyi) pamene Ibrahim adanena: “E Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa chitetezo, ndipo zipatseni nzika zake zipatso, amene akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro mwa iwo. Allah adati: “Nayenso wosakhulupirira ndinkondweretsa pang’ono; kenako ndidzamkankhira ku chilango cha Moto. Taonani kunyansa malo obwerera.
Ndipo (kumbukiraninso) pamene Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Allah): “E Mbuye wathu! Tilandireni (ntchito yathuyi), ndithudi, Inu ndinu Akumva; Odziwa.”
Kodi ndani anganyozere chipembedzo cha Ibrahim posakhala yemwe mtima wake uli wopusa? Ndithudi, tidamsankha (Ibrahim) pa dziko lapansi; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala m’modzi wa anthu abwino.”
Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi, chonchonso Ya’qub (adalangizanso ana ake kuti): “E inu ana anga! Ndithudi, Allah wakusankhirani chipembedzo; choncho musafe pokhapokha muli Asilamu (ogonjera Mulungu).”
Kapena inu (Ayuda ndi Akhrisitu) mudalipo pamene Ya’qub idamdzera imfa, pamene adati kwa ana ake: “Kodi pambuyo panga mudzapembedza yani?” Iwo adayankha nati: “Tidzapembedza Mulungu wako, Mulungu wa makolo ako; Ibrahim, Ismail ndi Ishâq; Mulungu mmodzi basi. Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”
Ndipo (Ayuda ndi Akhrisitu) adati (kwa Asilamu): “Khalani Ayuda kapena Akhrisitu mukhala oongoka.” Nena: “Koma (tikutsata) chipembedzo cha Ibrahim yemwe adaleka zipembedzo zopotoka, ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).”
Nenani (inu Asilamu kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu); “Takhulupirira Allah ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi zidzukulu (zake) ndi zimene adapatsidwa Mûsa, Isa (Yesu), ndiponso zimene adapatsidwa aneneri (ena) kuchokera kwa Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati pa mmodzi wa iwo (koma onse tikuwakhulupirira). Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”
Nena (iwe Muhammad {s.a.w} kwa Ayuda ndi Akhrisitu): “Ha! Mukutsutsana nafe za Allah (ponena kuti bwanji wapereka uneneri kumbali ya ife), pomwe Iye ndi Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu? (Pamene mudali olungama adakupatsani uneneri, ndipo pamene mudakhota adakulandani natipatsa ife). Ife tili ndi zochita zathu; inunso muli ndi zochita zanu, ndipo ife tikudzipereka kwathunthu kwa Iye (Allah).”
Choncho takusankhani (inu Asilamu) kukhala mpingo wabwino (wapakatikati) kuti mukhale mboni pa anthu ndi kuti Mtumiki (s.a.w) akhale mboni pa inu. Ndipo chibula (choyang’ana mbali ya ku Yerusalemu) chomwe udali nacho sitidachichite koma kuti timdziwitse (adziwike kwa anthu) amene akutsata Mtumiki (s.a.w), ndi yemwe akutembenukira m’mbuyo. Ndipo ndithudi, chidali chinthu chovuta kupatula kwa omwe Allah wawaongola. Ndipo nkosayenera kwa Allah kusokoneza Swala zanu, pakuti Allah Ngoleza kwabasi kwa anthu, Ngwachifundo chambiri. [6]
[6] Apa akutanthauza kuti pamene takutsogolerani ku njira yolunjika, takulolani inu ampingo wa Muhammad (s.a.w) kukhala anthu olungama, kulungama kosapyola nako muyeso ndiponso kopanda kuchepetsa chinthu chilichonse chazauzimu, ndi chamoyo wapadziko lino lapansi. Mpingo wa Asilamu ngwapakatikati mzokhulupilira zake zonse. Umalimbikira kugwira ntchito ya zinthu za mdziko ndiponso ya zinthu zauzimu mwakhama, chilichonse mwa zimenezi amachilimbikira mosapyoza muyeso. Limeneli ndilo tanthauzo la “mpingo wapakatikati.’’ Chisilamu sichilekelera munthu mmodzi kuti apondereze anthu ambirimbiri; ndiponso sichilekelera anthu ambiri kusalabadira za munthu mmodzi.
Ndipo awo adapatsidwa buku ngakhale utabwera ndi chisonyezo cha mtundu uliwonse satsata chibula chako, ngakhalenso iwe sutsata chibula chawo. Ndipo ena a iwo sali otsatira chibula cha ena (Akhrisitu satsata chibula cha Ayuda, ndipo Ayuda satsata chibula cha Akhrisitu). Ngati utsatira zofuna zawo, pambuyo pakuti kwakudzera kudziwa ndiye kuti ukhala mwa ochita zoipa.
Aja amene tidawapatsa buku akumuzindikira (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) monga momwe amawazindikilira ana awo. Koma ena mwa iwo akubisa choonadi uku akudziwa.
Ndipo ndithu tikuyesani ndi chinachake monga mantha, njala, kuchepa kwa chuma, kutaika kwa miyoyo ndi kuonongeka kwa mbeu. Tero auze nkhani yabwino opirira.
Ndipo mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi basi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha.[10]
[10] Tanthauzo la ndime iyi ndikuti Mulungu wanu wompembedza ndi mmodzi.
Palibe wompembedza mwachoonadi pa dziko lonse lapansi ndi kumwamba koma Iye Yekha. Iye Ngwachifundo chambiri, Wachisoni kwa zolengedwa Zake; Woyera ndiponso Wotukuka pachikhalidwe Chake chonse. Ndipo ali kutali ndi zimene akumunenerazo. Kodi asatukuke chotani ku zimene akumunenerazo chikhalirecho Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi zonse zam’menemo monga nyenyezi zikuluzikulu zomwe zikuyenda m’menemo mwadongosolo Lake lakuya popanda kuwombana ina ndi inzake. Ndipo m’dziko lapansi adaikamo zolengedwa zambiri zododometsa zomwe zikusonyeza mphamvu Zake zoposa, monga nyama zamoyo ndizomera zosiyanasiyana. Ndipo zikulozera kuti alipo amene adazilenga ndi amene akuziyang’anira yemwe ndi Allah. Dongosolo la zinthuzi likusonyeza kuti Allah ndi mmodzi chifukwa chakuti pakadakhala anzake othandizana naye pakadakhala chisokonezo, wina akadafuna china pomwe wina akufuna china.
Ndithudi, m’kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu-zikulu zomwe zikuyenda pa nyanja (zitasenza zinthu) zothandiza anthu, ndi madzi amene Allah wawatsitsa kuchokera ku mitambo, naukitsira nawo nthaka pambuyo pokhala youma, nawanditsa m’menemo mtundu uliwonse wa nyama (chifukwa cha madziwo), ndi m’kusinthanasinthana kwa mphepo, ndi mitambo yomwe yalamulidwa kuyenda pakati pa thambo ndi nthaka; ndithudi, (m’mzimenezo) muli zisonyezo kwa anthu anzeru, (kuti Allah alipo).
Ndipo fanizo la amene sadakhulupirire (omwe akulalikidwa mawu a Allah, ndi makani awo) lili ngati (mbusa) yemwe akukuwira ziweto zake ndi kuzikalipira pomwe izo sizimva tanthauzo la mawu oitanawo, koma kuitana (chabe) ndi kufuula. (Iwo) ndi agonthi, abubu ndi akhungu. Tero iwo sangazindikire.
Ndithudi, amene akubisa zomwe Allah adavumbulutsa m’buku (la Baibulo) m’malo mwake nasankha zinthu zamtengo wochepa, iwo sadya china mmimba mwawo koma moto basi; ndipo Allah sadzawayankhula tsiku lachimaliziro (mwachifundo koma mokwiya); ndipo sadzawayeretsa. Ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka.[14]
[14] Ibunu Abbas adati ndime iyi ikufotokoza za atsogoleri a Chiyuda monga Kaabi bun Ashirafi ndi Maliki bun Swaifi ndi Huyaye bun Akhatwabi. Anthuwa adali kulandira mphatso zambiri zochokera kwa anthu awo owatsatira. Pamene Muhammad (s.a.w) adampatsa uneneri iwo sadakhulupirire chifukwa choopa kuti sapeza mitulo yochokera kwa anthu awo. Tero anabisa kwa anthu za uneneri wa Muhammad (s.a.w). Apa mpamene Allah adavumbulutsa Ayah (ndime) iyi, yakuti “Ndithudi, amene akubisa zomwe Allah adavumbulutsa m’buku (la Baibulo) m’malo mwake nasankha zinthu za mtengo wochepa iwo sadya china m’mimba mwawo koma moto basi.”
Zimenezo nchifukwa chakuti Allah adavumbulutsa buku Lake mwa choonadi (ndipo iwo adalikana). Koma amene asemphana pa zabukuli ali mu nkangano wonkera nawo kutali kusiya choonadi.
Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali yakuvuma ndi kuzambwe (popemphera Swala); koma ubwino weniweni ndi (wa omwe) akukhulupirira Allah, tsiku lachimaliziro, angelo, buku ndi aneneri; napereka chuma - uku eni akuchifunabe - kwa achibale ndi amasiye, ndi masikini ndi a paulendo (omwe alibe choyendera), ndi opempha, ndi kuombolera akapolo; napemphera Swala, napereka chopereka (Zakaat); ndi okwaniritsa malonjezo awo akalonjeza, ndi opirira ndi umphawi ndi matenda ndi panthawi yankhondo. Iwowo ndi amene atsimikiza (Chisilamu chawo). Ndiponso iwowo ndi omwe ali oopa Allah.
E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu Qiswas (kubwezerana) molingana kwa ophedwa; mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo pa chinthu Chilichonse, atsatire ndi kulonjelera dipolo mwaubwino. (Nayenso wolipa) apereke kwa iye mwa ubwino. Kumeneko ndikufewetsa kumene kwachokera kwa Mbuye wanu, ndiponso chifundo. Ndipo amene alumphe malire pambuyo pa izi, iye adzapeza chilango chopweteka.[15]
[15] Apa akunena kuti, “mfulu kwa mfulu” kuthanthauza kuti aliyense amene wapha nayenso aphedwe. Sikuti aphe munthu wina m’malo mwake.
Chisilamu chisanadze kudali kuponderezana zedi. Mfulu yochokera kufuko la pamwamba, ngati atapha mfulu yafuko la pansi eni a wakuphayo adali kukana kumpereka kuti aphedwe. M’malo mwake amapereka kapolo kuti ndiye aphedwe m’malo mwake. Kapolo wa mfulu wa fuko lapamwamba akapha kapolo wa mfulu wa fuko lapansi sadali kumpereka kuti akaphedwe. Amati: “Kapolo wathuyo ngwapamwamba pomwe wanuyo ngonyozeka. Choncho palibe kufanana pakati pa awiriwa.” Ndipo ngati zitachitika motere kuti kapolo wa onyozeka nkupha kapolo wa odzitukumula, odzitukumulawa amakana kupha kapolo uja m’malo mwake amafuna mfulu yochokera kufuko lonyozekalo. Tero Qur’ani idaletsa machitidwe oterewa. Anthu onse ngofanana, palibe kusiyana pakati pawo. Amene wapha aphedwe yemweyo osati wina, ngakhale atakhala mfulu kapena kapolo. Ili ndilo tanthauzo la Ayah (ndime) imeneyi.
Tsono gawo lina limene likuti: “Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo...” tanthauzo lake nkuti amene wamphera m’bale wake akamkhululukira wakuphayo amlipiritse dipo la ndalama. Tero apa akumuuza iyeyo kuti ngati atamkhululukira m’bale wakeyo nangomulipiritsa ndalama, alonjelere dipolo mwa ubwino. Nayenso wolipayo apereke mwa ubwino. Asachedwetse mwadala namzunguzazunguza. Tsono gawo lachitatu landime yokhayokhayi likutiuza za chifundo chimene Allah watichitira potilekera ife eni kusankha chiweruzo pankhaniyi.
Munthu yemwe amphera m’bale wake akhoza kuchita izi:
a) Kuliuza boma kuti liphenso yemwe adapha m’bale wakeyo.
b) Kapena kumlipiritsa dipo.
c) Kapena kumkhululukira popanda kulipa chilichonse. Ndipo gawo lomaliza landimeyi akumchenjeza wokhululukayo kuti asangomkhululukira munthuyo pamaso pa anthu kenako nkumuchita chiwembu mobisa.
Kwalamulidwa kwa inu kuti mmodzi wanu imfa ikamuyandikira, ngati asiya chuma, apereke malangizo (pa zachumacho) kwa makolo ake awiri ndi achibale ake, mwa ubwino. Ichi nchilamulo kwa oopa Allah.[17]
[17] Kale malamulo ogawira chuma cha masiye asanafotokozedwe adampatsa ufulu aliyense kuti alembe wasiya pa zachuma chakecho m’mene mwini angaonere. Wasiyawo ukhale m’njira ya chilungamo yolingana ndi Shariya. Asachite chinyengo cha mtundu uliwonse.
E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu kusala (m’mwezi wa Ramadan) monga momwe kudalamulidwira kwa anthu akale, inu musadabwere kuti muope Allah (popewa zoletsedwa).
(Mwezi mwalamulidwa kusalawu ndi) mwezi wa Ramadan womwe mkati mwake Qur’an idavumbulutsidwa kuti ikhale chiongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera za chiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa (pakati pa choonadi ndi bodza). Ndipo mwa inu amene akhalepo (pa mudzi) m’mweziwu, asale. Koma amene ali wodwala, kapena ali pa ulendo, akwaniritse chiwerengero m’masiku ena (cha masiku amene sadasale). Allah akukufunirani zopepuka ndipo samakufunirani zovuta, ndiponso (akufuna) kuti mukwaniritse chiwerengerocho ndi kumlemekeza Allah chifukwa chakuti wakutsogolerani, ndikutinso mukhale othokoza.[20]
[20] Allah akufuna kuti tikwaniritse chiwerengero cha masiku makumi atatu (30) kapena makumi awiri ndi mphambu zisanu ndi zinayi (29) chifukwa choti phindu lakumanga silingapezeke mthupi la munthu pokhapokha kumangaku kutakwaniritsidwa m’masiku amenewa.
Ndipo akapolo anga akakufunsa za ine, (auze kuti) Ine ndili pafupi nawo. Ndimayankha zopempha za wopempha pamene akundipempha. Choncho iwo ayankhe kuitana kwanga ndipo andikhulupirire kuti aongoke. [21]
[21] Sikuti iwe wekha ndiwe uzipempha Allah kuti: “Ndipatseni chakuti; nchiritseni kumatenda akutiakuti,” pomwe iwe suvomera kuitana kwa Allah poleka zimene akukuletsa ndi kutsata zimene akukulamula. Yamba kumuvomera Allah usanayambe kumpempha ndiye kuti pempho lako lidzakhala laphindu.
Ndipo musadye chuma chanu pakati panu mwachinyengo pochipereka kwa oweruza (m’njira ya ziphuphu) ndi cholinga choti mudye gawo la chuma cha anthu mwa uchimo uku inu mukudziwa.
Akukufunsa za miyezi nena: “Imeneyi ndi miyeso ya nthawi yozindikilira anthu zinthu zawo ndi nthawi ya Hajj.” Ndipo Siubwino kulowera m’nyumba zanu mbali ya kumbuyo kwake, koma ubwino ndiwayemwe akuopa Allah. Ndipo lowerani m’nyumba podzera m’makomo ake. Opani Allah kuti inu mupambane.[23]
[23] M’nthawi ya umbuli anthu ankati akalowa m’mapemphero a Hajj sadali kulowa m’nyumba zawo podzera pakhomo pa nyumba. Ndipo sadalinso kutulukira pakhomo koma amaboola chibowo kuseri kwa nyumba nkumalowerapo ndi kutulukirapo namaganiza kuti kutero ndimapemphero okondweretsa Allah. Tsono apa Allah akuletsa mchitidwe umenewo.
Ndipo menyanani nao nkhondo pa njira ya Allah (modziteteza) amene akukuthirani nkhondo. Koma musalumphe malire (powamenya amene sadakuputeni), ndithu Allah sakonda olumpha malire.[24]
[24] lyi ndi imodzi mwa ndime zomwe zikufotokoza bodza la amene akunena kuti chisilamu chidafala ndi lupanga powathira anthu nkhondo mowakakamiza kuti alowe m’Chisilamu.
Limeneli, ndithu ndibodza lamkunkhuniza. Apa pakuonetsa kuti Allah akuwapatsa chilolezo asilamu kuti amenyane ndi amene akuwaputa. Palibe chilolezo kwa iwo chowamenyera anthu osawaputa.
Mwezi wopatulika kwa mwezi wopatulika; ndipo zinthu zopatulika paikidwa kubwezerana. Ndipo amene wakuchitirani mtopola, inunso mchitireni mtopola molingana ndi momwe wakuchitirani mtopola, ndipo opani Allah (musapyoze kuposa momwe wakuchitirani). Ndipo dziwani kuti Allah ali pamodzi ndi oopa.
Ndipo perekani chuma chanu pa njira ya Allah, ndiponso musadziponye ku chionongeko ndi manja anu; chitani zabwino. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino.
Ndipo alipo ena mwa iwo omwe akunena kuti: “E Mbuye wathu! tipatseni zabwino pa dziko lapansi komanso pa tsiku lachimaliziro mudzatipatsenso zabwino, ndi kutitchinjiriza ku chilango cha Moto.”
Ndipo mtamandeni Allah m’masiku owerengeka. Koma amene wachita changu pa masiku awiri okha (nabwerera kwawo) palibe tchimo pa iye. Ndipo amene wachedwerapo palibenso tchimo pa iye kwa amene akuopa Allah. Choncho opani Allah, ndipo dziwani kuti kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwa.
Ndipo mwa anthu alipo amene zoyankhula zake zikukondweretsa (iwe) pano pa dziko la pansi, (koma tsiku lachimaliziro kuipa kwake kudzadziwika). Ndipo iye akutsimikizira Allah kuti akhale mboni pa zomwe zili mu mtima mwake pomwe iye ndi wa makani kwambiri.[25]
[25] Tanthauzo lake nkuti alipo ena mwa anthu omwe angakukometsere zoyankhula zawo ndi kuthwa kwa lirime lawo pomwe iwo chikhalirecho akungoyankhula kuti apeze zinthu za m’dziko.
Ndimeyi ikufotokoza za Al-Akhnas bun Sharik yemwe amati akakumana ndi Mtumiki (s.a.w), amatamanda ndi kusonyeza chikhulupiliro chabodza. Koma akachoka pamaso pa mtumiki (s.a.w) amayenda pa dziko ncholinga choononga.
Umo ndi momwe alili makhalidwe a anthu ena, amangokometsa mawu pomwe zochita zawo nzauve. Tero tichenjere ndi anthu otere.
Ndipo akauzidwa kuti: “Opa Allah”, Akugwidwa ndi mwano womupititsa ku machimo, choncho Jahannam ikukwana kwa iye (kuwuchotsa mwano wakewo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!
E inu amene mwakhulupirira! Lowani m’Chisilamu chonse ndipo musatsatire mapazi a satana. Ndithu iye ndi mdani wanu woonekera poyera.[27]
[27] E inu amene mwakhulupilira! Inu eni mabuku, gonjerani Allah. Ndipo lowani m’Chisilamu kwathunthu posachisokoneza ndi chinachache. Mawuwa adanenedwa pamene Abdullahi bun Salaami adalowa m’Chisilamu yemwe adali mkulu wachiyuda. lye adapempha chilolezo kwa mtumiki (s.a.w) kuti aziliremekezabe tsiku la Sabata (la chiweru) ndi kuti aziwerenga mawu a m’Taurati mu Swala zake zausiku.
Kodi pali china chimene akuyembekeza posakhala kuwadzera Allah m’mithunzi ya mitambo ndi (kuwadzera) angelo; nkuweruzidwa chilamulo (chakuonongeka kwawo)? Komatu zinthu zonse zimabwezedwa kwa Allah.
Afunse ana a Israyeli kuti ndizizindikiro zingati zopenyeka zomwe tidawapatsa? Komatu amene angasinthe chisomo cha Allah pambuyo pomudzera, (Allah adzamulanga), ndithudi, Allah ngolanga mwaukali.
Moyo wa pa dziko lapansi wakometsedwa kwa amene sadakhulupirire, ndipo amawachitira chipongwe amene akhulupirira. Koma amene aopa Allah adzakhala pamwamba pawo tsiku la chiweruziro, ndipo Allah amapatsa amene wamfuna popanda chiwerengero.
Anthu onse adali a chipembedzo chimodzi (cha Chisilamu panthawi ya Adam kufikira Nuh kenako adayamba kupatukana), ndipo Allah adatumiza aneneri onena nkhani zabwino ndi ochenjeza; ndipo pamodzi nawo adavumbulutsa mabuku achoonadi kuti aweruzire pakati pa anthu pa zimene adasemphana. Ndipo sadasemphane pa zimenezo koma aja amene adapatsidwa mabukuwo pambuyo powadzera zizindikiro zoonekera poyera, chifukwa chakuchitirana dumbo pakati pawo. Koma Allah adawaongolera amene adakhulupirira kuchoonadi cha zomwe adasempaniranazo, mwachifuniro chake. Ndipo Allah amamutsogolera ku njira yolunjika amene wamfuna.
Akukufunsa kuti apereke chiyani? Nena: “Chuma chilichonse chimene mungachipereke, (chiperekeni) kwa makolo awiri, achibale, kwa ana amasiye, kwa osauka, ndi kwa apaulendo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, ndithudi, Allah akuchidziwa. ”[29]
[29] Adafunsa izi lisanadze lamulo lakagawidwe ka chuma chamasiye. Pamene lidadza lamulo la kagawidwe ka chuma chamasiye lidaletsa kupereka wasiya (chilawo) kwa anthu owagawira chumacho, chifukwa chakuti aliyense wa iwo Allah adampatsa gawo lakelake. Koma ngati munthu ukufuna kupereka wasiya (chilawo) pachuma chako, pereka wasiyawo iwe usanafe ndipo gawo la wasiyawo lisapyole pa 1/3.
Kwalamulidwa kwa inu kumenya nkhondo (yotetezera chipembedzo cha Allah ) pomwe iyo (nkhondoyo) njodedwa ndi inu. Komatu mwina mungachide chinthu pomwe icho chili chahwino kwa inu. Mwinanso mungakonde chinthu pomwe icho chili choipa kwa inu. Koma Allah ndiyemwe akudziwa, ndipo inu simudziwa.
Akukufunsa za (lamulo la) kumenya nkhondo m’miyezi yopatulika. nena: “Kumenya nkhondo m’miyeziyo ndi tchimo lalikulu. Komatu kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kumkana Allah, (ndi kuletsa anthu) ku Msikiti Wopatulikawo, ndi kutulutsa anthu m’menemo nditchimo loposa kwa Allah. Ndipo kutsekereza anthu kuchipembedzo chawo nzoipa kwabasi kuposa kupha. Ndipo sasiya kumenyana nanu kufikira akuchotseni m’chipembedzo chanu ngati angathe. Ndipo mwa inu amene atuluke m’chipembedzo chake, kenako namwalira uku ali osakhulipirira, iwo ndi omwe ntchito zawo zaonongeka pa dziko lapansi mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali.[30]
[30] Otsatira Mneneri (maswahaba) anakumana ndi osakhulupilira padeti ya 30, m’mwezi wa 6 pakalendala ya Chisilamu. Ena amaganiza kuti detilo la pa 30 lidali la m’mwezi wa Rajabu omwe ngoletsedwa kuchitamo nkhondo. Tero Aquraish adamnamizira Muhammad (s.a.w) kuti waswa ulemelero wa miyezi yopatulika. Ndipo adabwera kukamfunsa kuti: “Kodi ndimmene ukuchitira?” Umo ndi momwe Allah adawayankhira.
Ndithudi, amene akhulupirira, ndi amene asamuka namenya nkhondo pa njira ya Allah, iwo ndi amene akuyembekezera chifundo cha Allah. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Akukufunsa za mowa ndi njuga. Nena: “M’zimenezo muli (masautso ndi) uchimo waukulu, ndi zina zothandiza kwa anthu. Koma uchimo wake ngwaukulu zedi kuposa zothandiza zake.” Ndipo akukufunsa kuti aperekenji: Auze: “Chimene chapyolerapo (pa zofuna zanu).” Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah (malamulo) kuti mulingalire.[31]
[31] Apa akufotokoza kuti masautso ndi mavuto omwe mowa ndi njuga zimadzetsa ngaakulu zedi kuposa ubwino wake. Mowa umamchotsa munthu nzeru pomwe nzeru ndidalitso lalikulu kuposa chilichonse. Ndipo mowa umamuonongera munthu chuma ndi kumdzetsera matenda m’thupi mwake. Nayonso njuga nchimodzimodzi. Imawononga chuma ndi kuyambitsa chidani pakati pa anthu. Zonsezi zimadzetsa chisokonezo ku mtundu wa munthu.
Za m’dziko lapansi ndi (zinthu) za tsiku lachimaliziro. Ndipo akukufunsa za ana amasiye, nena: “Kuwachitira zabwino ndiwo ubwino; ngati mutasakanikirana nawo, (ndibwinonso). Iwo ndi abale anu; ndipo Allah akumdziwa woononga ndi wochita zabwino. Ndipo Allah akadafuna, akadakukhwimitsirani malamulo. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.”
Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu ya chikazi yopembedza mafano, ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) musawakwatitse kwa amuna osakhulupirira, mpaka akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yopembedza mafano, ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira ku Moto. Koma Allah akuitanira ku Munda wamtendere ndi ku chikhululuko mwa lamulo lake. Ndipo Iye akulongosola mwatsatanetsatane ndime za mawu ake kwa anthu, kuti athe kukumbukira.[32]
[32] Ndime iyi ikuletsa Asilamu kukwatirana ndi anthu osakhulupilira Allah kupatula Akhirisitu ndi Ayuda. Nkosaloledwa mwamuna wa Chisilamu kukwatira mkazi wopembedza mafano. Nkosaloledwa kuti mkazi wa Chisilamu akwatiwe ndi mwamuna wopembedza mafano. Koma mwamuna wa Chisilamu atha kukwatira mkazi wa Chikhrisitu kapena wa Chiyuda pomwe mkazi wa Chisilamu saloledwa kukwatiwa ndi mwamuna wa Chikhrisitu kapena wa Chiyuda.
Ndipo kulumbilira kwanu dzina la Allah musakuchite kukhala chokuletsani kuchita zinthu zabwino (za m’Chisilamu) ndi kuopa Allah, ndi kuyanjanitsa pakati pa anthu. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[33]
[33] Munthu ngati atalumbira kuti sachita chakutichakuti monga kunena kuti, “ndikulumbira Allah sindidzayankhulana naye uje”, asasiye kukamba naye munthuyo chifukwa chakuti adalumbilira kusayankhulana naye. Koma ayankhulane naye pambuyo popereka dipo kwa masikini pa zomwe adalumbirazo.
Allah sangakulangeni pa kulumbira kwanu kopanda pake, koma adzakulangani chifukwa cha malumbiro anu amene mitima yanu yatsimikiza mwa mphamvu. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza.
Ndipo akazi osiidwa (asakwatiwe) ayembekezere mpaka kuyeretsedwa kutatu kukwanire. Ndipo nkosafunika kwa iwo kubisa chimene Allah walenga m’mimba zawo, ngati akukhulupiriradi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amuna awo ali ndi udindo wowayenereza kuwabwerera m’nthawi imeneyi ngati akufuna kuchita chimvano. Nawonso azimayi ali ndi zofunika kuchitiridwa (ndi amuna awo) monga m’mene ziliri kwa azimayiwo kuchitira amuna awo mwachilamulo cha Shariya. Koma amuna ali ndi udindo okulirapo kuposa iwo. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya. [35]
[35] Mkazi ngati amsudzula ukwati saloledwa kukwatiwa ndi mwamuna wina mpaka Edda yake ithe. Ndipo Edda njosiyanasiyana kwa akazi. Eddayi njotere kusiyana kwake:
1. Mkazi akasiyidwa ali ndi mimba, pamenepo ndiye kuti Edda yake imatha akangobereka. Pompo mwamuna wina akhoza kumkwatira.
2. Ngati wosiidwayo ndi mkazi yemwe sadwala matenda akumwezi
(a) chifukwa chakukalamba
(b) kapena chifukwa chakuti sanakwane zaka zoyambira kudwala kumweziko
(c) kapena chifukwa chakuti chilengedwe chake chili momwemo
(d) kapena zifukwa zina zomwe zimachititsa kuti asadwale matenda akumwezi edda yawo onsewa ndimiyezi itatu. Asakwatiwe mpaka miyezi itatu ithe kuchokera patsiku lomwe adawasudzula.
3. Ngati wosudzulidwayo ndimkazi wodwala matenda akumwezi, Edda yake imatha akamaliza “khului” zitatu. Tsono tanthauzo lakhului maulama amamasulira mosiyanasiyana. Pamazihabi a Imam Shafii tanthauzo lake ndikuyeretsedwa kutatu (twahara zitatu). Choncho kuyeretsedwa kutatuku kukatha kuyambira pomwe adamsudzula, akhoza kukwatiwa. Koma pamazihabi a Kibazi tanthauzo lake ndikudwala kumwezi katatu (hizi zitatu). Kukatha kudwala kumwezi kutatu komwe kwachitika pambuyo pamsudzulo ndiye kuti akhoza kukwatiwa. Edda ngati siinathe mkazi saloledwa kukwatiwa. Ngati atakwatiwa ali mu edda ukwatiwo suvomerezeka. Ndiye kutinso nthawi yonse yomwe mkaziyo akukhala limodzi ndi mwamunayo akuchita naye chiwerewere. Ndipo amene akubadwa mu ukwati wotere ndi ana obadwira mu chiwerewere. Akazi omwe asiidwa ukwati akuwalangiza kuti asabise mimba kuti mwanayo adzadziwike tate wake. Ngati Edda siinathe ndiponso ngati kuchuluka kwa twalaka mwamuna sadamalize, mwamunayo ali ndi ufulu wobwererana ndi mkazi ngati atafuna. Tero padzangofunika kupeza mboni ziwiri zoti zimdziwitse mkaziyo kuti mwamuna wake wabwererana naye. Mkaziyo kapenanso abale ake saloledwa kukaniza zimenezo.
Kodi ndani angamkongoze Allah ngongole yabwino (yochokera m’chuma chake powapatsa amphawi ndi kupereka pa njira ya Allah) kuti amuonjezere zoonjezera zambiri? Ndipo Allah ndi yemwe amafumbata ndi kutambasula, ndipo kwa Iye nkumene mudzabwezedwa.[44]
[44] Apa anthu akuwalimbikitsa kuti azipereka chuma chawo pa njira zabwino ndipo Allah adzawalipira mphoto yambiri. Asachite umbombo kupereka chuma chawo m’njira zabwino pakuti sadaka siichepetsa chuma koma kuchichulukitsa.
Kodi sudamve nkhani ya akuluakulu a ana a Israyeli pambuyo pa Mûsa? Adanena kwa mneneri wawo: “Tidzozere mfumu kuti timenye nkhondo pa njira ya Allah.” Iye (mneneri wawoyo) adati: “Mwinatu simungamenye nkhondoyo ngati kutalamulidwa kwa inu. (Iwo) adati: “Nchotani kuti tisamenye nkhondo pa njira ya Allah pomwe tatulutsidwa m’nyumba zathu pamodzi ndi ana athu?” Koma pamene adalamulidwa kumenya nkhondoyo, adatembenuka, kupatula ochepa mwa iwo. Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za anthu ochita zoipa.
Ndipo mneneri wawo adawauza (kuti): “Ndithu chizindikiro cha ufumu wake, ndikukudzerani bokosi lomwe mkati mwake muli mpumulo wa miyoyo yanu wochokera kwa Mbuye wanu, ndi zotsalira zomwe adazisiya anthu a Mûsa ndi anthu a Harun, atanyamula angelo. Ndithu m’zimenezo muli chisonyezo kwa inu (chosonyeza kuyenera kwa ufumu wake pa inu) ngati mulidi okhulupirira.”
Choncho, Taluti pamene adapita ndi magulu (ake) a nkhondo, adati: “Allah akuyesani mayeso ndi mtsinje (womwe mukumane nawo panjira komwe mukupitako). Choncho amene akamwe mmenemo sali nane. Koma amene sakamwa adzakhala pamodzi nane kupatula amene watunga ndi dzanja lake (ndikumwa; iyeyo ndiye kuti sadalakwe). Koma (iwo) adamwa m’menemo kupatula ochepa mwa iwo. Choncho pamene adaoloka iye pamodzi ndi aja omwe adakhulupirira limodzi naye, (iwo) adati: “Lero sitingamuthe Jaluti ndi magulu ake a nkhondo.” Omwe adali ndi chitsimikizo chokumana ndi Allah adati: “Kodi ndimagulu angati ochepa amene adagonjetsa magulu ambiri mwa chilolezo cha Allah! Ndipo Allah Ali pamodzi ndi opirira.[45]
[45] Kumvera ndichinthu chachikulu kwabasi kuti zinthu za anthu ziyende bwino. Anthu osamvera zinthu zawo siziyenda bwino. Ndipo apa mfumuyi ikuchoka kupita ku nkhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo lomwe lidali losamvera. Choncho Allah adaiuza mfumu ija kuti iwayese mayeso oti asamwe madzi othetsa ludzu lonse. Amene samvera asawatenge kunka nawo ku bwalo lankhondo poona kuti angayambitse chisokonezo kumeneko.
Choncho, adawagonjetsa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo Daud adapha Jaluti; ndipo Allah adampatsa ufumu ndi uneneri, namphunzitsanso zimene adafuna. Allah akadapanda kuwakankha anthu ena kupyolera mwa ena ndiye kuti dziko likadaonongeka. Koma Allah ndi mwini kuchita zabwino pa zolengedwa zonse.[46]
[46] Mneneri Daud adali msirikali m’gulu la nkhondo la mfumu Taluti. Iye adamenya nkhondo ndi cholinga chabwino ndi mwaungwazi zedi mpaka adaipha mfumu ya adaniwo yomwe inkatchedwa Jaluti. Tsono Allah adampatsa ufumu chifukwa chakudzipereka kwakeko.
۞ Amenewo ndi aneneri tidawapatsa ulemelero mosiyanitsa pakati pawo, ena kuposa ena. Mwa iwo alipo amene Allah adawalankhula; ndipo ena adawakwezera kwambiri maulemelero awo. Naye Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zisonyezo zooneka, ndi kumlimbikitsa ndi Mzimu Woyera (rnngelo Gabriel). Allah akadafuna skadamenyana amene adalipo pambuyo pawo, (pa atumikiwo) pambuyo powadzera zizindikiro zooneka, koma adasiyana. Choncho mwa iwo alipo amene adakhulupirira, ndipo ena mwa iwo sadakhulupirire. Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna.[47]
[47] Ndime iyi ikusonyeza kuti atumiki maulemelero awo ngosiyanasiyana kwa Allah monga momwenso alili anthu ndi angelo ndi zinthu zinanso. Amaposana pakalandiridwe ka ulemelero wawo kwa Allah chifukwa chakusiyana zochita zawo. Zochita za ena nzazikulu zedi kapena zochuluka kwambiri kuposa zochita za anzawo. Ndipo apa Allah watchulapo atatu mwa atumiki akuluakulu omwe ndi:-
(a) Musa amene Allah adayankhula naye ndi kumpatsa zozizwitsa zoonekera.
(b) Ndi mneneri Isa (Yesu) yemwe adampatsa ulemelero waukulu
(c) ndi mneneri Muhammad (s.a.w). Enanso mwa aneneri akuluakulu pali mneneri Ibrahim ndi mneneri Nuh monga momwe ikufotokozera ndime ya chisanu ndi ziwiri (7) yam’surati Ahzab.
Allah palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chilichonse. Kusinza sikumgwira ngakhale tulo. Zonse za kumwamba ndi za pansi nza Iye. Kodi ndani angathe kuombola kwa Iye popanda chilolezo chake? Akudziwa za patsogolo ndi zomwe zili pambuyo pawo ndipo zolengedwazo sizidziwa chilichonse pa zomwe zili m’kudziwa Kwake kupatula chimene wafuna. Mpando wake wachifumu wakwanira kumwamba ndi pansi ndipo sizimamvuta kuzisunga zimenezo. Ndipo Iye (Yekha) Njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, (Ngolemekezeka kwambiri).[48]
[48] Ndime iyi ikutchedwa Ayat Kursii; ndime yolemekezeka kwambiri. Kwa msilamu aliyense nkofunika kuizindikira bwinobwino ndimeyi kuti azindikire kuti palibe yemwe angamuike patsogolo kapena pambuyo koma lye Allah wapamwambamwamba. Mu hadisi zambiri za Mtumiki akutilimbikitsa kuiwerenga ndimeyi m’malo awa:-
a) tikatha kuchita salamu pa Swala iliyonse ya Faradh
b) tisanagone
c) pamene tikutuluka m’nyumba
d) polowa m’nyumba
e) tikadzazidwa ndi mantha poopa chinthu chomwe tikuchiona ndi chomwe sitikuchiona
Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, amawatulutsa kumdima ndikuwalowetsa mkuunika, koma amene sadakhulupirire, atetezi awo ndi asatana. Amawatulutsa m’kuunika ndi kuwalowetsa mu mdima; iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali.
Kodi sudamve za yemwe adatsutsana ndi Ibrahim pa za Mbuye wake (Allah)? (Ankanyada) pachifukwa chakuti Allah adampatsa ufumu. Ibrahim adati: “Mbuye wanga ndi yemwe amapereka moyo ndi imfa.” Iye adati: “Inenso ndimapereka moyo ndi imfa.” Ibrahim Adati: “Ndithu Allah amatulutsa dzuwa ku vuma, choncho iwe ulitulutse ku zambwe.” Ndipo uja wosakhulupirira adangoti kakasi, (kusowa chonena). Ndipo Allah satsogolera anthu ochita zoipa.[50]
[50] M’nthawi ya mneneri Ibrahim padali mfumu ina yodzikuza yomwe inkadzitcha kuti ndimulungu ndipo anthu ake adali kuipembedza. Pamene mneneri Ibrahim adadza nayamba kuphunzitsa chipembedzo choona ndikuti iyeyo si mulungu, mfumuyo idati kwa mneneri Ibrahim: “Kodi Mulungu wako woonayo amachita chiyani?” Iye adati “Amapereka moyo ndi kuperekanso imfa.” Mfumuyo idachita ngati sidamvetse cholinga cha mawu a mneneri Ibrahim. Idati: “Nanenso ndimachita zimenezo. Taona mmene ndimachitira.” Pompo adalamula kuti abwere nawo anthu awiri omwe adawalamula kuti aphedwe. Iye adalamula kuti mmodzi aphedwe ndipo winayo amsiye. Choncho zidachitika. Tsono adamuuza Ibrahim: “Waona bwanji? Kodi wina sindidampatse moyo ndipo winayo imfa?” Mneneri Ibrahim pomwe anaona kuti mfumuyo ikungodzipusitsa daladala adaiuza chinthu chomwe iyo sikadatha kuchichita. Adati: “Allah amatulutsa dzuwa ku vuma ndipo iwe ulitulutse ku zambwe.” Pamenepo mfumuyo idangoti kakasi, sidachite chilichonse ndiponso sidanene chilichonse.
(Anthu) amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah napanda kutsatiza pa zomwe aperekazo kukumba, ndiponso masautso, iwo ali ndi mphoto kwa Mbuye wawo ndipo pa iwo sipadzakhala mantha; ndiponso sadzadandaula.
Kodi mmodzi wa inu angakonde kukhala ndi munda wa mitengo ya kanjedza ndi mphesa womwe pansi pake mitsinje ikuyenda, iye mmenemo napeza dzinthu dzamitundumitundu, numpeza ukalamba uku ali ndi ana ofooka; ndipo kamvuluvulu wa moto naugwera (mundawo), nupseleratu (angazikonde zimenezi)? Umo ndimomwe Allah akukulongosolerani ma Ayah (ndime za mawu Ake) kuti muganizire.
Satana amakuopsezani ndi umphawi ndi kukulamulirani kuchita zoipa (monga umbombo), pomwe Allah akukulonjezani chikhululuko kuchokera kwa Iye ndi ubwino (waukulu ngati mupereka); ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngodziwa.[54]
[54] (Ndime 268-271) apa Allah akuwalimbikitsa mtima amene akupereka kuti panthawi iliyonse pamene akupereka Allah adzawaonjezera. Ndipo akuwachenjeza kuti asamamvetsere udyerekezi wa satana umene amauthira m’mitima yawo powauza kuti: “Ngati mupereka, musauka.” Koma Allah akuwauza kuti: “Perekani simusauka. M’malomwake mupeza bwino pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro.”
M’ndime zomwezi Allah wafotokoza za (lonjezo) “naziri” kuti naziri iliyonse imene tikumlonjeza Allah akuidziwa.
Mawu oti “Naziri” nga Chiarabu. M’chichewa akuthandauza kuti, “ndikapeza chakuti ndidzachita chakutichakuti,” “kapena kuti, akachira m’bale wanga ndidzapereka chakutichakuti kwa Allah.”
Mawu anaziriwa siabwino pa malamulo a Chisilamu, ngakhale kuti anthu ambiri amakonda kuchita naziri poganizira kuti akatero Allah awayankha mwachangu namaganiziranso kuti naziri nchinthu chabwino m’Chisilamu pomwe chili chosafunika m’Chisilamu.
Kusafunika kwa naziri m’Chisilamu kuli kotere: Umati: “Allah akandichitira chakutichakuti inenso ndichita chakutichakuti.” Mawu oterewa sali mawu abwino ndiponso akusonyeza kupanda mwambo ndiponso akusonyeza umbombo.
Chifukwa chakuti munthu ofuna kupereka kanthu sanganene kuti: “Muyambe mwandichitira chakuti ndipo ndikupatsani.” Koma ngakhale zili choncho akwaniritsebe malonjezowo. Koma ngati malonjezowo ali pa chinthu choletsedwa asawakwaniritse, ndipo m’malo mwake apereke dipo.
Amene akupereka chuma chawo usiku ndi usana, mobisa ndi moonekera, ali ndi malipiro awo kwa Mbuye wawo; ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula.
Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali.[56]
[56] Ndime iyi yikuletsa kukongoza m’njira yakatapira. Allah akumuopseza mwamphamvu munthu wodya riba. Akumuuza kuti adziwe kuti ali pankhondo yolimbana ndi Allah. Allah akukalipa zedi kwa anthu ochita malonda akatapira. Tero pewani kuchita malonda akatapira.. Kodi inu muli ndi nyonga zomenyerana ndi Allah?
Ngati simuchita (zimenezo), dziwani kuti mukulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo ngati mulapa, maziko a chuma chanu ndi anu. Musapondereze, ndiponso musaponderezedwe.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
ಹುಡುಕಾಟದ ಫಲಿತಾಂಶಗಳು:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".