Check out the new design

ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ * - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ


ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅನ್ನೂರ್   ಶ್ಲೋಕ:
يُقَلِّبُ ٱللَّهُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبۡرَةٗ لِّأُوْلِي ٱلۡأَبۡصَٰرِ
Allah amasintha usiku ndi usana (pambuyo pa usiku, umadza usana, ndipo pambuyo pa usana, umadza usiku). Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa anthu ozindikira (zinthu).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَٱللَّهُ خَلَقَ كُلَّ دَآبَّةٖ مِّن مَّآءٖۖ فَمِنۡهُم مَّن يَمۡشِي عَلَىٰ بَطۡنِهِۦ وَمِنۡهُم مَّن يَمۡشِي عَلَىٰ رِجۡلَيۡنِ وَمِنۡهُم مَّن يَمۡشِي عَلَىٰٓ أَرۡبَعٖۚ يَخۡلُقُ ٱللَّهُ مَا يَشَآءُۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Ndipo Allah adalenga ndi madzi nyama iliyonse; (madzi ndicho chiyambi cha zolengedwa zonse). Zina mwa izo zimayendera mimba zawo; ndipo zina mwa izo zimayenda ndi miyendo iwiri; ndipo zina mwa izo zimayenda ndi inayi. Ndithu Allah amalenga chimene wafuna; ndithu Allah ali ndi mphamvu pa chilichonse.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
لَّقَدۡ أَنزَلۡنَآ ءَايَٰتٖ مُّبَيِّنَٰتٖۚ وَٱللَّهُ يَهۡدِي مَن يَشَآءُ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Ndithu tavumbulutsa Ayah (ndime) zofotokoza momveka (chilichonse chofunika pa chipembedzo). Ndipo Allah amamuongolera ku njira yolunjika amene wamfuna.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَيَقُولُونَ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَبِٱلرَّسُولِ وَأَطَعۡنَا ثُمَّ يَتَوَلَّىٰ فَرِيقٞ مِّنۡهُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَۚ وَمَآ أُوْلَٰٓئِكَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo akunena (kuti): “Takhulupirira Allah ndi Mtumiki, ndipo tamvera.” Kenako ena a iwo amatembenuka pambuyo pa zimenezo; ndipo iwowo sali okhulupirira.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَإِذَا دُعُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ لِيَحۡكُمَ بَيۡنَهُمۡ إِذَا فَرِيقٞ مِّنۡهُم مُّعۡرِضُونَ
Ndipo akawaitanira kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti awaweruze pakati pawo, ena a iwo akukana zimenezo (akadzizindikira okha kuti ngolakwa).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَإِن يَكُن لَّهُمُ ٱلۡحَقُّ يَأۡتُوٓاْ إِلَيۡهِ مُذۡعِنِينَ
Koma akaona kuti chilungamo chili kwa iwo, amam’dzera (Mtumiki mwachangu) uku akusonyeza kumvera.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
أَفِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ أَمِ ٱرۡتَابُوٓاْ أَمۡ يَخَافُونَ أَن يَحِيفَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ وَرَسُولُهُۥۚ بَلۡ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Kodi ali ndi matenda m’mitima mwawo? Kapena akukaika, kapena akuopa kuti Allah ndi Mtumiki Wake awachitira chinyengo? Koma iwo ndi amene ali osalungama.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
إِنَّمَا كَانَ قَوۡلَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ إِذَا دُعُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ لِيَحۡكُمَ بَيۡنَهُمۡ أَن يَقُولُواْ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَاۚ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
Ndithu yankho la okhulupirira akaitanidwa kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti aweruze pakati pawo silikhala lina koma kunena kuti: “Tamva ndipo titsatira.” Iwowo ndiwo opambana.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَيَخۡشَ ٱللَّهَ وَيَتَّقۡهِ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَآئِزُونَ
Ndipo amene amvera Allah ndi Mtumiki Wake, ndikumalemekeza Allah ndi kumuopa, iwowo ndiwo opambana.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
۞ وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَئِنۡ أَمَرۡتَهُمۡ لَيَخۡرُجُنَّۖ قُل لَّا تُقۡسِمُواْۖ طَاعَةٞ مَّعۡرُوفَةٌۚ إِنَّ ٱللَّهَ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ
Ndipo akulumbilira dzina la Allah, kulumbira kwakukulu kuti ukawalamula (kupita ku nkhondo), ndithu apita. Nena: “Musalumbire; kumvera kwanu nkodziwika (kuti nkwabodza); ndithu Allah akudziwa nkhani zonse zomwe muchita.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
 
ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅನ್ನೂರ್
ಅಧ್ಯಾಯಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ
 
ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ

ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಮುಚ್ಚಿ