Check out the new design

ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ * - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ


ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಝ್ಝುಖ್ರುಫ್   ಶ್ಲೋಕ:
وَإِنَّهُۥ لَعِلۡمٞ لِّلسَّاعَةِ فَلَا تَمۡتَرُنَّ بِهَا وَٱتَّبِعُونِۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
Ndipo iye (Isa (Yesu) adzakhala chizindikiro cha Qiyâma (kuti yayandikira). Choncho musaikaikire, koma nditsatireni. Imeneyi ndi njira yolunjika.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَلَا يَصُدَّنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ
Asakutsekerezeni satana; iye kwa inu ndi mdani woonekera.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَلَمَّا جَآءَ عِيسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالَ قَدۡ جِئۡتُكُم بِٱلۡحِكۡمَةِ وَلِأُبَيِّنَ لَكُم بَعۡضَ ٱلَّذِي تَخۡتَلِفُونَ فِيهِۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Ndipo pamene Isa (Yesu) adadza ndi zisonyezo zoonekera poyera, adati: “Ndakudzerani ndi nzeru (yopindulitsa), ndikuti ndikulongosolereni zina zimene mudali kusiyana mu izo; choncho, muopeni Allah ndiponso ndimvereni.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
“Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndi Mbuye wanunso; choncho mupembedzeni; imeneyi ndiyo njira yolunjika.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ عَذَابِ يَوۡمٍ أَلِيمٍ
Koma magulu adasemphana pakati pawo. Ndipo kuonongeka kuchokera mu chilango cha tsiku lowawa kudzakhala pa amene adzichitira okha zoipa.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا ٱلسَّاعَةَ أَن تَأۡتِيَهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Palibe chimene akuyembekeza, koma Qiyâma basi yomwe iwadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira (ali otanganidwa ndi za m’dziko).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
ٱلۡأَخِلَّآءُ يَوۡمَئِذِۭ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوٌّ إِلَّا ٱلۡمُتَّقِينَ
Abwenzi tsiku limenelo adzakhala odana, wina ndi mnzake, (chifukwa chakuti adali kuthandizana pa zinthu zosalungama ndi zamachimo) kupatula oopa Allah (amene adachita chibwenzi mwa Allah, pothandizana kukwaniritsa malamulo a Allah ndi kusiya zimene Allah waletsa).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
يَٰعِبَادِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ
(Allah adzati): E inu akapolo Anga (abwino)! Palibe kuopa kwa inu lerolino ndiponso simudandaula.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ مُسۡلِمِينَ
Amene adakhulupirira zisonyezo Zathu ndipo adali Asilamu (ogonjera Allah).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ أَنتُمۡ وَأَزۡوَٰجُكُمۡ تُحۡبَرُونَ
Lowani ku Munda wamtendere, inu ndi akazi anu musangalatsidwa.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
يُطَافُ عَلَيۡهِم بِصِحَافٖ مِّن ذَهَبٖ وَأَكۡوَابٖۖ وَفِيهَا مَا تَشۡتَهِيهِ ٱلۡأَنفُسُ وَتَلَذُّ ٱلۡأَعۡيُنُۖ وَأَنتُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Adzakhala akupititsidwa mbale zagolide ndi matambula (agolide); zonse zokomera moyo zidzakhala mmenemo ndi zokomera maso, ndipo inu mudzakhala mmenemo nthawi yaitali.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَتِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِيٓ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo umeneo ndi munda umene mwapatsidwa chifukwa cha (zabwino) zimene munkachita.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
لَكُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٞ كَثِيرَةٞ مِّنۡهَا تَأۡكُلُونَ
Inu mupeza mmenemo zipatso zambiri zomwe muzidya.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
 
ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಝ್ಝುಖ್ರುಫ್
ಅಧ್ಯಾಯಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ
 
ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ

ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಮುಚ್ಚಿ