Check out the new design

ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ * - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ


ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಲ್ -ಮಾಇದ   ಶ್ಲೋಕ:
وَحَسِبُوٓاْ أَلَّا تَكُونَ فِتۡنَةٞ فَعَمُواْ وَصَمُّواْ ثُمَّ تَابَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ ثُمَّ عَمُواْ وَصَمُّواْ كَثِيرٞ مِّنۡهُمۡۚ وَٱللَّهُ بَصِيرُۢ بِمَا يَعۡمَلُونَ
Ndipo ankaganiza kuti sipapezeka chilango; tero adali akhungu ndi agonthi. Kenako Allah adawalandira kulapa kwawo (pamene adalapa). Komabe ambiri a iwo adali akhungu, ndi ogontha. Ndipo Allah akuona zimene akuchita.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
لَقَدۡ كَفَرَ ٱلَّذِينَ قَالُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡمَسِيحُ ٱبۡنُ مَرۡيَمَۖ وَقَالَ ٱلۡمَسِيحُ يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ رَبِّي وَرَبَّكُمۡۖ إِنَّهُۥ مَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَقَدۡ حَرَّمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِ ٱلۡجَنَّةَ وَمَأۡوَىٰهُ ٱلنَّارُۖ وَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِنۡ أَنصَارٖ
Ndithudi am’kana Allah amene anena kuti, Mulungu ndiye Isa (Yesu) mwana wa Mariya.” Pomwe Mesiya adati: “Inu ana a Israyeli! Pembedzani Allah Yemwe ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.” Ndithudi, amene aphatikize Allah ndi chinthu china, ndithudi Allah waletsa kwa iye kukalowa ku Munda wamtendere, ndipo malo ake ndi ku Moto. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
لَّقَدۡ كَفَرَ ٱلَّذِينَ قَالُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ ثَالِثُ ثَلَٰثَةٖۘ وَمَا مِنۡ إِلَٰهٍ إِلَّآ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۚ وَإِن لَّمۡ يَنتَهُواْ عَمَّا يَقُولُونَ لَيَمَسَّنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٌ
Ndithudi, am’kana Allah amene amanena kuti “Ndithu Allah ndi mmodzi mwa (milungu) itatu,” pomwe palibe mulungu wina koma Mulungu Mmodzi yekha. Ngati sasiya zomwe akunenazo, ndithudi, mwa iwo amene sadakhulupirire chiwakhudza chilango chopweteka.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
أَفَلَا يَتُوبُونَ إِلَى ٱللَّهِ وَيَسۡتَغۡفِرُونَهُۥۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
Kodi salapa kwa Allah ndi kumpempha chikhululuko? Komatu Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
مَّا ٱلۡمَسِيحُ ٱبۡنُ مَرۡيَمَ إِلَّا رَسُولٞ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِهِ ٱلرُّسُلُ وَأُمُّهُۥ صِدِّيقَةٞۖ كَانَا يَأۡكُلَانِ ٱلطَّعَامَۗ ٱنظُرۡ كَيۡفَ نُبَيِّنُ لَهُمُ ٱلۡأٓيَٰتِ ثُمَّ ٱنظُرۡ أَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ
Mesiya mwana wa Mariya sali chilichonse koma ndi Mtumiki wa Allah chabe. Ndithudi, atumiki ambiri adapita kale patsogolo pake. Nayenso mayi wake ndi mkazi wachoonadi, onse awiri adali kudya chakudya, (ndipo chotsatira chake amapita kokadzithandiza. Nanga ndi milungu yotani yopita kukadzithandiza?) Taona momwe tikufotokozera kwa iwo zizindikiro. Taonanso mmene akutembenuziridwa (kusiya choonadi).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قُلۡ أَتَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَمۡلِكُ لَكُمۡ ضَرّٗا وَلَا نَفۡعٗاۚ وَٱللَّهُ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Nena: “Kodi mukupembedza chimene sichingakupatseni vuto ngakhale chabwino, kusiya Allah? Pomwe Allah ndiye Wakumva, Wodziwa.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قُلۡ يَٰٓأَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ لَا تَغۡلُواْ فِي دِينِكُمۡ غَيۡرَ ٱلۡحَقِّ وَلَا تَتَّبِعُوٓاْ أَهۡوَآءَ قَوۡمٖ قَدۡ ضَلُّواْ مِن قَبۡلُ وَأَضَلُّواْ كَثِيرٗا وَضَلُّواْ عَن سَوَآءِ ٱلسَّبِيلِ
Nena: “E inu anthu a buku! Musapyole malire pa chipembedzo chanu popanda choonadi ndipo musatsatire zofuna za anthu omwe adasokera kale, nawasokeretsanso ambiri, ndi kusokera kunjira yowongoka (yolungama).”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
 
ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಲ್ -ಮಾಇದ
ಅಧ್ಯಾಯಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ
 
ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ

ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಮುಚ್ಚಿ