Check out the new design

ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ * - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ


ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಲ್- ಅನ್ ಆಮ್   ಶ್ಲೋಕ:
هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّآ أَن تَأۡتِيَهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَوۡ يَأۡتِيَ رَبُّكَ أَوۡ يَأۡتِيَ بَعۡضُ ءَايَٰتِ رَبِّكَۗ يَوۡمَ يَأۡتِي بَعۡضُ ءَايَٰتِ رَبِّكَ لَا يَنفَعُ نَفۡسًا إِيمَٰنُهَا لَمۡ تَكُنۡ ءَامَنَتۡ مِن قَبۡلُ أَوۡ كَسَبَتۡ فِيٓ إِيمَٰنِهَا خَيۡرٗاۗ قُلِ ٱنتَظِرُوٓاْ إِنَّا مُنتَظِرُونَ
Kodi chilipo chimene akudikira kuposa kuwadzera angelo (kudzawachotsa miyoyo yawo?) Kapena kudza Mbuye wako (tsiku la Qiyâma kuzaweruza)? Kapena kudza zina mwa zizindikiro za Mbuye wako (zomwe adati zidzadza)? Tsiku lakudza zina mwa zizindikiro za Mbuye wako, munthu (wosakhulupirira) chikhulupiliro chake (panthawiyo) sichidzamthandiza, yemwe sadakhulupirirepo kale, kapena (msilamu) yemwe sanapindule nacho chikhulupiliro chake. Nena: “Dikirani. Nafenso tikudikira.”[175]
[175] Chisilamu kuti chikamthandize munthu nkofunika kuti achigwiritsire ntchito pa moyo wake wonse. Chisilamu chokha popanda kuchigwiritsira ntchito sichikwanira ndiponso sichingamtchinjirize munthu kuchilango cha Moto. Ndipo yemwe sali msilamu kuti Chisilamu chikamthandize nkofunika kuti alowe m’Chisilamu ali ndi moyo, osati pamene imfa yamufika. Ndipo nayenso msilamu wochita zoipa, akalapa imfa itamufika kale kulapa kwakeko sikungamthandize. Koma alape pamene ali ndi moyo wangwiro. Pamenepo ndiye kuti Allah alandira kulapa kwake. Osati kulapa uku imfa akuiona ndi maso ake.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
إِنَّ ٱلَّذِينَ فَرَّقُواْ دِينَهُمۡ وَكَانُواْ شِيَعٗا لَّسۡتَ مِنۡهُمۡ فِي شَيۡءٍۚ إِنَّمَآ أَمۡرُهُمۡ إِلَى ٱللَّهِ ثُمَّ يُنَبِّئُهُم بِمَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ
Ndithudi, anthu amene achigawa Chipembedzo chawo, nakhala Mipingomipingo, iwe Siuli nawo pachilichonse. Ndithu zotsatira zawo zili kwa Allah, (ndi yemwe adzawalanga. Ndipo panthawi yowalanga) adzawauza zomwe adali kuchita.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ عَشۡرُ أَمۡثَالِهَاۖ وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَلَا يُجۡزَىٰٓ إِلَّا مِثۡلَهَا وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Amene wachita chabwino alipidwa zabwino khumi zofanana ndi icho. Ndipo amene wachita choipa sadzalipidwa koma chonga icho (popanda kuonjezera). Ndipo iwo sadzaponderezedwa.[176]
[176] China mwa chifundo cha Allah pa zolengedwa zake ndiko kuti adzamulipira munthu pa tsiku la chimaliziro mosiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa. Ngati adachita chabwino chimodzi, adzamulipira mphoto ya zinthu khumi zoposera pa chabwino chimodzicho ndipo ngati adachita choipa, sadzamuonjezera malipiro a choipacho koma adzamulipira chofanana ndi choipacho. Tanthauzo lake nkuti chabwino chimodzi malipiro ake ndi zabwino khumi; pomwe choipa chimodzi mphoto yake ndi choipanso chimodzi.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قُلۡ إِنَّنِي هَدَىٰنِي رَبِّيٓ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ دِينٗا قِيَمٗا مِّلَّةَ إِبۡرَٰهِيمَ حَنِيفٗاۚ وَمَا كَانَ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Nena: “Ndithudi, ine Mbuye wanga wandiongolera ku njira yoongoka, kuchipembedzo cholingana, chomwe ndi chipembedzo cha Ibrahim, yemwe adali wolungama. Sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قُلۡ إِنَّ صَلَاتِي وَنُسُكِي وَمَحۡيَايَ وَمَمَاتِي لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Nena: “Ndithudi, Swala yanga, mapemphero anga onse, moyo wanga, ndi imfa yanga, (zonse) nza Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
لَا شَرِيكَ لَهُۥۖ وَبِذَٰلِكَ أُمِرۡتُ وَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
“Alibe wothandizana naye. Izi ndi zomwe ndalamulidwa, ndipo ine ndine woyamba mwa Asilamu (ogonjera Allah).”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قُلۡ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَبۡغِي رَبّٗا وَهُوَ رَبُّ كُلِّ شَيۡءٖۚ وَلَا تَكۡسِبُ كُلُّ نَفۡسٍ إِلَّا عَلَيۡهَاۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرۡجِعُكُمۡ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ فِيهِ تَخۡتَلِفُونَ
Nena: “Kodi ndifune mbuye wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Mbuye wa chinthu chilichonse? Ndipo mzimu uliwonse siuchita choipa koma ukudzichitira wokha. Mzimu wosenza machimo siudzasenza machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu (nonse) ndi kwa Mbuye wanu, (Allah), ndipo adzakuuzani zomwe mudali kusiyana.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَكُمۡ خَلَٰٓئِفَ ٱلۡأَرۡضِ وَرَفَعَ بَعۡضَكُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٖ دَرَجَٰتٖ لِّيَبۡلُوَكُمۡ فِي مَآ ءَاتَىٰكُمۡۗ إِنَّ رَبَّكَ سَرِيعُ ٱلۡعِقَابِ وَإِنَّهُۥ لَغَفُورٞ رَّحِيمُۢ
Ndipo Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala am’lowam’malo pa dziko (kulowa m’malo mwa anzanu omwe adaonongeka). Ndipo wawatukula pa ulemelero (ndi pa chuma) ena a inu pamwamba pa ena kuti akuyeseni pa zomwe wakupatsani. (Amene apatsidwa chuma ndi ulemelero athandize amene sadapatsidwe. Ndipo amene sadapatsidwe apirire asalande chinthu chamwini). Ndithudi, Mbuye wako Ngwachangu pokhaulitsa. Ndiponso Iye Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha.[177]
[177] Ndime iyi ikusonyeza kuti kukhupuka ndi ulemelero, sindizo zizindikiro zosonyeza kuti munthuyo ngofunika kwa Allah. Ndiponso kusauka ndi kunyozeka sizizindikiro kuti munthuyo ngosafunika kwa Allah kapena wonyozeka kwa Allah. Koma kulemera, ulemelero, kusauka ndi kunyozeka.zonsezi amazipereka m’njira ya mayeso.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
 
ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಲ್- ಅನ್ ಆಮ್
ಅಧ್ಯಾಯಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ
 
ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ

ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಮುಚ್ಚಿ