Check out the new design

ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ * - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ


ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಲ್- ಅಅ್ ರಾಫ್   ಶ್ಲೋಕ:
حَقِيقٌ عَلَىٰٓ أَن لَّآ أَقُولَ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّۚ قَدۡ جِئۡتُكُم بِبَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّكُمۡ فَأَرۡسِلۡ مَعِيَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
“Ndikofunika kwa ine kuti ndisamnenere Allah chilichonse koma choonadi basi. Ndithu ndakudzerani ndi chizindikiro choonekera kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho, aleke ndinke nawo ana a Israyeli.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قَالَ إِن كُنتَ جِئۡتَ بِـَٔايَةٖ فَأۡتِ بِهَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
(Farawo) adati: “Ngati wadza ndi chizindikiro, bwera nacho (tichione), ngati iwe ulidi mmodzi wa onena zoona.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
فَأَلۡقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ ثُعۡبَانٞ مُّبِينٞ
Choncho adaponya ndodo yake pansi. Mwadzidzidzi, idasanduka njoka yooneka.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَنَزَعَ يَدَهُۥ فَإِذَا هِيَ بَيۡضَآءُ لِلنَّٰظِرِينَ
Ndipo adatulutsa dzanja lake pompo lidakhala loyera, lowala kwa oliona.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِ فِرۡعَوۡنَ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ عَلِيمٞ
Nduna za mwa anthu a Farawo zidati: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa (kwambiri zamatsenga).”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
يُرِيدُ أَن يُخۡرِجَكُم مِّنۡ أَرۡضِكُمۡۖ فَمَاذَا تَأۡمُرُونَ
“Akufuna kukusamutsani mdziko mwanu. Nanga mukulangiza zotani?”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قَالُوٓاْ أَرۡجِهۡ وَأَخَاهُ وَأَرۡسِلۡ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ
(Iwo) adati (kwa Farawo): “Muleke pang’ono iye ndi m’bale wakeyu (usawaphe); ndipo tumiza osonkhanitsa m’mizinda kuti akusonkhanitsire (amatsenga onse akuluakulu).”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
يَأۡتُوكَ بِكُلِّ سَٰحِرٍ عَلِيمٖ
“Kuti akubweretsere wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri.”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَجَآءَ ٱلسَّحَرَةُ فِرۡعَوۡنَ قَالُوٓاْ إِنَّ لَنَا لَأَجۡرًا إِن كُنَّا نَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبِينَ
Amatsenga adadza kwa Farawo; nati: “Kodi ife tipeza malipiro ngati titapambana?”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قَالَ نَعَمۡ وَإِنَّكُمۡ لَمِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ
(Farawo) adati: “Inde, ndipo mudzakhala mwa oyandikitsidwa (mudzakhala nduna zanga).”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلۡقِيَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ نَحۡنُ ٱلۡمُلۡقِينَ
(Amatsenga) adati: “E iwe Mûsa! Kodi uyamba kuponya ndiwe (matsenga ako pamaso pa anthu), kapena ife tikhale oyambilira kuponya?”
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
قَالَ أَلۡقُواْۖ فَلَمَّآ أَلۡقَوۡاْ سَحَرُوٓاْ أَعۡيُنَ ٱلنَّاسِ وَٱسۡتَرۡهَبُوهُمۡ وَجَآءُو بِسِحۡرٍ عَظِيمٖ
Mûsa adati: “Ponyani.” Choncho pamene adaponya adalodza maso a anthu ndikuwaopseza. Ndipo adadza ndi matsenga aakulu zedi.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
۞ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَلۡقِ عَصَاكَۖ فَإِذَا هِيَ تَلۡقَفُ مَا يَأۡفِكُونَ
Ndipo tidamzindikiritsa Mûsa ndi chivumbulutso (kuti): “Ponya ndodo yako.” Pompo iyo idameza zamatsengazo.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
فَوَقَعَ ٱلۡحَقُّ وَبَطَلَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Choncho, choonadi chidatsimikizika, ndipo zidapita pachabe zomwe ankachita.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
فَغُلِبُواْ هُنَالِكَ وَٱنقَلَبُواْ صَٰغِرِينَ
Choncho adagonjetsedwa pamenepo, nakhala onyozeka.
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
وَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سَٰجِدِينَ
Ndipo amatsenga adadzigwetsa uku akulambira (Allah).
ಅರಬ್ಬಿ ವ್ಯಾಖ್ಯಾನಗಳು:
 
ಅರ್ಥಗಳ ಅನುವಾದ ಅಧ್ಯಾಯ: ಅಲ್- ಅಅ್ ರಾಫ್
ಅಧ್ಯಾಯಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ
 
ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ - ಅನುವಾದಗಳ ವಿಷಯಸೂಚಿ

ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಮುಚ್ಚಿ