Check out the new design

وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا * - پێڕستی وه‌رگێڕاوه‌كان


وه‌رگێڕانی ماناكان سوره‌تی: الأنعام   ئایه‌تی:
ذَٰلِكَ أَن لَّمۡ يَكُن رَّبُّكَ مُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ بِظُلۡمٖ وَأَهۡلُهَا غَٰفِلُونَ
Zimenezi nchifukwa choti Mbuye wako sali woononga midzi mwachinyengo pomwe eni ake ali oiwala. (Koma ankawatumizira aneneri kuti awachenjeze ndi kuwakumbutsa).[172]
[172] Allah sapereka chilango kwa anthu asanawatumizire Mtumiki. Ndiponso sangawalange pa zinthu zomwe nzosatheka kuzizindikira, pokhapokha Mtumiki atawaphunzitsa, monga kupemphera Swala, kusala m’mwezi wa Ramadan. Koma angawalange pazomwe iwo angathe kuzizindikira kuti nzoipa; monga munthu kumchenjelera mnzake ndi zina zotero.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَلِكُلّٖ دَرَجَٰتٞ مِّمَّا عَمِلُواْۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا يَعۡمَلُونَ
Ndipo onse adzakhala ndi nyota (za ulemelero) kuchokera m’zochita zawo. Ndipo Mbuye wako sali wamphwayi pa zimene akuchita.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَرَبُّكَ ٱلۡغَنِيُّ ذُو ٱلرَّحۡمَةِۚ إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ وَيَسۡتَخۡلِفۡ مِنۢ بَعۡدِكُم مَّا يَشَآءُ كَمَآ أَنشَأَكُم مِّن ذُرِّيَّةِ قَوۡمٍ ءَاخَرِينَ
Ndipo Mbuye wako Ngokwanira (Wolemera), Mwini chifundo. Ngati afuna angakuchotseni ndi kuwaika m’malo mwanu amene wawafuna monga momwe adakulengerani kuchokera m’mbumba ya anthu ena.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِنَّ مَا تُوعَدُونَ لَأٓتٖۖ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ
Ndithu (palibe chikaiko) zomwe mukulonjezedwa zifika. Ndipo simungathe kuzilepheretsa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
قُلۡ يَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَامِلٞۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن تَكُونُ لَهُۥ عَٰقِبَةُ ٱلدَّارِۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Nena: “E inu anthu anga! Chitani zanu (zimene mufuna) momwe mungathere. Nanenso ndichita zanga. Choncho mudzaziwa kuti ndani mapeto ake adzakhale ndi malo abwino. Ndithudi, sangapambane anthu ochita zoipa.”[173]
[173] Ayah iyi ikusonyeza kuti munthu wapatsidwa ufulu wochita kapena kusachita poopera kuti angadzanene kuti adakakamizidwa. Apa nzachidziwikire kuti amene wasankha chabwino adzapeza chabwino. Ndipo yemwe wasankha choipa adzapeza choipa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَجَعَلُواْ لِلَّهِ مِمَّا ذَرَأَ مِنَ ٱلۡحَرۡثِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ نَصِيبٗا فَقَالُواْ هَٰذَا لِلَّهِ بِزَعۡمِهِمۡ وَهَٰذَا لِشُرَكَآئِنَاۖ فَمَا كَانَ لِشُرَكَآئِهِمۡ فَلَا يَصِلُ إِلَى ٱللَّهِۖ وَمَا كَانَ لِلَّهِ فَهُوَ يَصِلُ إِلَىٰ شُرَكَآئِهِمۡۗ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ
Ampangira Allah (amugawira) gawo m’zomera ndi ziweto zimene (Allah) adalenga. Akunena: “Gawo ili ndi la Allah.” Mkuyankhula kwawo kwachabe: “Ndipo gawo ili ndi la aja omwe tikuwaphatikiza ndi Allah.” Choncho zomwe alinga kuwapatsa aphatikizi awo, sizingafike kwa Allah. Ndipo zimene zili za Allah, ndizomwe zingafike kwa aphatikizi awo (mafano awo). Kwaipitsitsa kuweruza kwaoku.[174]
[174] Kale anthu osakhulupilira pamene ankalima akafuna kubzala, minda yawo adali kuigawa zigawo ziwiri. Ankati: ‘‘Mbewu za chigawo ichi nza Allah, kuti mbewu zakezo adzazigwiritsa ntchito powapatsa masikini, ana a masiye ndi osowa. Ndipo ankatinso: “Mbewu za gawo ili nzamafano athu omwe ankati ngamnzake a Allah kuti zinthu zotuluka m’menemo ziperekedwe kwa anthu ogwira ntchito m’menemo. Choncho ngati patapezeka mliri pachigawo chomwe ankati zokolola zake nzamafano awo, amatenga chigawo chomwe amati dzinthu dzake nza Allah napereka ku mafano. Koma mliri ukagwera pa chigawo cha Allah, sadali kutenga zamafano nkupereka kwa Allah. Izi amachita ngati mafano ngabwino kuposa Allah.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَكَذَٰلِكَ زَيَّنَ لِكَثِيرٖ مِّنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ قَتۡلَ أَوۡلَٰدِهِمۡ شُرَكَآؤُهُمۡ لِيُرۡدُوهُمۡ وَلِيَلۡبِسُواْ عَلَيۡهِمۡ دِينَهُمۡۖ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا فَعَلُوهُۖ فَذَرۡهُمۡ وَمَا يَفۡتَرُونَ
Momwemo milungu yawo imawakometsera ambiri mwa ophatikiza Allah ndi mafano kupha ana awo (monga nsembe ya mafanowo) kuti awaononge ndikuwabweretsera chisokonezo pa chipembedzo chawo. Ndipo ngati Allah akadafuna, sakadachita zimenezo. Choncho asiye ndi izo zomwe akupeka.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
 
وه‌رگێڕانی ماناكان سوره‌تی: الأنعام
پێڕستی سوره‌ته‌كان ژمارەی پەڕە
 
وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا - پێڕستی وه‌رگێڕاوه‌كان

وەرگێڕان: خالد ئیبراهيم بيتالا.

داخستن