Kodi nchodabwitsa kwa anthu kuti tamuvumbulutsira (chivumbulutso) munthu wochokera mwa iwo (yemwe ndi Muhammad {s.a.w}) kuti: “Chenjeza anthu ndipo awuze nkhani yabwino amene akhulupirira kuti iwo adzapeza ulemelero waukulu kwa Mbuye wawo?” Osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wa matsenga (mfiti) wowonekera.’’[214]
[214] Allah akuti: Sikunayenere kwa anthu kudabwa ndi kutsutsa chivumbulutso chathu kwa munthu wochokera mwa iwo yemwe cholinga chake nkuti achenjeze anthu za chilango cha Allah ndi kuti awauze nkhani zabwino amene mwa iwo akhulupilira. Ndiponso nkosayenera kwa iwo kumunenera Muhammadi (s.a.w), Mtumiki wathu, kuti iye ndi wa matsenga.
Ndithu Mbuye wanu ndi Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zonse za m’menemo) m’masiku asanu ndi limodzi; (masiku omwe palibe yemwe akuwadziwa kutalika kwake koma Iye Yekha), kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, kukhazikika kwake akukudziwa ndi Iye Yekha basi). Amayendetsa zinthu (za zolengedwa Zake). Palibe muomboli (woombola wina) koma pambuyo pa chilolezo Chake (Allah). Uyo ndiye Allah Mbuye wanu; choncho mupembedzeni Iye. Kodi simungakumbukire (kuti mafanowo si milungu)?
Kobwerera kwanu nonsenu ndi kwa Iye. Ili ndilonjezo la Allah loona. Ndithu Iye ndi Yemwe adayamba kulenga (zolengedwa), ndiponso ndi Yemwe adzazibwereza (pambuyo pa imfa) kuti adzawalipire amene adakhulupirira ndi kumachita zabwino mwa chilungamo. Ndipo amene sadakhulupirire, akapeza zakumwa za madzi owira ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.
Iye (Allah) ndiYemwe adapanga dzuwa kukhala lowala, ndi mwezi kukhala wounika; ndipo adaukonzera mbuto (masitesheni) kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero chake. Allah sadalenge zimenezo koma mwachoonadi (ndi cholinga cha nzeru). Akufotokoza Ayah (Zake) kwa anthu ozindikira.[215]
[215] Mbuye wanu ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka. Ndipo dzuwa adalipanga kuti lizipereka kuwala ku zolengedwa; naonso mwezi kuti uzitumiza kuunika. Ndipo mwezi adaupangira njira momwe umayenda. Ndipo kuunika kwake kumakhala kosiyanasiyana chifukwa cha masitesheniwa. Izi nkuti zikuthangateni powerengera nthawi, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka. Allah adalenga zimenezi ncholinga chanzeru zakuya.
Mapemphero awo m’menemo adzakhala kunena: “Subuhanaka Lahuma’ Ulemelero ndi Wanu, E Inu Allah!” Ndipo kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala kunena: “Salaam (alayikum’) Mtendere (ukhale pa inu).” Ndipo duwa yawo yomaliza (idzakhala kuyamika ponena kuti) “Alham’du Lillah Rabil a’lamin’. Kuyamikidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zolengedwa.”[216]
[216] Pemphero la okhulupilira lidzakhala kumuyeretsa Allah kuzimene adali kumunenera osakhulupilira pa dziko lapansi. Nayenso Allah adzakhala akuwalonjera. Ndipo nawo adzakhala akulonjerananso wina ndi mnzake. Uku nkutsimikizira mtendere ndi kukhazikika kopanda kutekeseka ndi china chilichonse. Ndipo nthawi zonse kothera kwa mapemphero awo ndi kuthokoza Allah powalimbikitsa pa chikhulupiliro.
[217] Munthu vuto likamkhudza mthupi mwake, kapena pachuma chake ndi mwina motero apo mpomwe amazindikira za kufooka kwake. Amayamba kumkuwira Mbuye wake Allah ndi kumpempha m‘kakhalidwe kake konse- chogona, chokhala, choimilira kuti amchotsere mliri umene wamgwera. Koma Allah akamuyankha namchotsera vutolo amamfulatira Allah napitiriza kumlakwira naiwala ubwino wa Allah ngati kuti vuto silidamkhudze, ngati kutinso sadampempheko Allah. Ichi ndicho chikhalidwe cha anthu ambiri. Amadziwa Allah pomwe mavuto akawagwera. Koma akakhala pamtendere Allah amamuiwala.
Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, akunena amene sayembekezera kukumana ndi Ife: “Bwera ndi Qur’an (yogwirizana ndi zofuna zathu) osati iyi, kapena uyisinthe (pang’ono).” Nena: “Nkosatheka kwa ine kuisintha mwachifuniro changa. Sinditsata koma zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine. Ndithu ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”
Ndipo ndithudi anthu kalero (m’nthawi ya Adam) adali mpingo umodzi (opembedza Allah), koma adasiyana (pambuyo pake). Ndipo pakadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako, lomwe lidatsogola (lakuti adzawalanga tsiku la Qiyâma), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo m’zomwe adali kusiyana.[218]
[218] Ndithudi, anthu mchilengedwe chawo adali a mpingo umodzi wogonjera Allah mwa chilengedwe. Kenako Allah adawatumizira aneneri kuti awatsogolere kunjira Yake molingana ndi chilamulo chake Allah. Koma ngakhale zili tere anthu adali ndi ufulu mwa chilengedwe chawo kulandira choipa kapena chabwino. Potero, choipa chidawagonjetsa ena a iwo natsata zilakolako za satana. Nasiyana ndi anzawo chifukwa chazimenezo. Komatu padali lamulo la Allah la pachiyambi loti oipa sadzawalanga mwachangu koma kufikira nthawi yawo itakwana. Pakadapanda lamuloli ndiye kuti onse akadawalanga nthawi yomweyo.
Iye ndi Yemwe amakuyendetsani pa ntunda ndi pa nyanja; kufikira pomwe mumakhala m’zombo; ndipo zimayenda nawo (zombozo) ndi mphepo yabwino, naisangalalira. (Mwadzidzidzi) namondwe nkuzidzera (zombozo) ndipo mafunde nkuwadzera mbali zonse natsimikiza kuti azingidwa (ndi chionongeko); amampempha Allah modzipereka kwa Iye mukupempha kwawo (uku akunena): “Ngati mutipulumutsa pa ichi, tidzakhala m’gulu la oyamika (nthawi zonse)!”
Ndipo sikotheka Qur’an iyi kukhala yopekedwa, yosachokera kwa Allah (monga momwe munenera). Koma (yachokera kwa Allah) kutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake, ndi kulongosola za buku (lakale). Palibe chikaiko m’menemo (kuti) yachokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
Ndipo mwa iwo alipo ena amene akumvetsera kwa iwe, (koma osati ndi cholinga choti adziwe). Kodi iwe ungathe kuwamveretsa agonthi, chikhalirecho nzeru alibe?
E inu anthu! Ndithu ulaliki wakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu ndi machiritso a matenda omwe ali m’mitima mwanu, ndiponso nchiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira.
Nena: “Chifukwa cha ubwino wa Allah ndi chifundo Chake (mwapeza zimenezi), choncho asangalalire zimenezi.” Izi ndizabwino kwambiri kuposa zimene akusonkhanitsa (m’zinthu za dziko lapansi).
Kodi ali ndi ganizo lotani amene akumpekera Allah bodza pa za tsiku la Qiyâma? Ndithu Allah Ndi mwini ubwino wochuluka kwa anthu. Koma ambiri a iwo sathokoza.
Tamverani! Ndithu (zonse) za kumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndipo amene akupembedza zina kusiya Allah, satsatira aphatikizi (a Allah). Akungotsatira zoganizira, ndipo iwo sanena china koma bodza basi.
Iye (Allah) ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti muzipumamo, ndi (adakupangirani) usana kukhala wowala (kuti mupenye). Ndithu m’zimene muli zisonyezo (zosonyeza chifundo cha Allah pa zolengedwa Zake) kwa anthu akumva.
Akunena: “Allah wadzipangira mwana.” Wapatukana ndi zimenezo! Iye Ngokwanira, (salakalaka mwana ngakhale mthangati aliyense). NdiZake (zonse) za kumwamba ndi za pansi. Inu mulibe umboni pa zimenezi. Kodi mukumnenera Allah zomwe simukuzidziwa?
Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga.
Pambuyo pake tidawatumiza atumiki (ambiri) kwa anthu awo. Adawadzera ndi zisonyezo zoonekera poyera koma sadali okhulupirira zimene ena adazitsutsa kale, (adatsatira njira zomwezo za anzawo). Umo ndi momwe tikudindira zidindo m’mitima ya anthu opyola malire.
Kenako pambuyo pawo tidamtuma Mûsa ndi Haarun pamodzi ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adadzikweza. Tero adali anthu ochita zoipa.
Sadamkhulupirire Mûsa kupatula achinyamata a mwa anthu ake, chifukwa choopa Farawo ndi nduna zake kuti angawazunze. Ndithu Farawo adali wodzikuza pa dziko, ndithudi, adali m’modzi mwa opyola malire.
Ndipo tidavumbulutsa kwa Mûsa ndi m’bale wake mawu Athu (oti): “Apangireni nyumba anthu anu mu Eguputo ndipo nyumba zanu zichiteni kukhala misikiti (pakuti simungathe kukhala ndi misikiti yoonekera), ndipo pempherani Swala. Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira (kuti Allah awapatsa zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).”
Ndipo tidawaolotsa pa nyanja ana a Israyeli. Ndipo Farawo ndi asilikali ake ankhondo adawatsata moipitsa ndi mwamtopola, kufikira pamene kumira kudampeza; (iye) adati: “Ndakhulupirira kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Yemwe ana a Israyeli amkhulupirira. Ndipo ine ndine mmodzi mwa Asilamu (omugonjera monga iwo akumgonjera).”
“Ndiponso (ndauzidwa kuti): ‘Lungamitsa nkhope yako kuchipembedzo momuyeretsera Allah mapemphero Ake, ndipo usakhale mmodzi mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).’
Ndipo ngati Allah atakukhudza ndi masautso, palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni zedi.
Nena: “E inu anthu! Choonadi chakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene waongoka, (zabwino zake) zili pa iye mwini. Ndipo amene wasokera, ndithu zotsatira za kusokera zili pa iye mwini. Ndipo ine sindili muyang’aniri pa inu, (udindo wanga ndi kuchenjeza basi).”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Paieškos rezultatai:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".