Check out the new design

വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ * - വിവർത്തനങ്ങളുടെ സൂചിക


പരിഭാഷ അദ്ധ്യായം: സ്സുഖ്റുഫ്   ആയത്ത്:
وَٱلَّذِي نَزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٖ فَأَنشَرۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗاۚ كَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ
Ndiponso amene watsitsa madzi kuchokera kumwamba mwamuyeso; chifukwa cha madziwo tidaukitsa mudzi wakufa. Momwemonso inu mudzatulutsidwa (mmanda);
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡفُلۡكِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مَا تَرۡكَبُونَ
Ndiponso amene walenga zinthu zonse ziwiriziwiri (chachimuna ndi chachikazi). Ndipo adakupangirani zombo ndi ziweto zimene mukukwera,
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
لِتَسۡتَوُۥاْ عَلَىٰ ظُهُورِهِۦ ثُمَّ تَذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ رَبِّكُمۡ إِذَا ٱسۡتَوَيۡتُمۡ عَلَيۡهِ وَتَقُولُواْ سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَنَا هَٰذَا وَمَا كُنَّا لَهُۥ مُقۡرِنِينَ
Kuti mukhazikike mwaubwino pamisana paizo, kenako mukumbukire mtendere wa Mbuye wanu mukakhazikika pamenepo, ndipo munene: “Walemekezeka Amene watifewetsera ichi; ndipo sitikadatha kuchifewetsa ndi kuchigwiritsa ntchito.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَإِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا لَمُنقَلِبُونَ
“Ndipo ndithu ife kwa Mbuye wathu ndiko kobwerera.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَجَعَلُواْ لَهُۥ مِنۡ عِبَادِهِۦ جُزۡءًاۚ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٞ مُّبِينٌ
Ndipo amuikira gawo mwa akapolo Ake. (Kuti ndi ana a Allah.) Ndithu munthu, ngwamsulizo woonekera poyera!
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أَمِ ٱتَّخَذَ مِمَّا يَخۡلُقُ بَنَاتٖ وَأَصۡفَىٰكُم بِٱلۡبَنِينَ
Kodi wadzichitira ana achikazi mzimene wazilenga ndipo wakusankhirani inu ana achimuna?
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِمَا ضَرَبَ لِلرَّحۡمَٰنِ مَثَلٗا ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدّٗا وَهُوَ كَظِيمٌ
Koma akauzidwa (kuti wabereka mwana wamkazi) mmodzi wa iwo chomwe amamfanizira (Allah) Wachifundo chambiri, nkhope yake imakhala yakuda ndi kudandaula kwambiri!
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أَوَمَن يُنَشَّؤُاْ فِي ٱلۡحِلۡيَةِ وَهُوَ فِي ٱلۡخِصَامِ غَيۡرُ مُبِينٖ
Ha! Kodi amene waleredwa monga chokongoletsa, potsutsana iye sangathe kunena momveka? (Ameneyo ndiye mwampatsa Allah; omwe ndi ana aakazi).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَجَعَلُواْ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ ٱلَّذِينَ هُمۡ عِبَٰدُ ٱلرَّحۡمَٰنِ إِنَٰثًاۚ أَشَهِدُواْ خَلۡقَهُمۡۚ سَتُكۡتَبُ شَهَٰدَتُهُمۡ وَيُسۡـَٔلُونَ
Ndipo angelo omwe ndi akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri akuwatcha akazi. Kodi adaona kalengedwe kawo? Umboni wawo ulembedwa ndipo adzafunsidwa (pazimenezo)!
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالُواْ لَوۡ شَآءَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَا عَبَدۡنَٰهُمۗ مَّا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ
Ndipo (otsutsa) akunena: “Akadafuna (Allah) Wachifundo chambiri (kuti tisamapembedze mafano awa), sitikadawapembedza!” Iwo alibe kudziwa pa zimenezi (zomwe akunenazi). Koma akungonena mawu opeka.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبٗا مِّن قَبۡلِهِۦ فَهُم بِهِۦ مُسۡتَمۡسِكُونَ
Kapena tidawapatsa buku lina tisadapereke ili, kotero kuti iwo agwiritsitsa limenelo (ndi kugwirizana nazo zili mmenemo)?
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
بَلۡ قَالُوٓاْ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٖ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّهۡتَدُونَ
Koma akunena: “Ndithu ife tidawapeza makolo athu pa chipembedzo chimenechi, ndipo ife tikutsatira mapazi awo.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
 
പരിഭാഷ അദ്ധ്യായം: സ്സുഖ്റുഫ്
സൂറത്തുകളുടെ സൂചിക പേജ് നമ്പർ
 
വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ - വിവർത്തനങ്ങളുടെ സൂചിക

ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബേത്താല അതു വിവർത്തനം ചെയ്തു.

അടക്കുക