Check out the new design

വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ * - വിവർത്തനങ്ങളുടെ സൂചിക


പരിഭാഷ അദ്ധ്യായം: സ്സുഖ്റുഫ്   ആയത്ത്:
وَلِبُيُوتِهِمۡ أَبۡوَٰبٗا وَسُرُرًا عَلَيۡهَا يَتَّكِـُٔونَ
Ndipo nyumba zawo kukhala ndi zitseko ndi makama (mabedi) omwe amayadzamira (zonsezo kukhala za Siliva).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَزُخۡرُفٗاۚ وَإِن كُلُّ ذَٰلِكَ لَمَّا مَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَٱلۡأٓخِرَةُ عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُتَّقِينَ
Ndiponso ndi zokongoletsa za golide. Koma zonsezo sikanthu ayi, ndi chisangalalo chabe cha dziko lapansi (chosakhalira kutha); ndipo tsiku lachimaliziro lomwe lili kwa Mbuye wako ndi la oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمَن يَعۡشُ عَن ذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ نُقَيِّضۡ لَهُۥ شَيۡطَٰنٗا فَهُوَ لَهُۥ قَرِينٞ
Ndipo amene akunyozera kukumbukira (Allah) Wachifundo chambiri, timpatsa satana, kuti iye akhale bwenzi lake (lotsagana nalo).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَإِنَّهُمۡ لَيَصُدُّونَهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ
Ndipo iwo amawatsekereza ku njira zabwino ndi kumaganiza kuti iwo ngoongoka.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَنَا قَالَ يَٰلَيۡتَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَ بُعۡدَ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرِينُ
Kufikira pamene adzatidzera (tsiku la Qiyâma, uku akulowetsedwa ku Moto). Adzati (kumuuza satana): “Kalanga ine! Pakati pa ine ndi iwe pakadakhala ntunda wa pakati pa kuvuma ndi kuzambwe (kutalikirana kwathu).” Ha! Taonani kuipa kwa bwenzi!
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَن يَنفَعَكُمُ ٱلۡيَوۡمَ إِذ ظَّلَمۡتُمۡ أَنَّكُمۡ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ
(Allah adzawauza kuti): “Ndipo lero sikukuthandizani kukhala limodzi kwanu m’chilango pakuti mudadzichitira nokha zoipa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ أَوۡ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَمَن كَانَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Kodi ungathe kuwamveretsa agonthi, kapena ungathe kuwaongola akhungu ndi amene ali mkusokera koonekera?
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَإِمَّا نَذۡهَبَنَّ بِكَ فَإِنَّا مِنۡهُم مُّنتَقِمُونَ
Ngati titakuchotsa (padziko usadaone chilango chawo, usakhale ndi chikaiko), ndithu Ife tiwalanga iwo.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أَوۡ نُرِيَنَّكَ ٱلَّذِي وَعَدۡنَٰهُمۡ فَإِنَّا عَلَيۡهِم مُّقۡتَدِرُونَ
Kapena tikusonyeza zimene tidawalonjeza (uona ndi maso ako usadafe). Ndithu Ife tili ndi mphamvu pa iwo.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَٱسۡتَمۡسِكۡ بِٱلَّذِيٓ أُوحِيَ إِلَيۡكَۖ إِنَّكَ عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Choncho, gwiritsa zimene zavumbulutsidwa kwa iwe, ndithu iwe uli pa njira yolunjika.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَإِنَّهُۥ لَذِكۡرٞ لَّكَ وَلِقَوۡمِكَۖ وَسَوۡفَ تُسۡـَٔلُونَ
Ndithu iyi (Qur’an) ndi ulemelero wako ndi anthu ako; ndipo posachedwa mufunsidwa (za ulemelero umenewu).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَسۡـَٔلۡ مَنۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رُّسُلِنَآ أَجَعَلۡنَا مِن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ءَالِهَةٗ يُعۡبَدُونَ
Ndipo afunse atumiki Athu amene tidawatumiza iwe usadadze: “Kodi tidapanga milungu ina kuti ipembedzedwe, osati (Allah) Wachifundo chambiri?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَقَالَ إِنِّي رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndithu tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa Zathu kwa Farawo ndi nduna zake; ndipo adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa Mbuye wa zolengedwa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَلَمَّا جَآءَهُم بِـَٔايَٰتِنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَضۡحَكُونَ
Koma pamene adawadzera ndi zisonyezo zathu, basi iwo adali kuziseka.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
 
പരിഭാഷ അദ്ധ്യായം: സ്സുഖ്റുഫ്
സൂറത്തുകളുടെ സൂചിക പേജ് നമ്പർ
 
വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ - വിവർത്തനങ്ങളുടെ സൂചിക

ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബേത്താല അതു വിവർത്തനം ചെയ്തു.

അടക്കുക