Zimenezo (monga kulenga munthu ndi kumeretsa mmera, ndi umboni wosonyeza) kuti Allah Woona alipo; ndikuti Iye amaukitsa akufa, ndiponso Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.
Ndipo alipo mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika, (koma makani basi ndi kungotsata zimene akuziganizira).[288]
[288] Kutsutsana pa zinthu za chipembedzo popanda kudziwa ndi kukhala ndi umboni wokwanira nkoletsedwa zedi. Maphunziro enieni amene angamzindikiritse munthu za chipembedzo, ndi omwe akupezeka m’Qur’an ndi m’mahadisi a Mtumiki (s.a.w) omwe ali owona, ndi maphunziro amene akupezeka m’mabuku ophunzitsa malamulo achipembedzo omwe ali ovomerezeka ndi atsogoleri a Chisilamu, osati buku lililonse lolembedwa ndi munthu wamba.
(Yemwe) akupinda khosi lake (chifukwa chodzikuza) kuti asokereze (anthu powachotsa) kunjira ya Allah; pa iye pali chilango choyalutsa pa moyo uno, ndipo patsiku la Qiyâma tikamulawitsa chilango cha Moto wotentha.
Ndipo alipo wina mwa anthu amene akupembedza Allah cham’mphepete (mwachipembedzo). Chabwino chikampeza amatonthola nacho; koma masautso akamufika, amatembenuka ndi nkhope yake (posiya chikhulupiliro mwa Allah. Choncho) waluza moyo wa dziko lapansi ndi moyo wa tsiku la chimaliziro; kumeneko ndiko kuluza koonekera.[289]
[289] Allah watibweretsa pano padziko lapansi kuti tiyesedwe mayeso akulungama ndi kusalungama tsiku lachimaliziro lisanadze. Choncho tipirire ndi kugwiritsa zimene Allah ndi Mtumiki Wake atiuza. Tidziwe kuti pali mavuto pali zabwino.
Ndithu amene akhulupirira, ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi chipembedzo cha Sabia; ndi Akhrisitu, ndi Maajusi (opembedza moto), ndi ophatikiza Allah ndi mafano, ndithu Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chiweruziro (Qiyâma). (Osokera adzaponyedwa ku Moto ndipo olungama adzawalowetsa ku Munda wamtendere). Ndithu Allah ndi Mboni pa chinthu chilichonse.
Awa ndi magulu awiri amene akangana pa za Mbuye wawo (pa zomwe zili zomuyenera, ndi zosamuyenera, ndipo ena sadakhulupirire.) Choncho amene sadakhulupirire, adzawadulira nsalu za ku Moto ndi kuwaveka; ndipo pamwamba pa mitu yawo padzathiridwa madzi otentha.
Ndithu Allah adzalowetsa amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, ku Minda ya mtendere komwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi pasogolo) pake; m’menemo akavekedwa (ndi angelo) zibangili za golide ndi ngale; ndipo zovala zawo m’menemo zidzakhala za silika.
Ndithu. amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndipo nkumatsekereza ena ku njira ya Allah, (ndiponso nkumatsekereza kulowa) mu Msikiti Wopatulika umene tidauchita kuti ukhale wa anthu onse mofanana kwa amene akukhala m’menemo ndi kwa alendo, (anthu otere tidzawalanga ndi chilango chaukali), ndipo aliyense wofuna kuchita zopotoka m’menemo mosalungama, timulawitsa chilango chowawa zedi.
Ndipo (kumbukira) pamene tidamkhazika Ibrahim (ndi kumlondolera) pamalo pa Nyumba (yopatulikayo; tidamuuza kuti): “Usandiphatikize ndi chilichonse; ndipo iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuizungulira ndi kumakhala pompo (pochita mapemphero awo); ndi omwe amawerama ndi kugwetsa nkhope zawo pansi.[290]
[290] Allah akuuza Mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti akambire opembedza mafano zankhani ya Ibrahim yemwe iwo amati akumutsata pakupembedza kwawo mafano ndi kuichita nyumba yopatulikayo kukhala nyumba yopembedzera mafano kuti Ibrahim adamulondolera pamalo anyumbayo ndi kumlamula kuti aimange ndikuti asandiphatikize pamapemphero ndi china chilichonse, ndikuti aiyeretse nyumba ya Allah kuuve wamafano ndi uve wina uliwonse kuti pakhale pamalo pozungulira chifukwa choopa Allah. Nanga bwanji iwo apasankha kukhala popembedzera mafano.
Umo ndi momwe zikhalire; ndipo amene alemekeze zinthu zopatulika za Allah kutero ndi bwino kwa iyeyo pamaso pa Mbuye wake. Ndipo ziweto za miyendo inayi nzovomerezeka kwa inu kuzidya, kupatula zomwe zatchulidwa kwa inu (m’Qur’an kuti nzoletsedwa); choncho upeweni uve wa mafano, ndiponso pewani mawu abodza.
Uku mutapendekera kwa Allah Yekha, osati kum’phatikiza (Allah). Ndipo amene akuphatikiza Allah ndi mafano, ali ngati wogwa kuchokera kumwamba, kenako mbalame nkumuwakha, kapena mphepo kukamtaya malo akutali.
(Ziweto zimene mukutumiza ku Makka monga nsembe) muli nazo zithandizo mmenemo (monga kukwera ndi kukama mkaka) kufikira nthawi yodziwika, (yomwe ndi nthawi yozizingira); kenako malo ozizingira ndi pafupi ndi Nyumba yakalekaleyo.
Omwe atulutsidwa m’nyumba zawo popanda chilungamo, koma pachifukwa chakuti akunena: “Mbuye wathu ndi Allah.” Ndipo pakapanda Allah kukankha anthu ena kupyolera mwa ena, (popatsa ena mphamvu kuti agonjetse ena), ndiye kuti Masinagogi, Matchalitchi, nyumba zina zopempheleramo ndi Misikiti momwe dzina la Allah likutchulidwa mochuluka zikadagumulidwa. Ndithu Allah am’thangata amene akuthangata chipembedzo Chake; ndithu Allah Ngwanyonga, Wogonjetsa chilichonse.[291]
[291] M’ndime iyi, Allah akuti akadawalekelera anthu oipa, omwe cholinga chawo nkudzetsa chisokonezo pa dziko, popanda kusankha anthu ena kuti alimbane nawo, ndiye kuti nyumba zopempheleramo Ayuda, Akhrisitu ndi Asilamu, zikadagumulidwa. Koma Allah amasankha anthu olungama kuti alimbane ndi anthu oipawo kuti choonadi cha Allah chisazime. Ndipo amene akuteteza choonadi cha Allah, Iye walonjeza kumthangata.
Omwe akuti tikawakhazika pa dziko mwa ubwino, amachita mapemphero a Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, ndi kulamula zabwino ndi kuletsa zoipa; ndipo mabwelero a zinthu nkwa Allah basi.
Ndi midzi ingati tidaiononga yomwe inkachita zoipa? Zipupa zitagwera pa madenga ake. Ndipo ndi zitsime (zingati) zomwe zidasiidwa, ndi nyumba zikuluzikulu zomwe zidali zolimba?
Kodi sayendayenda pa dziko kuti akhale ndi mitima (yanzeru) yowazindikiritsa ndi makutu omvera? Ndithu maso sagwidwa khungu, (khungu loononga chipembedzo), koma mitima yomwe ili m’zifuwa ndi imene imagwidwa khungu (loononga chipembedzo).
Ndipo kuti adziwe amene apatsidwa kuzindikira kuti chimenechi n’choonadi chochokera kwa Mbuye wako ndi kuchikhulupirira ndikuti mitima yawo idzichepetse kwa Iye; ndithu Allah ndi Woongolera ku njira yolunjika amene akhulupirira.
Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
نتائج البحث:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".