Check out the new design

पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला । * - अनुवादहरूको सूची


अर्थको अनुवाद सूरः: स्सजिदः   श्लोक:
وَلَنُذِيقَنَّهُم مِّنَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَدۡنَىٰ دُونَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَكۡبَرِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndipo ndithudi, tiwalawitsa chilango chocheperapo (pa dziko lapansi) chisanafike chilango chachikulu (cha tsiku lachimaliziro), kuti atembenuke, (alape).
अरबी व्याख्याहरू:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ ثُمَّ أَعۡرَضَ عَنۡهَآۚ إِنَّا مِنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ مُنتَقِمُونَ
Kodi ndani wachinyengo kwambiri, woposa yemwe akukumbutsidwa Ayah za Mbuye wake, kenako nkuzikana? Ndithu Ife, tidzawabwezera zoipa anthu oipa.
अरबी व्याख्याहरू:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَلَا تَكُن فِي مِرۡيَةٖ مِّن لِّقَآئِهِۦۖ وَجَعَلۡنَٰهُ هُدٗى لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Choncho usakhale ndi chikaiko pa zakukumana Naye (Allah). Ndipo tidalichita (bukulo) kukhala chiongoko cha ana a Israyeli.
अरबी व्याख्याहरू:
وَجَعَلۡنَا مِنۡهُمۡ أَئِمَّةٗ يَهۡدُونَ بِأَمۡرِنَا لَمَّا صَبَرُواْۖ وَكَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يُوقِنُونَ
Ndipo ena mwa iwo tidawachita kukhala atsogoleri oongola (anthu) mwa lamulo lathu, pamene adapirira; ndipo adali kuvomereza motsimikiza Ayah Zathu.
अरबी व्याख्याहरू:
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَفۡصِلُ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Ndithudi Mbuye wako ndi Yemwe adzaweruze pakati pawo tsiku la Qiyâma pazimene amatsutsana.
अरबी व्याख्याहरू:
أَوَلَمۡ يَهۡدِ لَهُمۡ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ يَمۡشُونَ فِي مَسَٰكِنِهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍۚ أَفَلَا يَسۡمَعُونَ
Kodi sizidadziwike kwa iwo kuti ndimibadwo ingati imene tidaiononga patsogolo pawo; (chikhalirecho iwo) akudutsa mokhala mwawo? Ndithu m’zimenezo, muli zizindikiro, kodi sakumva?
अरबी व्याख्याहरू:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا نَسُوقُ ٱلۡمَآءَ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلۡجُرُزِ فَنُخۡرِجُ بِهِۦ زَرۡعٗا تَأۡكُلُ مِنۡهُ أَنۡعَٰمُهُمۡ وَأَنفُسُهُمۡۚ أَفَلَا يُبۡصِرُونَ
Kodi sakuona kuti timapereka madzi ku nthaka youma; ndipo ndi madziwo tikumeretsa mrnera umene ziweto zawo zimadya ndi iwo omwe; kodi sakupenya?
अरबी व्याख्याहरू:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡفَتۡحُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndipo akunena: “Kulamulidwa kumeneku (kwa tsiku la chimaliziro) kudzachitika liti, ngati mukunenadi zoona?”
अरबी व्याख्याहरू:
قُلۡ يَوۡمَ ٱلۡفَتۡحِ لَا يَنفَعُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِيمَٰنُهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ
Nena: “Tsiku la chiweruzirolo, amene sadakhulupirire, chikhulupiriro chawo sichidzawathandiza. Ndipo sadzapatsidwa nthawi yoyembekezera (kuti mizimu yawo isachoke ayambe akhulupirira kaye, mngero wa imfa akadzawadzera).”
अरबी व्याख्याहरू:
فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَٱنتَظِرۡ إِنَّهُم مُّنتَظِرُونَ
Choncho apatuke; ndipo yembekezera (zimene Allah wakulonjeza). Ndithu nawonso akuyembekezera (zimene Allah wawalonjeza).
अरबी व्याख्याहरू:
 
अर्थको अनुवाद सूरः: स्सजिदः
अध्यायहरूको (सूरःहरूको) सूची رقم الصفحة
 
पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला । - अनुवादहरूको सूची

यसलाई खालिद इब्राहिम पेटाला ले अनुवाद गरे।

बन्द गर्नुस्