Check out the new design

पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला । * - अनुवादहरूको सूची


अर्थको अनुवाद सूरः: गाफिर   श्लोक:
رَبَّنَا وَأَدۡخِلۡهُمۡ جَنَّٰتِ عَدۡنٍ ٱلَّتِي وَعَدتَّهُمۡ وَمَن صَلَحَ مِنۡ ءَابَآئِهِمۡ وَأَزۡوَٰجِهِمۡ وَذُرِّيَّٰتِهِمۡۚ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“E Mbuye wathu! Alowetseni ku Minda yamuyaya imene mudawalonjeza, ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo ndi akazi awo ndi ana awo. Ndithu inu ndi Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.”
अरबी व्याख्याहरू:
وَقِهِمُ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ وَمَن تَقِ ٱلسَّيِّـَٔاتِ يَوۡمَئِذٖ فَقَدۡ رَحِمۡتَهُۥۚ وَذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
“Ndipo apewetseni ku zoipa; tsono amene mudzampewetsa ku zoipa tsiku limenelo, ndiye kuti mwamchitira chifundo. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.”
अरबी व्याख्याहरू:
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُنَادَوۡنَ لَمَقۡتُ ٱللَّهِ أَكۡبَرُ مِن مَّقۡتِكُمۡ أَنفُسَكُمۡ إِذۡ تُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلۡإِيمَٰنِ فَتَكۡفُرُونَ
Ndithu amene akanira adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Mkwiyo wa Allah pa inu udali waukulu kuposa mkwiyo wanu pa mitima yanu (yomwe yakulowetsani ku chilango) pamene mudali kuitanidwa ku chikhulupiliro, (ku Chisilamu); ndipo mudali kukanira.”
अरबी व्याख्याहरू:
قَالُواْ رَبَّنَآ أَمَتَّنَا ٱثۡنَتَيۡنِ وَأَحۡيَيۡتَنَا ٱثۡنَتَيۡنِ فَٱعۡتَرَفۡنَا بِذُنُوبِنَا فَهَلۡ إِلَىٰ خُرُوجٖ مِّن سَبِيلٖ
Adzanena: “E Mbuye wathu! Mudatipatsa imfa kawiri; (imfa yoyamba tisanabadwe, ndipo imfa ya chiwiri pa dziko). Ndipo mudatipatsa moyo kawiri; (moyo woyamba wa pa dziko lapansi, ndipo moyo wachiwiri wakuuka kwa akufa). Choncho tavomereza machimo athu. Kodi pali njira yotulukira (ku chilango kuno)?”
अरबी व्याख्याहरू:
ذَٰلِكُم بِأَنَّهُۥٓ إِذَا دُعِيَ ٱللَّهُ وَحۡدَهُۥ كَفَرۡتُمۡ وَإِن يُشۡرَكۡ بِهِۦ تُؤۡمِنُواْۚ فَٱلۡحُكۡمُ لِلَّهِ ٱلۡعَلِيِّ ٱلۡكَبِيرِ
Zimenezi nchifukwa chakuti akapemphedwa Allah Yekha, mudali kutsutsa. Koma akaphatikizidwa (ndi milungu yabodza) mudali kukhulupirira. Choncho chiweruzo ncha Allah, Wotukuka, Wamkulu!
अरबी व्याख्याहरू:
هُوَ ٱلَّذِي يُرِيكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ وَيُنَزِّلُ لَكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ رِزۡقٗاۚ وَمَا يَتَذَكَّرُ إِلَّا مَن يُنِيبُ
Iye ndi Yemwe akukuonetsani zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Yake yoposa), ndipo akukutsitsirani madzi kumwamba chifukwa cha inu kuti abweretse zokupatsani moyo (monga chakudya ndi zina). Koma palibe amene akukumbukira kwenikweni kupatula amene watembenukira (kwa Allah).
अरबी व्याख्याहरू:
فَٱدۡعُواْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Choncho mpempheni Allah pomuyeretsera mapemphero Ake ngakhale (kumuyeretsera kwanu kwa mapempheroko) kuwaipire okanira.
अरबी व्याख्याहरू:
رَفِيعُ ٱلدَّرَجَٰتِ ذُو ٱلۡعَرۡشِ يُلۡقِي ٱلرُّوحَ مِنۡ أَمۡرِهِۦ عَلَىٰ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ لِيُنذِرَ يَوۡمَ ٱلتَّلَاقِ
Iye Ngotukuka ulemelero, Mwini Arsh (Mpando wachifumu); amapereka chivumbulutso (Chake) mwa lamulo lake kwa yemwe wamfuna mwa akapolo Ake kuti achenjeze (anthu za) tsiku lokumana (anthu onse).
अरबी व्याख्याहरू:
يَوۡمَ هُم بَٰرِزُونَۖ لَا يَخۡفَىٰ عَلَى ٱللَّهِ مِنۡهُمۡ شَيۡءٞۚ لِّمَنِ ٱلۡمُلۡكُ ٱلۡيَوۡمَۖ لِلَّهِ ٱلۡوَٰحِدِ ٱلۡقَهَّارِ
Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Allah). Ndipo palibe chilichonse chidzabisidwa kwa Allah (mzinthu zawo). (Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa): “Kodi ufumu ngwayani lero? Ngwa Allah, Mmodzi yekha, Wogonjetsa, (woweruza mmene akufunira kwa anthu Ake).”
अरबी व्याख्याहरू:
 
अर्थको अनुवाद सूरः: गाफिर
अध्यायहरूको (सूरःहरूको) सूची رقم الصفحة
 
पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला । - अनुवादहरूको सूची

यसलाई खालिद इब्राहिम पेटाला ले अनुवाद गरे।

बन्द गर्नुस्