Kenako tidakubwezerani kupambana pa iwo (omwe adakugonjetsani poyamba); ndipo tidakupatsani chuma ndi ana, ndi kukudalitsani kukhala ndi gulu lochuluka.
Ndipo tapanga usiku ndi usana (mkusinthana-sinthana kwake) monga zisonyezo ziwiri (zosonyeza umodzi wa Allah ndi mphamvu Zake zoposa); ndipo tidachifafaniza chisonyezo cha usiku (kuti chisakhale ndi kuunika) ndipo chisonyezo cha usana tidachipanga kuti chikhale ndi kuunika; kuti mufunefune ubwino wochokera kwa Mbuye wanu, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka ndichiwerengero (cha miyezi ndi masiku); ndipo chinthu chilichonse (chofunika pa chipembedzo ndi za m’dziko), tachilongosola bwinobwino, mwatsatanetsatane.
Ndimibadwo ingati imene tidaiononga pambuyo pa Nuh! Ndipo akukwanira Mbuye wako kudziwa bwinobwino ndi kuona bwinobwino uchimo wa akapolo Ake. (Palibe chobisika kwa Iye m’zochitachita za anthu).
Amene afuna zachangu (zosangalatsa za m’dziko ndikumaikirapo mtima pa izo), timpatsiratu mwachangu pa dziko lapansi chimene tikufuna kwa amene tafuna (kumpatsa;) koma (tsiku la chimaliziro) tamkonzera Jahannam adzailowa ali wonyozeka, wopirikitsidwa apa ndi apo.
Taona (ndi diso lolingalira) m’mene tawasiyanitsira mkupeza bwino, ena nkukhala pamwamba pa anzawo (pa chuma ndi pa moyo wangwiro); ndipo pa tsiku la chimaliziro kusiyana kwawo pa masitepe ndi ulemelero, nkwakukulu kwabasi.
Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze (wina) koma Iye Yekha, ndi kuti muchitire zabwino makolo (anu). Ngati m’modzi wa iwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenere mawu amnyozo, ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu.[254]
[254] M’ndimeyi Allah akulamula anthu Ake kuti apembedze Iye Yekha; asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, mwezi, nkhalango zowilira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma chikhulupiliro chathu chikhale mwa Allah yekha. Tikafuna kudziteteza tidziteteze ndi Allah. Ndiponso Allah watilamula kuchitira zabwino makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma tiwanenere mau aulemu.
[255] Tanthauzo la ndime iyi nkuti mkono wako usakhale wofumbata posiya kugawira ena zomwe ulinazo; ndikutinso usatambasule popatsa mosakaza koma kuchita zapakatikati; osachita umbombo ndiponso osasakaza. Anthu aumbombo ndi osakaza chuma, ndi abale a satana.
Izi ndi zina mwa za nzeru zomwe Mbuye wako wakuvumbulutsira. Usakhale ndi mulungu wina ndi kumphatikiza kwa Allah, kuti ungadzaponyedwe ku Jahannam uli wodzudzulidwa ndi wopirikitsidwa apa ndi apo.
Ndipo ndithu talongosola lamulo la chinthu chilichonse mwatsatanetsatane m’Qur’an iyi kuti akumbukire, ndipo (oipa) siikuwaonjezera (china) koma kuida ndi kuithawa.
Zonse zakumitambo isanu ndi iwiri ndi nthaka ndi zam’menemo, zikulemekeza Iye; ndipo palibe chilichonse koma chikumlememekeza ndi kumtamanda; koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo! Ndithudi Iye (Allah) Ngodekha, Ngokhululuka.
Ndipo apusitse amene ungawathe mwa iwo ndi liwu lako; ndipo asonkhanitsire gulu lako la nkhondo la okwera akavalo ndi loyenda ndi miyendo; tenga gawo lako pa chuma chawo ndi ana awo; ndipo alonjeze (malonjezo abodza).” Koma satana salonjeza china koma chinyengo basi.
Ndipo akakupezani masautso pa nyanja, amasowa amene mumakhala mukuwapembedza kupatula Iye (Allah). Koma akakupulumutsirani kumtunda, mukutembenuka ndi kunyoza Allah. Ndithu munthu ndi wokana (mtendere wa Allah sayamika.)
Kodi mukudziika pa chitetezo ndi chilango cha Allah (mukafika pa ntunda) kuti Allah sangakulowetseni pansi mbali iliyonse ya pa ntunda, kapena sangakutumizireni chigumula chamchenga (kapena miyala) kenako inu simudzapeza mtetezi (wokupulumutsani ku chilangocho)?
Ndipo ndithu adatsala pang’ono kukusokoneza pa zimene tavumbulutsa kwa iwe kuti utipekere zina zake m’malo mwa izi; pamenepo, akadakusankha kukhala bwenzi (lawo).
Pemphera Swala (za Farazi), dzuwa likapendeka mpaka mu mdima wausiku (zomwe ndi Swala za Dhuhri, Asri, Maghrib ndi Isha), ndipo pempheranso Swala ya Fajir: ndithu Swala ya Fajir amaichitira umboni (angelo).
Ndipo pakati pa usiku, dzuka mtulo ndi kupemphera Swala; ilo ndipemphero loonjezera pa iwe, kuti Mbuye wako akakuimike pamalo pa ulemu potamandidwa (ndi zolengedwa zonse pa tsiku la Qiyâma.)
Ndipo tikuivumbulutsa Qur’an yomwe imachiritsa (matenda a mmitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira. Komabe osalungama siikuwaonjezera (kanthu kena) koma kutayika.
Ndipo akukufunsa (iwe, Muhammad (s.a.w), anthu ako mokhwiriziridwa ndi Ayuda) za Mzimu. Nena: “Mzimu ndi chinthu chomwe akuchidziwa Mbuye wanga Yekha; ndipo inu simudapatsidwe nzeru (zozindikilira zinthu) koma pang’ono chabe, (poyerekeza ndi nzeru za Allah).”
Nena: “Ngakhale atasonkhana anthu ndi ziwanda (mothandizana) kuti abwere ndi buku longa ili la Qur’an (mukayalidwe ka mawu ndi matanthauzo ake), sangathe kubweretsa longa ilo, ngakhale atathandizana wina ndi mnzake.”
Kapena utigwetsere zidutswa za thambo pa mitu yathu monga momwe umatiopsezera, apo ayi, um’bweretse Allah ndi angelo (kuti) tionane nawo nkhope kwa nkhope (mwamasomphenya.)”
Kapena ukhale ndi nyumba ya golide, kapena ukwere kumwamba. Ndipo sitikukhulupirira kukwera kwako pokhapokha utatibweretsera buku (lochokera kwa Allah lomwe likulongosola za kuona kwako), kuti tidziliwerenga.” Nena (kwa iwo): “Mbuye wanga alemekezeke ndikupatukana ndi mbiri zopunguka! Ine sindine kanthu koma munthu, mtumiki (monga atumiki ena).”
Nena: “(Ngati mukutsutsa uthenga wanga) Allah wakwanira kukhala Mboni (ndi Muweruzi) pakati panga ndi pakati panu (zakuona kwa uthenga wanga kwa inu). Ndithu Iye Ngodziwa za akapolo Ake (zilakolako zawo) Ngowona (zochita zawo).
Ndipo yemwe Allah wamuongola, (chifukwa cha kukonzeka kwake kwa ubwino), iyeyo ndi amene waongoka; ndipo amene wamulekelera kusokera, (chifukwa cha kuipa kwa khalidwe lake), simungampezere athandizi kupatula Iye (Allah). Ndipo pa tsiku la chiweruziro tidzawasonkhanitsa uku akukokedwa ndi nkhope zawo ali osapenya, osalankhula ndi osamva. Malo awo okhala ndi ku Jahannam. Nthawi iliyonse (Motowo) ukatotobwa, tidzauonjezera kwa iwo kuyaka mwaukali.
Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa zizizwa zoonekera zisanu ndi zinayi (komabe osakhulupirira sadazikhulupirire). Afunse ana a Israyeli pamene adawadzera (Musayo), Farawo adati kwa iye (Mûsa): “Ndithu ine ndikukuona iwe Mûsa kuti walodzedwa.”
(Mûsa ndi anthu ake tidawapulumutsa). Ndipo tidati, kwa ana a Israyeli, pambuyo pake (pommiza Farawo): “Khalani m’dziko (loyera la Shami); ndipo likazadza lonjezo la moyo winawo, tidzakubweretsani nonsenu (muli m’chipwirikiti.)”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
د لټون پایلې:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".