Kuyamikidwa konse ndikwa Allah Yemwe zakumwamba ndi zapansi nzake. Ndipo kutamandidwa konse pa tsiku la chimaliziro Nkwake. ndiponso Iye Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa chilichonse.
Koma amene apatsidwa (dalitso la) kudziwa akuzindikira kuti zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako nzoona, ndipo zikuongolera ku njira ya Mwini mphamvu zoposa, Wotamandidwa.
(Allah akunena): “Kodi (akum’ganizira Muhammad kuti) wamupekera Allah bodza, kapena wagwidwa ndi misala? Iyayi, koma osakhulupirira za tsiku la chimaliziro adzakhala m’chilango ndi m’kusokera kwakukulu.”
Nayenso Sulaiman tidamgonjetsera mphepo (yomwe inkayenda mwa lamulo lake). Mayendedwe amphepoyo inkayenda kuyambira m’mawa mpaka masana ntunda wofanana ndi waulendo wa mwezi umodzi, ndiponso kuyambira masana mpaka madzulo inkayenda ntunda wofanana ndi waulendo wa mwezi umodzi. Ndipo tidamsungunulira kasupe wa mtovu. Ndiponso m’ziwanda (majini) zidaliponso zimene tidam’gonjetsera zomwe zinkam’gwilira ntchito mwa chilolezo cha Mbuye wake (Allah). Ndipo yense mwa iwo wonyoza lamulo Lathu (posiya kumumvera Sulaiman) timulawitsa chilango cha Moto woyaka.
Ndithu padali phunziro pa anthu a dziko la Saba mokhala mwawo: (Padali) minda iwiri, kumanja ndi kumanzere. (Tidati:) “Idyani zakudya zaulere zochokera kwa Mbuye wanu, ndipo mthokozeni. Mudzi wabwino ndi Mbuye Wokhululuka.”
Koma adanyozera (lamulo la Allah); choncho tidawatumizira chigumula champhamvu chamadzi otchingidwa (chomwe chidawamiza ndi kuononga minda yawo). Ndipo tidawasinthira minda yawo (yabwino) kukhala minda iwiri yazipatso zowawa, ndi mitengo ya bwemba ndi mitengo pang’ono ya masawu.[335]
[335] Anthu am’mudzi wa Saba’a komwe nkudziko la Yemeni, Allah adawapatsa madalitso ambiri pamene iwo amatsatira malamuio Ake ndi kumthokoza. Adawadalitsa ndi minda ya zipatso zokoma zomwe zidalibe nyengo yeniyeni yobalira, kotero kuti azimayi ankangosenza madengu nkumangoyenda pansi pa mitengo ndipo mwadzidzidzi ankangoona madengu ali odzaza ndi zipatso zoyoyoka m’mitengoyo. Koma pamene adasiya kumuyamika Allah ndi kutsatira malamulo Ake, adawaonongera mindayo ndi chigumula ndi kuwasinthitsira zipatso zawo ndi zipatso zopanda pake.
Ndipo pakati pawo ndi pakati pa midzi imene tidaidalitsa, tidaikapo midzi imene idali yoonekera; ndipo tidapima m’menemo malo apaulendo. (kotero kuti amachoka malo nkufika malo ena mosavutika. Tidawauza): “Yendani m’menemo usiku ndi usana mwamtendere.”
Ndipo iye adalibe nyonga pa iwo, koma chifukwa chakuti tionetse poyera ndani wokhulupirira tsiku la chimaliziro ndiponso ndani amene akulikaikira. Ndipo Mbuye wako Ngosunga chilichonse.[336]
[336] Pamene satana adatha kumsokeretsa Adam adaganizanso kuti adzatha kuwasokeretsa ana ake. Ndipo ana a Adam adamtsatiradi satanayo monga momwe iye ankaganizira. Komatu satana alibe mphamvu zomkakamizira mwana wa Adam kuti amtsate koma amangomuitana kupyolera m’kukometsera zilakolako zoipa.
Ndipo sitidakutumize (iwe, Mtumiki{s.a.w} kwa Arabu okha) koma kwa anthu onse, kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino ndi wochenjeza otsutsa. Koma anthu ambiri sadziwa (za uthenga wako).
Ndipo sichuma chanu ndi ana anu zomwe zingakuyandikitseni kwa Ife ulemelero, koma (chikhulupiliro cha) amene wakhulupirira ndi kuchita zabwino. Iwo adzapeza malipiro owonjezeka kwambiri pa zomwe adachita. Iwo adzakhala mwamtendere m’zipinda za ku Minda ya mtendere.
Nena: “Chilichonse ndakupemphani kukhala malipiro (othandizira kufikitsa uthenga kwa anthu) ndichanu, malipiro anga ali kwa Allah basi. Ndipo Iye ndi Mboni pachilichonse.”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
د لټون پایلې:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".