Check out the new design

Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala * - Índice de tradução


Tradução dos significados Surah: Al-Maidah   Versículo:
قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ ٱللَّهُمَّ رَبَّنَآ أَنزِلۡ عَلَيۡنَا مَآئِدَةٗ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ تَكُونُ لَنَا عِيدٗا لِّأَوَّلِنَا وَءَاخِرِنَا وَءَايَةٗ مِّنكَۖ وَٱرۡزُقۡنَا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ
Isa (Yesu) mwana wa Mariya adati: “Inu Allah Mbuye wathu! Titsitsireni chakudya kuchokera kumwamba kuti chikhale chikondwelero cha oyambilira ndi omalizira mwa ife, komanso chikhale chisonyezo chochokera kwa Inu; choncho tipatseni ndithu inu ndinu Abwino popatsa kuposa opatsa.”
Os Tafssir em língua árabe:
قَالَ ٱللَّهُ إِنِّي مُنَزِّلُهَا عَلَيۡكُمۡۖ فَمَن يَكۡفُرۡ بَعۡدُ مِنكُمۡ فَإِنِّيٓ أُعَذِّبُهُۥ عَذَابٗا لَّآ أُعَذِّبُهُۥٓ أَحَدٗا مِّنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Allah adati: “Ndithu Ine ndikuchitsitsa kwa inu. Koma amene adzatsutse mwa inu pambuyo pa ichi, ndithu Ine ndidzamulanga ndi chilango chomwe sindidamulangepo nacho aliyense mwa zolengedwa.”
Os Tafssir em língua árabe:
وَإِذۡ قَالَ ٱللَّهُ يَٰعِيسَى ٱبۡنَ مَرۡيَمَ ءَأَنتَ قُلۡتَ لِلنَّاسِ ٱتَّخِذُونِي وَأُمِّيَ إِلَٰهَيۡنِ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ قَالَ سُبۡحَٰنَكَ مَا يَكُونُ لِيٓ أَنۡ أَقُولَ مَا لَيۡسَ لِي بِحَقٍّۚ إِن كُنتُ قُلۡتُهُۥ فَقَدۡ عَلِمۡتَهُۥۚ تَعۡلَمُ مَا فِي نَفۡسِي وَلَآ أَعۡلَمُ مَا فِي نَفۡسِكَۚ إِنَّكَ أَنتَ عَلَّٰمُ ٱلۡغُيُوبِ
Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adzanena: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi iwe udauza anthu kuti: ‘Ndiyeseni ine ndi mayi wanga monga milungu iwiri m’malo mwa Allah?” (Mneneri Isa {Yesu}) adzaati: “Ulemelero ukhale pa Inu. Sikoyenera kwa ine kunena zomwe sizili zoyenera (kwa ine mawu amenewa ngabodza). Ngati ndikadanena, ndiye kuti mukadadziwa. Inu mukudziwa zomwe zili mu mtima mwanga, pomwe ine sindidziwa zomwe zili mwa Inu. Ndithudi, Inu ndinu Wodziwa zamseri.”
Os Tafssir em língua árabe:
مَا قُلۡتُ لَهُمۡ إِلَّا مَآ أَمَرۡتَنِي بِهِۦٓ أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ رَبِّي وَرَبَّكُمۡۚ وَكُنتُ عَلَيۡهِمۡ شَهِيدٗا مَّا دُمۡتُ فِيهِمۡۖ فَلَمَّا تَوَفَّيۡتَنِي كُنتَ أَنتَ ٱلرَّقِيبَ عَلَيۡهِمۡۚ وَأَنتَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ شَهِيدٌ
“Sindinawauze chilichonse kupatula chimene mudandilamula kuti: ‘Pembedzani Allah, Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.’ Ndipo ndinali mboni kwa iwo pamene ndidali nawo. Koma pamene mudanditenga, Inu ndiye mudali Muyang’aniri pa iwo; ndipo Inu ndinu Mboni ya chilichonse.”
Os Tafssir em língua árabe:
إِن تُعَذِّبۡهُمۡ فَإِنَّهُمۡ عِبَادُكَۖ وَإِن تَغۡفِرۡ لَهُمۡ فَإِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“Ngati muwalanga, ndithudi iwo ndi akapolo anu. Ndipo mukawakhululukira, ndithudi, Inu ndinu Mwini mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.”
Os Tafssir em língua árabe:
قَالَ ٱللَّهُ هَٰذَا يَوۡمُ يَنفَعُ ٱلصَّٰدِقِينَ صِدۡقُهُمۡۚ لَهُمۡ جَنَّٰتٞ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدٗاۖ رَّضِيَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ وَرَضُواْ عَنۡهُۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Allah adzati: “Ili ndi tsiku lomwe olankhula zoona kudzawathandiza kuona kwawo. Iwo adzalandira Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhala muyaya. Allah adzawayanja; naonso adzamuyanja. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
Os Tafssir em língua árabe:
لِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا فِيهِنَّۚ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرُۢ
Allah Yekha ndiye Mwini ufumu wa kumwamba ndi pansi, ndi zam’menemo. Ndipo Iye Ngokhoza chilichonse.
Os Tafssir em língua árabe:
 
Tradução dos significados Surah: Al-Maidah
Índice de capítulos Número de página
 
Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala - Índice de tradução

Tradução por Khaled Ibrahim Bitala.

Fechar