Alif-Lâm-Mîm-Râ. Izi ndi Ayah (ndime) za buku ili (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika); ndipo chomwe chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, nchoonadi; koma anthu ambiri sakhulupirira.
Allah ndi Yemwe adatukula thambo popanda mizati imene mukuiona; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wachifumu Waukulu, kukhazikika koyenera ndi Iye komwe kulibe chofanizira); ndipo adafewetsa dzuwa ndi mwezi (kwa anthu). Chilichonse mwa zimenezi chikupitilira kuyenda mpaka nyengo imene idaikidwa. Iye ndi Yemwe akuyendetsa zinthu; akulongosola Ayah (ndime) kuti mukhale ndi chitsimikizo pa zakukumana ndi Mbuye wanu.[236]
[236] Allah adafewetsa dzuwa ndi mwezi kuti zitumikire anthu Ake. Chilichonse mwa izo chikuyenda molingana ndi chikonzero cha Allah kufikira pamene lidzathera dziko lapansi. Allah ndi Yemwe akuyendetsa zinthu zonse za pa dziko ndi nzeru Zake zakuya, monga kuzipatsa moyo ndi kuzipatsa imfa ndi zina zotere. Allah akutifotokozera zonsezi kuti tikhale ndi chitsimikizo choti tidzakumana naye pambuyo pa imfa.
Ndipo akukufulumizitsa kuti ubweretse choipa (chomwe ndi chilango chawo) m’malo mwa chabwino; ndithu chikhalirecho zilango zambiri zidapita kale (zomwe akadayenera kuchenjera nazo)! Koma Mbuye wako ndi mwini chikhululuko kwa anthu pa uchimo wawo. Ndipo ndithu Mbuye wako Ngolanga mwaukali.[238]
[238] China chodabwitsa cha anthu osakhulupilira mwa Allah ndiko kupempha chilango kuti chiwadzere m’malo mopempha zabwino. Iwo ankanena monga momwe zilili m’ndime ya 32 m’Sûrat Anfal kuti: “Ngati izi zimene wadza nazo Muhammad (s.a.w) nzoona zochokera kwa inu (Allah), choncho timenyeni ndi chimvula chamiyala yochokera ku mitambo; kapena chilango china chilichonse chopweteka. Koma ife sitimutsatirabe.” Umo ndi momwe idalimbira mitima ya osakhulupilira.
Ndipo osakhulupirira akunena: “Bwanji sichidatsitsidwe kwa iye chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wake?” Ndithu iwe ndiwe mchenjezi, ndipo mtundu uliwonse wa anthu uli ndi muongoli (wakewake yemwe ali ndi njira zakezake zoongolera anthuwo, osati kutsata njira za muongoli wina).
Allah akudziwa chilichonse chimene mkazi asenza (m’mimba mwake) ndi zimene mimba zikupungula ndi zimene zikuonjezera. Chinthu chilichonse kwa Iye chili ndi mlingo (wake).
Ndi chimodzimodzi (kwa Iye Allah) amene akubisa liwu lake mwa inu ndi amene akulikweza ndi yemwe akudzibisa usiku ndi yemwe akuyenda usana, (onse akuwadziwa).
Ndipo mphezi imalemekeza Allah ndi kumthokoza, naonso angelo (amamlemekeza) momuopa. Ndipo Allah, amatumiza kumenya kwa mphezi ndi kummenya nako amene wamfuna. Ndipo iwo (okanira) akutsutsana pa za Allah (kuti alipo kapena palibe pomwe Iye alipo). Ndipo Iye Ngolanga mwaukali.
Kwa Iye ndiko kuli (kuvomera) pempho lachoonadi. Ndipo aja amene akupempha mafano kusiya Iye (Allah), sawayankha pa chilichonse koma (chikhalidwe chawo) chili ngati yemwe akutambasulira madzi manja ake awiri kuti afike m’kamwa mwake; koma sangafike. Ndipo mapemphero a osakhulupirira sali kanthu koma ndi otaika basi (opita pachabe).
Amene adavomera Mbuye wawo, adzapeza zabwino. Koma amene sadamuvomere, ngakhale akadakhala nazo zonse za m’dziko ndi zina zonga izo pamodzi, ndikuzipereka kuti adziombolere (sizikadavomerezedwa). Ndipo iwo adzakhala ndi chiwerengero choipa. Ndipo malo awo ndi ku Jahannam, taonani kuipa kwa malo okakhazikikamo!
Kodi amene akudziwa kuti zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako nzoona, angafanane ndi yemwe ali wakhungu? Ndithudi eni nzeru ndi okhawo olingalira.
Ndi omwenso amapirira chifukwa chofuna chiyanjo cha Mbuye wawo ndi kupemphera Swala ndi kupereka mu zomwe tawapatsa, mobisa ndi moonekera, ndi kuchotsa choipa ndi chabwino (pochita chabwino pa choipacho); iwo ndi omwe adzapeza malipiro (abwino) a ku Nyumba ya tsiku la chimaliziro.[241]
[241] Kunena koti: “Kupereka mobisa ndi moonekera.” kukusonyeza kuti sadaka zomwe munthu akupereka asazifunire nthawi yake yeniyeni yoperekera. Koma nthawi iliyonse. Ngati nkofunika kupereka mobisa kuopera kuti omwe akupatsidwawo asanyozeke kumaso kwa anthu, apereke mobisa. Ndipo ngati nkofunika kupereka moonetsera, ncholinga choti anthu ena atsanzire, monga kusonkhetsa kwa poyera, apereke moonekera. Tsono kunena kwakuti: “Kuchotsa choipa ndi chabwino,” kukutanthauza kuti anthu amenewa akawachitira zoipa ena, iwo sabwezera zoipazo. Koma amapitiriza kuchitira anthu oipawo zabwino.
Minda yamuyaya adzailowa iwo (pamodzi) ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo, akazi awo ndi ana awo; ndipo angelo azikalowa kwa iwo khomo lililonse.
(Uku akunena): “Salaamun Alayikumu (Mtendere uli pa inu) chifukwa chakupirira kwanu (pochita zabwino ndi kusiya zoipa ndi kukhala mwaubwino ndi anzanu)! Taona kukhala bwino zotsatira za Nyumba ya tsiku la chimaliziro.”
Koma amene akuswa lonjezo la Allah (ndi malonjezo a anthu anzawo) pambuyo polimanga motsimikiza, ndi kumadula chimene Allah walamula kuti chilumikizidwe, ndi kumaononga padziko, iwowo ndiwo adzapeza tembelero; ndiponso adzapeza Nyumba yoipa.
Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndipo amamfumbatiranso (kumchepetsera arnene wamfuna). Ndipo akusangalalira moyo wa pa dziko lapansi, suli kanthu moyo wapadziko poyerekeza ndi moyo wa pambuyo pa imfa, koma ndi chisangalalo chochepa basi.
Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji sichidatsitsidwe kwa iye chozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?”‘ Nena: “Ndithu Allah amalekelera kusokera amene wamfuna (chifukwa chosafuna kutembenukira kwa Iye Allah); ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye.”
Fanizo la Munda wamtendere umene alonjezedwa amene akuopa Allah (uli tere:) Pansi (ndi patsogolo) pake ikuyenda mitsinje. Zipatso zake ndi mthunzi wake nzanthawi zonse. Awa ndiwo malekezero a omwe akuopa Allah; koma malekezero a osakhulupirira ndi ku Moto basi.
Ndipo (ena mwa) omwe tidawapatsa mabuku (Ayuda ndi Akhrisitu), akusangalalira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (ndipo akulowa m’Chisilamu). Koma ena mu unyinji wa osakhulupirira akukana gawo lina la nkhaniyi. Nena: “Ndalamulidwa kupembedza Allah basi; ndi kusamphatikiza (ndi china). Ndikuitanira kwa Iye, ndipo kwa Iye ndiwo mabwelero anga.”
Ndipo ndithu tidatuma atumiki patsogolo pako iwe usanadze ndipo tidawalola kukhala ndi akazi ndi ana; (sichachilendo iwe kukhala ndi akazi ndi ana). Ndipo nkosatheka kwa mtumiki kudzetsa chozizwitsa koma pokhapokha ndi chilolezo cha Allah. Nyengo iliyonse ili ndi lamulo lake limene Allah adalilemba. (Nyengoyo ikakwana, lamulo limadza).
Koma amene adalipo kale iwo kulibe, adachita ziwembu; koma kuononga ziwembu zonsezo nkwa Allah basi. (Iye) akudziwa zimene cholengedwa chilichonse chachita. Ndipo osakhulupirira adzadziwa zotsatira zabwino za Nyumba ya tsiku la chimaliziro kuti zidzakhala zayani.
Ndipo amene sadakhulupirire akuti iwe sindiwe mtumiki. Nena: “Allah akukwanira kukhala mboni pakati panga ndi pakati panu (kuti ine ndine Mtumiki), ndiponso aja omwe ali ndi nzeru ya m’buku.” (Monga ena mwa Ayuda ndi Akhrisitu omwe adalowa Chisilamu).
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Igisubizo cy'ibyashatswe:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".