పవిత్ర ఖురాన్ యొక్క భావార్థాల అనువాదం - చిచియో అనువాదం * - అనువాదాల విషయసూచిక


భావార్ధాల అనువాదం సూరహ్: సూరహ్ అర్-రఅద్   వచనం:

సూరహ్ అర్-రఅద్

الٓمٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِۗ وَٱلَّذِيٓ أُنزِلَ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَ ٱلۡحَقُّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يُؤۡمِنُونَ
Alif-Lâm-Mîm-Râ. Izi ndi Ayah (ndime) za buku ili (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika); ndipo chomwe chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, nchoonadi; koma anthu ambiri sakhulupirira.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
ٱللَّهُ ٱلَّذِي رَفَعَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ بِغَيۡرِ عَمَدٖ تَرَوۡنَهَاۖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ يَجۡرِي لِأَجَلٖ مُّسَمّٗىۚ يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَ يُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّكُم بِلِقَآءِ رَبِّكُمۡ تُوقِنُونَ
Allah ndi Yemwe adatukula thambo popanda mizati imene mukuiona; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wachifumu Waukulu, kukhazikika koyenera ndi Iye komwe kulibe chofanizira); ndipo adafewetsa dzuwa ndi mwezi (kwa anthu). Chilichonse mwa zimenezi chikupitilira kuyenda mpaka nyengo imene idaikidwa. Iye ndi Yemwe akuyendetsa zinthu; akulongosola Ayah (ndime) kuti mukhale ndi chitsimikizo pa zakukumana ndi Mbuye wanu.[236]
[236] Allah adafewetsa dzuwa ndi mwezi kuti zitumikire anthu Ake. Chilichonse mwa izo chikuyenda molingana ndi chikonzero cha Allah kufikira pamene lidzathera dziko lapansi. Allah ndi Yemwe akuyendetsa zinthu zonse za pa dziko ndi nzeru Zake zakuya, monga kuzipatsa moyo ndi kuzipatsa imfa ndi zina zotere. Allah akutifotokozera zonsezi kuti tikhale ndi chitsimikizo choti tidzakumana naye pambuyo pa imfa.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَهُوَ ٱلَّذِي مَدَّ ٱلۡأَرۡضَ وَجَعَلَ فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۡهَٰرٗاۖ وَمِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِ جَعَلَ فِيهَا زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِۖ يُغۡشِي ٱلَّيۡلَ ٱلنَّهَارَۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
Ndipo Iye ndi Yemwe adatambasula nthaka ndikuika mapiri ndi mitsinje m’menemo. Ndipo mtundu uliwonse wazipatso adaupanga m’menemo kukhala mitundu iwiri iwiri, (yachimuna ndi yachikazi), amavindikira usiku ndi usana. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa anthu olingalira.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَفِي ٱلۡأَرۡضِ قِطَعٞ مُّتَجَٰوِرَٰتٞ وَجَنَّٰتٞ مِّنۡ أَعۡنَٰبٖ وَزَرۡعٞ وَنَخِيلٞ صِنۡوَانٞ وَغَيۡرُ صِنۡوَانٖ يُسۡقَىٰ بِمَآءٖ وَٰحِدٖ وَنُفَضِّلُ بَعۡضَهَا عَلَىٰ بَعۡضٖ فِي ٱلۡأُكُلِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
Ndipo m’nthaka muli zigawo zogundana, (koma kumeretsa kwake kwa zomera nkosiyanasiyana). Mulinso minda ya mphesa ndi mmera wina ndi kanjedza wokhala ndi nthambi ndi wopanda nthambi; (zonsezi) zikuthiliridwa ndi madzi amodzi ofanana, ndipo tikuzichita zina kukhala zabwino kuposa zina mkakomedwe kake. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo kwa anthu anzeru.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
۞ وَإِن تَعۡجَبۡ فَعَجَبٞ قَوۡلُهُمۡ أَءِذَا كُنَّا تُرَٰبًا أَءِنَّا لَفِي خَلۡقٖ جَدِيدٍۗ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡأَغۡلَٰلُ فِيٓ أَعۡنَاقِهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ndipo ngati ukudabwa, (basi) chodabwitsa kwambiri ndiko kuyankhula kwawo (koti): “Kodi tikadzakhala dothi, ndi zoona tidzakhala ndi chilengedwe chatsopano? (Allah sangathe zimenezi).” Iwowo ndi amene sadakhulupirire Mbuye wawo. Ndipo kwa iwowo mudzakhala magoli m’makosi mwawo; ndipo iwo ndi anthu a ku Moto, m’menemo adzakhala nthawi yaitali.[237]
[237] Allah akuti chodabwitsa zedi kwa anthu osakhulupilira ndiko kunena kwawo kwakuti: “Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi, tidzapatsidwanso moyo wina watsopano, zidzatheka bwanji zimenezi?” Ndithudi, kukana kwawo za kuuka kwa akufa nkododometsa pakuti amene adatha kulenga zinthu zikuluzikulu, monga thambo ndi nthaka, mitengo ndi zipatso, nyanja ndi mitsinje, ngokhoza kuwabweza pambuyo pa imfa yawo.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلسَّيِّئَةِ قَبۡلَ ٱلۡحَسَنَةِ وَقَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِهِمُ ٱلۡمَثُلَٰتُۗ وَإِنَّ رَبَّكَ لَذُو مَغۡفِرَةٖ لِّلنَّاسِ عَلَىٰ ظُلۡمِهِمۡۖ وَإِنَّ رَبَّكَ لَشَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ
Ndipo akukufulumizitsa kuti ubweretse choipa (chomwe ndi chilango chawo) m’malo mwa chabwino; ndithu chikhalirecho zilango zambiri zidapita kale (zomwe akadayenera kuchenjera nazo)! Koma Mbuye wako ndi mwini chikhululuko kwa anthu pa uchimo wawo. Ndipo ndithu Mbuye wako Ngolanga mwaukali.[238]
[238] China chodabwitsa cha anthu osakhulupilira mwa Allah ndiko kupempha chilango kuti chiwadzere m’malo mopempha zabwino. Iwo ankanena monga momwe zilili m’ndime ya 32 m’Sûrat Anfal kuti: “Ngati izi zimene wadza nazo Muhammad (s.a.w) nzoona zochokera kwa inu (Allah), choncho timenyeni ndi chimvula chamiyala yochokera ku mitambo; kapena chilango china chilichonse chopweteka. Koma ife sitimutsatirabe.” Umo ndi momwe idalimbira mitima ya osakhulupilira.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ ءَايَةٞ مِّن رَّبِّهِۦٓۗ إِنَّمَآ أَنتَ مُنذِرٞۖ وَلِكُلِّ قَوۡمٍ هَادٍ
Ndipo osakhulupirira akunena: “Bwanji sichidatsitsidwe kwa iye chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wake?” Ndithu iwe ndiwe mchenjezi, ndipo mtundu uliwonse wa anthu uli ndi muongoli (wakewake yemwe ali ndi njira zakezake zoongolera anthuwo, osati kutsata njira za muongoli wina).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
ٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا تَحۡمِلُ كُلُّ أُنثَىٰ وَمَا تَغِيضُ ٱلۡأَرۡحَامُ وَمَا تَزۡدَادُۚ وَكُلُّ شَيۡءٍ عِندَهُۥ بِمِقۡدَارٍ
Allah akudziwa chilichonse chimene mkazi asenza (m’mimba mwake) ndi zimene mimba zikupungula ndi zimene zikuonjezera. Chinthu chilichonse kwa Iye chili ndi mlingo (wake).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ ٱلۡكَبِيرُ ٱلۡمُتَعَالِ
(Iye ndi Yemwe ali) Wodziwa zamseri ndi zoonekera, Wamkulu, Wapamwambamwamba.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
سَوَآءٞ مِّنكُم مَّنۡ أَسَرَّ ٱلۡقَوۡلَ وَمَن جَهَرَ بِهِۦ وَمَنۡ هُوَ مُسۡتَخۡفِۭ بِٱلَّيۡلِ وَسَارِبُۢ بِٱلنَّهَارِ
Ndi chimodzimodzi (kwa Iye Allah) amene akubisa liwu lake mwa inu ndi amene akulikweza ndi yemwe akudzibisa usiku ndi yemwe akuyenda usana, (onse akuwadziwa).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
لَهُۥ مُعَقِّبَٰتٞ مِّنۢ بَيۡنِ يَدَيۡهِ وَمِنۡ خَلۡفِهِۦ يَحۡفَظُونَهُۥ مِنۡ أَمۡرِ ٱللَّهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُغَيِّرُ مَا بِقَوۡمٍ حَتَّىٰ يُغَيِّرُواْ مَا بِأَنفُسِهِمۡۗ وَإِذَآ أَرَادَ ٱللَّهُ بِقَوۡمٖ سُوٓءٗا فَلَا مَرَدَّ لَهُۥۚ وَمَا لَهُم مِّن دُونِهِۦ مِن وَالٍ
(Munthu aliyense) ali nalo gulu (la angelo) patsogolo pake ndi pambuyo pake (omwe) amamulondera (ndi kulemba zomwe akuchita) mwa lamulo la Allah. Ndithudi, Allah sasintha zomwe zilipo kwa anthu mpaka atasintha iwo zomwe zili m’mitima yawo. Ndipo Allah akawafunira anthu chilango, palibe chochitsekereza; ndipo alibe mtetezi m’malo mwake (Allah)[239]
[239] Ukaona anthu zinthu zawo sizikuwayendera bwino, dziwa kuti iwo eni ake asintha chikhalidwe chawo chabwino chomwe adali nacho chomwe chimawadzetsera madalitso. Munthu akasintha kusiya makhalidwe ake abwino, zinthu zake zonse zimaonongeka. Munthu amatchedwa munthu akakhala ndi makhalidwe abwino. Koma akaononga makhalidwe ake abwino ulemu wake wonse umaonongeka.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
هُوَ ٱلَّذِي يُرِيكُمُ ٱلۡبَرۡقَ خَوۡفٗا وَطَمَعٗا وَيُنشِئُ ٱلسَّحَابَ ٱلثِّقَالَ
Iye ndi Yemwe amakuonetsani kung’anima mokuopyezani (kuphedwa ndi mphezi) ndi mokupatsani chiyembekezo chabwino (chakudza mvula). Ndipo amabweretsa mitambo yolemera (ndi madzi amvula).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَيُسَبِّحُ ٱلرَّعۡدُ بِحَمۡدِهِۦ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ مِنۡ خِيفَتِهِۦ وَيُرۡسِلُ ٱلصَّوَٰعِقَ فَيُصِيبُ بِهَا مَن يَشَآءُ وَهُمۡ يُجَٰدِلُونَ فِي ٱللَّهِ وَهُوَ شَدِيدُ ٱلۡمِحَالِ
Ndipo mphezi imalemekeza Allah ndi kumthokoza, naonso angelo (amamlemekeza) momuopa. Ndipo Allah, amatumiza kumenya kwa mphezi ndi kummenya nako amene wamfuna. Ndipo iwo (okanira) akutsutsana pa za Allah (kuti alipo kapena palibe pomwe Iye alipo). Ndipo Iye Ngolanga mwaukali.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
لَهُۥ دَعۡوَةُ ٱلۡحَقِّۚ وَٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ لَا يَسۡتَجِيبُونَ لَهُم بِشَيۡءٍ إِلَّا كَبَٰسِطِ كَفَّيۡهِ إِلَى ٱلۡمَآءِ لِيَبۡلُغَ فَاهُ وَمَا هُوَ بِبَٰلِغِهِۦۚ وَمَا دُعَآءُ ٱلۡكَٰفِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ
Kwa Iye ndiko kuli (kuvomera) pempho lachoonadi. Ndipo aja amene akupempha mafano kusiya Iye (Allah), sawayankha pa chilichonse koma (chikhalidwe chawo) chili ngati yemwe akutambasulira madzi manja ake awiri kuti afike m’kamwa mwake; koma sangafike. Ndipo mapemphero a osakhulupirira sali kanthu koma ndi otaika basi (opita pachabe).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَلِلَّهِۤ يَسۡجُدُۤ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ طَوۡعٗا وَكَرۡهٗا وَظِلَٰلُهُم بِٱلۡغُدُوِّ وَٱلۡأٓصَالِ۩
Ndipo amene ali kumwamba ndi pansi amamgwadira Allah mwachifuniro ndi mopanda chifuniro; ndiponso zithunzi zawo (zimamgwadira) m’mawa ndi madzulo.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
قُلۡ مَن رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ قُلِ ٱللَّهُۚ قُلۡ أَفَٱتَّخَذۡتُم مِّن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ لَا يَمۡلِكُونَ لِأَنفُسِهِمۡ نَفۡعٗا وَلَا ضَرّٗاۚ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ أَمۡ هَلۡ تَسۡتَوِي ٱلظُّلُمَٰتُ وَٱلنُّورُۗ أَمۡ جَعَلُواْ لِلَّهِ شُرَكَآءَ خَلَقُواْ كَخَلۡقِهِۦ فَتَشَٰبَهَ ٱلۡخَلۡقُ عَلَيۡهِمۡۚ قُلِ ٱللَّهُ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٖ وَهُوَ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّٰرُ
Nena: “Ndani Mbuye wa thambo ndi nthaka?” Nena: “Ndi Allah.” Nena: “Mukudzipangira milungu ina kusiya Iye, (milungu) yomwe siingadzibweretsere zabwino kapena kudzichotsera sautso?” Nena: “Kodi angakhale ofanana wakhungu ndi wopenya? Kodi kapena ungafanane mdima ndi kuunika?” Kapena ampangira anzake Allah omwe adalenga zofanana ndi zomwe Allah adalenga kotero kuti zolengedwa (zambali ziwirizo) zikufanana kwa iwo? Nena: “Allah ndiye Mlengi wa chilichonse. Ndipo Iye ndi Mmodzi Wayekha, Wopambana (ndipo chimene Iye wafuna ndi chimene chimachitika)”
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَسَالَتۡ أَوۡدِيَةُۢ بِقَدَرِهَا فَٱحۡتَمَلَ ٱلسَّيۡلُ زَبَدٗا رَّابِيٗاۖ وَمِمَّا يُوقِدُونَ عَلَيۡهِ فِي ٱلنَّارِ ٱبۡتِغَآءَ حِلۡيَةٍ أَوۡ مَتَٰعٖ زَبَدٞ مِّثۡلُهُۥۚ كَذَٰلِكَ يَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡحَقَّ وَٱلۡبَٰطِلَۚ فَأَمَّا ٱلزَّبَدُ فَيَذۡهَبُ جُفَآءٗۖ وَأَمَّا مَا يَنفَعُ ٱلنَّاسَ فَيَمۡكُثُ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ كَذَٰلِكَ يَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡأَمۡثَالَ
Adatsitsa madzi, kuchokera ku mitambo, ndipo zigwa zidayendetsa madzi mwa mlingo wake. Ndipo msefukiro wamadzi udatenga thovu lomwe limayandama pamwamba pa madzi. Ndiponso zomwe amazisungunula pa moto chifukwa chofuna zodzikongoletseranazo kapena ziwiya (monga zagolide ndi siliva), mumakhalanso thovu chimodzimodzi. Umo ndi momwe Allah akuperekera fanizo lachoonadi ndi fanizo lachonama. Tsono thovu, limangopita monga zitakataka chabe; koma zimene zimathandiza anthu, zimakhazikika m’nthaka. Umo ndi m’mene Allah akuperekera mafanizo.[240]
[240] Nthawi zambiri zinthu zachabe zimagundika kwambiri, koma sizikhalira kuzimilira. Choncho.nkofunika kwa anthu kuchenjera ndi zinthu zotere. Asazikhulupirire chifukwa choona kuti zagundika, koma azipenyetsetse bwino, mofatsa kuti kuona kwake kwa zinthu kutsimikizike kwa iye.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
لِلَّذِينَ ٱسۡتَجَابُواْ لِرَبِّهِمُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَٱلَّذِينَ لَمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَهُۥ لَوۡ أَنَّ لَهُم مَّا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا وَمِثۡلَهُۥ مَعَهُۥ لَٱفۡتَدَوۡاْ بِهِۦٓۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ سُوٓءُ ٱلۡحِسَابِ وَمَأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمِهَادُ
Amene adavomera Mbuye wawo, adzapeza zabwino. Koma amene sadamuvomere, ngakhale akadakhala nazo zonse za m’dziko ndi zina zonga izo pamodzi, ndikuzipereka kuti adziombolere (sizikadavomerezedwa). Ndipo iwo adzakhala ndi chiwerengero choipa. Ndipo malo awo ndi ku Jahannam, taonani kuipa kwa malo okakhazikikamo!
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
۞ أَفَمَن يَعۡلَمُ أَنَّمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَ ٱلۡحَقُّ كَمَنۡ هُوَ أَعۡمَىٰٓۚ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ
Kodi amene akudziwa kuti zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako nzoona, angafanane ndi yemwe ali wakhungu? Ndithudi eni nzeru ndi okhawo olingalira.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
ٱلَّذِينَ يُوفُونَ بِعَهۡدِ ٱللَّهِ وَلَا يَنقُضُونَ ٱلۡمِيثَٰقَ
(Iwowo ndi) omwe akukwaniritsa lonjezo la Allah, ndipo saswa lonjezo lomangika (pakati pawo ndi anzawo).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَٱلَّذِينَ يَصِلُونَ مَآ أَمَرَ ٱللَّهُ بِهِۦٓ أَن يُوصَلَ وَيَخۡشَوۡنَ رَبَّهُمۡ وَيَخَافُونَ سُوٓءَ ٱلۡحِسَابِ
Ndiponso omwe akulumikiza zomwe Allah walamula kuti zilumikizidwe (monga chibale), pamodzi ndi kuopa Mbuye wawo ndi kuopanso chiwerengero choipa (chomwe chidzawapeza oipa tsiku lachimaliziro tero amayesetsa kuwapatuka machitidwe oipa).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَٱلَّذِينَ صَبَرُواْ ٱبۡتِغَآءَ وَجۡهِ رَبِّهِمۡ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَنفَقُواْ مِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ سِرّٗا وَعَلَانِيَةٗ وَيَدۡرَءُونَ بِٱلۡحَسَنَةِ ٱلسَّيِّئَةَ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عُقۡبَى ٱلدَّارِ
Ndi omwenso amapirira chifukwa chofuna chiyanjo cha Mbuye wawo ndi kupemphera Swala ndi kupereka mu zomwe tawapatsa, mobisa ndi moonekera, ndi kuchotsa choipa ndi chabwino (pochita chabwino pa choipacho); iwo ndi omwe adzapeza malipiro (abwino) a ku Nyumba ya tsiku la chimaliziro.[241]
[241] Kunena koti: “Kupereka mobisa ndi moonekera.” kukusonyeza kuti sadaka zomwe munthu akupereka asazifunire nthawi yake yeniyeni yoperekera. Koma nthawi iliyonse. Ngati nkofunika kupereka mobisa kuopera kuti omwe akupatsidwawo asanyozeke kumaso kwa anthu, apereke mobisa. Ndipo ngati nkofunika kupereka moonetsera, ncholinga choti anthu ena atsanzire, monga kusonkhetsa kwa poyera, apereke moonekera. Tsono kunena kwakuti: “Kuchotsa choipa ndi chabwino,” kukutanthauza kuti anthu amenewa akawachitira zoipa ena, iwo sabwezera zoipazo. Koma amapitiriza kuchitira anthu oipawo zabwino.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
جَنَّٰتُ عَدۡنٖ يَدۡخُلُونَهَا وَمَن صَلَحَ مِنۡ ءَابَآئِهِمۡ وَأَزۡوَٰجِهِمۡ وَذُرِّيَّٰتِهِمۡۖ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يَدۡخُلُونَ عَلَيۡهِم مِّن كُلِّ بَابٖ
Minda yamuyaya adzailowa iwo (pamodzi) ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo, akazi awo ndi ana awo; ndipo angelo azikalowa kwa iwo khomo lililonse.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
سَلَٰمٌ عَلَيۡكُم بِمَا صَبَرۡتُمۡۚ فَنِعۡمَ عُقۡبَى ٱلدَّارِ
(Uku akunena): “Salaamun Alayikumu (Mtendere uli pa inu) chifukwa chakupirira kwanu (pochita zabwino ndi kusiya zoipa ndi kukhala mwaubwino ndi anzanu)! Taona kukhala bwino zotsatira za Nyumba ya tsiku la chimaliziro.”
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَٱلَّذِينَ يَنقُضُونَ عَهۡدَ ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مِيثَٰقِهِۦ وَيَقۡطَعُونَ مَآ أَمَرَ ٱللَّهُ بِهِۦٓ أَن يُوصَلَ وَيُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱللَّعۡنَةُ وَلَهُمۡ سُوٓءُ ٱلدَّارِ
Koma amene akuswa lonjezo la Allah (ndi malonjezo a anthu anzawo) pambuyo polimanga motsimikiza, ndi kumadula chimene Allah walamula kuti chilumikizidwe, ndi kumaononga padziko, iwowo ndiwo adzapeza tembelero; ndiponso adzapeza Nyumba yoipa.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
ٱللَّهُ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ وَفَرِحُواْ بِٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا فِي ٱلۡأٓخِرَةِ إِلَّا مَتَٰعٞ
Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndipo amamfumbatiranso (kumchepetsera arnene wamfuna). Ndipo akusangalalira moyo wa pa dziko lapansi, suli kanthu moyo wapadziko poyerekeza ndi moyo wa pambuyo pa imfa, koma ndi chisangalalo chochepa basi.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ ءَايَةٞ مِّن رَّبِّهِۦۚ قُلۡ إِنَّ ٱللَّهَ يُضِلُّ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِيٓ إِلَيۡهِ مَنۡ أَنَابَ
Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji sichidatsitsidwe kwa iye chozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?”‘ Nena: “Ndithu Allah amalekelera kusokera amene wamfuna (chifukwa chosafuna kutembenukira kwa Iye Allah); ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye.”
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَتَطۡمَئِنُّ قُلُوبُهُم بِذِكۡرِ ٱللَّهِۗ أَلَا بِذِكۡرِ ٱللَّهِ تَطۡمَئِنُّ ٱلۡقُلُوبُ
(Awa ndi) amene akhulupirira, ndipo mitima yawo ikukhazikika pokumbukira Allah. Dziwani, pokumbukira Allah mitima imakhazikika (imatonthola).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ طُوبَىٰ لَهُمۡ وَحُسۡنُ مَـَٔابٖ
Amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chisangalalo nchawo ndi mabwelero abwino.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
كَذَٰلِكَ أَرۡسَلۡنَٰكَ فِيٓ أُمَّةٖ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِهَآ أُمَمٞ لِّتَتۡلُوَاْ عَلَيۡهِمُ ٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ وَهُمۡ يَكۡفُرُونَ بِٱلرَّحۡمَٰنِۚ قُلۡ هُوَ رَبِّي لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُ وَإِلَيۡهِ مَتَابِ
Momwemo takutuma kwa anthu omwe adapita patsogolo pawo anthu ena (ndipo amva nkhani zawo zonse); kuti uwawerengere zimene tikukuvumbulutsira; koma iwo akumkana (Allah) Wachifundo chambiri. Nena: “Iyeyo ndi Mbuye wanga! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; ndatsamira kwa Iye, ndipo kobwerera kwanga nkwa Iye basi.”
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَلَوۡ أَنَّ قُرۡءَانٗا سُيِّرَتۡ بِهِ ٱلۡجِبَالُ أَوۡ قُطِّعَتۡ بِهِ ٱلۡأَرۡضُ أَوۡ كُلِّمَ بِهِ ٱلۡمَوۡتَىٰۗ بَل لِّلَّهِ ٱلۡأَمۡرُ جَمِيعًاۗ أَفَلَمۡ يَاْيۡـَٔسِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَن لَّوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ لَهَدَى ٱلنَّاسَ جَمِيعٗاۗ وَلَا يَزَالُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ تُصِيبُهُم بِمَا صَنَعُواْ قَارِعَةٌ أَوۡ تَحُلُّ قَرِيبٗا مِّن دَارِهِمۡ حَتَّىٰ يَأۡتِيَ وَعۡدُ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُخۡلِفُ ٱلۡمِيعَادَ
Ndipo ikadakhalapo Qur’an yomwe chifukwa cha iyo mapiri akadayendetsedwa (panthawi yoiwerenga), kapena chifukwa cha iyo, nthaka ikadang’ambidwa, kapena chifukwa cha iyo, akufa akadayankhulitsidwa, (yochititsa zimenezi ikadakhala Qur’an iyi. Koma ntchito ya Qur’an siimeneyo)! Zinthu zonse nza Allah. Kodi sadadziwebe amene akhulupirira, kuti Allah akadafuna akadawaongolera anthu onse (ku Chisilamu; akadawalenga monga angelo opanda zilakolako, koma wawapatsa nzeru ndi zilakolako kuti alimbane ndi ziwirizi; ena apambane ndi kulowa ku Munda wamtendere). Ndipo tsoka silisiya kuwapeza amene sadakhulupirire chifukwa cha zomwe achita, kapena litsika pafupi ndi dziko lawo kufikira lonjezo la Allah lifike (lowachotsa moyo), ndithudi, Allah saswa malonjezo (Ake).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٖ مِّن قَبۡلِكَ فَأَمۡلَيۡتُ لِلَّذِينَ كَفَرُواْ ثُمَّ أَخَذۡتُهُمۡۖ فَكَيۡفَ كَانَ عِقَابِ
Ndipo ndithu adachitidwa chipongwe atumiki akale iwe usanadze koma ndidawalekelera amene sadakhulupirire (sindidawalange mwachangu), ndipo kenako ndidawalanga. Kodi chilango changa chidali chotani!
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
أَفَمَنۡ هُوَ قَآئِمٌ عَلَىٰ كُلِّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡۗ وَجَعَلُواْ لِلَّهِ شُرَكَآءَ قُلۡ سَمُّوهُمۡۚ أَمۡ تُنَبِّـُٔونَهُۥ بِمَا لَا يَعۡلَمُ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَم بِظَٰهِرٖ مِّنَ ٱلۡقَوۡلِۗ بَلۡ زُيِّنَ لِلَّذِينَ كَفَرُواْ مَكۡرُهُمۡ وَصُدُّواْ عَنِ ٱلسَّبِيلِۗ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٖ
Kodi amene akuimilira mzimu uliwonse pa zimene udapeza (kuti adzaulipire, sindiye woyenera kupembedzedwa)? Ndipo ampangira Allah anzake. Nena: “Atchuleni (anzakewo).” Kodi kapena mukumuuza zomwe sakuzidziwa pa dziko, kapena (zomwe mukunenazo) ndimawu chabe (opanda cholinga chilichonse)? Koma amene sadakhulupirire akometsedwa ndi bodza lawoli lamkunkhuniza, ndipo atsekerezedwa kunjira (ya choonadi). Ndipo amene Allah wamulekelera kusokera alibe muongoli (wina womuongolera).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
لَّهُمۡ عَذَابٞ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَشَقُّۖ وَمَا لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن وَاقٖ
Ali nacho chilango m’moyo wa dziko lapansi, koma chilango chapambuyo pa imfa nchokhwima zedi; ndipo sadzakhala ndi mtetezi kwa Allah.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
۞ مَّثَلُ ٱلۡجَنَّةِ ٱلَّتِي وُعِدَ ٱلۡمُتَّقُونَۖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ أُكُلُهَا دَآئِمٞ وَظِلُّهَاۚ تِلۡكَ عُقۡبَى ٱلَّذِينَ ٱتَّقَواْۚ وَّعُقۡبَى ٱلۡكَٰفِرِينَ ٱلنَّارُ
Fanizo la Munda wamtendere umene alonjezedwa amene akuopa Allah (uli tere:) Pansi (ndi patsogolo) pake ikuyenda mitsinje. Zipatso zake ndi mthunzi wake nzanthawi zonse. Awa ndiwo malekezero a omwe akuopa Allah; koma malekezero a osakhulupirira ndi ku Moto basi.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يَفۡرَحُونَ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَۖ وَمِنَ ٱلۡأَحۡزَابِ مَن يُنكِرُ بَعۡضَهُۥۚ قُلۡ إِنَّمَآ أُمِرۡتُ أَنۡ أَعۡبُدَ ٱللَّهَ وَلَآ أُشۡرِكَ بِهِۦٓۚ إِلَيۡهِ أَدۡعُواْ وَإِلَيۡهِ مَـَٔابِ
Ndipo (ena mwa) omwe tidawapatsa mabuku (Ayuda ndi Akhrisitu), akusangalalira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (ndipo akulowa m’Chisilamu). Koma ena mu unyinji wa osakhulupirira akukana gawo lina la nkhaniyi. Nena: “Ndalamulidwa kupembedza Allah basi; ndi kusamphatikiza (ndi china). Ndikuitanira kwa Iye, ndipo kwa Iye ndiwo mabwelero anga.”
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَٰهُ حُكۡمًا عَرَبِيّٗاۚ وَلَئِنِ ٱتَّبَعۡتَ أَهۡوَآءَهُم بَعۡدَ مَا جَآءَكَ مِنَ ٱلۡعِلۡمِ مَا لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن وَلِيّٖ وَلَا وَاقٖ
Ndipo momwemo taivumbulutsa (iyi Qur’an) m’Chiarabu kuti ikhale chilamulo (cha Allah). Ngati utsata zofuna zawo pambuyo pokufika kuzindikiraku, sudzakhala ndi bwenzi ngakhale mtetezi kwa Allah.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا رُسُلٗا مِّن قَبۡلِكَ وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ أَزۡوَٰجٗا وَذُرِّيَّةٗۚ وَمَا كَانَ لِرَسُولٍ أَن يَأۡتِيَ بِـَٔايَةٍ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۗ لِكُلِّ أَجَلٖ كِتَابٞ
Ndipo ndithu tidatuma atumiki patsogolo pako iwe usanadze ndipo tidawalola kukhala ndi akazi ndi ana; (sichachilendo iwe kukhala ndi akazi ndi ana). Ndipo nkosatheka kwa mtumiki kudzetsa chozizwitsa koma pokhapokha ndi chilolezo cha Allah. Nyengo iliyonse ili ndi lamulo lake limene Allah adalilemba. (Nyengoyo ikakwana, lamulo limadza).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
يَمۡحُواْ ٱللَّهُ مَا يَشَآءُ وَيُثۡبِتُۖ وَعِندَهُۥٓ أُمُّ ٱلۡكِتَٰبِ
Allah amafafaniza zimene wafuna ndi kulimbikitsa (kuti zisachoke zomwe wafuna), ndipo gwero la malamulo onse lili kwa Iye (Allah).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَإِن مَّا نُرِيَنَّكَ بَعۡضَ ٱلَّذِي نَعِدُهُمۡ أَوۡ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِنَّمَا عَلَيۡكَ ٱلۡبَلَٰغُ وَعَلَيۡنَا ٱلۡحِسَابُ
Ndipo ngati tikusonyeza zina mwa (zilango) zimene tawalonjeza, kapena kukupatsa imfa (usanazione zilangozo, ndithu ziwafikabe). Ndithu udindo wako ndi kufikitsa uthenga basi (umene walamulidwa kuufikitsa kwa iwo) ndipo Ife udindo wathu ndi kuwerengera (zochita zawo).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا نَأۡتِي ٱلۡأَرۡضَ نَنقُصُهَا مِنۡ أَطۡرَافِهَاۚ وَٱللَّهُ يَحۡكُمُ لَا مُعَقِّبَ لِحُكۡمِهِۦۚ وَهُوَ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ
Kodi sadaone kuti tikulidzera dziko lawo ndi kulichepetserachepetsera malire ake? Ndipo Allah amalamula (mwachilungamo) palibe wotsutsa lamulo Lake. Ndipo Iye Ngwachangu pakuwerengera.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَقَدۡ مَكَرَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَلِلَّهِ ٱلۡمَكۡرُ جَمِيعٗاۖ يَعۡلَمُ مَا تَكۡسِبُ كُلُّ نَفۡسٖۗ وَسَيَعۡلَمُ ٱلۡكُفَّٰرُ لِمَنۡ عُقۡبَى ٱلدَّارِ
Koma amene adalipo kale iwo kulibe, adachita ziwembu; koma kuononga ziwembu zonsezo nkwa Allah basi. (Iye) akudziwa zimene cholengedwa chilichonse chachita. Ndipo osakhulupirira adzadziwa zotsatira zabwino za Nyumba ya tsiku la chimaliziro kuti zidzakhala zayani.
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَسۡتَ مُرۡسَلٗاۚ قُلۡ كَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡ وَمَنۡ عِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلۡكِتَٰبِ
Ndipo amene sadakhulupirire akuti iwe sindiwe mtumiki. Nena: “Allah akukwanira kukhala mboni pakati panga ndi pakati panu (kuti ine ndine Mtumiki), ndiponso aja omwe ali ndi nzeru ya m’buku.” (Monga ena mwa Ayuda ndi Akhrisitu omwe adalowa Chisilamu).
అరబీ భాషలోని ఖుర్ఆన్ వ్యాఖ్యానాలు:
 
భావార్ధాల అనువాదం సూరహ్: సూరహ్ అర్-రఅద్
సూరాల విషయసూచిక పేజీ నెంబరు
 
పవిత్ర ఖురాన్ యొక్క భావార్థాల అనువాదం - చిచియో అనువాదం - అనువాదాల విషయసూచిక

చిచియో భాషలో అల్ ఖుర్ఆన్ అల్ కరీమ్ భావానువాదం - అనువాదం ఖాలిద్ ఇబ్రాహీమ్ బైతాలా - 2020 ముద్రణ.

మూసివేయటం