Check out the new design

Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala. * - Ishakiro ry'ibisobanuro


Ibisobanuro by'amagambo Isura: Al An’am   Umurongo:
فَمَن يُرِدِ ٱللَّهُ أَن يَهۡدِيَهُۥ يَشۡرَحۡ صَدۡرَهُۥ لِلۡإِسۡلَٰمِۖ وَمَن يُرِدۡ أَن يُضِلَّهُۥ يَجۡعَلۡ صَدۡرَهُۥ ضَيِّقًا حَرَجٗا كَأَنَّمَا يَصَّعَّدُ فِي ٱلسَّمَآءِۚ كَذَٰلِكَ يَجۡعَلُ ٱللَّهُ ٱلرِّجۡسَ عَلَى ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ
Choncho, amene Allah akufuna kumuongola, amamtsekula chifuwa chake kuti Chisilamu chilowemo, ndipo yemwe Allah akufuna kumulekelera kusokera amachichita chifuwa chake kukhala chobanika, chovutika kwambiri (kutsata Chisilamu) ngati kuti akukwera kumwamba. Umo ndi momwe Allah akuwaunjikira uve anthu omwe sakukhulupirira.
Ibisobanuro by'icyarabu:
وَهَٰذَا صِرَٰطُ رَبِّكَ مُسۡتَقِيمٗاۗ قَدۡ فَصَّلۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَذَّكَّرُونَ
Ndipo iyi (chipembedzo cha Chisilamu) ndi njira ya Allah yoongoka. Ndithu tazifotokoza zizindikiro momveka kwa anthu okumbukira.
Ibisobanuro by'icyarabu:
۞ لَهُمۡ دَارُ ٱلسَّلَٰمِ عِندَ رَبِّهِمۡۖ وَهُوَ وَلِيُّهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
(Anthu abwino) adzapeza Nyumba yamtendere kwa Mbuye wawo. Iye ndi Mtetezi wawo, chifukwa cha zomwe adali kuchita.
Ibisobanuro by'icyarabu:
وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعٗا يَٰمَعۡشَرَ ٱلۡجِنِّ قَدِ ٱسۡتَكۡثَرۡتُم مِّنَ ٱلۡإِنسِۖ وَقَالَ أَوۡلِيَآؤُهُم مِّنَ ٱلۡإِنسِ رَبَّنَا ٱسۡتَمۡتَعَ بَعۡضُنَا بِبَعۡضٖ وَبَلَغۡنَآ أَجَلَنَا ٱلَّذِيٓ أَجَّلۡتَ لَنَاۚ قَالَ ٱلنَّارُ مَثۡوَىٰكُمۡ خَٰلِدِينَ فِيهَآ إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۚ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٞ
Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawasonkhanitsa onse (nkuwauza): “E inu khamu la ziwanda! Ndithudi, mudatenga okutsatirani ambiri mwa anthu (powasokoneza).” Ndipo abwenzi awo mwa anthu adzati: “Mbuye wathu! Tidali kupindulitsana pakati pathu, ndipo tsopano taifikira nyengo yathu imene mudatiikira.” (Allah) adzati: “Malo anu ndi ku Moto. Mukakhala m’mmenemo nthawi yaitali, pokhapokha Allah akafuna.” Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri.
Ibisobanuro by'icyarabu:
وَكَذَٰلِكَ نُوَلِّي بَعۡضَ ٱلظَّٰلِمِينَ بَعۡضَۢا بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Chomwechi timaika chimvano pakati pawochita zoipa chifukwa cha machimo omwe adali kupeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa).
Ibisobanuro by'icyarabu:
يَٰمَعۡشَرَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ رُسُلٞ مِّنكُمۡ يَقُصُّونَ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِي وَيُنذِرُونَكُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَاۚ قَالُواْ شَهِدۡنَا عَلَىٰٓ أَنفُسِنَاۖ وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا وَشَهِدُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ أَنَّهُمۡ كَانُواْ كَٰفِرِينَ
(Tsiku la Qiyâma adzafunsidwa): “E inu magulu a ziwanda ndi anthu! Kodi sadakudzereni atumiki ochokera mwa inu, amene amakufotokozerani zizindikiro zanga, nakuchenjezani zokumana ndi tsiku lanu ili?” Adzati: “Tadziikira umboni tokha.” Ndipo moyo wa dziko lapansi udawanyenga. Ndipo adzaziikira okha umboni kuti iwo adali osakhulupirira.
Ibisobanuro by'icyarabu:
 
Ibisobanuro by'amagambo Isura: Al An’am
Urutonde rw'amasura numero y'urupapuro
 
Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala. - Ishakiro ry'ibisobanuro

Yasobanuwe na Khaled Ibrahim Betala.

Gufunga