Check out the new design

Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala. * - Ishakiro ry'ibisobanuro


Ibisobanuro by'amagambo Isura: Al An’am   Umurongo:
وَهُوَ ٱلَّذِي يَتَوَفَّىٰكُم بِٱلَّيۡلِ وَيَعۡلَمُ مَا جَرَحۡتُم بِٱلنَّهَارِ ثُمَّ يَبۡعَثُكُمۡ فِيهِ لِيُقۡضَىٰٓ أَجَلٞ مُّسَمّٗىۖ ثُمَّ إِلَيۡهِ مَرۡجِعُكُمۡ ثُمَّ يُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Iye ndiyemwe amakupatsani imfa (yatulo) nthawi yausiku, ndipo amadziwa zimene mwachita masana, kenako amakudzutsani mmenemo kuti ikwane nthawi yanu yoikidwa (yofera); kenako kwa Iye ndiko kobwerera kwanu, nadzakuuzani zimene munkachita.
Ibisobanuro by'icyarabu:
وَهُوَ ٱلۡقَاهِرُ فَوۡقَ عِبَادِهِۦۖ وَيُرۡسِلُ عَلَيۡكُمۡ حَفَظَةً حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ تَوَفَّتۡهُ رُسُلُنَا وَهُمۡ لَا يُفَرِّطُونَ
Iye ndi M’gonjesi pa akapolo Ake ndipo amakutumizirani (angelo) osunga, (olemba zochita zanu); kufikira mmodzi wanu imfa ikamdzera, angelo athuwo amampatsa imfa, ndipo iwo sanyozera (ntchito yawo).
Ibisobanuro by'icyarabu:
ثُمَّ رُدُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ مَوۡلَىٰهُمُ ٱلۡحَقِّۚ أَلَا لَهُ ٱلۡحُكۡمُ وَهُوَ أَسۡرَعُ ٱلۡحَٰسِبِينَ
Kenako adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona. Dziwani kuti kuweruza Nkwake. Iye Ngwachangu powerengera kuposa owerengera (onse).
Ibisobanuro by'icyarabu:
قُلۡ مَن يُنَجِّيكُم مِّن ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ تَدۡعُونَهُۥ تَضَرُّعٗا وَخُفۡيَةٗ لَّئِنۡ أَنجَىٰنَا مِنۡ هَٰذِهِۦ لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ
Nena: “Kodi ndani amakupulumutsani m’masautso a pamtunda ndi panyanja?” Mumampempha modzichepetsa ndi motsitsa mawu (kuti): “Ngati atipulumutsa m’mazunzo awa, ndithudi tidzakhala mwa othokoza.”
Ibisobanuro by'icyarabu:
قُلِ ٱللَّهُ يُنَجِّيكُم مِّنۡهَا وَمِن كُلِّ كَرۡبٖ ثُمَّ أَنتُمۡ تُشۡرِكُونَ
Nena: “Allah ndi Yemwe amakupulumutsani ku zimenezo ndi ku masautso a mtundu uliwonse. Kenako inu mukumphatikiza ndi mafano.
Ibisobanuro by'icyarabu:
قُلۡ هُوَ ٱلۡقَادِرُ عَلَىٰٓ أَن يَبۡعَثَ عَلَيۡكُمۡ عَذَابٗا مِّن فَوۡقِكُمۡ أَوۡ مِن تَحۡتِ أَرۡجُلِكُمۡ أَوۡ يَلۡبِسَكُمۡ شِيَعٗا وَيُذِيقَ بَعۡضَكُم بَأۡسَ بَعۡضٍۗ ٱنظُرۡ كَيۡفَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَفۡقَهُونَ
Nena: “Iye Ngokhoza kukutumizirani chilango kuchokera pamwamba panu kapena pansi pa miyendo yanu, kapena kudzetsa chisokonezo nkukhala magulumagulu (osamvana), ndipo (akhoza) kuwalawitsa ena a inu chilango cha mtopola wa ena.” Taona momwe tikufotokozera zizindikiro kuti iwo azindikire.
Ibisobanuro by'icyarabu:
وَكَذَّبَ بِهِۦ قَوۡمُكَ وَهُوَ ٱلۡحَقُّۚ قُل لَّسۡتُ عَلَيۡكُم بِوَكِيلٖ
Koma anthu ako aitsutsa iyo (Qur’an) pomwe ili yoona. Nena: “Ine sindili muyang’anili pa inu.”
Ibisobanuro by'icyarabu:
لِّكُلِّ نَبَإٖ مُّسۡتَقَرّٞۚ وَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ
Nkhani iliyonse (yomwe yatchulidwa apa) ili ndi nthawi yake yodziwika (yofikira). Ndipo posachedwapa mudziwa (izi).
Ibisobanuro by'icyarabu:
وَإِذَا رَأَيۡتَ ٱلَّذِينَ يَخُوضُونَ فِيٓ ءَايَٰتِنَا فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ يَخُوضُواْ فِي حَدِيثٍ غَيۡرِهِۦۚ وَإِمَّا يُنسِيَنَّكَ ٱلشَّيۡطَٰنُ فَلَا تَقۡعُدۡ بَعۡدَ ٱلذِّكۡرَىٰ مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo (iwe Msilamu weniweni) ukawaona omwe akuchita chipongwe ndi Ayah Zathu, apatuke mpaka anene nkhani ina. Ndipo ngati satana atakuiwalitsa, (nkukhala nawo pomwe iwo akukambirana zotere), choncho, pambuyo pokumbukira usakhale pamodzi ndi anthu ochita zoipa.
Ibisobanuro by'icyarabu:
 
Ibisobanuro by'amagambo Isura: Al An’am
Urutonde rw'amasura numero y'urupapuro
 
Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala. - Ishakiro ry'ibisobanuro

Yasobanuwe na Khaled Ibrahim Betala.

Gufunga