E iwe Mneneri! Muope Allah, ndipo usamvere osakhulupirira ndi achiphamaso. Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri; Wanzeru zakuya (m’zoyankhula ndi m’zochita Zake).[316]
[316] Sura iyi ikutchedwa Sura ya Ahzab kutanthauza kuti namtindi wa anthu. Zimenezi zidali chonchi kuti pamene Chisilamu chimafala mu mzinda wa Madina momwe mumakhalanso Ayuda, adachita nsanje yaikulu Ayudawo. Ndipo akuluakulu awo adaganiza zopita ku Makka kukakopa Arabu akumeneko kuti athandizane kuthira nkhondo Asilamu. Choncho Arabu a ku Makka adauza mitundu yonse yopembedza mafano kuti akamthire nkhondo Muhammad (s.a.w) ndi kuthetseratu chipembedzo cha Chisilamu. Tero adagwirizana ndipo adauzinga mzinda wa Madina mbali zonse. Koma Allah adatumiza angelo ndi chimphepo chamkuntho chomwe chidamwazamwaza katundu wawo. Pachifukwa ichi, onse adathawa.
Allah sadaike m’chifuwa cha munthu mitima iwiri. Ndipo sadachite akazi anu amene mukuwayesa ena mwa iwo monga amayi anu, kukhala mayi anu enieni. Ndipo sadachite ana anu ongowalera kukhala ana anu enieni (monga inu mukuwatchulira). Zimenezo ndi zolankhula zanu za pakamwa panu chabe. Koma Allah akunena choona; Iye akuongolera ku njira yoongoka.
Aitaneni ndi maina a atate awo. Kutero ndichilungamo kwa Allah. Koma ngati simukuwadziwa atate awo, (aitaneni ngati) ndiabale anu pachipembedzo; ndiponso ndi anzanu. Palibe uchimo kwa inu pa zimene mwazichita molakwitsa (mosazindikira). Koma (pali uchimo) pa zimene mitima yanu yachita mwadala. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
Mneneri ngofunika kwambiri kwa okhulupirira kuposa moyo wawo, (matupi awo ndi chuma chawo); ndipo akazi ake ndi amayi awo (amayi a Asilamu; nkoletsedwa kuwakwatira pambuyo pa imfa yake). Ndipo achibale pakati pawo ngoyenera (kulandira zamasiye pamalamulo a) m’buku la Allah kuposa Asilamu ena ngakhalenso Amuhajirina (amene adasamuka ku Makka kupita ku Madina chifukwa cha chipembedzo cha Chisilamu). Kupatula ngati mutachita zabwino kwa anzanu (sikolakwika). Izi zidalembedwa kale m’buku.[317]
[317] Ayah iyi ikufotokoza zakuletsedwa kukwatira akazi a Mtumiki (s.a.w), mwini wake atamwalira chifukwa choti akazi a Mtumiki (s.a.w) ndiamayi a Asilamu onse.
Ndipo (akumbutse) pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri onse pangano lawo. Ndi kwa iwe, ndi kwa Nuh, Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano lamphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah).
Kuti (Allah) adzafunse owona (aneneri) (tsiku la chimaliziro) pa zimene adanena (kwa anthu awo zakufikitsa uthenga woonadi kwa iwo). Ndipo Allah wawakonzera (osakhulupirira) chilango chopweteka.
E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani chisomo cha Allah chimene chili pa inu, pamene adakudzerani magulu a nkhondo. Ndipo tidawatumizira mphepo ndi magulu a nkhondo (a angelo) amene simudawaone. Ndipo Allah akuona (zonse) zimene mukuchita.[318]
[318] Pamene Mtumiki (s.a.w) adali mu mzinda wa Madina adamzinga magulu ambiri a nkhondo omwe ena a iwo adali a mtundu wa Ghatfan, Ayuda a Chikuraidha ndi Ayuda a Bani Nadhir. Adali ochuluka 12,000.
Pamene Mtumiki (s.a.w) adamva za kudza kwawo adakumba chidzenje chachikulu kumbali ina ya mzinda wa Madina yomwe adaiganizira kuti adani angalowereko. Izi zidachitika potsatira malangizo a Salman Farisiyu. Kenako Mtumiki (s.a.w) adatuluka ndi ankhondo ake okwana 3,000 nakamanga mahema awo pafupi ndi chidzenjecho moyang’anizana ndi adani awo. Asilamu adagwidwa ndi mantha aakulu kotero kuti achiphamaso adayamba kuthawa. Koma pompo Allah adatumizira adaniwo chimphepo ndi magulu a nkhondo a angelo omwe sadathe kuwaona ndi maso awo, nawabalalitsa adaniwo ndi kuwatayira katundu wawo kutali.
Pamene adakudzerani cha kumtunda kwanu, ndi kunsi kwanu (kumtunda kwa dambo ndi kumunsi kwake), pamene maso adangoti tong’oo chammbali ndipo mitima idafika kum’mero (chifukwa cha mantha ndi kunjenjemera) uku mukumganizira Allah maganizo osiyanasiyana.
Ndipo pamene ankanena achiphamaso (achinyengo) ndi omwe m’mitima mwawo muli matenda: “Palibe chomwe adatilonjeza Allah ndi Mtumiki Wake koma chinyengo basi.”
Ndipo pamene gulu lina mwa iwo lidanena: “E inu nzika za mu Yathiriba (Madina)! Palibe njira kwa inu yokhalira (pa nkhondo yogonjayi). Choncho bwererani (ku nyumba zanu; msiyeni Muhammad alimbane yekha ndi adani ake).” Ndipo gulu lina la nkhondo lochokera mwa iwo limapempha chilolezo kwa Mneneri (s.a.w) ( chobwelera ku Madina) ponena (kuti): “Ndithu nyumba zathu nzamaliseche (zopanda chitetezo).” Koma izo sizamaliseche. Sakufuna china, koma kuthawa basi.
Ndipo akadawalowera (magulu ankhondo a adaniwo), mbali zonse (za Mzindawo), kenako nkupemphedwa kuti atuluke m’Chisilamu ndi kumenyana ndi Asilamu, akadachita zimenezo; ndipo sakadayembekezera koma nthawi yochepa basi.
Ndipo ndithu (awa amene adathawa pabwalo la nkhondo), adali atamulonjeza kale Allah (kuti iwo) sadzatembenuza misana (kuthawa). Ndipo lonjezo la Allah nlofunsidwa. (Choncho iwo adzafunsidwa pa zomwe adalonjeza kwa Allah).
Ndithu Allah akuwadziwa amene akudziletsa mwa inu (kupita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) ndi kuletsanso anthu ena), ndi amene akuuza abale awo: “Bwerani kwa ife; (m’thaweni Muhammad {s.a.w}).” Ndiponso sapita ku nkhondo koma pang’ono pokha.
Okuchitirani inu umbombo (pa chikondi ndi pa chifundo; sakufunirani zabwino). Koma mantha akadza uwaona akukuyang’ana, uku maso awo akutembenuka (mophethiraphethira) monga a amene wakomoledwa ndi imfa. Koma mantha akachoka, akukupatsani masautso ndi malirime awo akuthwa; mbombo pa chabwino chilichonse. Iwowo sadakhulupirire ndipo choncho Allah wagwetsa malipiro a zochita zawo. Zimenezo nzosavuta kwa Allah.
(Kufikira tsopano chifukwa cha mantha awo) akuganiza kuti magulu a nkhondo (adani) sadapitebe; ndipo magulu amenewo akadadzanso, akadalakalaka akadakhala kuchipululu pamodzi ndi arabu a kuchimidzi ndi kuti azikangofunsa za nkhani zanu. Akadakhala pamodzi ndi inu sadakamenyana (ndi adani) koma pang’ono pokha.[319]
[319] Kuyambira ndime 12 mpaka 20, Allah akufotokoza makhalidwe a anthu ena amene adangolowa m’Chisilamu ndi lirime lokha pomwe mitima yawo siidakhulupirire. Nthawi zambiri ankamchitira Mtumiki (s.a.w) zachinyengo. Mtumiki (s.a.w) akalamula lamulo loti akalimbane ndi adani achipembedzo cha Chisilamu, iwo amagwetsa ulesi anthu kuti asapite ku nkhondoko. Nthawi zambiri samawafunira Asilamu zabwino. Akangouzidwa kuti tiyeni ku nkhondo, amagwidwa ndi mantha.
Ndithu muli nacho chitsanzo chabwino mwa Mthenga wa Allah (m’kudzipereka kwake ndi khama lake pa njira ya Allah, ndi kupirira kwake ndi masautso) kwa yemwe akuopa Allah ndi tsiku lachimaliziro, namatchula Allah kwambiri.
Ndipo pamene okhulupirira adaona magulu a nkhondo (a adani atawazinga mbali zonse), adati: “Ichi ndichimene Allah ndi Mtumiki Wake adatilonjeza (kuti tidzapeza masautso, kenako nkupambana), ndipo Allah ndi Mtumiki Wake adanena zoona.” Ndipo (ichi) sichidawaonjezere china, koma chikhulupiliro (mwa Allah) ndi kudzipereka.
Mwa okhulupirira alipo amuna ena amene adakwaniritsa zomwe adamlonjeza Allah (kuti sadzathawa pa nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w), ena mwa iwo adamaliza moyo wawo (nakwaniritsa lonjezo lawo pofera pa njira ya Allah). Ndipo ena mwa iwo akuyembekezerabe (kufera pa njira ya Allah). Ndipo sadasinthe konse (lonjezo lawo).[320]
[320] Imamu Ibnu Jarir Taburiyu adalemba m’buku lake kuti Anasi Bun Malik adati:- M’bale wa bambo anga, Anasi bun Nadhari sadakhale nawo pa nkhondo ya Badri, ndipo adati: “Sindidakhale pamodzi ndi Mtumiki pa nkhondo yoyamba. Ngati Allah atandifikitsa pa nkhondo ina Allah adzaona zimene ndidzachita pomenya nkhondo modzipereka.” Pa tsiku la nkhondo ya Uhud, pamene Asilamu adabalalikana kuthawa ndipo iye adati:- “E Allah! Ine ndikudzipatula ku zomwe achita awa, osakhulupilira. Ndiponso ndikudandaula mzimene achita awa, Asilamu amene athawa.” Kenako adayenda ndi lupanga lake nakumana ndi Saad bun Muadhi, nati: “E iwe Saad! Ine ndikumva fungo la ku Munda wa mtendere pafupi ndi phiri ili la Uhud.” Kenako adachita nkhondo kufikira adaphedwa. Ndipo Saad adati: “E iwe Mtumiki wa Allah! Sindinathe kuchita chimene iye adachita.” Anasi bun Malik adati: “Tidampeza ali m’gulu lophedwa uku ali ndi mabala okwanira 80, ena otemedwa ndi malupanga, ndipo ena olasidwa ndi mikondo ndi mipaliro. Sitidamzindikire kufikira pamene adadza mlongo wake naamzindikira kupyolera m’nsonga za zala zake.” Ndipo Anasi adatinso: “Tidali kukambirana kuti ndime iyi ikukamba za iye.”
Ndipo Allah adawabweza amene sadakhulupirire uku ali odzazidwa ndi mkwiyo m’mitima mwawo; sadapeze chabwino; (sadagonjetse Asilamu ndi kupeza zimene ankaziyembekezera monga zotola za pa nkhondo). Ndipo Allah adawakwaniritsira okhulupirira nkhondo (powatumizira adani mphepo yamkuntho ndi angelo). Ndipo, Allah Ngwamphamvu, Ngopambana, (sapambanidwa ndi chilichonse).
Ndipo adawatsitsa m’malinga mwawo amene adathandiza adaniwo mwa anthu a buku (Ayuda). Ndipo adathira mantha m’mitima mwawo. Ena mumawapha; ndipo ena mumawagwira.[321]
[321] Awa ndi Ayuda amene adasakanikirana ndi osakhulupilira (akafiri) a Chiarabu ochokera mu mtundu wa Banu Quraidhwa omwe adali ndi mapangano ndi Mtumiki (s.a.w) okhalirana mwa mtendere. Koma pamene adaswa mapangano pothandizana ndi adani a Mtumiki kuthira nkhondo Asilamu Mtumiki Muhammad (s.a.w) adawapitira ku malinga awo. Ndipo ena adawapha, pomwe ena adawagwira monga akaidi a pankhondo.
E iwe Mneneri! Nena kwa akazi ako (m’njira yowalangiza): “Ngati mufuna moyo wa dziko lapansi ndi zosangalatsa zake (ine ndilibe zosangalatsa za m’dziko, ndipo sindingakukakamizeni kuti mukhale ndi ine mu moyo wa umphawi; ngati mufuna) bwerani ndikupatsani cholekanira, chokusangalatsani, kenako ndikusiyeni kusiyana kwabwino (kopanda masautso).”
E inu akazi a Mneneri! Inu simuli monga mmodzi wa akazi ena (omwe siakazi a Mtumiki, paulemelero) ngati muopa Allah. Choncho musalobodole mawu (mowakometsa poyankhulana ndi amuna,) kuti asalakelake (kuchita zoipa ndi inu) yemwe mu mtima mwake muli matenda (achiwerewere). Koma nenani zonena zabwino.
Ndipo khalani mnyumba zanu, ndipo musadzionetsere (kwa amuna) uku mutadzikongoletsa monga mmene ankaonetsera zokongoletsa zawo (akazi) a m’nthawi ya umbuli wakale. Ndipo pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat, mverani Allah ndi Mtumiki Wake. Ndithu Allah akufuna kukuchotserani uve e, inu a kunyumba (ya Mneneri)! Ndi kuti akuyeretseni ndithu.
Ndipo lowezani pamtima zimene zikunenedwa m’nyumba zanu; ndime za mawu a Allah ndi (zonena za Mtumiki) zanzeru. Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika kwambiri, ndi zapoyera.
Ndithu Asilamu achimuna ndi Asilamu achikazi; okhulupirira achimuna ndi okhulupirira achikazi; omvera achimuna ndi omvera achikazi; owona achimuna ndi owona achikazi; opirira achimuna ndi opirira achikazi; odzichepetsa achimuna ndi odzichepetsa achikazi; opereka sadaka achimuna ndi opereka sadaka achikazi; osala achimuna ndi osala achikazi; osunga umaliseche wawo (kuchiwerewere) achimuna ndi osunga umaliseche wawo achikazi; otamanda Allah kwambiri achimuna ndi otamanda Allah kwambiri achikazi, Allah wawakonzera chikhululuko ndi malipiro aakulu.
Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Allah ndi Mtumiki Wake akalamula chinthu, iwo nkukhala ndi chisankho pa zinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu wasokera; kusokera koonekera.[323]
[323] Ndime iyi ikunenetsa kuti sikoyenera kwa Msilamu kutsata maganizo ake pa chinthu chimene Allah ndi Mtumiki walamulapo lamulo, koma afunika kutsatira lamulo la Allah ndi Mtumiki, ndipo asakhale ndi chifuniro pa zinthu zomwe nza chipembedzo koma agonjere zimene Allah walamula ndi Mtumiki Wake. Kunyoza lamulo la Allah ndi Mtumiki kumachititsa kuti munthu atayike.
Palibe tchimo pa Mneneri pa zimene Allah wamulamula. Chimenechi ndichizolowezi cha Allah (njira ya Allah) pa amene adanka kale. Ndipo lamulo la Allah ndi chikonzero (chomwe) chidakonzedwa. (Ndipo sichisinthidwa). [325]
[325] Ndime iyi ikumuuza Mtumiki (s.a.w) kuti palibe vuto pa iye ngakhale tchimo kapena kudzudzulidwa pa chomwe Allah wamulamula kuchichita monga kukwatira akazi ambiri. Ayuda amamunyoza ndi kumudzudzula chifukwa chokwatira akazi ambiri. Koma Allah adawayankha ndi mawu ake oti: “Iyi ndi njira ya Allah yomwe idalipo pa Aneneri akale! Daud adakwatira akazi 100. Ndipo Sulaimani akazi 300.
(Aneneri) amene amafikitsa uthenga wa Allah (kwa anthu) uku akumuopa Iye, ndipo samamuopa aliyense koma Allah (yekha). Ndipo Allah Akukwana kukhala wowerengera (zochita za akapolo Ake).[326]
[326] Ndime iyi ikumuuza Mtumiki kuti amene adamulamula kuti awatsanzire pa zimene ankachita ndi iwo amene ankafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu, ndipo samaopa kudzudzulidwa ndi aliyense pa chomwe Allah wawalamula kuchita, koma ankangoopa Allah Yekha. Choncho nawenso tsanzira khalidwe lawo ndi kuopa Allah Yekha.
Muhammad (s.a.w) sali tate wa aliyense mwa amuna anu, koma iye ndi Mtumiki wa Allah, ndiponso wotsiriza mwa Aneneri. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.[327]
[327] (“Khaatamu Nabiyyina) “Mneneri wotsirizira” tanthauzo lake ndi kuti Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndimneneri womalizira; palibe mneneri wina pambuyo pake mpaka kutha kwadziko lapansi. Ayah imeneyi ikutsutsa zonena za Akadiyani ndi enanso omwe akumutcha mtsogoleri wawo kuti ndi mneneri.
Iye ndi Amene akukuchitirani chifundo (ndi kukufunirani zabwino) nawonso Angelo Ake (akukupemphelerani kwa Allah) kuti akutulutseni mu mdima ndi kukuikani m’kuunika. Ndipo (Iye) Ngwachisoni zedi kwa okhulupirira.
E iwe Mneneri (wa Allah)! Ndithu Ife takutuma (kuti ukhale) mboni (pa anthu ako ndi pa mibadwo yonse). Wonena nkhani zabwino (kwa oopa Allah), ndi mchenjezi (kwa onyoza Allah).
E iwe Mneneri! Ndithu Ife takuloleza (kukhala nawo pamodzi) akazi ako amene wawapatsa chiwongo chawo, ndi chimene dzanja lako lamanja lapeza (omwe ndi akazi ogwidwa pa nkhondo) chomwe Allah wakupatsa, ndi ana achikazi a m’bale wa atate ako, ndi ana achikazi a mlongo wa atate ako, ndi ana achikazi a atsibweni ako, ndi ana achikazi a m’bale wa mayi ako amene adasamuka pamodzi ndi iwe, ndi mkazi wokhulupirira atadzipereka yekha kwa Mneneri ngati Mneneri akufuna kumkwatira, chilolezo ichi ncha iwe wekha, osati okhulupirira onse. Ndithu tikudziwa malamulo amene tawakhazikitsa kwa iwo pa akazi awo, ndi chimene manja awo akumanja apeza; (takuchitira zimenezi iwe wekha Mneneri Muhammad {s.a.w}) kuti pasakhale masautso pa iwe (ngati ukufuna kukwatira mkazi wina chifukwa chofalitsa chipembedzo) ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni chosatha.
Pambuyo (pa akazi awa amene uli nawo) nkosaloledwa kwa iwe kukwatira akazi ena, (poonjezera pa chiwerengero cha akazi amene uli nawo). Ndiponso usasinthe (ofanana ndi chiwerengero chawo), (zonsezi nzoletsedwa kwa iwe) ngakhale kuti ubwino wawo utakusangalatsa, kupatula chimene dzanja lako lakumanja lapeza; ndipo Allah ndi M’yang’aniri wa chinthu chilichonse.
E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba za Mneneri pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kukadya, osati kukhala nkuyembekezera kupsa kwa chakudya. Koma mukaitanidwa, lowani. Ndipo mukamaliza kudya, balalikani; ndiponso musakambe nkhani zocheza. Chifukwa kutero kumavutitsa Mneneri. Ndipo iye amakuchitirani manyazi (kuti akutulutseni); koma Allah alibe manyazi ponena choona. Ndipo inu mukamawafunsa (akazi ake) za ziwiya, afunseni uku muli kuseri kwa Chotsekereza. Zimenezo ndi zoyera zedi ku mitima yanu ndi mitima yawo. Sikoyenera kwa inu kumvutitsa Mtumiki wa Allah, ndiponso nkosayenera kwa inu kukwatira akazi ake pambuyo pa imfa yake mpaka muyaya. Ndithu kutero ndi tchimo lalikulu kwa Allah.[330]
[330] Anasi (r.a) adanena kuti ndime iyi idatsika chifukwa cha anthu ena omwe ankangocheza m’nyumba ya Mtumiki (s.a.w), osatulukamo. Izi zidali motere: Pamene Mtumiki (s.a.w) adakwatira Zainabu Binti Jahashi, adachita phwando la chakudya ndipo adaitana anthu. Pamene adatha kudya ena a iwo adangokhala nkumacheza m’nyumba ya Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye). Pamenepo nkuti mkazi wake atayang’anitsa nkhope yake ku khoma la nyumba. Zoterezi zidamuvuta Mtumiki (s.a.w) kuti awatulutse m’nyumbamo. Apa mpamene Allah adavumbulutsa ndimeyi.
Palibe tchimo pa iwo (akazi) kuonana ndi atate awo ngakhale ana awo, alongo awo, ana amuna alongo awo, ana a amuna a abale awo, akazi anzawo, ndi amene manja awo akumanja apeza. Ndipo opani Allah (inu akazi). Ndithu Allah ndimboni pa chilichonse.
Ndithu amene akumukwiyitsa Allah ndi kumuvutitsa Mtumiki Wake (ponyozera malamulo ake) Allah wawatembelera pa dziko lapansi (mpaka) pa tsiku la chimaliziro, ndipo wawakonzera chilango chosambula.
E iwe Mneneri! Uza akazi ako, ndi ana ako aakazi, ndi akazi a okhulupirira, kuti adziphimbe ndi nsalu zawo (akamatuluka m’nyumba), kutero kuchititsa kuti adziwike, asazunzidwe (ndi anthu achipongwe). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni.
Anthu akukufunsa za (kudza kwa) nthawi (ya tsiku la chitsiriziro). Nena: “Kuzindikira kwa nthawiyo kuli ndi Allah (Yekha). Nanga nchiyani chikudziwitse kuti nthawi ya chimaliziro iri pafupi?”
E inu amene mwakhulupirira! Musakhale monga amene adamvutitsa Mûsa; koma Allah adamuyeretsa kuzimene ankamnenera. Ndipo iye kwa Allah adali wolemekezeka.[331]
[331] M’ndime iyi, Allah akulangiza Asilamu kuti asamuvutitse Mtumiki ndi kumnenera mawu opanda ulemu monga momwe Ayuda ankamunenera Musa. Ana a Israeli adamunamizira Musa kuti ali ndi khate pathupi lake, kapena kuti ali ndi matenda a mwera (phudzi). Koma Allah adamuyeretsa kuzomwe adali kumunamizirazo. Adamuyeretsa motere monga momwe Bukhari akunenera muhadisi yomwe idalandiridwa kuchokera kwa Abu Huraira (r.a) kuti Mtumiki (s.a.w) adati: Musa adali munthu wamanyazi, ndipo amabisa thupi lake. Khungu lake silimaoneka chifukwa cha manyazi ake. Ndipo adamuvutitsa ena mwa ana a Israeli. Adati: “Sangadzibise motere koma pa khungu lake pali chochititsa manyazi, mwina khate kapena matenda amphepo yamwera (phudzi), kapena matenda ena aliwonse!” Ndipo Allah adafuna kumuyeretsa ku zimene ankamunamizirazo. Tsiku lina Musa adakhala payekha navula nsalu zake naika pa mwala. Kenako adayamba kusamba. Pamene adamaliza kusamba adacheukira komwe adaika nsalu zake kuti azitenge. Adaona mwala ukuthawitsa nsalu zake. Musa adatenga ndodo yake nkumathamangira mwalawo uku akunena: “Nsalu zanga, iwe mwala! Nsalu zanga iwe mwala!’’ Mpaka adadutsa pomwe adakhala akuluakulu a ana a Israeli namuona thupi lake lili losalala kwabasi; lopanda chilema chilichonse. Potero Allah adamuyeretsa ku zomwe ankamunenerazo.
Ndithu Ife tidapereka udindo (otsatira malamulo) ku thambo ndi nthaka ndi mapiri; koma zidakana kuwusenza (udindowo); ndipo zidauopa. Koma munthu adawusenza; ndithu iye ngwachinyengo kwambiri ndiponso mbuli.
Kuti Allah adzawalange achiphamaso aamuna ndi aakazi, ndi opembedza mafano achimuna ndi achikazi ndi kuti adzawakhululukire okhulupirira achimuna ndi achikazi. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
అన్వేషణ ఫలితాలు:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".