Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - الترجمة الشيشيوا * - Indise ng mga Salin


Salin ng mga Kahulugan Surah: At-Talāq   Ayah:

At-Talāq

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِذَا طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَطَلِّقُوهُنَّ لِعِدَّتِهِنَّ وَأَحۡصُواْ ٱلۡعِدَّةَۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ رَبَّكُمۡۖ لَا تُخۡرِجُوهُنَّ مِنۢ بُيُوتِهِنَّ وَلَا يَخۡرُجۡنَ إِلَّآ أَن يَأۡتِينَ بِفَٰحِشَةٖ مُّبَيِّنَةٖۚ وَتِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِۚ وَمَن يَتَعَدَّ حُدُودَ ٱللَّهِ فَقَدۡ ظَلَمَ نَفۡسَهُۥۚ لَا تَدۡرِي لَعَلَّ ٱللَّهَ يُحۡدِثُ بَعۡدَ ذَٰلِكَ أَمۡرٗا
E iwe Mneneri (s.a.w) ngati mufuna kusudzula akazi ukwati, asudzuleni mnyengo yowerengera Edda yawo (kuwerengera Edda kumayambika mkazi akakhala ndi Twahara akachira matenda akumwezi), ndipo werengerani nyengo ya Edda. Ndipo muopeni Allah Mbuye wanu. Ndipo musawatulutse m’nyumba zawo ndiponso asatuluke kupatula akachita tchimo lalikulu loonekera (loyenera chilango, apo atha kutulutsidwa). Ndipo amenewa ndiwo malire a Allah (amene wawakhazikitsa kwa anthu Ake). Ndipo amene apyola malire a Allah wadzichitira yekha zoipa. Sukudziwa (cholinga cha malamulo amenewa) mwina Allah adzadzetsa chinthu pambuyo pake (chosonyeza kuyanjana).
Ang mga Tafsir na Arabe:
فَإِذَا بَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَأَمۡسِكُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٍ أَوۡ فَارِقُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٖ وَأَشۡهِدُواْ ذَوَيۡ عَدۡلٖ مِّنكُمۡ وَأَقِيمُواْ ٱلشَّهَٰدَةَ لِلَّهِۚ ذَٰلِكُمۡ يُوعَظُ بِهِۦ مَن كَانَ يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِۚ وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يَجۡعَل لَّهُۥ مَخۡرَجٗا
Choncho pamene iwo (osiyidwawo) nyengo yawo (Edda) itayandikira kutha, abwelereni mwa ubwino kapena asiyeni mwaubwino (polekelera nyengoyo kuti ithe); ndipo (powabwerera) funani mboni ziwiri zolungama zochokera mwa inu (zimene zichitire umboni kuti inu mukubwererana) ndipo perekani umboni chifukwa choopa Allah. Zimenezo ndizo akulangizidwa nazo amene akhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene akumuopa Allah (potsatira malamulo Ake), amkonzera njira yotulukira (m’mavuto).
Ang mga Tafsir na Arabe:
وَيَرۡزُقۡهُ مِنۡ حَيۡثُ لَا يَحۡتَسِبُۚ وَمَن يَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِ فَهُوَ حَسۡبُهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بَٰلِغُ أَمۡرِهِۦۚ قَدۡ جَعَلَ ٱللَّهُ لِكُلِّ شَيۡءٖ قَدۡرٗا
Ndipo ampatsa rizq kuchokera momwe samayembekezeramo. Ndipo amene akutsamira kwa Allah (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Allah ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse), ndithu Allah Ngokwaniritsa cholinga Chake ndi chofuna Chake. Ndithu chinthu chilichonse Allah wachipatsa mlingo wake woyenera (ndipo sichingaupyole).
Ang mga Tafsir na Arabe:
وَٱلَّٰٓـِٔي يَئِسۡنَ مِنَ ٱلۡمَحِيضِ مِن نِّسَآئِكُمۡ إِنِ ٱرۡتَبۡتُمۡ فَعِدَّتُهُنَّ ثَلَٰثَةُ أَشۡهُرٖ وَٱلَّٰٓـِٔي لَمۡ يَحِضۡنَۚ وَأُوْلَٰتُ ٱلۡأَحۡمَالِ أَجَلُهُنَّ أَن يَضَعۡنَ حَمۡلَهُنَّۚ وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يَجۡعَل لَّهُۥ مِنۡ أَمۡرِهِۦ يُسۡرٗا
Ndipo Edda ya amene asiya kudwala kumwezi mwa akazi anu chifukwa cha kukula, ngati mukukaika (nthawi ya Edda yawo), Edda yawo ndi miyezi itatu. Ndi omwe sadathe nsinkhu Edda yawo ndi momwemonso. Tsono akazi apakati nthawi yothera Edda yawo ndipomwe abereka. Ndipo amene aopa Allah amfewetsera zinthu zake (kuti zikhale zosavuta.)
Ang mga Tafsir na Arabe:
ذَٰلِكَ أَمۡرُ ٱللَّهِ أَنزَلَهُۥٓ إِلَيۡكُمۡۚ وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يُكَفِّرۡ عَنۡهُ سَيِّـَٔاتِهِۦ وَيُعۡظِمۡ لَهُۥٓ أَجۡرًا
Limenelo ndilamulo la Allah (lomwe) walikhazikitsa kwa inu. Ndipo amene aopa Allah (posunga malamulo ake), amam’fafanizira zoipa zake, ndiponso amamkulitsira malipiro ake.
Ang mga Tafsir na Arabe:
أَسۡكِنُوهُنَّ مِنۡ حَيۡثُ سَكَنتُم مِّن وُجۡدِكُمۡ وَلَا تُضَآرُّوهُنَّ لِتُضَيِّقُواْ عَلَيۡهِنَّۚ وَإِن كُنَّ أُوْلَٰتِ حَمۡلٖ فَأَنفِقُواْ عَلَيۡهِنَّ حَتَّىٰ يَضَعۡنَ حَمۡلَهُنَّۚ فَإِنۡ أَرۡضَعۡنَ لَكُمۡ فَـَٔاتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ وَأۡتَمِرُواْ بَيۡنَكُم بِمَعۡرُوفٖۖ وَإِن تَعَاسَرۡتُمۡ فَسَتُرۡضِعُ لَهُۥٓ أُخۡرَىٰ
Akhazikeni (osiyidwawo) m’mene mukukhala inumo monga momwe kulili kupeza kwanu (ndi mphamvu zanu ngakhale kuti mwawasiya ukwati). Musawavute ndi cholinga chowapana (kuti athawe okha). Ngati ali ndi pakati, apatseni zonse zofunika pa moyo mpaka adzabereke. Ngati akukuyamwitsirani ana anu apatseni malipiro awo mokwanira; gwirizanani pakati panu mwa ubwino ndi mofatsa. Ngati wina apereka mavuto kwa mnzake (ndiye kuti mwanayo) adzamuyamwitsira (mkazi) wina.
Ang mga Tafsir na Arabe:
لِيُنفِقۡ ذُو سَعَةٖ مِّن سَعَتِهِۦۖ وَمَن قُدِرَ عَلَيۡهِ رِزۡقُهُۥ فَلۡيُنفِقۡ مِمَّآ ءَاتَىٰهُ ٱللَّهُۚ لَا يُكَلِّفُ ٱللَّهُ نَفۡسًا إِلَّا مَآ ءَاتَىٰهَاۚ سَيَجۡعَلُ ٱللَّهُ بَعۡدَ عُسۡرٖ يُسۡرٗا
Wopeza bwino apereke malinga ndi kupeza bwino kwake; ndipo amene wachepekedwa rizq lake, apereke (kangachepe) pa zomwe Allah wampatsa. Allah sakakamiza aliyense kupatula zomwe wampatsa. Allah apereka kupeza bwino pambuyo pa masautso.
Ang mga Tafsir na Arabe:
وَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ عَتَتۡ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهَا وَرُسُلِهِۦ فَحَاسَبۡنَٰهَا حِسَابٗا شَدِيدٗا وَعَذَّبۡنَٰهَا عَذَابٗا نُّكۡرٗا
Ndipo ndimidzi ingati yomwe idanyoza lamulo la Mbuye wawo ndi Atumiki Ake, ndipo tidawawerenga ndi chiwerengero chokhwima (posanthula zochita zawo zonse). Ndiponso tidawalanga ndi chilango chaukali.
Ang mga Tafsir na Arabe:
فَذَاقَتۡ وَبَالَ أَمۡرِهَا وَكَانَ عَٰقِبَةُ أَمۡرِهَا خُسۡرًا
Choncho adalawa kuipa kwa zinthu zawo ndipo mapeto azinthu zawo adali kutayika (kuonongeka kwakukulu).
Ang mga Tafsir na Arabe:
أَعَدَّ ٱللَّهُ لَهُمۡ عَذَابٗا شَدِيدٗاۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ قَدۡ أَنزَلَ ٱللَّهُ إِلَيۡكُمۡ ذِكۡرٗا
Allah wawakonzera iwo chilango chokhwima, choncho muopeni Allah, E inu eni nzeru, amene mwakhulupirira, ndithu Allah wavumbulutsa chikumbutso (cholemekezeka kwa inu).
Ang mga Tafsir na Arabe:
رَّسُولٗا يَتۡلُواْ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ مُبَيِّنَٰتٖ لِّيُخۡرِجَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِۚ وَمَن يُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ وَيَعۡمَلۡ صَٰلِحٗا يُدۡخِلۡهُ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدٗاۖ قَدۡ أَحۡسَنَ ٱللَّهُ لَهُۥ رِزۡقًا
Mtumiki (amene) akukuwerengerani ndime za Allah zolongosola (choonadi ndi chonama) kuti awatulutse mu mdima ndi kuwaika ku dangalira amene wakhulupirira ndi kumachita zabwino. Ndipo amene akhulupirira Allah ndi kumachita zabwino, adzamlowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake; akakhala m’menemo muyaya. Ndithu Allah wamkonzera rizq (dalitso) labwino (Jannah)[367]
[367] Riziki ndi mawu a Chiarabu amene akutanthauza chilichonse chimene chimathandiza
Ang mga Tafsir na Arabe:
ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٖ وَمِنَ ٱلۡأَرۡضِ مِثۡلَهُنَّۖ يَتَنَزَّلُ ٱلۡأَمۡرُ بَيۡنَهُنَّ لِتَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ وَأَنَّ ٱللَّهَ قَدۡ أَحَاطَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عِلۡمَۢا
Allah ndiYemwe adalenga thambo zisanu ndi ziwiri, nthakanso chimodzimodzi. Malamulo Ake akutsika pakati pa izo kuti mudziwe kuti ndithu Allah pachilichonse ndi Wokhoza ndikutinso Allah wachizinga chilichonse m’kuchidziwa.
Ang mga Tafsir na Arabe:
 
Salin ng mga Kahulugan Surah: At-Talāq
Indise ng mga Surah Numero ng Pahina
 
Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - الترجمة الشيشيوا - Indise ng mga Salin

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

Isara