Check out the new design

قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا * - ترجمے کی لسٹ


معانی کا ترجمہ سورت: فُصّلت   آیت:

Fussilat

حمٓ
Hâ-Mîm:
عربی تفاسیر:
تَنزِيلٞ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
(Qur’an iyi) ndichivumbulutso chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.
عربی تفاسیر:
كِتَٰبٞ فُصِّلَتۡ ءَايَٰتُهُۥ قُرۡءَانًا عَرَبِيّٗا لِّقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ
(Ili) ndi buku lomwe ma Ayah ake afotokozedwa (bwino pokhudza malamulo a zamdziko ndi tsiku lachimaliziro); chowerengedwa (chimene chavumbulutsidwa) m’chiyankhulo cha Chiarabu kwa anthu ozindikira (tsatanetsatane wa malamulo ake).
عربی تفاسیر:
بَشِيرٗا وَنَذِيرٗا فَأَعۡرَضَ أَكۡثَرُهُمۡ فَهُمۡ لَا يَسۡمَعُونَ
Likunena nkhani yabwino (kwa ochita zabwino) ndi kuchenjeza (anthu ochita zoipa); koma ambiri a iwo (Aquraish) ainyoza kotero kuti sakumva; (kumva kothandizidwa nalo ndi kulilingalira).
عربی تفاسیر:
وَقَالُواْ قُلُوبُنَا فِيٓ أَكِنَّةٖ مِّمَّا تَدۡعُونَآ إِلَيۡهِ وَفِيٓ ءَاذَانِنَا وَقۡرٞ وَمِنۢ بَيۡنِنَا وَبَيۡنِكَ حِجَابٞ فَٱعۡمَلۡ إِنَّنَا عَٰمِلُونَ
Ndipo akunena (kuti): “Mitima yathu (yaphimbidwa) m’zivindikiro, ku zomwe ukutiitanirazo, ndipo m’makutu mwathu muli kulemera kwa ugonthi; choncho pakati pathu ndi pakati pa iwe pali chotsekereza (chotchinga); tero chita (zakozo); nafe tichita (zathu; aliyense wa ife asalowelere za mnzake).”
عربی تفاسیر:
قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يُوحَىٰٓ إِلَيَّ أَنَّمَآ إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞ فَٱسۡتَقِيمُوٓاْ إِلَيۡهِ وَٱسۡتَغۡفِرُوهُۗ وَوَيۡلٞ لِّلۡمُشۡرِكِينَ
Nena: “Ndithu, ine ndi munthu monga inu; kukuvumbulutsidwa kwa ine (kuchokera kwa Allah) kuti ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; choncho lungamani kwa Iye ndipo mpempheni chikhululuko (pa zimene mwakhala mukumchimwira)” Ndipo kuonongeka kwakukulu kuli pa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).
عربی تفاسیر:
ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ
Amene sapereka chopereka (Zakaat), ndiomwe akukanira za tsiku lachimaliziro.
عربی تفاسیر:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونٖ
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, pa iwo padzakhala malipiro osadukiza (osatha).
عربی تفاسیر:
۞ قُلۡ أَئِنَّكُمۡ لَتَكۡفُرُونَ بِٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَرۡضَ فِي يَوۡمَيۡنِ وَتَجۡعَلُونَ لَهُۥٓ أَندَادٗاۚ ذَٰلِكَ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Nena: “Kodi inu mukumkanira yemwe adalenga nthaka mmasiku awiri (okha)? Ndipo mukumpangira milungu (ina)? Iyeyo ndiye Mbuye wa zolengedwa zonse.”
عربی تفاسیر:
وَجَعَلَ فِيهَا رَوَٰسِيَ مِن فَوۡقِهَا وَبَٰرَكَ فِيهَا وَقَدَّرَ فِيهَآ أَقۡوَٰتَهَا فِيٓ أَرۡبَعَةِ أَيَّامٖ سَوَآءٗ لِّلسَّآئِلِينَ
Ndipo adaika pamenepo mapiri ataliatali pamwamba pake, ndi kudalitsapo (ndi madzi, mmera, ndi ziweto), ndipo adayesa mmenemo zakudya zake (za okhala pa nthakapo; zimenezi adadzichita) mmasiku anayi; (izi) nzokwanira kwa ofunsa (zakalengedwe ka nthaka ndi zamkati mwake).
عربی تفاسیر:
ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰٓ إِلَى ٱلسَّمَآءِ وَهِيَ دُخَانٞ فَقَالَ لَهَا وَلِلۡأَرۡضِ ٱئۡتِيَا طَوۡعًا أَوۡ كَرۡهٗا قَالَتَآ أَتَيۡنَا طَآئِعِينَ
Kenako adalunjika ku thambo (malunjikidwe ogwirizana ndimomwe Iye alili mosafanana ndi zolengedwa zake), pomwe ilo (thambolo) lidali utsi. Ndipo adati kwa ilo ndi nthaka: “Idzani, mofuna kapena mokakamizidwa (tsatirani lamulo Langa).” Izo zidayankha kuti: “Tadza mofuna.”
عربی تفاسیر:
 
معانی کا ترجمہ سورت: فُصّلت
سورتوں کی لسٹ صفحہ نمبر
 
قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا - ترجمے کی لسٹ

خالد ابراہیم پیٹالا نے ترجمہ کیا۔

بند کریں