Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима * - Таржималар мундарижаси


Маънолар таржимаси Оят: (1) Сура: Қурайш сураси

Қурайш сураси

لِإِيلَٰفِ قُرَيۡشٍ
Cholinga chakuwachita Maquraish kuti apitirize chizolowezi chawo,[486]
[486] (Ndime 1-4) Al-Kaaba, ndizachidziwikire kuti, adali malo opatulika kwa Arabu onse kuyambira nyengo ya Ibrahim (Abraham) (a.s) yemwe adamanga nyumbayi potsatira lamulo la Allah. Aquraish amene ankasunga ndi kuyang’anira Nyumba yopatulikayi, adali kupatsidwa ulemu ndi Arabu ena onse. Ndipo pa chifukwa chimenechi adali kutha kuyenda ulendo wopita ku Yemen nthawi ya dzinja, ndiponso ku Sham nthawi yachirimwe kukachita malonda ndikubwerera bwinobwino. Sadali kuputidwa ndi achifwamba m’njira, pophedwa kapena kulandidwa chuma chawo momwe ankachitiridwa Arabu ena. Pamene idamveka nkhani ya njovu kulemekezedwa kwawo kudaonjezeka kuchokera kwa mitundu yonse ya Arabu. Mu Sura imeneyi, Allah akuwakumbutsa za madalitso amenewa ndiponso akuwauza kuti adawafewetsera kayendedwe ka maulendo awo nthawi ya dzinja ndi chilimwe kuti akachite malonda ndikupeza chakudya ndi zina zofunika pa moyo wawo. Adawapatsa chitetezo posakhala ndi mantha m’njira; mantha omwe mitundu ina ya Arabu idali nawo. Madalitso onsewa ankawapeza chifukwa cha nyumba ya Al-Kaaba. Choncho kudali koyenera kwa iwo kumupembedza Mwini nyumbayo, osati mafano.
Pakadapanda nyumba Yakeyo sakadatha kumayenda maulendo mwa chitetezo, ndiponso sibwenzi kukudza aliyense ku mzindawo (Makka) chifukwa mukadakhala mulibe chodzetsa alendo.
Арабча тафсирлар:
 
Маънолар таржимаси Оят: (1) Сура: Қурайш сураси
Суралар мундарижаси Бет рақами
 
Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима - Таржималар мундарижаси

Қуръон Карим маъноларининг чевача таржимаси, мутаржим: Холид Иброҳим Бетала, 2020 йилда нашр қилинган

Ёпиш