Kuyamikidwa konse nkwa Allah (Yekha) Muumbi wa thambo ndi nthaka (popanda chofanizira), amene adachita angelo kukhala atumwi eni mapiko, awiriawiri; atatuatatu; ndi anayianayi. Amaonjezera mkulenga monga momwe afunira, (palibe chimene chingakanike kwa Iye). Ndithu Allah Ngokhoza chilichonse.[338]
[338] (Ndime 1-2) Iye Allah ali ndi mphamvu pa chilichonse; chimene afuna kuti chichitike chimachitika. Ndipo palibe chimene chingakanike kulengeka ndi Iye ngati atafuna kuti chilengeke. Allah wadzitamanda m’ndime ziwirizi ndi makhalidwe Ake awiri a pamwamba. Khalidwe loyamba, ndikukhoza komwe ndikusalephera chilichonse chimene wafuna. Khalidwe Lake lachiwiri ndikupereka madalitso osiyanasiyana pa zolengedwa Zake. Allah adalenga thambo ndi nthaka popanda chofanizira, natukula thambo kumwamba popanda mzati nalikongoletsa ndi nyenyezi. Iye ndi Yemwe adayalanso nthaka naika mmenemo mmera monga chakudya cha za moyo, nang’ambamo nyanja ndi mitsinje ndi akasupe ndi zina zotero zomwe zikusonyeza mphamvu Zake zoposa ndi luso Lake. Ndime yachiwiriyi ikutiphunzitsa kuti chimene Allah wachipereka kwa munthu monga chuma kukhala ndi moyo wangwiro, kukhala ndi nzeru zakuthwa, palibe amene angazitsekereze zimenezi. Ndipo chimene Allah wam’mana munthu, palibe amene angathe kuchipereka kwa iye.
E inu anthu! Kumbukirani chisomo cha Allah chomwe chili pa inu (pomthokoza). Kodi alipo Mlengi wina osati Allah amene angakupatseni rizq kuchokera kumwamba ndi pansi? Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi, koma Iye. Nanga mukutembenuzidwira kuti?
E inu anthu! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ngakhale mdyerekezi uja wamkulu (Iblis), asakunyengeni pa za Allah.[339]
[339] M’ndime iyi Allah akutichenjeza kuti tisanyengedwe ndi malangizo a Satana akuti: “Chitani mmene mungafunire, Allah Wachifundo chambiri adzakukhululukirani.”
Ndithu satana ndi mdani wanu; choncho mchiteni kukhala mdani. Iye amaliitanira gulu lake kuti likhale gulu la anthu a ku Moto.[340]
[340] Allah watifotokozera kuti satana ndi mdani wathu wakalekale; iye ndi amene adatulutsitsa tate wathu Adam m’Munda wa mtendere pomulakwitsa. Ndipo iye adalumbira kuti adzapitiriza kutisokeretsa.
Amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake), pa iwo padzakhala chilango chaukali; koma amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, iwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu.
Ndipo Allah adakulengani ndi dothi; kenako ndi dontho la umuna; kenako adakupangani amuna ndi akazi. Ndipo mkazi aliyense satenga mimba ndiponso sabala koma kupyolera m’kudziwa Kwake (Allah). Ndipo amene wapatsidwa moyo, sapatsidwa moyo wautali ndiponso sachepetsedwa moyo wake, koma zonsezo zili m’buku (la Allah). Ndithu zimenezo kwa Allah nzosavuta.
Amalowetsa usiku mu usana, ndi kulowetsa usana mu usiku; dzuwa ndi mwezi adazichita kuti zigonjere (malamulo Ake). Zonse zikuyenda (usana ndi usiku) kufikira nthawi yake yodziwika. Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanu, Mwini ufumu. Ndipo amene mukuwapembedza, osati Iye, alibe ngakhale khoko la chipatso cha kanjedza.
E inu anthu! Inu ndiosaukira (chinthu chilichonse) kwa Allah; koma Allah Ngwachikwanekwane (sasaukira chilichonse kwa inu); Wotamandidwa (ndi zolengedwa zonse).
Ndipo amoyo ndi akufa safanana (amene mitima yawo ili ndi moyo pokhala ndi chikhulupiliro, ndi amene mitima yawo ili yakufa posakhala ndi chikhulupiliro, ngosafanana). Ndithu Allah akumumveretsa amene wam’funa; koma iwe sungathe kumumveretsa amene ali m’manda.
Ndithu Ife takutuma mwachoona kuti unene nkhani yabwino (yokalowa ku Munda wamtendere kwa amene akhulupirira), ndi kuti uchenjeze (za chilango cha Moto kwa amene sadakhulupirire). Ndipo palibe m’badwo uliwonse koma mchenjezi adapitamo.
Ndipo mwa anthu ndi nyama zokwawa, ndi ziweto, nchimodzimodzinso; nzosiyana maonekedwe ake (utoto wake). Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Allah mwa akapolo Ake. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri.
Ndithu amene akuwerenga buku la Allah uku nkumapemphera Swala moyenera napereka m’zimene tawapatsa mwanseri ndi moonetsera, iwo akuyembekezera malonda osaonongeka.
Kenako tidawapatsa buku (Qur’an) amene tidawasankha mwa akapolo Athu, koma alipo ena mwa iwo odzichitira okha chinyengo (pochulukitsa machimo), ena mwa iwo ngaapakatikati; ndipo ena mwa iwo ngopikisana pochita zabwino mwa chifuniro cha Allah. Kuteroko ndiwo ubwino waukulu.
Koma amene sadakhulupirire, wawo ndi moto wa Jahannam sikudzaweruzidwa kwa iwo kuti afe, ngakhale chilango chake sichidzachepetsedwa pa iwo. Umo ndimmene tikumlipirira aliyense wokanira (mtendere wa Allah).
Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala osiyirana pa dziko lapansi (akufa ena, ena nkulowa m’malo mwawo). Ndipo amene sadakhulupirire, kuipa kwa kusakhulupirirako kuli kwa iye mwini. Ndipo kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse kwa Mbuye wawo, koma mkwiyo basi. Ndiponso kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse, koma kutayika basi.
Nena: “Kodi mwawaona aphatikizi anu (awa) amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah? Tandionetsani, ndimbali iti ya nthaka adalenga; kapena iwo ali ndi gawo m’thambo; (gawo lakulenga thambo?) Kapena tidawapatsa buku (Qur’an iyi isadadze) kotero kuti ali ndi umboni wapoyera wochokera m’menemo (wotsimikizira chipembedzo chawo chamafano)? Koma ochita zoipa salonjezana ena kwa ena china chake koma zachinyengo basi.
Chifukwa cha kudzikweza pa dziko ndi kuchita chiwembu choipa. Ndipo chiwembu choipa sichingamuzinge aliyense koma mwini (yemwe) wachitayo. Kodi akuyembekeza china chosakhala machitidwe (a Allah) amene adawapititsa pa anthu akale. Koma supeza kusintha pa machitidwe a Allah. Ndipo supeza kutembenuka pa machitidwe a Allah.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Излов натижалари:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".