Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio * - Mục lục các bản dịch


Ý nghĩa nội dung Chương: Chương Al-Hadid   Câu:

Chương Al-Hadid

سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Chilichonse chakumwamba ndi chapansi chikulemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe opunguka) ndipo Iye ndi Mwini Mphamvu, Wanzeru zakuya.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ
Ufumu wakumwamba ndi pansi, Ngwake amapereka moyo ndi imfa. ndipo Iye Ngwamphamvu pa chilichonse.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
هُوَ ٱلۡأَوَّلُ وَٱلۡأٓخِرُ وَٱلظَّٰهِرُ وَٱلۡبَاطِنُۖ وَهُوَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٌ
Iye ndi Oyamba (adalipo chilichonse chisadayambe); Wamuyaya (zonse zikadzatha); Woonekera (mzisonyezo pa chinthu chilichonse), Wobisika mkati kwambiri (saonedwa ndi maso pamoyo uno), Iye Ngodziwa chilichonse (kunja ndi mkati mwake).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ يَعۡلَمُ مَا يَلِجُ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا يَخۡرُجُ مِنۡهَا وَمَا يَنزِلُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ وَمَا يَعۡرُجُ فِيهَاۖ وَهُوَ مَعَكُمۡ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ
Iye ndi Amene adalenga kumwamba ndi pansi (ndi zonse zammenemo) m’masiku asanu ndi limodzi kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu monga momwe Iye adziwira polongosola ufumu Wake). Akudziwa chilichonse cholowa m’nthaka ndi chimene chikutuluka m’menemo; ndi chilichonse chimene chikutsika kuchokera kumwamba ndi chimene chikukwera kumeneko. Ndipo Iye ali nanu paliponse pamene muli. Ndithu Allah amaona chilichonse chimene mukuchita, (sichibisika chilichonse kwa Iye).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لَّهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ
Ufumu wakumwamba ndi pansi Ngwake ndipo kwa Allah nkobwerera zinthu (zonse).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِۚ وَهُوَ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Usiku amawulowetsa mu usana, ndipo usana amawulowetsa mu usiku. (Choncho kumasiyana kutalika kwake); ndipo Iye Ngodziwa zobisika za m’zifuwa (ndi zoganiza za m’mitima).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ءَامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَأَنفِقُواْ مِمَّا جَعَلَكُم مُّسۡتَخۡلَفِينَ فِيهِۖ فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنكُمۡ وَأَنفَقُواْ لَهُمۡ أَجۡرٞ كَبِيرٞ
Khulupirirani Allah ndi Mthenga Wake, ndipo perekani (pa njira ya Allah m’chuma chimene Allah wakupatsani uchiyang’anira. Choncho mwa inu amene akhulupirira (mwa Allah ndi mthenga Wake) ndikupereka (zimene awapatsa) iwo ali ndi malipiro aakulu (kwa Allah).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَمَا لَكُمۡ لَا تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلرَّسُولُ يَدۡعُوكُمۡ لِتُؤۡمِنُواْ بِرَبِّكُمۡ وَقَدۡ أَخَذَ مِيثَٰقَكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ
Kodi nchifukwa ninji simukhulupirira Allah pomwe Mtumiki akukuitanani kuti mukhulupirire Mbuye wanu (ndi kukulimbitsani pa zimenezo) chikhalirecho (Iye) adalandira lonjezo lanu, (muli mumsana wa tate wanu Adam kuti mdzakhulupirira,) ngati mulidi okhulupirira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
هُوَ ٱلَّذِي يُنَزِّلُ عَلَىٰ عَبۡدِهِۦٓ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖ لِّيُخۡرِجَكُم مِّنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ بِكُمۡ لَرَءُوفٞ رَّحِيمٞ
Iye ndi Amene akuvumbulutsa kwa kapolo Wake Ayah (ndime) zofotokoza mwatsatanetsatane kuti akutulutseni mum’dima (wa kusokera) ndi kukuikani ku chiongoko cha kuunika. Ndipo ndithu Allah Ngoleza kwa inu, Ngwachisoni.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَمَا لَكُمۡ أَلَّا تُنفِقُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَلِلَّهِ مِيرَٰثُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَا يَسۡتَوِي مِنكُم مَّنۡ أَنفَقَ مِن قَبۡلِ ٱلۡفَتۡحِ وَقَٰتَلَۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَعۡظَمُ دَرَجَةٗ مِّنَ ٱلَّذِينَ أَنفَقُواْ مِنۢ بَعۡدُ وَقَٰتَلُواْۚ وَكُلّٗا وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ
Kodi ndichifukwa chiani simukupereka pa njira ya Allah (chuma chanu) pamene Allah Ndimwini wa zosiyidwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Sali ofanana mwa inu amene adapereka chuma (panjira ya Allah) pamodzi ndi kumenya nkhondo usadagonjetsedwe (mzinda wa Makka), iwowo ndiomwe ali ndi ulemelero waukulu kuposa amene apereka chuma chawo ndi kumenya nkhondo pambuyo. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino (ngakhale ali osiyana ulemelero wawo); ndipo Allah akudziwa zonse zimene muchita. (Choncho aliyense adzalipidwa molingana ndi zimene amachita).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
مَّن ذَا ٱلَّذِي يُقۡرِضُ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا فَيُضَٰعِفَهُۥ لَهُۥ وَلَهُۥٓ أَجۡرٞ كَرِيمٞ
Kodi ndani (okhulupirira) amene angamkongoze Allah ngongole yabwino kuti amuchulukitsire malipiro ake? Ndipo iye adzalandira malipiro aulemu (pa tsiku la chiweruziro).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَوۡمَ تَرَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ يَسۡعَىٰ نُورُهُم بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَبِأَيۡمَٰنِهِمۖ بُشۡرَىٰكُمُ ٱلۡيَوۡمَ جَنَّٰتٞ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Tsiku limene udzaona okhulupirira aamuna ndi aakazi dangalira lawo likuyenda patsogolo pawo ndi mbali ya kumanja kwao (uku angelo akunena kwa iwo): “Chisangalalo chanu lero ndi minda imene pansi pake pakuyenda mitsinje. Mukhala m’menemo nthawi yaitali! Kumeneku ndiko kupambana kwakukulu (kwa inu).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَوۡمَ يَقُولُ ٱلۡمُنَٰفِقُونَ وَٱلۡمُنَٰفِقَٰتُ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱنظُرُونَا نَقۡتَبِسۡ مِن نُّورِكُمۡ قِيلَ ٱرۡجِعُواْ وَرَآءَكُمۡ فَٱلۡتَمِسُواْ نُورٗاۖ فَضُرِبَ بَيۡنَهُم بِسُورٖ لَّهُۥ بَابُۢ بَاطِنُهُۥ فِيهِ ٱلرَّحۡمَةُ وَظَٰهِرُهُۥ مِن قِبَلِهِ ٱلۡعَذَابُ
Tsiku limene achinyengo aamuna ndi achinyengo aakazi adzauza okhulupirira (kuti:) “Tidikireni kuti tipeze kuunika kwanu!” Kudzanenedwa (mwachipongwe): “Bwererani pambuyo panu mukafune kuunika kumeneko!” Choncho padzaikidwa mpanda pakati pawo (okhulupirira ndi achinyengo) umene udzakhala ndi khomo, mkati mwake muli chifundo ndi mtendere; kunja kwake kuli mazunzo ndi chilango.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يُنَادُونَهُمۡ أَلَمۡ نَكُن مَّعَكُمۡۖ قَالُواْ بَلَىٰ وَلَٰكِنَّكُمۡ فَتَنتُمۡ أَنفُسَكُمۡ وَتَرَبَّصۡتُمۡ وَٱرۡتَبۡتُمۡ وَغَرَّتۡكُمُ ٱلۡأَمَانِيُّ حَتَّىٰ جَآءَ أَمۡرُ ٱللَّهِ وَغَرَّكُم بِٱللَّهِ ٱلۡغَرُورُ
(Achinyengo) adzaitana okhulupirira ponena kuti: “Kodi sitidali nanu limodzi (pa dziko ndi kumatsagana nanu?” (Okhulupirira) adzati: “Inde! (Mudali nafe monga momwe mukunenera). Koma inu munadziononga nokha ndipo mumayembekezera (kuti okhulupirira awapeze mavuto ndi kuonongeka); mudakaikira (zinthu za chilengedwe chanu); choncho zikhulupiliro zanu zonama zidakunyengani pomwe mudali angwiro mpaka lamulo la Allah (imfa) lidakupezani, komanso adakunyengani onyenga (satana) za Allah.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
فَٱلۡيَوۡمَ لَا يُؤۡخَذُ مِنكُمۡ فِدۡيَةٞ وَلَا مِنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ مَأۡوَىٰكُمُ ٱلنَّارُۖ هِيَ مَوۡلَىٰكُمۡۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ
Basi lero sililandiridwa dipo lochokera kwa inu (limene mungalipereke kuti mudzipulumutse ku chilango ngakhale likhale lamtengo wotani). Ndiponso sililandiridwa dipo lochokera kwa osakhulupirira (amene adalingana nanu n’kusakhulupirira kwawo Allah) malo anu nonsenu ndi ku Moto basi. Amenewa ndi malo okuyenerani. Kumeneko ndiko kobwerera koipa kwabasi!
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
۞ أَلَمۡ يَأۡنِ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَن تَخۡشَعَ قُلُوبُهُمۡ لِذِكۡرِ ٱللَّهِ وَمَا نَزَلَ مِنَ ٱلۡحَقِّ وَلَا يَكُونُواْ كَٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلُ فَطَالَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡأَمَدُ فَقَسَتۡ قُلُوبُهُمۡۖ وَكَثِيرٞ مِّنۡهُمۡ فَٰسِقُونَ
Kodi siidakwane nthawi kwa okhulupirira kuti mitima yawo idzichepetse pokumbukira Allah ndi zomwe zidavumbulutsidwa za chowonadi (Qur’an yolemekezeka)? Ndi kuti asakhale monga omwe adapatsidwa buku kale (Ayuda ndi Akhrisitu) amene nthawi yawo yosiyana ndi aneneri awo idali yaitali. Choncho mitima yawo idauma ndipo ambiri a iwo adatuluka m’chilamulo (cha Allah).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يُحۡيِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۚ قَدۡ بَيَّنَّا لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ
Dziwani kuti ndithu Allah amaukitsa nthaka itauma (poitsitsira mvula kuti mmera umere). Choncho takulongosolerani zisonyezo kuti inu mukhale ndi nzeru.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
إِنَّ ٱلۡمُصَّدِّقِينَ وَٱلۡمُصَّدِّقَٰتِ وَأَقۡرَضُواْ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا يُضَٰعَفُ لَهُمۡ وَلَهُمۡ أَجۡرٞ كَرِيمٞ
Ndithu amene akupereka sadaka amuna ndi akazi, ndi kumamkongoza Allah ngongole yabwino (Allah) adzawaonjezera malipiro pa zimenezi. Ndipo ali ndi malipiro aulemu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦٓ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلصِّدِّيقُونَۖ وَٱلشُّهَدَآءُ عِندَ رَبِّهِمۡ لَهُمۡ أَجۡرُهُمۡ وَنُورُهُمۡۖ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَحِيمِ
Ndipo amene akhulupirira Allah ndi aneneri Ake, iwowo ndiwo owona (pa chikhulupiliro); ndi ofera pa njira ya Allah (onsewo) azapeza malipiro awo ndi kuwala kwawo kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire ndi kutsutsa zisonyezo zathu iwowo ndi eni a ku Jahena.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا لَعِبٞ وَلَهۡوٞ وَزِينَةٞ وَتَفَاخُرُۢ بَيۡنَكُمۡ وَتَكَاثُرٞ فِي ٱلۡأَمۡوَٰلِ وَٱلۡأَوۡلَٰدِۖ كَمَثَلِ غَيۡثٍ أَعۡجَبَ ٱلۡكُفَّارَ نَبَاتُهُۥ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَىٰهُ مُصۡفَرّٗا ثُمَّ يَكُونُ حُطَٰمٗاۖ وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِ عَذَابٞ شَدِيدٞ وَمَغۡفِرَةٞ مِّنَ ٱللَّهِ وَرِضۡوَٰنٞۚ وَمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَآ إِلَّا مَتَٰعُ ٱلۡغُرُورِ
Dziwani kuti ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndimasewera, chibwana, chokometsera chabe, chonyadiritsana pakati panu (pa ulemelero) ndi kuchulukitsa chuma ndi ana (pomwe zonsezo sizikhala nthawi yayitali;) fanizo lake lili ngati mvula yomwe mmera wake umakondweretsa alimi; kenako umafota, ndipo uuona uli wachikasu; kenako nkukhala odukaduka (oonongeka). Koma tsiku lachimaliziro kuli chilango cha ukali; ndi chikhululuko komanso chikondi chochokera kwa Allah. Moyo wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma ndichisangalalo chonyenga basi.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
سَابِقُوٓاْ إِلَىٰ مَغۡفِرَةٖ مِّن رَّبِّكُمۡ وَجَنَّةٍ عَرۡضُهَا كَعَرۡضِ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ أُعِدَّتۡ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦۚ ذَٰلِكَ فَضۡلُ ٱللَّهِ يُؤۡتِيهِ مَن يَشَآءُۚ وَٱللَّهُ ذُو ٱلۡفَضۡلِ ٱلۡعَظِيمِ
Chitani changu (pa zinthu zokupatitsani) chikhululuko chochokera kwa Mbuye wanu ndi Munda wamtendere womwe mulifupi mwake muli ngati kutambasuka kwa kumwamba ndi pansi; wakonzedwera amene akhulupirira Allah ndi aneneri Ake; umenewo ndi ubwino wa Allah womwe akuupereka kwa amene wamfuna. Allah ndi Mwini ubwino waukulu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
مَآ أَصَابَ مِن مُّصِيبَةٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِيٓ أَنفُسِكُمۡ إِلَّا فِي كِتَٰبٖ مِّن قَبۡلِ أَن نَّبۡرَأَهَآۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٞ
Silipezeka tsoka lililonse panthaka (monga chilala) ngakhale pamatupi anu koma lidalembedwa kale m’buku (la Allah) tisadalilenge ndi kulipereka. Ndithu zimenezo kwa Allah nzofewa.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لِّكَيۡلَا تَأۡسَوۡاْ عَلَىٰ مَا فَاتَكُمۡ وَلَا تَفۡرَحُواْ بِمَآ ءَاتَىٰكُمۡۗ وَٱللَّهُ لَا يُحِبُّ كُلَّ مُخۡتَالٖ فَخُورٍ
(Takudziwitsani zimenezi) kuti musadandaule ndi chimene chakudutsani, ndi kutinso musakondwere monyada ndi chimene wakupatsani. Allah sakonda aliyense wodzitama, wonyada.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱلَّذِينَ يَبۡخَلُونَ وَيَأۡمُرُونَ ٱلنَّاسَ بِٱلۡبُخۡلِۗ وَمَن يَتَوَلَّ فَإِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
Amene akuchita umbombo (ndi chuma chawo; ndipo osapereka pa njira ya Allah) ndi kumalamula anthu ena kuchita umbombo. Ndipo amene atembenuke (adzalandira chilango chachikulu), ndithu Allah Ngolemera, (sasaukira chilichonse kwa wina), Ngotamandidwa.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا رُسُلَنَا بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَأَنزَلۡنَا مَعَهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡمِيزَانَ لِيَقُومَ ٱلنَّاسُ بِٱلۡقِسۡطِۖ وَأَنزَلۡنَا ٱلۡحَدِيدَ فِيهِ بَأۡسٞ شَدِيدٞ وَمَنَٰفِعُ لِلنَّاسِ وَلِيَعۡلَمَ ٱللَّهُ مَن يَنصُرُهُۥ وَرُسُلَهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ إِنَّ ٱللَّهَ قَوِيٌّ عَزِيزٞ
Ndithu tidatuma atumiki Athu pamodzi ndi zozizwitsa. Ndipo tidavumbulutsa pamodzi ndi iwo mabuku ndi muyeso wa choonadi kuti anthu achite chilungamo. Ndipo tidalenga chitsulo momwe muli mphamvu zambiri (pa nkhondo) ndiponso chithandizo kwa anthu (akakhala pa mtendere ndi kupindula nacho pochita zowathandiza pa moyo wawo). Ndi kuti Allah amuonetsere poyera, amene angachiteteze (chipembedzo Chake) ndi atumiki Ake (kupyolera m’chitsulocho) pomwe Iye sakumuona. Ndithu Allah Ngwamphamvu (pa chilichonse) Ngopambana.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحٗا وَإِبۡرَٰهِيمَ وَجَعَلۡنَا فِي ذُرِّيَّتِهِمَا ٱلنُّبُوَّةَ وَٱلۡكِتَٰبَۖ فَمِنۡهُم مُّهۡتَدٖۖ وَكَثِيرٞ مِّنۡهُمۡ فَٰسِقُونَ
Ndipo ndithu tidatuma Nuh ndi Ibrahim ndi kukhazikitsa uneneri m’mbumba yawo ndi mabuku (achiongoko). Ena mwa iwo adayenda pa njira yolungama, koma ambiri a iwo adapatuka pa njira yolungamayo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ثُمَّ قَفَّيۡنَا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم بِرُسُلِنَا وَقَفَّيۡنَا بِعِيسَى ٱبۡنِ مَرۡيَمَ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡإِنجِيلَۖ وَجَعَلۡنَا فِي قُلُوبِ ٱلَّذِينَ ٱتَّبَعُوهُ رَأۡفَةٗ وَرَحۡمَةٗۚ وَرَهۡبَانِيَّةً ٱبۡتَدَعُوهَا مَا كَتَبۡنَٰهَا عَلَيۡهِمۡ إِلَّا ٱبۡتِغَآءَ رِضۡوَٰنِ ٱللَّهِ فَمَا رَعَوۡهَا حَقَّ رِعَايَتِهَاۖ فَـَٔاتَيۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنۡهُمۡ أَجۡرَهُمۡۖ وَكَثِيرٞ مِّنۡهُمۡ فَٰسِقُونَ
Kenako tidatsatiza pambuyo pawo ndi atumiki Athu ndipo tidasatiza ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndipo tidampatsa Injili ndipo tidaika kufatsa ndi chifundo m’mitima ya omwe adamtsatira. Koma kusakwatira, adakuyambitsa okha; sitidawalamule zimenezo koma (adayambitsa zimenezo) chifukwa chofuna chikondi cha Allah; koma sadazisunge moyenera. Choncho amene adakhulupirira pakati pawo tidawapatsa malipiro awo, koma ambiri a iwo ngopandukira malamulo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَءَامِنُواْ بِرَسُولِهِۦ يُؤۡتِكُمۡ كِفۡلَيۡنِ مِن رَّحۡمَتِهِۦ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ نُورٗا تَمۡشُونَ بِهِۦ وَيَغۡفِرۡ لَكُمۡۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo khulupirirani mthenga Wake, akupatsani zigawo ziwiri za chifundo Chake. Ndipo akupangirani kuunika koongoka nako (poyenda patsiku la chiweruziro.) Ndiponso akukhululukirani ndipo Allah Ngokhululuka mochuluka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لِّئَلَّا يَعۡلَمَ أَهۡلُ ٱلۡكِتَٰبِ أَلَّا يَقۡدِرُونَ عَلَىٰ شَيۡءٖ مِّن فَضۡلِ ٱللَّهِ وَأَنَّ ٱلۡفَضۡلَ بِيَدِ ٱللَّهِ يُؤۡتِيهِ مَن يَشَآءُۚ وَٱللَّهُ ذُو ٱلۡفَضۡلِ ٱلۡعَظِيمِ
(Allah akupatsani zonsezi) kuti adziwe amene adapatsidwa buku (omwe sadamkhulupirire Mtumiki{s.a.w}) kuti iwo sangathe kudzisankhira okha chilichonse mu mtendere wa Allah. Ndipo ndithu ubwino wonse uli m’manja mwa Allah Yekha. Amapatsa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wochuluka.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
 
Ý nghĩa nội dung Chương: Chương Al-Hadid
Mục lục các chương Kinh Số trang
 
Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio - Mục lục các bản dịch

Bản dịch ý nghĩa nội dung Kinh Qur'an bằng tiếng Chichio, do Khalid Ibrahim Petala dịch thuật, bản dịch năm 2020.

Đóng lại