Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 赛智德   段:

As-Sajdah

الٓمٓ
Alif-Lâm-Mîm.
阿拉伯语经注:
تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ لَا رَيۡبَ فِيهِ مِن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Chivumbulutso cha buku (la Qur’an) chilibe chikaiko mkati mwake chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
阿拉伯语经注:
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۚ بَلۡ هُوَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أَتَىٰهُم مِّن نَّذِيرٖ مِّن قَبۡلِكَ لَعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ
Kapena akunena kuti: “Walipeka yekha (bukulo)?” Iyayi, ichi nchoona chimene chachokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu ndi chimenechi, amene sadawadzere mchenjezi iwe usadadze. Kuti aongoke (ndi kutsatira njira yolungama).
阿拉伯语经注:
ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ مَا لَكُم مِّن دُونِهِۦ مِن وَلِيّٖ وَلَا شَفِيعٍۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ
Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu); (kukhazikika kolingana ndi ulemelero Wake, kumene Iye Mwini wake akukudziwa). Inu mulibe mtetezi ngakhale muomboli kupatula Iye. Nanga kodi bwanji simulingalira?[315]
[315] M’ndime iyi Allah akutiuza kuti adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi. Komatu nthawi ya masiku amenewa, palibe amene akudziwa tsatanetsatane wake koma Allah Yekha. Choncho tisaganizire kuti masikuwo adali olingana ndi masiku a moyo uno wadziko lapansi.
阿拉伯语经注:
يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ يَعۡرُجُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٖ كَانَ مِقۡدَارُهُۥٓ أَلۡفَ سَنَةٖ مِّمَّا تَعُدُّونَ
(Iye) akuyendetsa zinthu (zonse) kuchokera kumwamba kupita pansi. Kenako zidzakwera kubwerera kwa Iye, pa tsiku lolingana ndi zaka chikwi chimodzi (poyerekeza ndi zaka zadziko lapansi) mzomwe inu mumawerengera.
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكَ عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Ameneyo (ndi Allah), Wodziwa zobisika ndi zoonekera; Mwini mphamvu zoposa Wachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
ٱلَّذِيٓ أَحۡسَنَ كُلَّ شَيۡءٍ خَلَقَهُۥۖ وَبَدَأَ خَلۡقَ ٱلۡإِنسَٰنِ مِن طِينٖ
Yemwe adakonza bwino chilichonse (chomwe) adalenga. Ndipo adayambitsa chilengedwe cha munthu (Adam) kuchokera ku dongo.
阿拉伯语经注:
ثُمَّ جَعَلَ نَسۡلَهُۥ مِن سُلَٰلَةٖ مِّن مَّآءٖ مَّهِينٖ
Kenako adachita mbumba yake kuti ipangike kuchokera m’madzi enieni onyozeka.
阿拉伯语经注:
ثُمَّ سَوَّىٰهُ وَنَفَخَ فِيهِ مِن رُّوحِهِۦۖ وَجَعَلَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ
Kenako adamkonza ndi kuuziramo mzimu Wake. Ndipo adakuikirani kumva, kupenya ndi mitima. Kuthokoza kwanu mpang’ono ndithu.
阿拉伯语经注:
وَقَالُوٓاْ أَءِذَا ضَلَلۡنَا فِي ٱلۡأَرۡضِ أَءِنَّا لَفِي خَلۡقٖ جَدِيدِۭۚ بَلۡ هُم بِلِقَآءِ رَبِّهِمۡ كَٰفِرُونَ
Ndipo (otsutsa kuuka ku imfa) akunena: “Kodi tikadzatayika m’nthaka (ndi kusakanikirana ndi dothi), tidzakhalanso mkalengedwe katsopano?” (Iyayi), koma iwo sakhulupirira za kukumana ndi Mbuye wawo.
阿拉伯语经注:
۞ قُلۡ يَتَوَفَّىٰكُم مَّلَكُ ٱلۡمَوۡتِ ٱلَّذِي وُكِّلَ بِكُمۡ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ تُرۡجَعُونَ
Nena: “Adzachotsa mizimu yanu Mngelo wa imfa yemwe wapatsidwa udindo umenewu pa inu. Kenako mudzabwerera kwa Mbuye wanu.”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 赛智德
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭