《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 亚斯   段:

亚斯

يسٓ
Yâ-Sîn.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡحَكِيمِ
Ndikulumbira Qur’an (iyi yomwe yakonzedwa mwaluso) yodzazidwa ndi mawu anzeru.
阿拉伯语经注:
إِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndithu iwe (Muhammad {s.a.w}) ndimmodzi wa atumiki (amene Allah adawatuma kwa anthu kuti akawasonyeze chiongoko).
阿拉伯语经注:
عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
(Uli) panjira yolunjika.
阿拉伯语经注:
تَنزِيلَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ
(Qur’an iyi) nchivumbulutso cha Mwini Mphamvu zoposa; (palibe chokanika kwa Iye) Wachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أُنذِرَ ءَابَآؤُهُمۡ فَهُمۡ غَٰفِلُونَ
Kuti uwachenjeze anthu omwe makolo awo sadachenjezedwe; choncho iwo ngoiwala (zomwe zili zofunika kuchitira Allah ndi kudzichitira okha pamodzi ndi anthu ena).
阿拉伯语经注:
لَقَدۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَىٰٓ أَكۡثَرِهِمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndithu mawu (onena za chilango) atsimikizika pa ambiri a iwo; poti iwo sakhulupirira.
阿拉伯语经注:
إِنَّا جَعَلۡنَا فِيٓ أَعۡنَٰقِهِمۡ أَغۡلَٰلٗا فَهِيَ إِلَى ٱلۡأَذۡقَانِ فَهُم مُّقۡمَحُونَ
Ndithu Ife taika magoli m’makosi mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti mitu yawo yayang’ana mmwamba; (siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana).
阿拉伯语经注:
وَجَعَلۡنَا مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ سَدّٗا وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ سَدّٗا فَأَغۡشَيۡنَٰهُمۡ فَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ
Ndipo tawaikira chotsekereza patsogolo pawo ndi chotsekereza pambuyo pawo, ndipo (maso awo) tawaphimba, tero iwo saona (zapatsogolo ndi pambuyo pawo).
阿拉伯语经注:
وَسَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndipo kwa iwo nchimodzimodzi, uwachenjeze ngakhale usawachenjeze sangakhulupirire.
阿拉伯语经注:
إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلذِّكۡرَ وَخَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِۖ فَبَشِّرۡهُ بِمَغۡفِرَةٖ وَأَجۡرٖ كَرِيمٍ
Ndithu kuchenjeza kwako kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa (Allah) Wachifundo chambiri ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya chikhululuko (chochokera kwa Allah pa machimo ake) ndi malipiro aulemu.
阿拉伯语经注:
إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَنَكۡتُبُ مَا قَدَّمُواْ وَءَاثَٰرَهُمۡۚ وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ فِيٓ إِمَامٖ مُّبِينٖ
Ndithu Ife tidzaukitsa akufa, ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo), ndipo chinthu chilichonse tachilemba m’kaundula wopenyeka (wofotokoza chilichonse).
阿拉伯语经注:
وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلًا أَصۡحَٰبَ ٱلۡقَرۡيَةِ إِذۡ جَآءَهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Ndipo pereka kwa iwo (iwe Mneneri) fanizo la (nkhani ya) eni mudzi pamene atumiki (a Allah) adaudzera mudziwo (kuti akaaongole eni mudziwo).
阿拉伯语经注:
إِذۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱثۡنَيۡنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزۡنَا بِثَالِثٖ فَقَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَيۡكُم مُّرۡسَلُونَ
Pamene tidatumiza atumiki awiri kwa iwo adawatsutsa; ndipo tidawalimbitsa iwo (awiriwo) potumiza wachitatu. (Atumiki atatuwo) adati: “Ife tatumidwa kwa inu.”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ مَآ أَنتُمۡ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُنَا وَمَآ أَنزَلَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَكۡذِبُونَ
(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu ngati ife; (Allah) Wachifundo chambiri sadavumbulutse chilichonse (kwa munthu); inu simuli kanthu koma mukunena bodza.”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ رَبُّنَا يَعۡلَمُ إِنَّآ إِلَيۡكُمۡ لَمُرۡسَلُونَ
(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.”
阿拉伯语经注:
وَمَا عَلَيۡنَآ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
“Ndipo palibe china pa ife, koma kufikitsa mwachimvekere (uthenga wa Allah).”
阿拉伯语经注:
قَالُوٓاْ إِنَّا تَطَيَّرۡنَا بِكُمۡۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهُواْ لَنَرۡجُمَنَّكُمۡ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٞ
(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza tsoka chifukwa cha inu; ngati simusiya (ulaliki wanuwo wofuna kutichotsa ku chipembedzo chathu) tikugendani ndi miyala; ndipo kuchokera kwa ife chikukhudzani chilango chowawa.”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ طَٰٓئِرُكُم مَّعَكُمۡ أَئِن ذُكِّرۡتُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ مُّسۡرِفُونَ
(Atumiki) adati: “Tsoka lanu lili ndi inu (chifukwa cha kukana kwanu ndi kupitiriza kupembedza mafano). Kodi mukakumbutsidwa (ndi mawu omwe m’kati mwake muli mtendere wanu mukuti takudzetserani masoka; ndi kumatiopseza ndi chilango chowawa)? Koma inu ndi anthu olumpha malire.”
阿拉伯语经注:
وَجَآءَ مِنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ رَجُلٞ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُواْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Kenako munthu adadza akuthamanga kuchokera ku malekezero a mzindawo (ndipo) adati: “E inu anthu anga! Atsateni atumikiwa.”
阿拉伯语经注:
ٱتَّبِعُواْ مَن لَّا يَسۡـَٔلُكُمۡ أَجۡرٗا وَهُم مُّهۡتَدُونَ
“Atsateni omwe sakupemphani malipiro (pa kukulangizani kwawo), ndipo iwo ngoongoka.”
阿拉伯语经注:
وَمَالِيَ لَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
“Kodi nchiyani chingandiletse ine kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa Iye ndi komwe inu nonse mudzabwerera.”.
阿拉伯语经注:
ءَأَتَّخِذُ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةً إِن يُرِدۡنِ ٱلرَّحۡمَٰنُ بِضُرّٖ لَّا تُغۡنِ عَنِّي شَفَٰعَتُهُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا يُنقِذُونِ
“Kodi ndidzipangire milungu kusiya Iye (Allah)? Chipulumutso chawo sichingandipindulire chilichonse ngati (Allah) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira zoipa; ndipo siingandipulumutse.”
阿拉伯语经注:
إِنِّيٓ إِذٗا لَّفِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ
“Ndithu ine ngati nditatero ndiye kuti ndili mchisokero choonekera poyera”.
阿拉伯语经注:
إِنِّيٓ ءَامَنتُ بِرَبِّكُمۡ فَٱسۡمَعُونِ
“Ndithu ine ndakhulupirira Mbuye wanu choncho ndimvereni.”
阿拉伯语经注:
قِيلَ ٱدۡخُلِ ٱلۡجَنَّةَۖ قَالَ يَٰلَيۡتَ قَوۡمِي يَعۡلَمُونَ
Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa m’Munda wamtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga akadadziwa!”
阿拉伯语经注:
بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ
“Momwe Mbuye wanga wandikhululukira ndikundichita kukhala mmodzi wa opatsidwa ulemu (akadakhulupirira).”
阿拉伯语经注:
۞ وَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنۢ بَعۡدِهِۦ مِن جُندٖ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَمَا كُنَّا مُنزِلِينَ
Ndipo anthu ake sitidawatsitsire ankhondo ochokera kumwamba pambuyo pake (kuti awaononge). Ndipo pachizolowezi chathu sititsitsa (ankhondo kumwamba tikafuna kuononga, koma Mngelo mmodzi amakwanira).
阿拉伯语经注:
إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَإِذَا هُمۡ خَٰمِدُونَ
(Kuonongeka kwawo) kudali mkuwe umodzi, ndipo nthawi yomweyo adali akufa (izi zidachitika pamene mngelo Gabuliyele adawakuwira mkuwe wamphamvu).
阿拉伯语经注:
يَٰحَسۡرَةً عَلَى ٱلۡعِبَادِۚ مَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ha! Nzodandaulitsa kwa akapolo! Palibe pamene mtumiki adawadzera popanda kumchitira chipongwe (ndi kukana kumtsata)!
阿拉伯语经注:
أَلَمۡ يَرَوۡاْ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ أَنَّهُمۡ إِلَيۡهِمۡ لَا يَرۡجِعُونَ
Kodi sadalingalire za mibadwo yambirimbiri imene tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo iwo sangabwelerenso kwa iwo.
阿拉伯语经注:
وَإِن كُلّٞ لَّمَّا جَمِيعٞ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ
Ndipo zolengedwa zonse zidzaonekera kwa Ife.
阿拉伯语经注:
وَءَايَةٞ لَّهُمُ ٱلۡأَرۡضُ ٱلۡمَيۡتَةُ أَحۡيَيۡنَٰهَا وَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهَا حَبّٗا فَمِنۡهُ يَأۡكُلُونَ
Ndipo chisonyezo chawo ndi nthaka yakufa; timaiukitsa (ndi madzi) ndi kutulutsa m’menemo njere, zomwe zina mwa izo amadya.
阿拉伯语经注:
وَجَعَلۡنَا فِيهَا جَنَّٰتٖ مِّن نَّخِيلٖ وَأَعۡنَٰبٖ وَفَجَّرۡنَا فِيهَا مِنَ ٱلۡعُيُونِ
Ndipo tapanga m’menemo minda ya kanjedza ndi mphesa; ndipo tatulutsa m’menemo akasupe.
阿拉伯语经注:
لِيَأۡكُلُواْ مِن ثَمَرِهِۦ وَمَا عَمِلَتۡهُ أَيۡدِيهِمۡۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ
Kuti azidya zipatso zake pomwe sizidapangidwe ndi manja awo. Kodi bwanji sathokoza (Allah)?
阿拉伯语经注:
سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا مِمَّا تُنۢبِتُ ٱلۡأَرۡضُ وَمِنۡ أَنفُسِهِمۡ وَمِمَّا لَا يَعۡلَمُونَ
Alemekezeke (Allah), Amene adalenga zinthu zonse, chachimuna ndi chachikazi, kuchokera m’zimene nthaka ikutulutsa, ndi iwo omwe ndi zina zimene (anthu) sakudziwa.
阿拉伯语经注:
وَءَايَةٞ لَّهُمُ ٱلَّيۡلُ نَسۡلَخُ مِنۡهُ ٱلنَّهَارَ فَإِذَا هُم مُّظۡلِمُونَ
Ndiponso chisonyezo chawo ndiusiku. M’menemo timachotsamo usana (womwe umabisa usiku), ndipo (anthu) amangozindikira ali mu mdima.
阿拉伯语经注:
وَٱلشَّمۡسُ تَجۡرِي لِمُسۡتَقَرّٖ لَّهَاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ
۞ Ndipo dzuwa; limayenda m’njira ndi m’nthawi yake imene idakonzedwa kwa ilo. Chikonzero chimenecho ncha (Allah) Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡقَمَرَ قَدَّرۡنَٰهُ مَنَازِلَ حَتَّىٰ عَادَ كَٱلۡعُرۡجُونِ ٱلۡقَدِيمِ
Ndiponso mwezi; tidaukonzera malo oimirapo mpaka kukafika pomwe umabwerera ndi kukhala wochepa ndi wokhota monga nthambi ya mtengo wa kanjedza, youma komanso yokhota.[341]
[341] Ndime iyi ikufotokoza za kayendedwe ka mwezi kuti adaupangira malo 28 oimirapo. Umayamba pamalo woyamba uli wochepa ndi wokhota. Ndipo umanka nukula kuchoka pa malo ena nkufika pa malo ena mpaka kukafika pamalo pomwe umakhala wokwanira mkuwala ndi m’maonekedwe ake. Pamenepa mpamalo a 14. Tsono kuchoka apa, umayamba kuchepa pang’onopang’ono ndi kubisika mpaka utafika pa malo a 28 pomwe umabisikiratu wonse. Kayendedwe ka mwezi ndiko kamazindikiritsa anthu kutha kwa mwezi ndi chaka, pomwe kayendedwe ka dzuwa kamazindikiritsa anthu kutha kwa tsiku.
阿拉伯语经注:
لَا ٱلشَّمۡسُ يَنۢبَغِي لَهَآ أَن تُدۡرِكَ ٱلۡقَمَرَ وَلَا ٱلَّيۡلُ سَابِقُ ٱلنَّهَارِۚ وَكُلّٞ فِي فَلَكٖ يَسۡبَحُونَ
Nkosatheka kwa dzuwa kukumana ndi mwezi (njira yake); nawonso usiku sungathe kupambana usana (pakudza nthawi yausana isadathe, koma zimasinthana). Ndipo chilichonse mwa izo chimasambira m’njira yake (imene Allah adachikonzera).
阿拉伯语经注:
وَءَايَةٞ لَّهُمۡ أَنَّا حَمَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ
Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo (chosonyeza madalitso Athu pa iwo). Ndithu tidaukweza mtundu wawo mchombo chodzazidwa (ndi zonse zamoyo).
阿拉伯语经注:
وَخَلَقۡنَا لَهُم مِّن مِّثۡلِهِۦ مَا يَرۡكَبُونَ
Ndipo tidawapangira chonga icho chomwe akuchikwera.[342]
[342] Allah ndi Yemwe adapanga zombo ngakhale kuti zidapangidwa ndi manja a anthu, chifukwa Iye ndi Amene adaphunzitsa anthu kupanga zombozo.
阿拉伯语经注:
وَإِن نَّشَأۡ نُغۡرِقۡهُمۡ فَلَا صَرِيخَ لَهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنقَذُونَ
Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza m’madzi, ndipo sangapezeke wowathandiza, ndiponso sangapulumutsidwe.
阿拉伯语经注:
إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّنَّا وَمَتَٰعًا إِلَىٰ حِينٖ
Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha chifundo Chathu pa iwo ndi kuti asangalale kufikira nthawi yawo (yofera).
阿拉伯语经注:
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّقُواْ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيكُمۡ وَمَا خَلۡفَكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo panu ndi zomwe ziri pambuyo panu kuti muchitiridwe chifundo.” (Iwo akunyoza malangizowo).
阿拉伯语经注:
وَمَا تَأۡتِيهِم مِّنۡ ءَايَةٖ مِّنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِمۡ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ
Ndipo palibe chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo (zosonyeza umodzi Wake ndi kukhoza Kwake) chomwe chidawadzera popanda kuchinyoza (ndi kuchikana).
阿拉伯语经注:
وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ أَنفِقُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنُطۡعِمُ مَن لَّوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ أَطۡعَمَهُۥٓ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (amphawi) zimene Allah wakupatsani.” Osakhulupirira amanena kwa okhulupirira: “Kodi tidyetse yemwe Allah akadafuna akadamdyetsa; (titsutsane ndi cholinga cha Allah)? Ndithu inu simuli kanthu koma muli m’kusokera koonekeratu.”
阿拉伯语经注:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndipo akunena (mwachipongwe kwa okhulupirira): “Kodi lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro), lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”
阿拉伯语经注:
مَا يَنظُرُونَ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ تَأۡخُذُهُمۡ وَهُمۡ يَخِصِّمُونَ
Palibe chimene akuyembekeza, koma ndi mkuwe umodzi womwe udzawamaliza mwadzidzidzi uku iwo akukangana.
阿拉伯语经注:
فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ تَوۡصِيَةٗ وَلَآ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndipo sangathe kuuza wina mawu pa chinthu, ndiponso sangathe kubwerera ku maanja awo.
阿拉伯语经注:
وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَإِذَا هُم مِّنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ يَنسِلُونَ
Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa akufa); iwo adzangozindikira akutuluka m’manda kunka kwa Mbuye wawo uku akuthamanga.
阿拉伯语经注:
قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا مَنۢ بَعَثَنَا مِن مَّرۡقَدِنَاۜۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَصَدَقَ ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Adzati: “Kalanga ife! Kodi ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza): “Izi ndi zimene adalonjeza (Allah), Wachifundo chambiri ndi zimene adanena atumiki moona.”
阿拉伯语经注:
إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَإِذَا هُمۡ جَمِيعٞ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ
Sipadzakhala (china) koma mkuwe umodzi basi; adzangozindikira iwo onse atabweretsedwa patsogolo Pathu.
阿拉伯语经注:
فَٱلۡيَوۡمَ لَا تُظۡلَمُ نَفۡسٞ شَيۡـٔٗا وَلَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Ndipo mzimu uliwonse lero suponderezedwa pa chilichonse. Ndipo mulipidwa pa zokhazo munkachita.”
阿拉伯语经注:
إِنَّ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ ٱلۡيَوۡمَ فِي شُغُلٖ فَٰكِهُونَ
Ndithu anthu aku Jannah (Munda wamtendere) lero akhala wotanganidwa ndi chisangalalo.
阿拉伯语经注:
هُمۡ وَأَزۡوَٰجُهُمۡ فِي ظِلَٰلٍ عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ مُتَّكِـُٔونَ
Iwo ndi akazi awo ali m’mithunzi uku atatsamira mipando (ya mtengo wapamwamba).
阿拉伯语经注:
لَهُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٞ وَلَهُم مَّا يَدَّعُونَ
M’menemo apeza (mtundu uliwonse) wa zipatso ndiponso apeza chilichonse chimene akuchifuna.
阿拉伯语经注:
سَلَٰمٞ قَوۡلٗا مِّن رَّبّٖ رَّحِيمٖ
“Mtendere (pa iwo)!” Limeneli ndi liwu lochokera kwa Mbuye (wawo), Wachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
وَٱمۡتَٰزُواْ ٱلۡيَوۡمَ أَيُّهَا ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Ndipo dzipatuleni lero, inu oipa!
阿拉伯语经注:
۞ أَلَمۡ أَعۡهَدۡ إِلَيۡكُمۡ يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ أَن لَّا تَعۡبُدُواْ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ
Kodi sindidakulangizeni, E inu ana a Adam kuti musapembedze satana? Ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa inu?
阿拉伯语经注:
وَأَنِ ٱعۡبُدُونِيۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
Ndikuti ndipembedzeni Ine? Imeneyi ndi njira yolunjika.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ أَضَلَّ مِنكُمۡ جِبِلّٗا كَثِيرًاۖ أَفَلَمۡ تَكُونُواْ تَعۡقِلُونَ
Ndithu (satana) adasokeretsa anthu ambiri mwa inu. Kodi simumaganizira mwanzeru?
阿拉伯语经注:
هَٰذِهِۦ جَهَنَّمُ ٱلَّتِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ
Iyi ndi Jahena yomwe mumalonjezedwa.
阿拉伯语经注:
ٱصۡلَوۡهَا ٱلۡيَوۡمَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ
Iloweni lero, chifukwa cha kunkana kwanu (Allah).
阿拉伯语经注:
ٱلۡيَوۡمَ نَخۡتِمُ عَلَىٰٓ أَفۡوَٰهِهِمۡ وَتُكَلِّمُنَآ أَيۡدِيهِمۡ وَتَشۡهَدُ أَرۡجُلُهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Lero titseka kukamwa kwawo. Ndipo manja awo atiyankhula ndipo miyendo yawo ichitira umboni pa zomwe amachita.
阿拉伯语经注:
وَلَوۡ نَشَآءُ لَطَمَسۡنَا عَلَىٰٓ أَعۡيُنِهِمۡ فَٱسۡتَبَقُواْ ٱلصِّرَٰطَ فَأَنَّىٰ يُبۡصِرُونَ
Ndipo tikadafuna, tikadafafaniza maso awo; ndipo akadakhala akuthamangira njira; koma akadapenya chotani?
阿拉伯语经注:
وَلَوۡ نَشَآءُ لَمَسَخۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمۡ فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مُضِيّٗا وَلَا يَرۡجِعُونَ
Ndipo tikadafuna, tikadawasintha kukhala ndi maonekedwe a nyama pamalo pawo pomwepo (pamene adali), kotero kuti sakadatha kuyenda (kunka patsogolo) ngakhale kubwerera pambuyo.
阿拉伯语经注:
وَمَن نُّعَمِّرۡهُ نُنَكِّسۡهُ فِي ٱلۡخَلۡقِۚ أَفَلَا يَعۡقِلُونَ
Ndipo amene tikumtalikitsira moyo wake, timam’bwezeranso pambuyo m’kalengedwe kake (ndi kukhala ngati mwana). Kodi bwanji saganizira mwanzeru?
阿拉伯语经注:
وَمَا عَلَّمۡنَٰهُ ٱلشِّعۡرَ وَمَا يَنۢبَغِي لَهُۥٓۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ وَقُرۡءَانٞ مُّبِينٞ
Ndipo sitidamphunzitse (Mtumiki {s.a.w}) ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa iye (kukhala mlakatuli). Qur’an sichina, koma ndichikumbutso ndi buku lomwe likulongosola chilichonse.
阿拉伯语经注:
لِّيُنذِرَ مَن كَانَ حَيّٗا وَيَحِقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ
Kuti liwachenjeze amene ali moyo, ndi kuti litsimikizike liwu (la chilango) pa osakhulupirira.
阿拉伯语经注:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا خَلَقۡنَا لَهُم مِّمَّا عَمِلَتۡ أَيۡدِينَآ أَنۡعَٰمٗا فَهُمۡ لَهَا مَٰلِكُونَ
Kodi saona kuti Ife tawalengera nyama, m’zimene manja Athu akonza, zomwe iwo akuti nzawo.
阿拉伯语经注:
وَذَلَّلۡنَٰهَا لَهُمۡ فَمِنۡهَا رَكُوبُهُمۡ وَمِنۡهَا يَأۡكُلُونَ
Ndi kuti tazichita kukhala zowatumikira? Zina mwa izo amazikwerapo; ndipo zina mwa izo amazidya.
阿拉伯语经注:
وَلَهُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ وَمَشَارِبُۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ
Ndipo m’menemo (m’nyama) muli zowathandiza (zambiri) ndiponso zakumwa. Nanga bwanji sathokoza?
阿拉伯语经注:
وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةٗ لَّعَلَّهُمۡ يُنصَرُونَ
Ndipo adzipangira milungu (yabodza) kusiya Allah kuti athandizidwe nayo.
阿拉伯语经注:
لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَهُمۡ وَهُمۡ لَهُمۡ جُندٞ مُّحۡضَرُونَ
(Koma) siingathe kuwathandiza; ndipo iwo (kwa milunguyo) ndi asilikali amene akonzedwa kulondera (mafanowo ndi kuwatumikira).
阿拉伯语经注:
فَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّا نَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَ
Mawu awo (onyoza Allah ndi okutsutsa iwe) asakudandaulitse. Ndithu Ife tikudziwa zimene akubisa ndi zimene akuzionetsera poyera.
阿拉伯语经注:
أَوَلَمۡ يَرَ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن نُّطۡفَةٖ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٞ مُّبِينٞ
Kodi munthu sazindikira kuti Ife tidamulenga ndi dontho la umuna? Koma iye wakhala wotsutsa woonekera.
阿拉伯语经注:
وَضَرَبَ لَنَا مَثَلٗا وَنَسِيَ خَلۡقَهُۥۖ قَالَ مَن يُحۡيِ ٱلۡعِظَٰمَ وَهِيَ رَمِيمٞ
Ndipo akutiponyera fanizo (lotsutsa kukhoza Kwathu kuukitsa akufa) ndi kuiwala chilengedwe chake (chochokera kumadzi opanda pake). Akunena: “Ndani angaukitse mafupa pomwe ali ofumbwa?”
阿拉伯语经注:
قُلۡ يُحۡيِيهَا ٱلَّذِيٓ أَنشَأَهَآ أَوَّلَ مَرَّةٖۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلۡقٍ عَلِيمٌ
Nena: “Adzawaukitsa Yemwe adawalenga panthawi yoyamba. Ndipo Iye Ngodziwa kalengedwe ka mtundu uliwonse.
阿拉伯语经注:
ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلشَّجَرِ ٱلۡأَخۡضَرِ نَارٗا فَإِذَآ أَنتُم مِّنۡهُ تُوقِدُونَ
Yemwe adakupangirani moto kuchokera mu mtengo wauwisi; kenako inu mumakoleza moto m’menemo.
阿拉伯语经注:
أَوَلَيۡسَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۚ بَلَىٰ وَهُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ
Kodi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka (mukuganiza kuti) siwokhoza kuwalenga (iwo kachiwiri) monga momwe alili? Inde! Iye ndi Mlengi Wamkulu, Wodziwa kwambiri!
阿拉伯语经注:
إِنَّمَآ أَمۡرُهُۥٓ إِذَآ أَرَادَ شَيۡـًٔا أَن يَقُولَ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ
Ndithu machitidwe Ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika (nthawi yomweyo).
阿拉伯语经注:
فَسُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٖ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pa chinthu chilichonse; ndipo kwa Iye (ndiko) mudzabweerera nonse.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 亚斯
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭