《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 嘉斯亚   段:

嘉斯亚

حمٓ
Hâ-Mîm.
阿拉伯语经注:
تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ
Chivumbulutso cha buku (ili) chochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
阿拉伯语经注:
إِنَّ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ لَأٓيَٰتٖ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndithu kuthambo ndi m’nthaka muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa okhulupirira.
阿拉伯语经注:
وَفِي خَلۡقِكُمۡ وَمَا يَبُثُّ مِن دَآبَّةٍ ءَايَٰتٞ لِّقَوۡمٖ يُوقِنُونَ
Ndiponso mkalengedwe kanu ndi zimene wazifalitsa mmenemo, mu zamoyo ndizisonyezo kwa anthu amene akutsimikiza.
阿拉伯语经注:
وَٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مِن رِّزۡقٖ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَا وَتَصۡرِيفِ ٱلرِّيَٰحِ ءَايَٰتٞ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
Ndi kusinthana kwa usana ndi usiku, ndi mvula imene Allah akutsitsa kuchokera kumwamba, akuukitsa nthaka ndi mvulayo, itafa (itauma), ndi kuyendetsa mphepo mosinthasintha; (zonsezi) ndi zisonyezo kwa anthu anzeru.
阿拉伯语经注:
تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱللَّهِ نَتۡلُوهَا عَلَيۡكَ بِٱلۡحَقِّۖ فَبِأَيِّ حَدِيثِۭ بَعۡدَ ٱللَّهِ وَءَايَٰتِهِۦ يُؤۡمِنُونَ
Izi ndi Ayah (ndime) za Allah; tikukuwerengera iwe mwachoonadi. Kodi ndi nkhani yanji adzaikhulupirire atapanda kulabadira nkhani ya Allah ndi Ayah Zake?
阿拉伯语经注:
وَيۡلٞ لِّكُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٖ
Kuonongeka kuli pa aliyense wopeka zinthu, wamachimo ambiri.
阿拉伯语经注:
يَسۡمَعُ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ثُمَّ يُصِرُّ مُسۡتَكۡبِرٗا كَأَن لَّمۡ يَسۡمَعۡهَاۖ فَبَشِّرۡهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٖ
Amene akumva Ayah za Allah zikuwerengedwa kwa iye kenako nkumapitiriza (zochita zake zosalungama) uku akudzikweza ngati kuti sadazimve ayazo; muuze nkhani ya chilango chowawa.
阿拉伯语经注:
وَإِذَا عَلِمَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا شَيۡـًٔا ٱتَّخَذَهَا هُزُوًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٞ مُّهِينٞ
Ndipo akadziwa chinthu chochepa chochokera mma Ayah athu, amachichitira chipongwe; amenewa ndi amene adzakhala ndi chilango chosambula.
阿拉伯语经注:
مِّن وَرَآئِهِمۡ جَهَنَّمُۖ وَلَا يُغۡنِي عَنۡهُم مَّا كَسَبُواْ شَيۡـٔٗا وَلَا مَا ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡلِيَآءَۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٌ
Jahannam ili (kuwayembekezera) kuseri kwawo; ndipo zimene adachita sizidzawathandiza chilichonse, ngakhale atetezi amene adadzipangira kusiya Allah (sadzawathandiza); ndipo adzapeza chilango chachikulu.
阿拉伯语经注:
هَٰذَا هُدٗىۖ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ لَهُمۡ عَذَابٞ مِّن رِّجۡزٍ أَلِيمٌ
Ichi ndi chiongoko; ndipo amene adakanira Ayah za Mbuye wawo, adzakhala ndi chilango chachikulu chochokera mchilango chowawa.
阿拉伯语经注:
۞ ٱللَّهُ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَكُمُ ٱلۡبَحۡرَ لِتَجۡرِيَ ٱلۡفُلۡكُ فِيهِ بِأَمۡرِهِۦ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Allah ndi Amene wakugonjetserani nyanja kuti zombo ziziyenda mmenemo mwa lamulo Lake; ndikuti munke mufunafuna chifundo Chake kuti muthokoze.
阿拉伯语经注:
وَسَخَّرَ لَكُم مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا مِّنۡهُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
Ndipo wakugonjetserani za kumwamba ndi zam’nthaka, zonse zikuchokera kwa Iye. Ndithu mzimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amalingalira.
阿拉伯语经注:
قُل لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَغۡفِرُواْ لِلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ أَيَّامَ ٱللَّهِ لِيَجۡزِيَ قَوۡمَۢا بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Nena kwa amene akhulupirira kuti awakhululukire amene sakuopa masiku a Allah (a chilango; mmasiku amenewo) kuti awalipire anthu pa zomwe amachita (zoipa).
阿拉伯语经注:
مَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَنۡ أَسَآءَ فَعَلَيۡهَاۖ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ تُرۡجَعُونَ
Amene akuchita chabwino akudzichitira yekha ndipo amene akuchita zoipa, zidzakhala paiye mwini. Kenako m’dzabwezedwa kwa Mbuye wanu.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحُكۡمَ وَٱلنُّبُوَّةَ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndithu tidawapatsa ana a Israyeli buku, ulamuliro ndi uneneri; ndiponso tidawapatsa zina mwa zinthu zabwino ndikuwalemekeza pamwamba pa mitundu ina (ya nthawiyo).
阿拉伯语经注:
وَءَاتَيۡنَٰهُم بَيِّنَٰتٖ مِّنَ ٱلۡأَمۡرِۖ فَمَا ٱخۡتَلَفُوٓاْ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُ بَغۡيَۢا بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Ndipo tidawapatsa zisonyezo zoonekera pazinthu zachipembedzo chawo; sadapatukane mpaka pomwe kudawadzera kudziwa, chifukwa chadumbo pakati pawo. Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsemphana.
阿拉伯语经注:
ثُمَّ جَعَلۡنَٰكَ عَلَىٰ شَرِيعَةٖ مِّنَ ٱلۡأَمۡرِ فَٱتَّبِعۡهَا وَلَا تَتَّبِعۡ أَهۡوَآءَ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ
Kenako tidakuika iwe pa malamulo a zinthu za chipembedzo (Chathu). Choncho tsatira malamulo (Athu), ndipo usatsate zilakolako za amene sadziwa (njira yoona).
阿拉伯语经注:
إِنَّهُمۡ لَن يُغۡنُواْ عَنكَ مِنَ ٱللَّهِ شَيۡـٔٗاۚ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ بَعۡضُهُمۡ أَوۡلِيَآءُ بَعۡضٖۖ وَٱللَّهُ وَلِيُّ ٱلۡمُتَّقِينَ
Ndithu iwo (amene akutsata njira zonama) sangakuthandize chilichonse kwa Allah; ndithu achinyengo ena a iwo amatetezana wina ndi nzake; koma Allah ndi Mtetezi wa oopa (Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa).
阿拉伯语经注:
هَٰذَا بَصَٰٓئِرُ لِلنَّاسِ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّقَوۡمٖ يُوقِنُونَ
Iyi (Qur’an imene yavumbulutsidwa kwa iwe), ndizisonyezo kwa anthu chiongoko ndi chifundo kwa anthu omwe akutsimikiza (kuti lilipo tsiku la chiweruziro).
阿拉伯语经注:
أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ ٱجۡتَرَحُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ أَن نَّجۡعَلَهُمۡ كَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَوَآءٗ مَّحۡيَاهُمۡ وَمَمَاتُهُمۡۚ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ
Kodi amene adadzichitira zoipa akuganiza kuti tingawachite monga omwe adakhulupirira ndi kuchita zabwino kuti afanane pa moyo wawo ndi pa imfa yawo? Ndi kuweruza koipa kumene iwo akuweruza.
阿拉伯语经注:
وَخَلَقَ ٱللَّهُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّ وَلِتُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Ndipo Allah adalenga thambo ndi nthaka moona ndi kuti mzimu uliwonse ulipidwe zimene udadzichitira, (zoipa kapena zabwino) ndipo iwo sadzaponderezedwa.
阿拉伯语经注:
أَفَرَءَيۡتَ مَنِ ٱتَّخَذَ إِلَٰهَهُۥ هَوَىٰهُ وَأَضَلَّهُ ٱللَّهُ عَلَىٰ عِلۡمٖ وَخَتَمَ عَلَىٰ سَمۡعِهِۦ وَقَلۡبِهِۦ وَجَعَلَ عَلَىٰ بَصَرِهِۦ غِشَٰوَةٗ فَمَن يَهۡدِيهِ مِنۢ بَعۡدِ ٱللَّهِۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
Kodi wamuona amene wachichita chilakolako chake kukhala mulungu wake wompembedza? Ndipo Allah wamlekelera kuti asokere, kupyolera mkudziwa Kwake; ndipo wamdinda (chidindo) mmakutu mwake ndi mu mtima mwake ndi kumuika chivindikiro mmaso mwake. Choncho ndani angamuongole pambuyo pa Allah? Kodi simukumbukira?
阿拉伯语经注:
وَقَالُواْ مَا هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا ٱلدُّنۡيَا نَمُوتُ وَنَحۡيَا وَمَا يُهۡلِكُنَآ إِلَّا ٱلدَّهۡرُۚ وَمَا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَظُنُّونَ
Ndipo (okanira kuuka ku imfa) adanena: “Kulibe (moyo wina) koma moyo wathu womwewu wa padziko lapansi; timafa ndi kukhala ndi moyo; palibe chikutiononga koma nthawi basi.” Koma iwo alibe kudziwa pa zimene akunenazo; akungoganizira chabe.
阿拉伯语经注:
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٖ مَّا كَانَ حُجَّتَهُمۡ إِلَّآ أَن قَالُواْ ٱئۡتُواْ بِـَٔابَآئِنَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndipo Ayah Zathu zikawerengcdwa kwa iwo zolongosola chilichonse momveka, alibe mtsutso wina koma kunena kuti: “Tibweretsereni makolo Athu (aukitseni akhale ndi moyo) ngati inu muli owona!”
阿拉伯语经注:
قُلِ ٱللَّهُ يُحۡيِيكُمۡ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يَجۡمَعُكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Nena (kwa iwo iwe Mtumiki): “Allah amakupatsani moyo. Kenako amakupatsani imfa. Kenako adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko.” Koma anthu ambiri sakudziwa.
阿拉伯语经注:
وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يَوۡمَئِذٖ يَخۡسَرُ ٱلۡمُبۡطِلُونَ
Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah, ndipo tsiku limene Qiyâma idzachitika, (anthu) ogwirizana ndi zonama adzaonongeka patsikulo.
阿拉伯语经注:
وَتَرَىٰ كُلَّ أُمَّةٖ جَاثِيَةٗۚ كُلُّ أُمَّةٖ تُدۡعَىٰٓ إِلَىٰ كِتَٰبِهَا ٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَوۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo udzaliona gulu lililonse litagwada (uku nkhope zili zyoli); gulu lililonse lidzaitanidwa ku kaundula wake (kukamuwerenga): “Lero mulipidwa zimene mudali kuchita!”
阿拉伯语经注:
هَٰذَا كِتَٰبُنَا يَنطِقُ عَلَيۡكُم بِٱلۡحَقِّۚ إِنَّا كُنَّا نَسۡتَنسِخُ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Uyu kaundula Wathu akunena zoona za inu; ndithu Ife tidali kulemba zimene mudali kuchita.”
阿拉伯语经注:
فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَيُدۡخِلُهُمۡ رَبُّهُمۡ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡمُبِينُ
Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, Mbuye wawo adzawalowetsa ku chifundo Chake; kumeneko ndiko kupambana koonekera.
阿拉伯语经注:
وَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَفَلَمۡ تَكُنۡ ءَايَٰتِي تُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فَٱسۡتَكۡبَرۡتُمۡ وَكُنتُمۡ قَوۡمٗا مُّجۡرِمِينَ
Ndipo amene adakanira, (adzauzidwa kuti): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu? Koma inu mudadzikweza; ndipo mudali anthu oipa.”
阿拉伯语经注:
وَإِذَا قِيلَ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَٱلسَّاعَةُ لَا رَيۡبَ فِيهَا قُلۡتُم مَّا نَدۡرِي مَا ٱلسَّاعَةُ إِن نَّظُنُّ إِلَّا ظَنّٗا وَمَا نَحۡنُ بِمُسۡتَيۡقِنِينَ
Ndipo kukanenedwa kuti lonjezo la Allah ndiloona, ndikuti Qiyâma ilibe chikaiko, mudali kunena: “Sitikudziwa Qiyâma kuti nchiyani; tikungoganizira chabe, ndipo tilibe chitsimikizo (cha Kiyamayo).”
阿拉伯语经注:
وَبَدَا لَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا عَمِلُواْ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Choncho, kuipa kwa zimene adachita kudzawaonekera, ndipo zidzawazinga zimene ankazichitira chipongwe.
阿拉伯语经注:
وَقِيلَ ٱلۡيَوۡمَ نَنسَىٰكُمۡ كَمَا نَسِيتُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَا وَمَأۡوَىٰكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن نَّٰصِرِينَ
Kudzanenedwanso kwa iwowa: “Lero tikuiwalani (pokusiyani mchilango) monga momwe inu mudaiwalira kukumana ndi tsiku lanu ili. Ndipo malo anu ndi ku Moto, ndipo mulibe wokupulumutsani.”
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكُم بِأَنَّكُمُ ٱتَّخَذۡتُمۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ هُزُوٗا وَغَرَّتۡكُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ فَٱلۡيَوۡمَ لَا يُخۡرَجُونَ مِنۡهَا وَلَا هُمۡ يُسۡتَعۡتَبُونَ
“Zimenezi nchifukwa chakuti inu mudazichitira chipongwe Ayah za Allah, ndipo moyo wa pa dziko udakunyengani.” Choncho lero satulutsidwa mmenemo ndipo madandaulo awo savomerezedwa.
阿拉伯语经注:
فَلِلَّهِ ٱلۡحَمۡدُ رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَرَبِّ ٱلۡأَرۡضِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Tero kutamandidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wakumwamba ndi Mbuye wa pa dziko lapansi; Mbuye wazolengedwa.
阿拉伯语经注:
وَلَهُ ٱلۡكِبۡرِيَآءُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Ndipo ukulu ndi Wake, kumwamba ndi pansi; ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya!
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 嘉斯亚
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭