Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 穆罕默德   段:

Muhammad

ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ أَضَلَّ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Amene adam’kana (Allah ndi Mthenga Wake) ndi kutsekereza anthu kuyenda panjira ya Allah (powaletsa kulowa m’Chisilamu), Allah waononga zonse zabwino zimene adachita.
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَءَامَنُواْ بِمَا نُزِّلَ عَلَىٰ مُحَمَّدٖ وَهُوَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّهِمۡ كَفَّرَ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡ وَأَصۡلَحَ بَالَهُمۡ
Ndipo amene akhulupirira nkumachita zabwino, nkuzikhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa Muhammad (s.a.w), zimene zili zoona zochokera kwa Mbuye wawo, wawafafanizira zolakwa zawo, ndipo awakonzera chikhalidwe chawo (patsiku lachimaliziro ndi padziko lapansi).
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱتَّبَعُواْ ٱلۡبَٰطِلَ وَأَنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّبَعُواْ ٱلۡحَقَّ مِن رَّبِّهِمۡۚ كَذَٰلِكَ يَضۡرِبُ ٱللَّهُ لِلنَّاسِ أَمۡثَٰلَهُمۡ
Zimenezi nchifukwa chakuti amene sadakhulupirire adatsata chonama, ndipo amene adakhulupirira adatsatira choonadi chochokera kwa Mbuye wawo. M’menemu ndim’mene Allah akuperekera kwa anthu mafanizo awo (kuti alingalire ndi kupeza phunziro).
阿拉伯语经注:
فَإِذَا لَقِيتُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَضَرۡبَ ٱلرِّقَابِ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَثۡخَنتُمُوهُمۡ فَشُدُّواْ ٱلۡوَثَاقَ فَإِمَّا مَنَّۢا بَعۡدُ وَإِمَّا فِدَآءً حَتَّىٰ تَضَعَ ٱلۡحَرۡبُ أَوۡزَارَهَاۚ ذَٰلِكَۖ وَلَوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ لَٱنتَصَرَ مِنۡهُمۡ وَلَٰكِن لِّيَبۡلُوَاْ بَعۡضَكُم بِبَعۡضٖۗ وَٱلَّذِينَ قُتِلُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ فَلَن يُضِلَّ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Ndipo mukakumana nawo pankhondo amene sanakhulupirire amenyeni makosi awo (aduleni), mpaka mwafooketse pochuluka ophedwa mwa iwo; kenako amangeni ndi zingwe (otsalawo). Ngati mutafuna kuwamasula popanda dipo kapena kuti apereke dipo, (zili kwa inu). Kufikira nkhondo itatha. Limenelo ndi lamulo la Allah. Ndithu Allah akadafuna akadathana nawo Iye mwini powaononga onse psiti; koma (wakulamulani kuti muchite nkhondo) ncholinga choti awayese mayeso ena a inu pa ena (okhulupirira pa okanitsitsawo). Ndipo amene aphedwa panjira ya Allah, ntchito yawo sadzaipititsa pachabe.
阿拉伯语经注:
سَيَهۡدِيهِمۡ وَيُصۡلِحُ بَالَهُمۡ
Awaongolera (ku zimene zingawapindulitse pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro) ndi kuwakonzera zinthu zawo ndi chikhalidwe chawo.
阿拉伯语经注:
وَيُدۡخِلُهُمُ ٱلۡجَنَّةَ عَرَّفَهَا لَهُمۡ
Ndi kukawalowetsa ku Munda wamtendere umene adawadziwitsa.
阿拉伯语经注:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِن تَنصُرُواْ ٱللَّهَ يَنصُرۡكُمۡ وَيُثَبِّتۡ أَقۡدَامَكُمۡ
E inu amene mwakhulupirira! Ngati muteteza chipembedzo cha Allah, (Iye) adzakutetezani (kwa adani anu) ndi kulimbikitsa mapazi anu (pa nkhondo).
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَتَعۡسٗا لَّهُمۡ وَأَضَلَّ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Koma amene akana (Allah ndi Ayah Zake) kuwonongeka nkwawo ndipo awaonongera zochita zawo.
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَرِهُواْ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ فَأَحۡبَطَ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo azida zomwe Allah adavumbulutsa (monga Qur’an ndi malamulo ake;) choncho waziononga zochita zawo.
阿拉伯语经注:
۞ أَفَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ دَمَّرَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡۖ وَلِلۡكَٰفِرِينَ أَمۡثَٰلُهَا
Kodi sadayendeyende padziko nkuona kuti adali bwanji mapeto a amene adawatsogolera (monga Âdi ndi Samudi, ndi anthu a Luti ndi ena otero)? Allah adawaononga psiti, ndipo chilango ngati chimenecho chidzakhalanso kwa osakhulupirira.
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ مَوۡلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَأَنَّ ٱلۡكَٰفِرِينَ لَا مَوۡلَىٰ لَهُمۡ
Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, koma osakhulupirira alibe mtetezi.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 穆罕默德
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭