ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الصافات
آية:
 

الصافات

وَٱلصَّـٰٓفَّـٰتِ صَفّٗا
“Ndikulumbira (angelo) amene amandanda m’mizere yondondozana, (popembedza ndi kugonjera Mbuye wawo).
التفاسير العربية:
فَٱلزَّـٰجِرَٰتِ زَجۡرٗا
“Ndi omwe amaletsa zoipa.
التفاسير العربية:
فَٱلتَّـٰلِيَٰتِ ذِكۡرًا
“Ndi omwe amalalika ulaliki (wa Allah ndi kumtamanda mochulukira).
التفاسير العربية:
إِنَّ إِلَٰهَكُمۡ لَوَٰحِدٞ
“Ndithu Mulungu wanu ndi mmodzi basi.
التفاسير العربية:
رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَرَبُّ ٱلۡمَشَٰرِقِ
“Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; ndiponso Mbuye wa kuvuma konse.
التفاسير العربية:
إِنَّا زَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِزِينَةٍ ٱلۡكَوَاكِبِ
“Ndithu tidalikongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi chokongoletsa cha nyenyezi (zowala).
التفاسير العربية:
وَحِفۡظٗا مِّن كُلِّ شَيۡطَٰنٖ مَّارِدٖ
“Ndi kuti lisungidwe ku satana aliyense wogalukira (lamulo la Allah).
التفاسير العربية:
لَّا يَسَّمَّعُونَ إِلَى ٱلۡمَلَإِ ٱلۡأَعۡلَىٰ وَيُقۡذَفُونَ مِن كُلِّ جَانِبٖ
“Kuti asamvere (zomwe zikunenedwa ndi) gulu lolemekezeka (la angelo). Ndipo akugendedwa (ndi kupirikitsidwa) mbali zonse.
التفاسير العربية:
دُحُورٗاۖ وَلَهُمۡ عَذَابٞ وَاصِبٌ
“Kuthamangitsidwa mwamphamvu; ndipo chilango chonkerankera patsogolo chili pa iwo.
التفاسير العربية:
إِلَّا مَنۡ خَطِفَ ٱلۡخَطۡفَةَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٞ ثَاقِبٞ
“Kupatula amene wazembetsa mawu (akumwamba), ndipo chikumtsatira iye chenje cha moto chowala kwambiri.
التفاسير العربية:
فَٱسۡتَفۡتِهِمۡ أَهُمۡ أَشَدُّ خَلۡقًا أَم مَّنۡ خَلَقۡنَآۚ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّن طِينٖ لَّازِبِۭ
“Tawafunsa (otsutsa zouka ku imfa): “Kodi iwo ngovuta kuwalenga kuposa zimene tidalenga, (monga: thambo, nthaka, nyenyezi ndi zina zotere)?” Ndithu Ife tidawalenga kuchokera ku dongo lonyata.
التفاسير العربية:
بَلۡ عَجِبۡتَ وَيَسۡخَرُونَ
“Koma iwe (Mneneri) ukudabwa (za kutsutsa kwawo kuuka ku imfa pomwe zisonyezo zilipo zambirimbiri), ndipo akukuchitira chipongwe (kudabwa kwako).
التفاسير العربية:
وَإِذَا ذُكِّرُواْ لَا يَذۡكُرُونَ
“Ndipo akalalikiridwa, salalikirika.
التفاسير العربية:
وَإِذَا رَأَوۡاْ ءَايَةٗ يَسۡتَسۡخِرُونَ
“Ndipo akachiona chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah,) amachichitira chipongwe.
التفاسير العربية:
وَقَالُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّبِينٌ
“Ndipo osakhulupirira amanena: “Palibe chilipo apa, koma ndi matsenga woonekera poyera.”
التفاسير العربية:
أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ
““Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, tidzatulutsidwanso (kuchokera m’manda tili amoyo)?”
التفاسير العربية:
أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ
““Pamodzi ndi makolo athu akale?”
التفاسير العربية:
قُلۡ نَعَمۡ وَأَنتُمۡ دَٰخِرُونَ
“Nena (iwe Mneneri): “Inde (mudzaukitsidwa inu pamodzi ndi makolo anu) uku inu muli onyozeka.”
التفاسير العربية:
فَإِنَّمَا هِيَ زَجۡرَةٞ وَٰحِدَةٞ فَإِذَا هُمۡ يَنظُرُونَ
“Ndithu (kuukako) ndimkuwe umodzi adzangodzidzimuka ali moyo, akuyang’ana.
التفاسير العربية:
وَقَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا هَٰذَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ
“Ndipo adzanena (okanawo): “Kalanga ife! Kuonongeka nkwathu! Ili nditsiku lija lamalipiro!”
التفاسير العربية:
هَٰذَا يَوۡمُ ٱلۡفَصۡلِ ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ
“(Adzawauza): “Ili nditsiku la chiweruziro lomwe mumalitsutsa lija.”
التفاسير العربية:
۞ٱحۡشُرُواْ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ وَأَزۡوَٰجَهُمۡ وَمَا كَانُواْ يَعۡبُدُونَ
“(Kudzanenedwa kwa angelo): “Asonkhanitseni amene adali osalungama pamodzi ndi akazi awo (okana Allah) ndi milungu yawo imene amaipembedza,”
التفاسير العربية:
مِن دُونِ ٱللَّهِ فَٱهۡدُوهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡجَحِيمِ
““Kusiya Allah, ndipo asonyezeni njira ya ku Jahannam.”
التفاسير العربية:
وَقِفُوهُمۡۖ إِنَّهُم مَّسۡـُٔولُونَ
““Koma aimikeni pano chifukwa iwo afunsidwa (za chikhulupiliro chawo ndi zochita zawo):”
التفاسير العربية:

مَا لَكُمۡ لَا تَنَاصَرُونَ
““Kodi nchifukwa ninji inu (opembedza mafano) simukupulumutsana (monga mumanenera pa dziko lapansi kuti mudzapulumutsana)?”
التفاسير العربية:
بَلۡ هُمُ ٱلۡيَوۡمَ مُسۡتَسۡلِمُونَ
“Koma iwo pa tsikulo adzagonjera ndi kudzipereka (ku lamulo la Allah).
التفاسير العربية:
وَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ
“Ndipo adzatembenukirana ndi kuyamba kufunsana (ndi kudzudzulana).
التفاسير العربية:
قَالُوٓاْ إِنَّكُمۡ كُنتُمۡ تَأۡتُونَنَا عَنِ ٱلۡيَمِينِ
“Ndipo (ofooka) adzanena (kwa odzikweza): “Inu mumatidzera kumbali komwe timakuganizira kuti nkwabwino (ndi kutichotsako kunka nafe ku njira yopotoka).
التفاسير العربية:
قَالُواْ بَل لَّمۡ تَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ
“(Odzikweza) adzayankha: “Koma simudali okhulupirira.”
التفاسير العربية:
وَمَا كَانَ لَنَا عَلَيۡكُم مِّن سُلۡطَٰنِۭۖ بَلۡ كُنتُمۡ قَوۡمٗا طَٰغِينَ
““Ndipo tidalibe nyonga zokuponderezerani inu, koma mudali anthu opyola malire (ndi kutuluka ku choonadi cha Allah).”
التفاسير العربية:
فَحَقَّ عَلَيۡنَا قَوۡلُ رَبِّنَآۖ إِنَّا لَذَآئِقُونَ
““Choncho mawu a Mbuye wathu (onena za chilango) atsimikizika pa ife; ndithu ife tichilawa (chilango).”
التفاسير العربية:
فَأَغۡوَيۡنَٰكُمۡ إِنَّا كُنَّا غَٰوِينَ
““Tidakusokeretsani; nafenso tidali osokera. (Choncho musatidzudzule).”
التفاسير العربية:
فَإِنَّهُمۡ يَوۡمَئِذٖ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ
“Ndithu iwo akathandizana chilango tsiku limenelo (la chiweruziro).
التفاسير العربية:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَفۡعَلُ بِٱلۡمُجۡرِمِينَ
“Ndithu (chilango chonga chimenecho) ndimomwe timawachitira olakwira (Allah).
التفاسير العربية:
إِنَّهُمۡ كَانُوٓاْ إِذَا قِيلَ لَهُمۡ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱللَّهُ يَسۡتَكۡبِرُونَ
“Ndithu iwo ankati akauzidwa kuti palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Allah ankadzitukumula.
التفاسير العربية:
وَيَقُولُونَ أَئِنَّا لَتَارِكُوٓاْ ءَالِهَتِنَا لِشَاعِرٖ مَّجۡنُونِۭ
“Ndipo ankanena: “Kodi ife tisiye kupembedza milungu yathu chifukwa cha zonena za mlakatuli, wopenga?”
التفاسير العربية:
بَلۡ جَآءَ بِٱلۡحَقِّ وَصَدَّقَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Iyayi koma adawadzera ndi choonadi (Mthenga wawo Muhammad yemwe siwamisala kapena wolakatula zopeka) ndipo adawatsimikizira za atumiki.
التفاسير العربية:
إِنَّكُمۡ لَذَآئِقُواْ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَلِيمِ
“Ndithu inu (osakhulupirira) mudzalawa chilango chowawa.
التفاسير العربية:
وَمَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Ndipo simudzalipidwa kupatula zokhazo zimene mumachita.
التفاسير العربية:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Kupatula akapolo a Allah oyeretsedwa.
التفاسير العربية:
أُوْلَـٰٓئِكَ لَهُمۡ رِزۡقٞ مَّعۡلُومٞ
“Kwa iwo kuli zopatsidwa zodziwika (ndi Mbuye wawo Allah),
التفاسير العربية:
فَوَٰكِهُ وَهُم مُّكۡرَمُونَ
“Zipatso (zamtundu uliwonse); ndipo iwo adzalandira ulemu (waukulu),
التفاسير العربية:
فِي جَنَّـٰتِ ٱلنَّعِيمِ
“M’minda ya mtendere.
التفاسير العربية:
عَلَىٰ سُرُرٖ مُّتَقَٰبِلِينَ
“Adzakhala pa makama (a mtengo wapatali) uku akuyang’anizana.
التفاسير العربية:
يُطَافُ عَلَيۡهِم بِكَأۡسٖ مِّن مَّعِينِۭ
“Uku zikuwazungulira zikho zodzazidwa ndi zakumwa zochokera m’kasupe woyenda nthawi zonse.
التفاسير العربية:
بَيۡضَآءَ لَذَّةٖ لِّلشَّـٰرِبِينَ
“Woyera, wokoma kwa akumwa (zakumwazo).
التفاسير العربية:
لَا فِيهَا غَوۡلٞ وَلَا هُمۡ عَنۡهَا يُنزَفُونَ
“(M’zakumwazo) mulibe zopweteketsa mutu (kwa ozimwa) ndiponso iwo sadzaledzera nazo.
التفاسير العربية:
وَعِندَهُمۡ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ عِينٞ
“Ndipo kwa iwo kudzakhala akazi oyang’ana iwo okha, ophanuka maso (okongola).
التفاسير العربية:
كَأَنَّهُنَّ بَيۡضٞ مَّكۡنُونٞ
“Onga ngati dzira (la nthiwatiwa) losungidwa (m’mapiko).
التفاسير العربية:
فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ
“Ndipo adzayang’anizana ndi kuyamba kufunsana (pakati pawo.)
التفاسير العربية:
قَالَ قَآئِلٞ مِّنۡهُمۡ إِنِّي كَانَ لِي قَرِينٞ
“Adzanena wonena mmodzi wa iwo: “Ine ndidali ndi mnzanga (wopembedza mafano amene amatsutsana nane za chipembedzo ndi zophunzitsa za Qur’an yolemekezeka).”
التفاسير العربية:

يَقُولُ أَءِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُصَدِّقِينَ
“Yemwe amandiuza: “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ovomereza?”
التفاسير العربية:
أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَدِينُونَ
““Zakuti tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, (tidzaukanso) ndi kulandira malipiro (pa zochita zathu)?”
التفاسير العربية:
قَالَ هَلۡ أَنتُم مُّطَّلِعُونَ
“(Wokhulupirira) adzanena (kwa anzake: “Inu anthu a kumtendere) kodi simungasuzumire (nane ku moto kuti timuone)?”
التفاسير العربية:
فَٱطَّلَعَ فَرَءَاهُ فِي سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ
“Choncho adzayang’ana ndipo adzamuona ali mkatikati mwa moto.
التفاسير العربية:
قَالَ تَٱللَّهِ إِن كِدتَّ لَتُرۡدِينِ
“Adzanena: “Ndikulumbilira Allah! Udatsala pang’ono kuti undiononge (ndikadakuvomera paja pa dziko lapansi).”
التفاسير العربية:
وَلَوۡلَا نِعۡمَةُ رَبِّي لَكُنتُ مِنَ ٱلۡمُحۡضَرِينَ
““Ndipo pakadapanda chisomo cha Mbuye wanga, ndikadakhala mmodzi mwa opezeka ku Moto.”
التفاسير العربية:
أَفَمَا نَحۡنُ بِمَيِّتِينَ
““Kodi zili choncho kuti sitidzafanso (tizingosangalala m’Munda wamtendere).”
التفاسير العربية:
إِلَّا مَوۡتَتَنَا ٱلۡأُولَىٰ وَمَا نَحۡنُ بِمُعَذَّبِينَ
““Kupatula imfa yathu yoyamba ija, ndi kutinso ife sitilangidwa?”
التفاسير العربية:
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
“Ndithu izi (zimene Allah waika m’Munda wamtendere) ndiko kupambana kwakukulu.
التفاسير العربية:
لِمِثۡلِ هَٰذَا فَلۡيَعۡمَلِ ٱلۡعَٰمِلُونَ
“(Pofuna kupeza) zonga zimenezi ogwira ntchito agwire.
التفاسير العربية:
أَذَٰلِكَ خَيۡرٞ نُّزُلًا أَمۡ شَجَرَةُ ٱلزَّقُّومِ
“Kodi zimenezo ndilo phwando labwino kapena mtengo wa Zaqqum (wowawa kwambiri womwe anthu a ku Moto azikadya)?
التفاسير العربية:
إِنَّا جَعَلۡنَٰهَا فِتۡنَةٗ لِّلظَّـٰلِمِينَ
“Ndithu Ife taupanga (mtengo umenewu) kukhala mayeso ndi chilango cha anthu ochimwa (podzichitira okha chinyengo ndi kupembedza mafano.)
التفاسير العربية:
إِنَّهَا شَجَرَةٞ تَخۡرُجُ فِيٓ أَصۡلِ ٱلۡجَحِيمِ
“Umenewu ndimtengo omwe umatuluka pakatikati pa Jahannam (adaulenga kuchokera ku Moto).
التفاسير العربية:
طَلۡعُهَا كَأَنَّهُۥ رُءُوسُ ٱلشَّيَٰطِينِ
“Zipatso zake (nzoipa) ngati mitu ya asatana.
التفاسير العربية:
فَإِنَّهُمۡ لَأٓكِلُونَ مِنۡهَا فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ
“Ndithu iwo akadya mtengowo ndi kudzaza mimba zawo ndi zipatso zake (pakuti sakapeza chakudya china kupatula zipatso za mtengowo).
التفاسير العربية:
ثُمَّ إِنَّ لَهُمۡ عَلَيۡهَا لَشَوۡبٗا مِّنۡ حَمِيمٖ
“Kenako, ndithu kuwawa kwa mtengowo kosakanikirana ndi madzi owira kuzakhala pa iwo.
التفاسير العربية:
ثُمَّ إِنَّ مَرۡجِعَهُمۡ لَإِلَى ٱلۡجَحِيمِ
“Kenako ndithu kobwerera kwawo ndi ku Jahannam.
التفاسير العربية:
إِنَّهُمۡ أَلۡفَوۡاْ ءَابَآءَهُمۡ ضَآلِّينَ
“Ndithu iwo adapeza makolo awo ali osokera.
التفاسير العربية:
فَهُمۡ عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِمۡ يُهۡرَعُونَ
“Ndipo iwonso adatsata mapazi awo mothamanga.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ ضَلَّ قَبۡلَهُمۡ أَكۡثَرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Ndipo, ndithu akale ambiri adasokera patsogolo pawo.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا فِيهِم مُّنذِرِينَ
“Ndipo, ndithu tidatuma achenjezi kwa iwo.
التفاسير العربية:
فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ
“Tapenya momwe adalili mapeto a omwe adachenjezedwa.
التفاسير العربية:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Kupatula akapolo a Allah, oyeretsedwa (iwo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere).
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ نَادَىٰنَا نُوحٞ فَلَنِعۡمَ ٱلۡمُجِيبُونَ
“Ndithu Nuh adatiitana, (ndipo tidamuyankha mayankho abwino), taonani kukhala bwino Ife Oyankha.
التفاسير العربية:
وَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ
“Ndipo tidampulumutsa iye ndi anthu ake ku vuto lalikulu.
التفاسير العربية:

وَجَعَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُۥ هُمُ ٱلۡبَاقِينَ
“Ndipo tidazichita zidzukulu zake kukhala zotsala (pa dziko, oipa ataonongeka).
التفاسير العربية:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
“Ndipo tidamsiira mbiri yabwino kwa mibadwo yodza pambuyo pake.
التفاسير العربية:
سَلَٰمٌ عَلَىٰ نُوحٖ فِي ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Mtendere ukhale pa Nuh pa zolengedwa zonse.
التفاسير العربية:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
“Ndithu umu ndimomwe Ife tilipirira ochita zabwino.
التفاسير العربية:
إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
“Ndithu iye ndi mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira.
التفاسير العربية:
ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ
“Kenako tidawamiza enawo.
التفاسير العربية:
۞وَإِنَّ مِن شِيعَتِهِۦ لَإِبۡرَٰهِيمَ
“Ndipo ndithu m’gulu lake (la Nuh) muli Ibrahim.
التفاسير العربية:
إِذۡ جَآءَ رَبَّهُۥ بِقَلۡبٖ سَلِيمٍ
“Kumbuka pamene adadza kwa Mbuye wake ndi mtima wabwino (wogonjera malamulo).
التفاسير العربية:
إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَاذَا تَعۡبُدُونَ
“Pomwe adanena kwa bambo wake ndi anthu ake: “Mukupembedza chiyani?”
التفاسير العربية:
أَئِفۡكًا ءَالِهَةٗ دُونَ ٱللَّهِ تُرِيدُونَ
““Ha! Milungu yopeka kusiya Allah, ndi imene mukuifuna?”
التفاسير العربية:
فَمَا ظَنُّكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
““Kodi maganizo anu ngotani pa Mbuye wa zolengedwa zonse?”
التفاسير العربية:
فَنَظَرَ نَظۡرَةٗ فِي ٱلنُّجُومِ
“Ndipo adayang’ana nyenyezi mozama.
التفاسير العربية:
فَقَالَ إِنِّي سَقِيمٞ
“Ndipo adanena: “Ine ndine wodwala!”
التفاسير العربية:
فَتَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ مُدۡبِرِينَ
“Choncho iwo adatembenuka ndi kumsiya.
التفاسير العربية:
فَرَاغَ إِلَىٰٓ ءَالِهَتِهِمۡ فَقَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ
“(Ibrahim) adapita mozemba ku mafano awo, ndipo adawauza (mwachipongwe:) “Bwanji simukudya (chakudya chomwe chaikidwa patsogolo panupo)?”
التفاسير العربية:
مَا لَكُمۡ لَا تَنطِقُونَ
““Bwanji simukuyankhula?”
التفاسير العربية:
فَرَاغَ عَلَيۡهِمۡ ضَرۡبَۢا بِٱلۡيَمِينِ
“Atatero adawatembenukira ndi kuwamenya (mwamphamvu) ndi dzanja lamanja.
التفاسير العربية:
فَأَقۡبَلُوٓاْ إِلَيۡهِ يَزِفُّونَ
“(Pamene adamva eni mafanowo) adadza kwa iye akuthamanga.
التفاسير العربية:
قَالَ أَتَعۡبُدُونَ مَا تَنۡحِتُونَ
“Anati: “Kodi mukupembedza (miyala) imene mwasema?”
التفاسير العربية:
وَٱللَّهُ خَلَقَكُمۡ وَمَا تَعۡمَلُونَ
““Chikhalirecho Allah ndiye adakulengani ndi zimene mukuchita!”
التفاسير العربية:
قَالُواْ ٱبۡنُواْ لَهُۥ بُنۡيَٰنٗا فَأَلۡقُوهُ فِي ٱلۡجَحِيمِ
“Iwo adati: “Mmangireni ng’anjo, ndipo mponyeni m’motowo.”
التفاسير العربية:
فَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدٗا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَسۡفَلِينَ
“Adafuna kumchita chiwembu (kuti amuphe ndi moto), koma tidawachita kukhala onyozeka.
التفاسير العربية:
وَقَالَ إِنِّي ذَاهِبٌ إِلَىٰ رَبِّي سَيَهۡدِينِ
“Ndipo (Ibrahim) adati: “Ndithu ine ndikupita kwa Mbuye wanga, Iye andiongolera.”
التفاسير العربية:
رَبِّ هَبۡ لِي مِنَ ٱلصَّـٰلِحِينَ
““E Mbuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale (mmodzi) mwa olungama!”
التفاسير العربية:
فَبَشَّرۡنَٰهُ بِغُلَٰمٍ حَلِيمٖ
“Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (mwanayo ndi Ismaila).
التفاسير العربية:
فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ ٱلسَّعۡيَ قَالَ يَٰبُنَيَّ إِنِّيٓ أَرَىٰ فِي ٱلۡمَنَامِ أَنِّيٓ أَذۡبَحُكَ فَٱنظُرۡ مَاذَا تَرَىٰۚ قَالَ يَـٰٓأَبَتِ ٱفۡعَلۡ مَا تُؤۡمَرُۖ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلصَّـٰبِرِينَ
“Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana nsinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (owona ochokera kwa Allah omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Allah). Nanga ukuti bwanji?” (Mwana wabwino) adanena: “Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamulidwa. Ngati Allah afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira.”
التفاسير العربية:

فَلَمَّآ أَسۡلَمَا وَتَلَّهُۥ لِلۡجَبِينِ
“Pamene adagonjera onse awiri (chofuna cha Allah), ndipo (Ibrahim) adam’goneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha).
التفاسير العربية:
وَنَٰدَيۡنَٰهُ أَن يَـٰٓإِبۡرَٰهِيمُ
“Ndipo tidamuitana: “E iwe Ibrahim!”
التفاسير العربية:
قَدۡ صَدَّقۡتَ ٱلرُّءۡيَآۚ إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
““Ndithu wavomereza maloto! (Choncho usamuphe mwana wakoyo).” Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino.
التفاسير العربية:
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡبَلَـٰٓؤُاْ ٱلۡمُبِينُ
“Ndithu amenewa ndimayeso oonekera.
التفاسير العربية:
وَفَدَيۡنَٰهُ بِذِبۡحٍ عَظِيمٖ
“Ndipo tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apereke nsembe).
التفاسير العربية:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
“Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).
التفاسير العربية:
سَلَٰمٌ عَلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ
“Mtendere ukhale pa Ibrahim!
التفاسير العربية:
كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
“M’menemo ndi mornwe timawalipirira ochita zabwino.
التفاسير العربية:
إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
“Ndithu iye adali mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira.
التفاسير العربية:
وَبَشَّرۡنَٰهُ بِإِسۡحَٰقَ نَبِيّٗا مِّنَ ٱلصَّـٰلِحِينَ
“Ndiponso tidamuuza nkhani yabwino (yoti akhala ndi mwana wotchedwa) Isihaqa; mneneri; wam’gulu la olungama.
التفاسير العربية:
وَبَٰرَكۡنَا عَلَيۡهِ وَعَلَىٰٓ إِسۡحَٰقَۚ وَمِن ذُرِّيَّتِهِمَا مُحۡسِنٞ وَظَالِمٞ لِّنَفۡسِهِۦ مُبِينٞ
“Ndipo tidamdalitsa iye ndi (mwana wake) Isihaqa; ndipo m’mbumba ya awiriwa mudapezeka abwino ndi odzichitira zoipa owonekera.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ
“Ndipo ndithu tidawachitira zabwino Mûsa ndi Haruna, (powapatsa uneneri ndi madalitso ambiri).
التفاسير العربية:
وَنَجَّيۡنَٰهُمَا وَقَوۡمَهُمَا مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ
“Ndipo tidawapulumutsa (awiriwa) ndi anthu awo ku vuto lalikulu.
التفاسير العربية:
وَنَصَرۡنَٰهُمۡ فَكَانُواْ هُمُ ٱلۡغَٰلِبِينَ
“Ndipo tidawathangata (powagonjetsera adani awo), ndipo iwo adali opambana.
التفاسير العربية:
وَءَاتَيۡنَٰهُمَا ٱلۡكِتَٰبَ ٱلۡمُسۡتَبِينَ
“Ndipo tidawapatsa (Mûsa ndi Haruna) buku losonyeza poyera (malamulo).
التفاسير العربية:
وَهَدَيۡنَٰهُمَا ٱلصِّرَٰطَ ٱلۡمُسۡتَقِيمَ
“Ndipo tidawaongolera ku njira yolunjika.
التفاسير العربية:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِمَا فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
“Ndiponso tidawasiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pawo).
التفاسير العربية:
سَلَٰمٌ عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ
“Mtendere ukhale pa Mûsa ndi Haruna!
التفاسير العربية:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
“Ndithu umu ndi momwe Ife timawalipirira ochita zabwino.
التفاسير العربية:
إِنَّهُمَا مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
“Ndithu awiriwa adali m’gulu la akapoio Athu okhulupirira.
التفاسير العربية:
وَإِنَّ إِلۡيَاسَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Ndipo ndithu Iliyasa ndi mmodzi wa atumiki.
التفاسير العربية:
إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَلَا تَتَّقُونَ
“(Kumbuka) pamene adanena kwa anthu ake: “Bwanji simuopa (Allah)?”
التفاسير العربية:
أَتَدۡعُونَ بَعۡلٗا وَتَذَرُونَ أَحۡسَنَ ٱلۡخَٰلِقِينَ
““Mukupembedza (fano lotchedwa) Ba’la ndi kusiya (kupembedza) Wabwino zedi mwa olenga onse.”
التفاسير العربية:
ٱللَّهَ رَبَّكُمۡ وَرَبَّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ
““Allah, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu akale?”
التفاسير العربية:

فَكَذَّبُوهُ فَإِنَّهُمۡ لَمُحۡضَرُونَ
“Koma adamtsutsa; ndithu iwo adzaonekera (ku Moto).
التفاسير العربية:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Kupatula akapolo a Allah amene ayeretsedwa (ndi Allah).
التفاسير العربية:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
“Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).
التفاسير العربية:
سَلَٰمٌ عَلَىٰٓ إِلۡ يَاسِينَ
“Mtendere ukhale pa Iliyasiin!
التفاسير العربية:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
“Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino.
التفاسير العربية:
إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
“Ndithu iye ndimmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira.
التفاسير العربية:
وَإِنَّ لُوطٗا لَّمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Ndithu Luti ndi mmodzi wa atumiki.
التفاسير العربية:
إِذۡ نَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ
“(Kumbuka) pamene tidampulumutsa iye ndi anthu ake onse.
التفاسير العربية:
إِلَّا عَجُوزٗا فِي ٱلۡغَٰبِرِينَ
“Kupatula nkhalamba yachikazi; idali mwa otsalira.
التفاسير العربية:
ثُمَّ دَمَّرۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ
“Kenako tidawaononga enawo (omwe adali oipa).
التفاسير العربية:
وَإِنَّكُمۡ لَتَمُرُّونَ عَلَيۡهِم مُّصۡبِحِينَ
“Ndithu inu (a mumzinda wa Makka) mumadutsa pa malo pawopo m’mawa,
التفاسير العربية:
وَبِٱلَّيۡلِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
“Ndi usiku. Kodi bwanji simuzindikira?
التفاسير العربية:
وَإِنَّ يُونُسَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Ndithu Yunusu ndi mmodzi wa atumiki.
التفاسير العربية:
إِذۡ أَبَقَ إِلَى ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ
“(Kumbuka) pamene adathawira m’chombo chodzazidwa (ndi katundu).
التفاسير العربية:
فَسَاهَمَ فَكَانَ مِنَ ٱلۡمُدۡحَضِينَ
“Choncho adachita mayere, ndipo adali m’gulu la omgwera (mayerewo).
التفاسير العربية:
فَٱلۡتَقَمَهُ ٱلۡحُوتُ وَهُوَ مُلِيمٞ
“Choncho nsomba idammeza uku ali wodzudzulidwa.
التفاسير العربية:
فَلَوۡلَآ أَنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلۡمُسَبِّحِينَ
“Kukadapanda kuti iye adali m’modzi mwa otamanda ndi kulemekeza Allah).
التفاسير العربية:
لَلَبِثَ فِي بَطۡنِهِۦٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
“Akadakhala m’mimba mwake mpaka tsiku loukitsidwa (zolengedwa ku imfa).
التفاسير العربية:
۞فَنَبَذۡنَٰهُ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ سَقِيمٞ
“Koma tidamponya pa gombe uku ali wodwala.
التفاسير العربية:
وَأَنۢبَتۡنَا عَلَيۡهِ شَجَرَةٗ مِّن يَقۡطِينٖ
“Ndipo tidammeretsera mmera wa mtundu wa nkhaka.
التفاسير العربية:
وَأَرۡسَلۡنَٰهُ إِلَىٰ مِاْئَةِ أَلۡفٍ أَوۡ يَزِيدُونَ
“Ndipo (atachira) tidamtuma ku anthu okwana zikwi zana limodzi (100,000) kapena kupambana apa.
التفاسير العربية:
فَـَٔامَنُواْ فَمَتَّعۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ حِينٖ
“Ndipo adakhulupirira (ndi kuvomereza ulaliki wake); choncho tidawapatsa chisangalalo kufikira nthawi (ya imfa yawo).
التفاسير العربية:
فَٱسۡتَفۡتِهِمۡ أَلِرَبِّكَ ٱلۡبَنَاتُ وَلَهُمُ ٱلۡبَنُونَ
“Choncho afunse: “Kodi Mbuye wako ndiye woyenera ana aakazi, ndipo iwo aamuna? (Pomwe iwo akabereka mwana wamkazi amanyansidwa naye)!”
التفاسير العربية:
أَمۡ خَلَقۡنَا ٱلۡمَلَـٰٓئِكَةَ إِنَٰثٗا وَهُمۡ شَٰهِدُونَ
“Kapena kuti tidalenga angelo kukhala akazi, iwo akuona?
التفاسير العربية:
أَلَآ إِنَّهُم مِّنۡ إِفۡكِهِمۡ لَيَقُولُونَ
“Chenjera ndi bodza lawolo, ndithu iwo akunena:
التفاسير العربية:
وَلَدَ ٱللَّهُ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ
““Allah wabereka.” Ndithu iwo ndi abodza.
التفاسير العربية:
أَصۡطَفَى ٱلۡبَنَاتِ عَلَى ٱلۡبَنِينَ
“Kodi Iye adasankha ana aakazi kusiya aamuna?
التفاسير العربية:

مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ
“Kodi nchiyani chakupezani (kuti muweruze mopanda chilungamo); nanga mukuweruza bwanji (zimenezi)?
التفاسير العربية:
أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
“Kodi bwanji simukumbukira, (mwaiwala zisonyezo Zake zodabwitsa ndi kupatukana kwake ndi zimenezo)?
التفاسير العربية:
أَمۡ لَكُمۡ سُلۡطَٰنٞ مُّبِينٞ
“Kapena inu muli ndi umboni woonekera (wochokera kumwamba)?
التفاسير العربية:
فَأۡتُواْ بِكِتَٰبِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
“Tabweretsani buku lanulo (momwe mwalembedwa zimenezi) ngati mukunena zoona.
التفاسير العربية:
وَجَعَلُواْ بَيۡنَهُۥ وَبَيۡنَ ٱلۡجِنَّةِ نَسَبٗاۚ وَلَقَدۡ عَلِمَتِ ٱلۡجِنَّةُ إِنَّهُمۡ لَمُحۡضَرُونَ
“Ndipo adapeka chibale pakati pa Iye (Allah) ndi ziwanda; (pomwe ziwanda nzobisika kwa iwo). Ndithu ziwanda zimadziwa kuti iwo osakhulupirira akaonekera (kwa Allah kuti aweruzidwe)!
التفاسير العربية:
سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ
“Walemekezeka Allah! Ndi kupatukana ndi zimene akumnamizira!
التفاسير العربية:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Koma akapolo a Allah oyeretsedwa (ali kutali ndi zimene akusimba osakhulupirirazi).
التفاسير العربية:
فَإِنَّكُمۡ وَمَا تَعۡبُدُونَ
“Ndithu inu (osakhulupirira) ndi zimene mukuzipembedza (kusiya Allah),
التفاسير العربية:
مَآ أَنتُمۡ عَلَيۡهِ بِفَٰتِنِينَ
“Ndi zimenezo simungamsokeretse aliyense.
التفاسير العربية:
إِلَّا مَنۡ هُوَ صَالِ ٱلۡجَحِيمِ
“Kupatula yemwe (Allah adadziwa kuti) ngolowa ku Jahannam.
التفاسير العربية:
وَمَامِنَّآ إِلَّا لَهُۥ مَقَامٞ مَّعۡلُومٞ
“Ndipo (angelo adanena): “Aliyense mwa ife ali ndi malo ake odziwika.”
التفاسير العربية:
وَإِنَّا لَنَحۡنُ ٱلصَّآفُّونَ
““Ndipo ndithu (ena mwa) ife ngondanda m’mizere (ya mapemphero nthawi zonse).”
التفاسير العربية:
وَإِنَّا لَنَحۡنُ ٱلۡمُسَبِّحُونَ
““Ndipo (ena mwa) ife ngolemekeza (Allah nthawi zonse ndi kumtamanda ndi kumpatula ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero wake).”
التفاسير العربية:
وَإِن كَانُواْ لَيَقُولُونَ
“Ndipo (osakhulupirira) ankati:
التفاسير العربية:
لَوۡ أَنَّ عِندَنَا ذِكۡرٗا مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ
““Tikadakhala ndi buku monga lomwe anthu akale adali nalo.”
التفاسير العربية:
لَكُنَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
““Tikadakhala akapolo a Allah, oyeretsedwa.”
التفاسير العربية:
فَكَفَرُواْ بِهِۦۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
“Koma (pamene lidawadzera bukulo), adalikana; choncho posachedwa adziwa (zotsatira zake).
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ سَبَقَتۡ كَلِمَتُنَا لِعِبَادِنَا ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Ndipo ndithu liwu lathu lidatsogola kwa akapolo athu otumidwa.
التفاسير العربية:
إِنَّهُمۡ لَهُمُ ٱلۡمَنصُورُونَ
“(Kuti) ndithu iwo ngopulumutsidwa.
التفاسير العربية:
وَإِنَّ جُندَنَا لَهُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ
“Ndipo ndithu asilikali Athu ndi opambana.
التفاسير العربية:
فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ حِينٖ
“Choncho, asiye kwa kanthawi kochepa.
التفاسير العربية:
وَأَبۡصِرۡهُمۡ فَسَوۡفَ يُبۡصِرُونَ
“Ndipo ingowayang’ana basi; posachedwapa aona!
التفاسير العربية:
أَفَبِعَذَابِنَا يَسۡتَعۡجِلُونَ
“Kodi chilango chathu akuchifulumizitsa?
التفاسير العربية:
فَإِذَا نَزَلَ بِسَاحَتِهِمۡ فَسَآءَ صَبَاحُ ٱلۡمُنذَرِينَ
“Choncho chikadzatsika pabwalo lawo, udzakhala mmawa woipa kwa ochenjezedwa!
التفاسير العربية:
وَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ حِينٖ
“Ndipo asiye kwa kanthawi kochepa.
التفاسير العربية:
وَأَبۡصِرۡ فَسَوۡفَ يُبۡصِرُونَ
“Ndipo ingowayang’ana basi; posachedwapa aona.
التفاسير العربية:
سُبۡحَٰنَ رَبِّكَ رَبِّ ٱلۡعِزَّةِ عَمَّا يَصِفُونَ
“Mbuye wako, Mwini ulemelero, wapatukana ndi zimene akumnamizira (osakhulupirira).
التفاسير العربية:
وَسَلَٰمٌ عَلَى ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Ndipo mtendere ukhale pa atumiki onse.
التفاسير العربية:
وَٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Ndipo kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الصافات
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق