للإطلاع على الموقع بحلته الجديدة

ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: المزمل   آية:

سورة المزمل - AL-Muzzammil

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمُزَّمِّلُ
E iwe wadzifunditsa (ndi nsalu!)
التفاسير العربية:
قُمِ ٱلَّيۡلَ إِلَّا قَلِيلٗا
Imilira usiku (upemphere), kupatula nthawi yochepa.
التفاسير العربية:
نِّصۡفَهُۥٓ أَوِ ٱنقُصۡ مِنۡهُ قَلِيلًا
Theka lake kapena chepetsa thekalo pang’ono (mpaka ufike chimodzi mwa zigawo zitatu za usiku).
التفاسير العربية:
أَوۡ زِدۡ عَلَيۡهِ وَرَتِّلِ ٱلۡقُرۡءَانَ تَرۡتِيلًا
Kapena wonjezapo (mpaka ufike zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za usiku;) ndipo werenga Qur’an mofatsa (lemba ndi lemba).
التفاسير العربية:
إِنَّا سَنُلۡقِي عَلَيۡكَ قَوۡلٗا ثَقِيلًا
Ife tikuvumbulutsira iwe (Mneneri) mawu olemera (yomwe ndi Qur’an).
التفاسير العربية:
إِنَّ نَاشِئَةَ ٱلَّيۡلِ هِيَ أَشَدُّ وَطۡـٔٗا وَأَقۡوَمُ قِيلًا
Ndithu kudzuka usiku ndi kuchita mapemphero kumalowelera (mu mtima) kwambiri, ndipo zoyankhula zake zimakhala zoongoka ndi zolunjika bwino (kuposa mapemphero amasana).
التفاسير العربية:
إِنَّ لَكَ فِي ٱلنَّهَارِ سَبۡحٗا طَوِيلٗا
Ndithu masana uli ndi zochitachita zambiri; (umatanganidwa ndi ntchito yauthenga; dzipatse danga usiku polimbika kupemphera).
التفاسير العربية:
وَٱذۡكُرِ ٱسۡمَ رَبِّكَ وَتَبَتَّلۡ إِلَيۡهِ تَبۡتِيلٗا
Ndipo tchula dzina la Mbuye wako (Amene adalenga ndi kulera zinthu), ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye.
التفاسير العربية:
رَّبُّ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَٱتَّخِذۡهُ وَكِيلٗا
(Iye ndiye) Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe; palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Mchiteni kukhala Mtetezi (wanu pa zinthu zanu zonse).
التفاسير العربية:
وَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَٱهۡجُرۡهُمۡ هَجۡرٗا جَمِيلٗا
Ndipo pirira pa zimene akunena. Ndipo apewe (ndi mtima wako); kupewa kwabwino.
التفاسير العربية:
وَذَرۡنِي وَٱلۡمُكَذِّبِينَ أُوْلِي ٱلنَّعۡمَةِ وَمَهِّلۡهُمۡ قَلِيلًا
Ndisiye Ine ndi otsutsa eni kupeza bwino; ndipo alekelere kanthawi kochepa.
التفاسير العربية:
إِنَّ لَدَيۡنَآ أَنكَالٗا وَجَحِيمٗا
Ndithudi, tili ndi mitundumitundu ya unyolo ndi Moto woyaka,
التفاسير العربية:
وَطَعَامٗا ذَا غُصَّةٖ وَعَذَابًا أَلِيمٗا
Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa.
التفاسير العربية:
يَوۡمَ تَرۡجُفُ ٱلۡأَرۡضُ وَٱلۡجِبَالُ وَكَانَتِ ٱلۡجِبَالُ كَثِيبٗا مَّهِيلًا
Tsiku limene nthaka ndi mapiri zidzagwedezeka; (kugwedezeka kwa mphamvu kotero kuti) mapiri adzakhala ngati mulu wa mchenga woyoyoka.
التفاسير العربية:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ رَسُولٗا شَٰهِدًا عَلَيۡكُمۡ كَمَآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ رَسُولٗا
Ndithu Ife takutumizirani Mthenga amene adzakhala mboni yanu (tsiku la chimaliziro; monga momwe tidamtumizira (Mûsa) kukhala Mtumiki kwa Firiauni.
التفاسير العربية:
فَعَصَىٰ فِرۡعَوۡنُ ٱلرَّسُولَ فَأَخَذۡنَٰهُ أَخۡذٗا وَبِيلٗا
Koma Firiauni adamnyoza Mtumikiyo; ndipo tidamulanga chilango chokhwima.
التفاسير العربية:
فَكَيۡفَ تَتَّقُونَ إِن كَفَرۡتُمۡ يَوۡمٗا يَجۡعَلُ ٱلۡوِلۡدَٰنَ شِيبًا
Kodi mungadzitchinjirize chotani ngati mukana (chilango cha) tsiku (lomwe) lidzachititsa ana kukhala ndi imvi?
التفاسير العربية:
ٱلسَّمَآءُ مُنفَطِرُۢ بِهِۦۚ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَفۡعُولًا
Thambo (pamodzi ndi mphamvu zake ndi kukula kwake), lidzang’ambika (tsiku limenelo) chifukwa cha kuopsa kwa tsikulo, lonjezo la (Allah) lidzakwaniritsidwa (palibe wolipinga).
التفاسير العربية:
إِنَّ هَٰذِهِۦ تَذۡكِرَةٞۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلًا
Ndithudi, ma Ayah awa (amene akunena za kuwopsa kwa Qiyâma) ndichikumbutso. Choncho amene akufuna (kuthandizika nawo) ayende panjira ya Mbuye wake (pokwaniritsa malamulo Ake ndi kuleka zoipa).
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني سورة: المزمل
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا - فهرس التراجم

ترجمها خالد إبراهيم بيتالا.

إغلاق