ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: البروج
آية:
 

البروج

وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡبُرُوجِ
“Ndikulumbilira thambo lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi zikuluzikulu).
Tanthauzo la ‘kufewetsa’ ndiko kuti Shariya ya Chisilamu (malamulo) siili yovuta kuyikwaniritsa monga momwe adalili malamulo a zipembedzo zoyamba. Ndipo ndi malamulo othandiza anthu onse, nthawi zonse ndi pamalo paliponse.
التفاسير العربية:
وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡمَوۡعُودِ
“Ndi tsiku lolonjezedwa (kuwerengedwa ndi kulipidwa),
التفاسير العربية:
وَشَاهِدٖ وَمَشۡهُودٖ
“Ndi woikira umboni, ndi woikiridwa umboni.
Tanthauzo la apa sikuti Mtumiki (s.a.w) alalikire pokhapokha waona kuti ulalikiwo uthandiza ayi, koma alalikire ndithu kaya kulalikirako kuthandiza kapena ayi, monga momwe zalongosolera Ayah zotsatirazi. Kuyankhula kotere, Arabu amakutcha “iktifa.”
التفاسير العربية:
قُتِلَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأُخۡدُودِ
“Atembeleredwa eni ngalande zamoto (zomwe adali kuwazunzira okhulupirira Allah, achimuna ndi achikazi).
“Wamavuto ambiri” apa, ndiko kuzunzika ndi matsoka. Allah akumutcha kafiri kuti “Wamavuto ambiri” chifukwa chakuti ali ndi mavuto padziko lino lapansi mpaka pa tsiku lachimaliziro. Mazunzo a tsiku lachimaliziro monga momwe tidziwira ndi chilango cha Moto chomwe chikumuyembekeza. Tsono “chilango cha padziko lapansi” ndiko kuti alibe chinthu chomutonthoza likampeza tsoka kapena vuto lililonse. Msilamu likampeza vuto amadzitonthoza ndi chikhulupiliro chake chakuti moyo wa munthu suwonjezeka ndiponso suchepa, ndikuti munthu amamwalira akamaliza moyo wake. Koma kafiri saganiza choncho; amangokukuta zala ndi kuwatukwana ma dokotala kuti sadziwa kanthu akadachita mwakutimwakuti munthuyo sakadafa. Msilamu kukampeza kusauka amadzitonthoza ndi kupilira pamodzi ndi chikhulupiliro choti “chilichonse chimachitika mchifuniro cha Allah.” Ndipo amakhala woyembekezera kuti lero kapena mawa, Allah amupatsa chisomo Chake. Koma anthu opanda chikhulupiliro amangoona kuti aponderezedwa; amayesetsa kufunafuna chuma mnjira zosayenera, ndipo akalephera amadzudzula uyu kapena kumenyana ndi uyu, ndipo amangodziona ngati wonyozeka kwambiri pa maso pa munthu wolemera.
Kotero kuti atauzidwa kuti amulambire wolemera uja kuti amupatse ndalama akhoza kuchita zotero. Ndipo tsiku lililonse njiru imamuondetsa; mwina amangodzipha monga momwe tionera masiku ano. Palibe mazunzo aakulu kuposa amenewa. Ngati muyang’ana ma Ayah 16 ndi 17 muona kuti akuthilira umboni pa zimene talongosolazi.
التفاسير العربية:
ٱلنَّارِ ذَاتِ ٱلۡوَقُودِ
“(Ngalande) za moto wankhuni (zambiri zomwe adali kuzikoleza ndikuotchera okhulupirira),
التفاسير العربية:
إِذۡ هُمۡ عَلَيۡهَا قُعُودٞ
“Pamene iwo adali chikhalire m’mphepete mwa ngalandezo.
التفاسير العربية:
وَهُمۡ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ شُهُودٞ
“Uku iwo akuyang’ana zomwe amawachitira okhulupirira, (pootchedwa ndi moto).
التفاسير العربية:
وَمَا نَقَمُواْ مِنۡهُمۡ إِلَّآ أَن يُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَمِيدِ
“Sadaone choipa chilichonse mwa iwo koma chifukwa choti adakhulupirira Allah mwini mphamvu zonse ndiponso mwini kuyamikidwa,
التفاسير العربية:
ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ شَهِيدٌ
“Yemwe ufumu wakumwamba ndi pansi ndiWake; ndipo Allah ndi mboni pachilichonse.
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلَّذِينَ فَتَنُواْ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ لَمۡ يَتُوبُواْ فَلَهُمۡ عَذَابُ جَهَنَّمَ وَلَهُمۡ عَذَابُ ٱلۡحَرِيقِ
“Ndithu amene ayesa mayeso okhulupirira achimuna ndi achikazi (pa chipembedzo chawo ndi mazunzo ndi chilango cha moto), pambuyo pake osalapa (pa zimenezi), adzalandira chilango cha Jahena ndiponso chilango cha moto wopsereza,
Tanthauzo lake ndikuti amene wadziyeretsa posiya kumuphatikiza Allah ndi zolengedwa ndi kumchimwira ndi machimo onse. Machimo amaletsa ulaliki wabwino kulowa mu mtima wa munthu. (yang’anani ndemanga ya 14 mu surat ya Al-Mutaffifin).
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّـٰلِحَٰتِ لَهُمۡ جَنَّـٰتٞ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡكَبِيرُ
“Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere (momwe) mitsinje ikuyenda pansi pake; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
التفاسير العربية:
إِنَّ بَطۡشَ رَبِّكَ لَشَدِيدٌ
“Ndithu kulanga kwa Mbuye wako (kwa anthu achinyengo), ndi kwaukali kwambiri.
Mawu akuti “wapambana amene wadziyeretsa ndi kumkumbukira Mbuye wake ndi kumapemphera,” ndiponso kuti: “ tsiku lachimaliziro ndilabwino kuposa dziko lapansi” mawuwa adanenedwanso m’mabuku oyamba; sikuti Qur’an ndiyo yayamba kunena zimenezi.
التفاسير العربية:
إِنَّهُۥ هُوَ يُبۡدِئُ وَيُعِيدُ
“Iye, (Mmodzi yekha) ndi amene adayambitsa zolengedwa ndiponso ndi Yemwe adzazibweze (pambuyo poonongeka);
التفاسير العربية:
وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلۡوَدُودُ
“Iye, ndi Wokhululuka (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Wokonda kwambiri (amene akumkonda ndi kumumvera),
التفاسير العربية:
ذُو ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡمَجِيدُ
“Mwini Arsh (Mpando wachifumu), (ndiponso) Wolemekezeka (mmene alili ndi mbiri Zake),
التفاسير العربية:
فَعَّالٞ لِّمَا يُرِيدُ
“Wochita zimene wafuna, (ndipo chimene wafuna sichikanika).
التفاسير العربية:
هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡجُنُودِ
“Kodi yakufika nkhani ya magulu a nkhondo,
التفاسير العربية:
فِرۡعَوۡنَ وَثَمُودَ
“Firiaun (Farawo) ndi Samudu, (ndi chilango chimene chidawapeza chifukwa chakulimbikira kwawo pa zinthu zopanda pake)?
التفاسير العربية:
بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي تَكۡذِيبٖ
“Koma amene sadakhulupirire ali mkati motsutsa basi.
التفاسير العربية:
وَٱللَّهُ مِن وَرَآئِهِم مُّحِيطُۢ
“Koma Allah awazinga mbali zonse.
التفاسير العربية:
بَلۡ هُوَ قُرۡءَانٞ مَّجِيدٞ
“Koma iyi ndi Qur’an yolemekezeka.
التفاسير العربية:
فِي لَوۡحٖ مَّحۡفُوظِۭ
“Yomwe idachokera mu ubawo (chisileti chachikulu) wotetezedwa (ndi manja alionse, osintha kanthu kapena kuonjezerapo).
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: البروج
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق